Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 40

Masomphenya a Ezekiele, kukonzekanso kwa Kachisi ndi mabwalo ake

1 Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mzindawo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.

2 M’masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m’dziko la Israele, nandikhalitsa paphiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mzinda kumwera.

3 Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m’dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye.

4 Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m’makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona.

5 Ndipo taonani, panali linga kunja kwake kwa nyumba ya Kachisi poizinga, ndi m’dzanja lake la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uliwonse mkono kudza chikhato; ndipo anayesa chimangidwecho kuchindikira kwake bango limodzi, ndi msinkhu wake bango limodzi.

6 Pamenepo anafika kuchipata choloza kum’mawa, nakwera pa makwerero ake; ndipo anayesa chiundo cha chipata, bango limodzi kuchindikira kwake; ndicho chiundo choyamba, bango limodzi.

7 Ndi chipinda cha alonda, chonse ncha bango limodzi m’litali mwake, ndi bango limodzi kupingasa kwake, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi chiundo cha chipata kumbali ya kukhonde la kuchipata m’katimo, bango limodzi.

8 Anayesanso khonde la kuchipata kumbali ya ku Kachisi, bango limodzi. Pamenepo anayesa khonde la kuchipata mikono isanu ndi itatu,

9 ndi mphuthu zake mikono iwiri; ndi khonde la kuchipata linaloza ku Kachisi.

10 Ndi zipinda za alonda za kuchipata cha kum’mawa ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, chakuno ndi chauko.

11 Ndipo anayesa kupingasa kwa chipata pakhoma pake mikono khumi, ndi utali wake wa chipata mikono khumi ndi itatu;

12 ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi chakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi chauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko.

13 Ndipo anayesa chipata kuyambira kutsindwi la chipinda cha alonda chimodzi, kufikira kutsindwi la chinzake, kupingasa kwake ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.

14 Anamanganso nsanamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa chipata lidafikira kunsanamira.

15 Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la chipata kufikira khomo la khonde la chipata m’katimo ndiko mikono makumi asanu.

16 Ndipo panali mazenera amkati okhazikika pazipinda ndi m’makoma a pakati pao, m’kati mwa chipata pozungulira ponse; momwemonso pamphuthu; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m’katimo, ndi pa nsanamirazo panali akanjedza.

17 Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.

18 Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wake wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.

19 Pamenepo anayesa kupingasa kwake kuyambira pakhomo pake pachipata chakunsi, kufikira kumaso kwake kwa bwalo la m’kati kunja kwake, mikono zana kum’mawa, ndi kumpoto.

20 Ndi chipata cha bwalo lakunja choloza kumpoto anachiyesa m’litali mwake, ndi kupingasa kwake zonse mikono zana.

21 Ndi zipinda zake ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, ndi makoma a pakati pake; ndi mphuthu zake zinali monga mwa muyeso wa chipata choyambacho, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

22 Ndi mazenera ake, ndi mphuthu zake, ndi akanjedza ake, anali monga mwa muyeso wa chipata choloza kum’mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi mphuthu zake zinali pakhomo.

23 Ndipo panali chipata cha bwalo lam’kati, chopenyana ndi chipata chinzake chakunja kumpoto, ndi cha kum’mawa; ndipo anayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata mikono zana.

24 Ndipo ananditsogolera kunka kumwera, ndipo taonani, panali chipata kumwera, nayesa makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake, monga mwa miyeso yomweyi.

25 Ndimo munali mazenera m’menemo, ndi m’mphuthu zake pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

26 Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi mphuthu zake kumaso kwake; ndi pa nsanamira zake chakuno ndi chauko panali akanjedza.

27 Ndipo panali chipata cha bwalo lam’kati chakuloza kumwera, nayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata kumwera mikono zana.

