Ejipito adzagonjetsedwa ndi mfumu ya ku Babiloni
1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo!
3 Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo yaamitundu.
4 Ndi lupanga lidzadzera Ejipito, ndi mu Kusi mudzakhala kuwawa kwakukulu, pakugwa ophedwa mu Ejipito; ndipo adzachotsa aunyinji ake, ndi maziko ake adzagadamuka.
5 Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Libiya, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.
6 Atero Yehova, Iwonso ochirikiza Ejipito adzagwa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatsika, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene adzagwa m’kati mwake ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.
7 Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yopasuka.
8 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto mu Ejipito, naonongeka onse akumthandiza.
9 Tsiku ilo mithenga idzatuluka pamaso panga m’zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukulu pakati pao, monga tsiku la Ejipito, pakuti taona, likudza.
10 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Ejipito ndi dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni.
11 Iye ndi anthu ake pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Ejipito malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.
12 Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m’dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse zili m’mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndachinena.
13 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.
14 Ndipo ndidzasandutsa Patirosi labwinja, ndi kuika moto mu Zowani, ndi kukwaniritsa maweruzo mu No.
15 Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika penipeni pa Ejipito, ndi kulikha aunyinji a No.
16 Ndipo ndidzaika moto mu Ejipito; Sini adzamva kuwawa kwakukulu, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.
17 Anyamata a Oni ndi Pibeseti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.
18 Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m’menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.
19 Motero ndidzakwaniritsa maweruzo mu Ejipito, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
20 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi woyamba, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
21 Wobadwa ndi munthu iwe, ndathyola dzanja laFaraomfumu ya Aejipito, ndipo taona, silinamangidwe kuti lipole, kulikulunga ndi nsalu, kulilimbitsa ligwire lupanga.
22 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Farao mfumu ya Aejipito, ndidzathyola manja ake, lolimba ndi lothyokalo, ndi kutayitsa lupanga m’dzanja lake.
23 Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m’maiko.
24 Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m’dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.
25 Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni, nalitambasula iye padziko la Ejipito.
26 Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa mwa amitundu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/30-42693f5ca2cabb372e2a4682a75d345d.mp3?version_id=1068—