Categories
ESTERE

ESTERE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za Estere, mtsikana wina wachiyuda, amene ankakonda kwambiri anthu a mtundu wake, naonetsa kulimba mtima kwake pothandiza kuwapulumutsa Ayudawo kwa adani ao. Lifotokozanso za chiyambi chake komanso tanthauzo la chikondwerero cha Chiyuda chotchedwa Purimu.

Za mkatimu

Estere asankhidwa kuti akhale mfumukazi kudziko la Persiya

1.1—2.23

Hamani apanga chiwembu chofuna kuwonongeratu fuko la Ayuda

3.1—5.14

Hamani atsutsidwa naphedwa

6.1—7.10

Ayuda agonjetsa adani ao

8.1—10.3

Categories
ESTERE

ESTERE 1

Madyerero a Ahasuwero

1 Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.

2 Masiku ajawo, pokhala Ahasuwero pa mpando wa ufumu wake uli m’chinyumba cha ku Susa,

3 chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake,

4 pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.

5 Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m’chinyumba cha ku Susa, aakulu ndi aang’ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku chinyumba cha mfumu;

6 panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.

7 Nawapatsa chakumwa m’zomwera zagolide, zomwerazo nzosiyanasiyana, ndi vinyo wachifumu anachuluka, monga mwa ufulu wa mfumu.

8 Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yake motero, kuti achite monga momwe akhumba aliyense.

Vasiti akana kuoneka kumadyerero

9 Vasiti yemwe, mkazi wamkulu, anakonzera akazi madyerero m’nyumba yachifumu ya mfumu Ahasuwero.

10 Tsiku lachisanu ndi chiwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahasuwero,

11 abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pa mfumu ndi korona wachifumu, kuonetsa anthu ndi akulu kukoma kwake; popeza anali wokongola maonekedwe ake.

12 Koma Vasiti mkazi wamkuluyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wake unatentha m’kati mwake.

Vasiti achotsedwa

13 Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m’tsogolo, mfumu inkatero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,

14 a pafupi naye ndiwo Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Persiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba mu ufumu.

15 Anati, Tidzachitanji naye mkazi wamkulu Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanachite chomuuza mfumu Ahasuwero mwa adindo?

16 Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m’maiko onse a mfumu Ahasuwero.

17 Pakuti machitidwe awa a mkazi wamkuluyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahasuwero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pake, koma sanadze iye.

18 Inde tsiku lomwelo akazi a akulu a Persiya ndi Mediya, atamva machitidwe a mkazi wamkuluyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi chipeputso ndi mkwiyo zidzachuluka.

19 Chikakomera mfumu, atuluke mau achifumu pakamwa pake, nalembedwe m’malamulo a Apersiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahasuwero; ndi mfumu aninkhe chifumu chake kwa mnzake womposa iye.

20 Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka mu ufumu wake wonse, (pakuti ndiwo waukulu), akazi onse adzachitira amuna ao ulemu, aakulu ndi aang’ono.

21 Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inachita monga mwa mau a Memukana,

22 natumiza makalata kumaiko onse a mfumu, kudziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi kumtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, kuti mwamuna aliyense akhale wamkulu m’nyumba yakeyake, nawabukitse monga mwa chinenedwe cha anthu a mtundu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/1-a9c8d8271fc50291d3b8b867bd30a7e5.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 2

Ahasuwero akwatira Estere

1 Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahasuwero, anakumbukira Vasiti, ndi chochita iye, ndi chomlamulidwira.

2 Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;

3 ndi mfumu aike oyang’anira m’maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m’chinyumba cha ku Susa, m’nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;

4 ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkulu m’malo mwa Vasiti. Ndipo chinthuchi chinamkonda mfumu, nachita chomwecho.

5 Panali Myuda m’chinyumba cha ku Susa, dzina lake ndiye Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini;

6 uyu anatengedwa ndende kuYerusalemu, pamodzi ndi andende anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adamtenga ndende.

7 Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wake wamng’ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wake ndi mai wake, Mordekai anamtenga akhale mwana wake.

8 Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lake, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m’chinyumba cha ku Susa, awasunge Hegai, anamtenga Estere yemwe, alowe m’nyumba ya mfumu, amsunge Hegai wosunga akazi.

9 Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m’nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m’malo okometsetsa m’nyumba ya akazi.