28 Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m’bwalo lam’kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;

29 ndi zipinda zake, ndi makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m’menemo, ndi m’mphuthu zake pozungulirapo; m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

30 Ndipo panali mphuthu pozungulirapo, m’litali mwake mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu.

31 Ndi mphuthu zake zinaloza kubwalo lakunja, ndi pa nsanamira zake panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu.

32 Ndipo analowa ndine m’bwalo lam’kati kuloza kum’mawa, nayesa chipata cha kum’mawa monga mwa miyeso yomweyi;

33 ndi zipinda zake, ndi makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m’menemo, ndi m’mphuthu zake pozungulirapo, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

34 Ndi mphuthu zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu.

35 Pamenepo anabwera nane kuchipata cha kumpoto, nachiyesa monga mwa miyeso yomweyi;

36 zipinda zake, makoma a pakati pake, ndi mphuthu zake; ndimo munali mazenera m’menemo pozungulirapo, m’litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.

37 Ndi nsanamira zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu.

38 Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi chitseko chake; pamenepo anatsuka nsembe yopsereza.

39 Ndipo m’khonde la pachipata munali magome awiri chakuno, ndi magome awiri chauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula.

40 Ndi kumbali ina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa chipata cha kumpoto, kunali magome awiri, ndi kumbali inzake ya kuchipata kunali magome awiri.

41 Magome anai chakuno, ndi magome anai chauko, kumbali ya chipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe.

42 Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m’litali mwake mkono ndi nusu, kupingasa kwake mkono ndi nusu, msinkhu wake mkono umodzi; pamenepo ankaika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera.

43 Ndi zichiri zangowe, chikhato m’litali mwake, zinamangika m’katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe.

44 Ndi kunja kwa chipata cha m’kati kunali tinyumba ta oimba m’bwalo lam’kati, kumbali ya chipata cha kumpoto; ndipo tinaloza kumwera, kena kumbali ya chipata cha kum’mawa kanaloza kumpoto.

45 Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwera nka ansembe odikira Kachisi.

46 Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.

47 Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m’litali mwake, ndi mikono zana kupingasa kwake, laphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.

48 Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko.

49 M’litali mwake mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi chakuno, ndi imodzi chauko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/40-8aec0ea6c80347fc88f71918f3079199.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 41

Kukonzekanso kwa Kachisi: malo opatulika kwambiri

1 Ndipo anadza nane ku Kachisi, nayesa nsanamira zake, kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko, ndiko kupingasa kwa chihema chija.

2 Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m’litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.

3 Nalowa m’katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri.

4 Anayesanso m’kati mwa Kachisi m’tsogolomo, m’litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m’mopatulika kwambiri.

5 Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kuchindikira kwake mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwake kwa zipinda za m’mphepete mikono inai, pozungulira pake ponse pa Kachisi.

6 Ndipo zipinda za m’mphepete zinasanjikizana china pa chinzake; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, ndipo zinalowa kukhoma lochirikiza zipinda za m’mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwe ndi khoma la nyumba.

7 Ndipo zipinda za m’mphepete zinakula m’kupingasa kwao, pozinga nyumba m’kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pake pa nyumba; motero kupingasa kwake kwa nyumba kunakula kumwamba kwake, momwemonso anakwera kuyambira chipinda chakunsi, kupita chapakati, kufikira cham’mwamba.

8 Ndinaonanso kuti kunyumba kunali chiunda pozungulira pake; maziko a zipinda za m’mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikulu.

9 Kuchindikira kwa khoma la kuzipinda za m’mphepete kunja kwake kunali mikono isanu; ndipo mpata wake unali malo olowera m’zipinda za m’mphepete za Kachisi.

10 Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pake ponse pa nyumba.

11 Ndi makomo a zipinda za m’mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwera; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwake pozungulira pake.

12 Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwake; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pake linali la mikono isanu kuchindikira kwake; ndi m’litali mwake mikono makumi asanu ndi anai.

13 Momwemo anayesa Kachisi m’litali mwake mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ake, mikono zana limodzi;

14 kupingasa kwake komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi kumpatawo kum’mawa, mikono zana limodzi.

