Categories
EZARA

EZARA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Nkhani imene ili mu buku la

Ezara

ikutsatana ndi nkhani za m’mabuku awiri a

Mbiri

, ndipo ikulongosola za kubwerera kwa ena mwa Ayuda kuchokera ku Babiloni kumene anatengedwa ngati akapolo. Bukuli likufotokozanso za kubwezeretsedwa kwa moyo ndi chipembedzo mu Yerusalemu. Nkhanizi zaperekedwa m’magawo atatu: Gawo loyamba ndi la gulu la Ayuda amene anabwerera kuchokera ku Babiloni potsatira lamulo limene adapereka Kirusi amene anali mfumu ya Persiya. Gawo lachiwiri likunena za kumangidwanso ndi kupatulidwa kwa Kachisi komanso za kukonzedwanso kwa chipembedzo cha Mulungu ku Yerusalemu. Gawo lachitatu likunena za gulu lina la Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu motsogozedwa ndi Ezara, amene anali katswiri pa Malamulo a Mulungu, ndipo iye anawathandiza anthu kuti akonzenso chikhalidwe ndi moyo wa chipembedzo pofuna kusunga miyambo ya chipembedzo mu Israele.

Za mkatimu

Gulu loyamba la anthu libwerera

1.1—2.70

Kachisi amangidwanso napatulidwa

3.1—6.22

Ezara abwerera ndi anthu ena

7.1—10.44

Categories
EZARA

EZARA 1

Mulungu apangira Kirusi alole Ayuda abwere kwao kukamanga Kachisi

1 Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m’kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,

2 Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam’mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba muYerusalemu, ndiwo mu Yuda.

3 Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.

4 Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndisiliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.

5 Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.

6 Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.

Kirusi abweza zipangizo za Kachisi

7 Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa mu Yerusalemu, ndi kuziika m’nyumba ya milungu yake;

8 zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.

9 Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;

10 zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.

11 Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/1-d4bfde8d5f981aaca5e1f02e9ea7e505.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 2

Maina a Ayuda obwera ku Yerusalemu ndi Zerubabele

1 Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m’ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka kuYerusalemundi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:

2 ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:

3 ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

4 Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

5 Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu.

6 Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri.

7 Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

8 Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu.

9 Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

10 Ana a Bani, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.

11 Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

12 Ana a Azigadi, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi awiri ndi awiri.

13 Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi.

14 Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

15 Ana a Adini, mazana anai mphambu makumi asanu kudza anai.

16 Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu.

17 Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu.

18 Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

19 Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

20 Ana a Gibara, makumi asanu ndi anai mphambu asanu.

21 Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.

22 Anthu a ku Netofa, makumi asanu mphambu asanu ndi mmodzi.

23 Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

24 Ana a Azimaveti, makumi anai mphambu awiri.

25 Ana a Kiriyati-Arimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.

26 Ana a Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

27 Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

28 Anthu a ku Betele ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

29 Ana a Nebo, makumi asanu mphambu awiri.

30 Ana a Magabisi, zana limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

31 Ana a Elamu wina, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

32 Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.

33 Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza asanu.

34 Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

35 Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.

36 Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.

37 Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

38 Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.

39 Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.

40 Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.

41 Oimba: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

42 Ana a odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, onse pamodzi ndiwo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anai.

43 Antchito a m’kachisi: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,

44 ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni,

45 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu,

46 ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani,

47 ana a Gidele, ana a Gahara, ana a Reaya,

48 ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu,

49 ana a Uza, ana a Paseya, ana a Besai,

50 ana a Asina, ana a Meunimu, ana a Nefisimu,

51 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,

52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,

53 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,

54 ana a Neziya, ana a Hatifa.

55 Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,

56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele,

57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Ami.

58 Antchito onse a m’kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.

59 Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele:

60 ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

61 Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.

62 Awa anafunafuna maina ao m’buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe chao, koma osawapeza; potero anachotsedwa ku ntchito ya nsembe monga odetsedwa.

63 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndiUrimu ndi Tumimu.

64 Msonkhano wonse pamodzi ndiwo wa zikwi makumi anai ndi awiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,

65 osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri.

66 Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu;

67 ngamirazao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.

68 Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake.

69 Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina yasilivazikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi.

70 Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m’kachisi, anakhala m’midzi mwao, ndi Aisraele onse m’midzi mwao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/2-07bda91fdb85273b79feb6b054be8301.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 3

Limangidwa guwa la nsembe

1 Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri, ana a Israele ali m’midzimo, anthuwo anasonkhana ngati munthu mmodzi kuYerusalemu.

2 Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m’chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.