10 Estere sadawulule mtundu wake ndi chibale chake; pakuti Mordekai adamuuzitsa kuti asadziwulule.

11 Ndi Mordekai akayendayenda tsiku ndi tsiku kubwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi chimene chidzamchitikira.

12 Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta amure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

13 Ndipo namwali aliyense analowa kwa mfumu motero, zilizonse anafuna anampatsa zochokera m’nyumba ya akazi, alowe nazo kunyumba ya mfumu.

14 Madzulo ake analowamo, nabwera m’mawa mwake kunka kunyumba yachiwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi aang’ono a mfumu; iyeyu sanalowenso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumtchula dzina lake, ndiko.

15 Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng’ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.

16 Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.

17 Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pake, namuyesa mkazi wamkulu m’malo mwa Vasiti.

18 Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akulu ake onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.

19 Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yachiwiri Mordekai anali wa m’bwalo la mfumu.

20 Estere sadawulule chibale chake kapena mtundu wake, monga Mordekai adamuuza; popeza Estere anachita mau a Mordekai monga m’mene analeredwa naye.

Mordekai awulula chiwembu chofuna kupha mfumu

21 Masiku awa pokhala Mordekai wa m’bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.

22 Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai.

23 Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napachikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anachilemba m’buku la mbiri pamaso pa mfumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/2-6467998a4abb2f90d80dbbdaafe464df.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 3

Mordekai akana kugwadira Hamani

1 Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye.

2 Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m’chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira.

3 Ndipo anyamata a mfumu okhala m’chipata cha mfumu anati kwa Mordekai, Ulakwiranji pa lamulo la mfumu?

4 Kunali tsono, pomalankhula naye tsiku ndi tsiku, osawamvera iye, anauza Hamani, kuona ngati mlandu wa Mordekai udzakoma; popeza iye adawauza kuti ali Myuda.

5 Ndipo Hamani, pakuona kuti Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira, mtima wake unadzala mkwiyo.

6 Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala mu ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.

Hamani apangira mfumu kuti uphedwe mtundu wonse wa Ayuda

7 Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, chaka chakhumi ndi chiwiri cha mfumu Ahasuwero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.

8 Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahasuwero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m’maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; chifukwa chake mfumu siiyenera kuwaleka.

9 Chikakomera mfumu, chilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente asilivazikwi khumi m’manja a iwo akusunga ntchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m’nyumba za chuma cha mfumu.

10 Ndipo mfumu inavula mphete yake pa chala chake, naipereka kwa Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda.

11 Ndipo mfumu idati kwa Hamani, siliva akhale wako, ndi anthu omwe; uchite nao monga momwe chikukomera.

12 Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang’anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m’dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.

13 Ndipo anatumiza makalata ndi amtokoma kumaiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha.

14 Mau a cholembedwacho, ndiwo kuti lichitike lamulo m’maiko onse, analalikidwa kwa anthu onse, kuti akonzekeretu tsiku lomwelo.

15 Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m’chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mzinda wa Susa unadodoma.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/3-eea79e6d2ebfc5a02b411ef5478a965a.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 4

Mordekai adandaulira Estere anenere Ayuda kwa mfumu

1 Koma podziwa Mordekai zonse zidachitikazi, Mordekai anang’amba zovala zake, navala chiguduli ndi mapulusa, natuluka pakati pa mzinda, nafuula, nalira kulira kwakukulu ndi kowawa,

2 nafika popenyana ndi chipata cha mfumu; popeza sanathe munthu kulowa kuchipata cha mfumu wovala chiguduli.

3 Ndi m’maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro aakulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m’chiguduli ndi mapulusa ambiri.

4 Ndipo anamwali a Estere ndi adindo ake anadza, namuuza; ndi mkazi wamkulu anawawidwa mtima kwambiri, natumiza chovala aveke Mordekai, ndi kumchotsera chiguduli chake; koma sanachilandire.

5 Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Mordekai, kuti adziwe ichi nchiyani ndi chifukwa chake ninji.

6 Natuluka Hataki kunka kwa Mordekai kukhwalala la mzinda linali popenyana ndi chipata cha mfumu.

7 Ndipo Mordekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wake wa ndalama adati Hamani adzapereka m’nyumba ya chuma cha mfumu pa Ayuda, kuwaononga.