15 Momwemo anayesa m’litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am’mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m’katimo, ndi makonde a kubwalo;

16 ziundo, ndi mazenera amkati okhazikika, ndi makonde am’mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa chiundo, otchinga ndi matabwa pozungulira pake, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;

17 kufikira kumwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m’katimo, ndi kunja kwake, ndi khoma lonse kwete m’kati ndi kunja, monga mwa miyeso.

18 Ndipo panalembedwapo ndiakerubindi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi aliyense anali ndi nkhope zake ziwiri;

19 nkhope ya munthu kuloza kukanjedza chakuno, ndi nkhope ya mwanawamkango kuloza kukanjedza chauko, momwemo m’nyumba monse pozungulira pake.

20 Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kachisi.

21 Mphuthu za Kachisi zinali zaphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a Kachisi.

22 Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m’litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.

23 Ndipo Kachisi ndi malo opatulika kwambiri anali nazo zitseko ziwiri.

24 Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, china chopatukana pa khomo lina china pa linzake.

25 Ndipo panalembedwa pamenepo pa zitseko za Kachisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakoma; ndipo panali matabwa ochindikira pakhomo pakhonde panja.

26 Ndipo panali mazenera amkati okhazikika, ndi akanjedza chakuno ndi chauko, kumbali zake za khonde; momwemonso pa zipinda za m’mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ochindikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/41-4de6676b8abb8d904adf0a2941a37301.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 42

Kukonzekanso kwa Kachisi: zipinda zopatulika

1 Pamenepo anatuluka nane kunka kubwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane kunyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.

2 Chakuno cha m’litali mwake mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwake mikono makumi asanu.

3 Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam’kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam’mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri.

4 Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwake mikono khumi m’kati mwake, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.

5 Ndipo zipinda zapamwamba zinachepa, pakuti makonde am’mwamba analanda pamenepo, chifukwa chake zinachepa koposa zapansi ndi zapakati m’nyumba yazipinda.

6 Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; chifukwa chake zam’mwambazo zinachepa koposa zakunsi ndi pakati kuyambira pansi.

7 Ndipo linga linali kunjalo, lolingana ndi nyumba yazipinda, kuloza kubwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m’litali mwake munali mikono makumi asanu.

8 Pakuti kupingasa kwake kwa nyumba yazipinda inali m’bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza kukhomo la Kachisi inali mikono zana limodzi.

9 Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum’mawa, poloweramo kuchoka kubwalo lakunja.

10 M’kuchindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, chakuno cha mpatawo, chakuno cha nyumba, panali nyumba yazipinda.

11 Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe njira ya kunyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m’litali mwake, momwemonso kupingasa kwake; ndi m’matulukiro mwake monse munali monga mwa machitidwe a inzake, ndi monga mwa makomo a inzake.

12 Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwera panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum’mawa polowamo.

13 Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.

14 Atalowa ansembe asatulukenso m’malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.

15 Atatha tsono kuyesa nyumba ya m’katimo, anatuluka nane njira ya chipata choloza kum’mawa nayesa bwalo pozungulira pake.

16 Anayesa mbali ya kum’mawa, ndi bango loyesera, mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.

17 Anayesa mbali ya kumpoto mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.

18 Anayesa mbali ya kumwera mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.

19 Anatembenukira kumbali ya kumadzulo, nayesa mikono mazana asanu ndi bango loyesera.

20 Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/42-233009028c0d1a808737e99e171f8ed2.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 43

Kukonzekanso kwa Kachisi: ulemerero wa Mulungu

1 Pamenepo anamuka nane kuchipata choloza kum’mawa,

2 ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum’mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.

3 Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mzinda; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.

4 Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa mu Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum’mawa.

5 Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m’kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

6 Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali mu Kachisi, naima nane munthu.

7 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,

8 ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga.