3 Ndipo anakhazika guwa la nsembe patsinde pake chifukwa cha kuopa iwo anthu a m’maikomo; nakwezera Yehova nsembe zopsereza pamenepo, nsembe zopsereza zam’mawa ndi zamadzulo.

4 Nachitachikondwerero cha Misasamonga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;

5 atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu.

6 Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova.

7 Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.

Aika maziko a Kachisi

8 Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang’anire ntchito ya nyumba ya Yehova.

9 Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ake ndi abale ake, Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, kuyang’anira ogwira ntchito m’nyumba ya Mulungu, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi.

10 Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israele.

11 Ndipo anathirirana mang’ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.

12 Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau aakulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera.

13 Potero anthu sanazindikire phokoso la kufuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anafuulitsa kwakukulu, ndi phokoso lake lidamveka kutali.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/3-4480ab26f86bbfc901605439f8579809.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 4

Asamariya aneneza Ayuda omanga Kachisi kwa Ahasuwero

1 Atamva tsono adani a Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israele Kachisi,

2 anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno.

3 Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira.

4 Pamenepo anthu a m’dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga,

5 nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Kirusi mfumu ya Persiya, mpaka ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.

6 Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala mu Yuda ndi muYerusalemu.

7 Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.

8 Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi, wakutsutsana naye Yerusalemu motere:

9 nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,

10 ndiamitunduotsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m’mizinda ya Samariya, ndi m’dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate.

11 Zolembedwa m’kalatayo anazitumiza kwa Arita-kisereksesi mfumu: ife akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, tikupatsani moni.

12 Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mzinda uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake.

13 Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mzinda uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m’njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu.

14 Popeza tsono timadya mchere wa m’nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; chifukwa chake tatumiza ndi kudziwitsa mfumu,

15 kuti afunefune m’buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m’buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mzinda uwu ndi mzinda wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m’menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mzinda uwu.

16 Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mzindawu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.

Mfumu iwaletsa asamange Kachisi

17 Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala mu Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Moni, ndi nthawi yakuti.

18 Kalatayo mwatitumizira anandiwerengera momveka.

19 Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mzinda uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe, ndi kuti akachitamo mpanduko ndi kudziyendera.

20 Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m’njira.

21 Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mzinda uwu, mpaka ndidzalamulira ndine.

22 Chenjerani mungadodomepo, chidzakuliranji chisauko cha kusowetsa mafumu?

23 Pamenepo atawerenga malemba a kalata ya mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.

24 Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/4-82a07869b218914d2883af4d0ac3377e.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 5

Zerubabele ndi Yesuwa apitirira kumanga Kachisi

1 Ndipo aneneri, Hagaimneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi muYerusalemu; m’dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.

2 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.

3 Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

4 Nanena naonso motere, Maina ao a anthu omanga chimangidwe ichi ndiwo ayani?

5 Koma diso la Mulungu wao linali pa akulu a Ayuda, ndipo sanawaletse mpaka mlandu unamdzera Dariusi, nabweza mau a mlanduwo m’kalata.

Tatenai awaneneza kwa Dariusi

6 Zolembedwa m’kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,

7 anatumiza kalata kwa iyeyo m’menemo munalembedwa motere, kwa Dariusi mfumu, mtendere wonse.

8 Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, ndi kuikidwa mitengo pamakoma, ndipo inachitika mofulumira ntchitoyi, ndipo inayenda bwino m’dzanja mwao.

9 Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

10 Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera.

11 Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi, tilikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikulu ya Israele.

12 Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni Mkaldeya, amene anaononga nyumba ino, natenga anthu ndende kunka nao ku Babiloni.

13 Koma chaka choyamba cha Kirusi mfumu ya Babiloni, Kirusi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.

14 Ndiponso zipangizo za golide ndisilivaza nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;

15 nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike mu Kachisi ali mu Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pake.

16 Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu ili mu Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano ilinkumangidwa, koma siinatsirizike.

17 Ndipo tsono chikakomera mfumu, munthu asanthule m’nyumba ya chuma cha mfumu ili komwe ku Babiloni, ngati nkuterodi, kuti Kirusi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa chinthuchi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/5-90c7b1f322227b04a56b144ddac47a5b.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 6

Dariusi anenetsa kuti Kachisi amangidwe

1 Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m’nyumba ya mabuku mosungira chuma mu Babiloni.

2 Napeza ku Ekibatana m’nyumba ya mfumu m’dera la Mediya, mpukutu, ndi m’menemo munalembedwa motere, chikhale chikumbutso:

3 Chaka choyamba cha Kirusi mfumu, analamulira Kirusi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu kuYerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ake, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu ndi limodzi;

4 ndi mipambo itatu ya miyala yaikulu, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndalama zochokera kunyumba ya mfumu.