9 Ataye tsono chigololo chao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.

10 Wobadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israele Kachisiyu, kuti achite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wake.

11 Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite.

12 Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba paphiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi.

13 Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m’mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.

14 Ndi kuyambira kunsi kwake kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwake mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling’ono kufikira phaka lalikulu mikono inai; ndi kupingasa kwake mkono.

15 Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto paguwa padzatuluka nyanga zinai.

16 Ndi pamoto paguwa, m’litali mwake mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwake khumi ndi iwiri, laphwamphwa mbali zake zinai.

17 Ndi phaka, m’litali mwake mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi inai kumbali zake zinai; ndi mkuzi wake pozungulira pake mkono wa nusu, ndi tsinde lake mkono pozungulira pake, ndi makwerero ake aloza kum’mawa.

18 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;

19 Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang’ombe, akhale wa nsembe yauchimo.

20 Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.

21 Utengenso ng’ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pamalo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika.

22 Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng’ombeyo.

23 Utatha kuliyeretsa upereke mwanawang’ombe wopanda chilema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda chilema.

24 Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mchere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.

25 Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang’ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema.

26 Masiku asanu ndi awiri achite chotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule.

27 Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m’tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika paguwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/43-e77b8c498a090a08716e1505fe587e3d.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 44

Kukonzekanso kwa Kachisi utumiki wa Alevi ndi ansembe

1 Pamenepo anandibweza njira ya kuchipata chakunja cha malo opatulika choloza kum’mawa, koma chinatsekedwa.

2 Ndipo Yehova anati kwa ine, Chipata ichi chitsekeke, chisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israele walowerapo; chifukwa chake chitsekeke.

3 Koma kunena za kalonga, iye akhale m’menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi.

4 Atatero anamuka nane njira ya chipata cha kumpoto kukhomo kwa Kachisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.

5 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m’makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ake onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi matulukidwe ake onse a malo opatulika.

6 Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israele inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse;

7 popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m’mtima, osadulidwa m’thupi akhale m’malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.

8 Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m’malo anga opatulika.

9 Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m’mtima, wosadulidwa m’thupi, alowe m’malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele.

10 Koma Aleviwo anandichokera kunka kutaliwo, posokera Israele, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.

11 Koma adzakhala atumiki m’malo anga opatulika, akuyang’anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira mu Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira.

12 Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala chokhumudwitsa cha mphulupulu cha nyumba ya Israele, chifukwa chake ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.

13 Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira ntchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga zilizonse zopatulika kwambirizo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazichita.

14 Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa Kachisi kwa utumiki wake wonse, ndi zonse zakumachitika m’mwemo.

15 Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;

16 iwowa adzalowa m’malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.

17 Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam’kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m’zipata za bwalo la m’kati, ndi mu Kachisi.

18 Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m’chuuno mwao; asavale m’chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta.

19 Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m’zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.

20 Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingoyepula tsitsi la mitu yao.

21 Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa kubwalo la m’katimo.

22 Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.

23 Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.

24 Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitsemasabataanga.

25 Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.

26 Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.

27 Ndipo tsiku loti alowa m’malo opatulika, bwalo lam’kati, kutumikira m’malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova.

28 Ndipo adzakhala nacho cholowa; Ine ndine cholowa chao; musawapatsa cholandira chao mu Israele; Ine ndine cholandira chao.

29 Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.

30 Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.

31 Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi chilombo, ngakhale mbalame, kapena nyama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/44-c3408ef48043d94f88e9515dd8fa00ed.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 45

Chigawo cha dziko

1 Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m’litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m’malire ake onse pozungulira pake.

2 Kutengako malo opatulika akhale nayo mikono mazana asanu m’litali mwake, ndi mazana asanu kupingasa kwake, laphwamphwa pozungulira pake; ndi pabwalo pake poyera pozungulira pake mikono makumi asanu.

3 Ndipo kuyambira poyesedwapo uyese mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m’menemo ndimo mukhale malo opatulika, ndiwo opatulika, ndiwo opatulika kwambiri.

4 Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a kwa malo opatulika.

5 Ndipo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndilo gawo la Alevi, atumiki a Kachisi; likhale laolao la mizinda yokhalamo.

6 Ndipo dziko lake la mzindawo mulipereke la mikono zikwi zisanu kupingasa kwake, ndi mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, pa mbali ya chipereko chopatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israele.

7 Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lake mbali ina ndi mbali inzake ya chipereko chopatulika, ndi ya dziko la mzinda, kutsogolo kwa chipereko chopatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mzinda, mbali ya kumadzulo, ndi mbali ya kum’mawa; ndi m’litali mwake mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira kumalire a kumadzulo kufikira malire a kum’mawa.

8 M’dzikomo ili lidzakhala lakelake mu Israele; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israele monga mwa mafuko ao.

9 Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m’zolowa zao, ati Ambuye Yehova.

10 Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona.

11 Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.

12 Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu.

13 Chopereka muchipereke ndicho limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele;

14 ndi gawo lonenedwa la mafuta, la bati wa mafuta, ndilo limodzi la magawo khumi la bati, kulitapa pa kori; ndiwo mabati khumi, ndiwo homeri; pakuti mabati khumi ndiwo homeri;

15 ndimwanawankhosammodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wochokera kumadimba a Israele, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwachitira chotetezera, ati Ambuye Yehova.

16 Anthu onse a m’dziko azipereka chopereka ichi chikhale cha kalonga wa mu Israele.

17 Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pamasabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.

Nsembe ya pa mwezi woyamba

18 Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwanawang’ombe wopanda chilema, ndipo uyeretse malo opatulika.

19 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo, naupake pa mphuthu za Kachisi, ndi pangodya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za chipata cha bwalo lam’kati.

20 Tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo uchitire momwemo aliyense wolakwa ndi wopusa; motero muchitire Kachisiyo chomtetezera.

Za Paska

21 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, muzichitaPaska, chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda chotupitsa.

22 Ndipo tsiku lomwelo kalonga adzikonzere yekha ndi anthu onse a m’dziko ng’ombe, ikhale ya nsembe yauchimo.

23 Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng’ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo.

24 Nakonze nsembe yaufa, kung’ombe kukhale efa; ndi kunkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta.

25 Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, pachikondwerero, achite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yauchimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/45-6758b70849ec027f07a9050379b004e6.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 46

Za Sabata ndi pokhala mwezi

1 Atero Ambuye Yehova, Pa chipata cha bwalo lam’kati choloza kum’mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito; koma tsiku laSabatapatsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.

2 Ndipo kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipatacho, kunja kwake, naime kunsanamira ya chipata; ndipo ansembe akonze nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, nalambire iye kuchiundo cha chipata; atatero atuluke; koma pachipata pasatsekedwe mpaka madzulo.

3 Ndipo anthu a m’dziko alambire pa chitseko cha chipata ichi pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi.

4 Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo anaankhosa asanu ndi mmodzi opanda chilema, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema,

5 ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.

6 Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwanawang’ombe wopanda chilema, ndi anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda chilema;

7 ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng’ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.

8 Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipata, natuluke njira yomweyo.

Malangizo a popereka nsembe

9 Koma pofika anthu a m’dziko pamaso pa Yehova m’zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m’tsogolo mwake.

10 Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi.

11 Ndi pazikondwerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng’ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.

12 Ndipo kalonga akapereka chopereka chaufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa chipata choloza kum’mawa; ndipo azipereka nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, monga umo amachitira tsiku la Sabata; atatero atuluke; ndipo atatuluka, wina atseke pachipata.

13 Uziperekanso kwa Yehova mwanawankhosa wa chaka chimodzi akhale nsembe yopsereza wopanda chilema, tsiku ndi tsiku, m’mawa ndi m’mawa, uzimpereka.