5 Ndi zipangizo za golide ndisilivaza nyumba ya Mulungu, zimene anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kunka nazo ku Babiloni, azibwezere, nabwere nazo ku Kachisi ali ku Yerusalemu, chilichonse ku malo ake; naziike m’nyumba ya Mulungu.

6 Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;

7 lekani ntchito iyi ya Mulungu, osaivuta; kazembe wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amange nyumba iyi ya Mulungu pambuto pake.

8 Ndilamuliranso za ichi muzichitira akulu awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko chuma cha mfumu, ndicho msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawachedwetse.

9 Ndipo zosowa zao, anaang’ombe, ndi nkhosa zamphongo, ndi anaankhosa, zikhale nsembe zopsereza za Mulungu wa Kumwamba; tirigu, mchere, vinyo, mafuta, monga umo adzanena ansembe ali ku Yerusalemu, ziperekedwe kwa iwo tsiku ndi tsiku, zisasoweke;

10 kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.

11 Ndalamuliranso kuti aliyense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwake, namkweze, nampachike pomwepo; niyesedwa dzala nyumba yake chifukwa cha ichi;

12 ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lake komweko agwetse mafumu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akutulutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu. Ine Dariusi ndalamulira, chichitike msanga.

13 Pamenepo Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariusi adatumiza mau, anachita momwemo chofulumira.

14 Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwamneneriHagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya.

15 Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lachitatu la mwezi wa Adara, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Dariusi mfumu.

Apereka Kachisi nachita Paska

16 Ndipo ana a Israele, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera.

17 Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng’ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, anaankhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisraele onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwake kwa mafuko a Israele.

18 Naika ansembe m’magawo mwao, ndi Alevi m’magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m’buku la Mose.

19 Ndipo ana a ndende anachitaPaskatsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba.

20 Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paska chifukwa cha ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.

21 Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa chaamitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza,

22 nasungachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsamasiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/6-a5cf11d4c1eaac589bb46fa40243126e.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 7

Arita-kisereksesi atumiza Ezara ku Yerusalemu akonzenso chipembedzo cha Yehova

1 Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,

2 mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi,

3 mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraiyoti,

4 mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,

5 mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.

6 Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m’chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.

7 Nakweranso kunka kuYerusalemuena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m’kachisi, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.

8 Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.

9 Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku loyamba la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake.

10 Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa mu Israele malemba ndi maweruzo.

11 Malemba a kalatayo mfumu Arita-kisereksesi anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ake kwa Israele, ndi awa:

12 Arita-kisereksesi mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weniweni, ndi pa nthawi yakuti.

13 Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, mu ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.

14 Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m’dzanja lako,

15 ndi kumuka nazosilivandi golide, zimene mfumu ndi aphungu ake, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israele, mokhala mwake muli mu Yerusalemu,

16 pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m’dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;

17 m’mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng’ombe, nkhosa zamphongo, anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka paguwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.

18 Ndipo chilichonse chidzakomera iwe ndi abale ako kuchita nazo siliva ndi golide zotsala, ichi muchite monga mwa chifuniro cha Mulungu wanu.

19 Ndipo zipangizozo akupatsa za utumiki wa nyumba ya Mulungu wako, uzipereka pamaso pa Mulungu wa ku Yerusalemu.

20 Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zochokera kunyumba ya chuma cha mfumu.

21 Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira;

22 mpaka matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zana limodzi, ndi mitsuko ya vinyo zana limodzi, ndi mitsuko ya mafuta zana limodzi, ndi mchere wosauwerenga.

23 Chilichonse Mulungu wa Kumwamba achilamulire chichitikire mwachangu nyumba ya Mulungu wa Kumwamba; pakuti padzakhaliranji mkwiyo pa ufumu wa mfumu ndi ana ake?

24 Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, antchito a m’kachisi, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.

25 Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m’dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.

26 Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m’dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m’kaidi.

27 Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,

28 nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/7-451eec82469f172e328a43118122e93a.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 8

Maina a opita ndi Ezara. Ulendo wao mpaka Yerusalemu

1 Ndipo akulu a nyumba za makolo ndi awa, ndi chibadwidwe cha iwo okwera nane limodzi kuchokera ku Babiloni, pokhala mfumu Arita-kisereksesi, ndi ichi:

2 wa ana a Finehasi, Geresomo; wa ana a Itamara, Daniele; wa ana a Davide, Hatusi.

3 Wa ana a Sekaniya, wa ana a Parosi, Zekariya; ndi pamodzi naye, powawerenga monga mwa chibadwidwe chao, amuna zana limodzi mphambu makumi asanu.