14 Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m’mawa ndi m’mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusakaniza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.

15 Momwemo aperekemwanawankhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m’mawa ndi m’mawa, nsembe yopsereza kosalekeza.

Mapatsidwe a kalonga

16 Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wake wina wamwamuna mphatso idzakhala cholowa chake, ndicho chaochao cha ana ake, cholowa chao.

17 Koma akapatsa mphatso yotenga kucholowa chake kwa wina wa anyamata ake, idzakhala yake mpaka chaka cha ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma cholowa chake chikhale cha ana ake.

18 Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m’dziko lake.

Pophikira ansembe

19 Pamenepo anapita ndi ine podzera paja pali kumbali ya chipata kunka kuzipinda zopatulika za ansembe zoloza kumpoto; ndipo taonani, kunali malo chauko kumadzulo.

20 Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziotcha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu.

21 Pamenepo anatulukira nane kubwalo lakunja, nandipititsa kungodya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m’ngodya monse munali bwalo.

22 M’ngodya zinai za bwalo munali mabwalo ochingika, m’litali mwake mikono makumi anai, kupingasa kwake makumi atatu; awa anai m’ngodyazi analingana muyeso wake.

23 Ndipo panali maguwa pozungulira pake m’menemo, pozungulira pake pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pake pozungulirapo.

24 Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a Kachisi aziphikira nsembe ya anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/46-9abfe4c06f586fbedee22c91dca9184e.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 47

Masomphenya a madzi otuluka mu Kachisi watsopano

1 Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa chiundo cha nyumba kum’mawa; pakuti khomo lake la nyumba linaloza kum’mawa; ndipo madzi anatsika kuchokera pansi pa nyumba, kumbali ya lamanja lake, kumwera kwa guwa la nsembe.

2 Pamenepo anatuluka nane njira ya kuchipata cha kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kunka kuchipata chakunja, njira ya kuchipata choloza kum’mawa; ndipo taonani, panatuluka madzi pa mbali ya kulamanja.

3 Potuluka munthuyu kunka kum’mawa ndi chingwe choyesera m’dzanja lake, anayesa mikono chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m’kakolo.

4 Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m’maondo. Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m’chuuno.

5 Atatero anayesanso chikwi chimodzi, ndipo mtsinje wosakhoza kuoloka ine, popeza madzi adakula, madzi osambira, mtsinje wosaoloka munthu.

6 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, waona ichi? Nanditenga kundikwezetsa ndi mtsinje.

7 Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija.

8 Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa atulukira kudera la kum’mawa, natsikira kuchidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ake.

9 Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zochuluka zidzakhala ndi moyo kulikonse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzachuluka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m’nyanja; ndipo kulikonse mtsinje ufikako zilizonse zidzakhala ndi moyo.

10 Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.

11 Koma pali matope ake ndi zithaphwi zake sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamchere.

12 Ndipo kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya, osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ake atumphuka m’malo opatulika; ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa.

Malire a dziko

13 Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.

14 Ndipo mudzakhala nalo cholowa chanu wina ndi mnzake yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani cholowa chanu.

15 Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku Nyanja Yaikulu, kutsata njira ya ku Hetiloni, kufikira polowera ku Zedadi;

16 Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere-Hatikoni ndiwo kumalire a Haurani.

17 Ndi malire ochokera kunyanja ndiwo Hazar-Enoni, kumalire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati. Ndiyo mbali ya kumpoto.

18 Ndi mbali ya kum’mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum’mawa. Ndiyo mbali ya kum’mawa.

19 Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.

20 Ndi mbali ya kumadzulo ndiyo Nyanja Yaikulu, kuyambira malire a kumwera kufikira pandunji polowera ku Hamati. Ndiyo mbali ya kumadzulo.

21 Motero mudzigawire dziko ili monga mwa mafuko a Israele.

22 Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m’dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.

23 Ndipo kudzatero kuti kufuko kumene mlendo akhalako kumeneko mumpatse cholowa chake, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/47-d2b89dd125db9b72a1cf11dd99369f0f.mp3?version_id=1068—

Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 48

Magawidwe a dziko mwa mafuko khumi ndi awiri

1 Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum’mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.

2 Ndi m’malire a Dani, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Asere, limodzi.

3 Ndi m’malire a Asere, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafutali, limodzi.

4 Ndi m’malire a Nafutali, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.

5 Ndi m’malire a Manase, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efuremu, limodzi.

6 Ndi m’malire a Efuremu, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.

7 Ndi m’malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.

8 Ndi m’malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale chopereka muchipereke, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake, ndi m’litali mwake lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pake.

9 Chopereka muchipereke kwa Yehova chikhale cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, ndi zikwi khumi kupingasa kwake.

10 Ndipo m’mwemo mudzakhala chopereka chopatulika cha ansembe kumpoto, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, ndi kumadzulo mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kum’mawa mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kumwera mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake; ndi pakati pake pakhale malo opatulika a Yehova.

11 Chidzakhala cha ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israele, ndi muja anasokera Alevi.

12 Ndi chiperekocho chikhale chao chotapa pa chopereka cha dziko, ndicho chopatulika kwambiri pa malire a Alevi.

13 Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m’litali mwake monse ndimo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi khumi.

14 Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti lili lopatulika la Yehova.

15 Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m’kupingasa kwake, chakuno cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za ntchito wamba za mzinda, za kumangapo zapabusa; ndi mzinda ukhale pakati pake.

16 Ndi miyeso yake ndi iyi: mbali ya kumpoto, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwera, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kum’mawa, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu.

17 Ndipo mzindawo ukhale ndi busa lake; kumpoto mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwera mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum’mawa mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mikono mazana awiri mphambu makumi asanu.

18 Ndipo madera otsalawo m’litali mwake alingane ndi chopereka chopatulika, ndicho mikono zikwi khumi kum’mawa, ndi mikono zikwi khumi kamadzulo, alingane ndi chopereka chopatulika; ndi zipatso zake zikhale za chakudya cha iwo ogwira ntchito m’mzinda.

19 Iwo ogwira ntchito m’mzinda mwa mafuko onse a Israele alimeko.

20 Chopereka chonse ndicho mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m’litali mwake, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake; muchipereke chopereka chopatulika chaphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mzindawo.

21 Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali ina ndi ina ya chopereka chopatulika ndi ya dziko la mzinda, kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu za chopereka kumalire a kum’mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kumalire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo cha kalonga; ndipo chopereka chopatulika ndi malo opatulika a Kachisi zidzakhala pakati pake.

22 Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mzinda, ndiwo a pakati pa magawo ake a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.

23 Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira kumbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi.

24 Ndi kumalire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.

25 Ndi kumalire a Simeoni kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.

26 Ndi kumalire a Isakara, kuyambira mbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi.

27 Ndi kumalire a Zebuloni, kuyambira kumbali ya kum’mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.

28 Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu.

29 Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israele ndi kuchita maere, likhale cholowa chao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.

30 Ndipo malekezero a mzinda ndi awa: mbali ya kumpoto ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu;

31 ndi zipata za mzinda zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israele; zipata zitatu kumpoto: chipata chimodzi cha Rubeni, chipata chimodzi cha Yuda, chipata chimodzi cha Levi;

32 ndi ku mbali ya kum’mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Yosefe, chipata chimodzi cha Benjamini, chipata chimodzi cha Dani;

33 ndi kumbali ya kumwera ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Simeoni, chipata chimodzi cha Isakara, chipata chimodzi cha Zebuloni;

34 kumbali ya kumadzulo mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zake zitatu: chipata cha Gadi, chipata chimodzi cha Asere, chipata chimodzi cha Nafutali.

35 Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mzindawo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/48-8f0b9a7bb7686811b4fd4df6c6de6cb7.mp3?version_id=1068—