4 Wa ana a Pahatimowabu, Eliehoenai mwana wa Zerahiya; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri.

5 Wa ana a Sekaniya, mwana wa Yahaziele; ndi pamodzi naye amuna mazana atatu.

6 Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu.

7 Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri.

8 Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaele; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu.

9 Wa ana a Yowabu, Obadiya mwana wa Yehiyele; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu.

10 Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosofiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi.

11 Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu.

12 Ndi wa ana a Azigadi, Yohanani mwana wa Hakatani; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi.

13 Ndi a ana otsiriza a Adonikamu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeiyele, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi.

14 Ndi wa ana a Bigivai, Utai ndi Zakuri, ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi awiri.

15 Ndipo ndinawasonkhanitsa ku mtsinje wopita ku Ahava, ndi komweko tinakhala m’misasa masiku atatu; ndipo ndinapenyerera anthu ndi ansembe, koma sindinapezapo wa ana a Levi.

16 Pamenepo ndinatumiza munthu kuitana Eliyezere, Ariyele, Semaya, ndi Elinatani, ndi Yaribu, ndi Elinatani, ndi Natani, ndi Zekariya, ndi Mesulamu, ndiwo akulu; ndi Yoyaribu ndi Elinatani, ndiwo aphunzitsi.

17 Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkulu, kumalo dzina lake Kasifiya; ndinalonganso m’kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ake antchito a m’kachisi, pamalo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.

18 Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israele; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ake ndi abale ake khumi mphambu asanu ndi atatu;

19 ndi Hasabiya, ndi pamodzi naye Yesaya wa ana a Merari, abale ake ndi ana ao makumi awiri;

20 ndi antchito a m’kachisi, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, antchito a m’kachisi mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo otchulidwa maina.

21 Pamenepo ndinalalikira chosala komweko kumtsinje wa Ahava, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang’ono athu, ndi chuma chathu chonse.

22 Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya.

23 Momwemo tinasala ndi kupempha ichi kwa Mulungu wathu; nativomereza Iye.

24 Pamenepo ndinapatula akulu a ansembe khumi ndi awiri, ndiwo Serebiya, Hasabiya, ndi abale ao khumi pamodzi nao,

25 ndi kuwayeserasiliva, ndi golide, ndi zipangizo, ndizo chopereka cha kwa nyumba ya Mulungu wathu, chimene mfumu, ndi aphungu ake, ndi akalonga ake, ndi Aisraele onse anali apawa, adapereka.

26 Ndipo ndinawayesera m’dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi,

27 ndi zikho zagolide makumi awiri za madariki chikwi chimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golide.

28 Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golide, ndizo chopereka chaufulu cha kwa Yehova Mulungu wa makolo anu.

29 Mukhale maso ndi kuzisunga mpaka muziyesera pamaso pa ansembe aakulu ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo a Israele kuYerusalemu, m’zipinda za nyumba ya Yehova.

30 Potero ansembe ndi Alevi analandira kulemera kwake kwa siliva ndi golide ndi zipangizo, abwere nazo ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.

31 Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m’dzanja la mdani ndi wolalira m’njira.

32 Ndipo tinafika ku Yerusalemu ndi kukhalako masiku atatu.

33 Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m’nyumba ya Mulungu wathu, m’dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi;

34 zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwake konse kunalembedwa nthawi yomweyo.

35 Otengedwa ndende, atatuluka m’ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng’ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.

36 Ndipo napereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/8-21896ee61cfeea48a89c0f6bcf80a020.mp3?version_id=1068—

Categories
EZARA

EZARA 9

Mwankhawa Ezara apempherera Ayuda okwatira achilendo kwa Mulungu

1 Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israele, ndi nsembe, ndi Alevi, sanadzilekanitse ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito, ndi Aamori.

2 Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.

3 Ndipo pakumva mau awa ndinang’amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m’kudabwa.

4 Nandisonkhanira aliyense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israele, chifukwa cha kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m’kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.

5 Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m’kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong’ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;

6 ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.

7 Chiyambire masiku a makolo athu tapalamula kwakukulu mpaka lero lino; ndi chifukwa cha mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m’dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kuchitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.

8 Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m’malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m’maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang’ono mu ukapolo wathu.

9 Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga mu Yuda ndi muYerusalemu.

10 Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ichi? Pakuti tasiya malamulo anu,

11 amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale cholowa chanu ndilo dziko lodetsedwa mwa chidetso cha anthu a m’maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga ina kufikira nsonga inzake ndi utchisi wao.

12 Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m’dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse.

13 Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;

14 kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatirana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?

15 Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m’kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/9-4c62b7e4e238101916a660e46ebb7b22.mp3?version_id=1068—