8 Anampatsanso chitsanzo cha lamulo lolembedwa adalibukitsa mu Susa, kuwaononga, achionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ake kwa iye.

9 Nadza Hataki, namuuza Estere mau a Mordekai.

10 Pamenepo Estere ananena ndi Hataki, namtuma akauze Mordekai, ndi kuti,

11 Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m’maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m’katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.

12 Ndipo anamuuza Mordekai mau a Estere.

13 Koma Mordekai anawauza ambwezere mau Estere, kuti, Usamayesa m’mtima mwako kuti udzapulumuka m’nyumba ya mfumu koposa Ayuda ena onse.

14 Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi.

15 Pamenepo Estere anati ambwezere mau Mordekai,

16 Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.

17 Napita Mordekai, nachita monga mwa zonse adamlamulira Estere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/4-cb926a6a03089c2fc13f8f1f62a652de.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 5

Estere alowa kwa mfumu nampempha iye ndi Hamani azidya naye

1 Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m’bwalo la m’kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m’nyumba yachifumu, pandunji polowera m’nyumba.

2 Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m’bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m’dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.

3 Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

4 Ndipo Estere anati, Chikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.

5 Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, achitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere.

6 Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

7 Nayankha Estere, nati, Pempho langa ndi kufuna kwanga ndiko,

8 ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu.

Hamani amangitsa popachika Mordekai

9 Ndipo Hamani anatuluka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Mordekai kuchipata cha mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Mordekai.

10 Koma Hamani anadziletsa, namuka kwao, natumiza munthu kukatenga mabwenzi ake, ndi Zeresi mkazi wake.

11 Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.

12 Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkulu sanalole mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.

13 Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndilikuona Mordekai Myudayo alikukhala kuchipata cha mfumu.

14 Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/5-e7a4c7f6f71f6e042737b74502072b00.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 6

Ahasuwero aona chifukwa cha kuchitira Mordekai ulemu

1 Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.

2 Napeza mudalembedwa kuti Mordekai adawulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.

3 Niti mfumu, Anamchitira Mordekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamchitire kanthu.

4 Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m’bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupachika Mordekai pamtengo adaukonzeratu.

5 Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe.

6 Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amchitire chiyani munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwake, Ndaniyo mfumu ikondwera kumchitira ulemu koposa ine?

7 Nati Hamani kwa mfumu, Munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu,

8 amtengere chovala chachifumu amachivala mfumu, ndi kavalo amakwerapo mfumu, naike korona wachifumu pamutu pake,

9 napereke chovala ndi kavalo m’dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, naveke nacho munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m’khwalala la m’mzinda, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.

10 Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga chovala ndi kavalo monga umo wanenera, nuchitire chotero Mordekai Myudayo, wokhala pa chipata cha mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.

11 Ndipo Hamani anatenga chovala ndi kavalo, naveka Mordekai, namuyendetsa pa kavalo m’khwalala la m’mzinda, nafuula pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.

12 Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake.

13 Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.

14 Akali chilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kunka naye kumadyerero adawakonzera Estere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/6-27c76f2781e0383f3aede7a9a2152c0f.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 7

Hamani aululidwa napachikidwa

1 Motero inadza mfumu ndi Hamani kumwa naye mkazi wamkulu Estere.

2 Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.

3 Nayankha mkazi wamkulu Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo chikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;

4 pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu a mtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule. Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala chete; chinkana wosautsa sakadatha kubwezera kusowa kwa mfumu.

5 Pamenepo mfumu Ahasuwero inalankhula, niti kwa mkazi wamkulu Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wake kuti azitero?

6 Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkulu.

7 Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa.

8 Nibwera mfumu kumunda wa maluwa wa kuchinyumba kulowanso m’nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkulu pamaso panga m’nyumba? Potuluka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.

9 Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m’nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo.

10 Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/7-efd0056250ce2adcc1446396331db1d9.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 8

Ahasuwero avomereza pempho la Estere, Ayuda napulumuka

1 Tsiku lomwelo mfumu Ahasuwero anampatsa mkazi wamkulu Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda. Nafika Mordekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za chibale chake.

2 Ndipo mfumu inavula mphete yake adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Mordekai. Ndi Estere anaika Mordekai akhale woyang’anira nyumba ya Hamani.

3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda.

4 Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.

5 Nati, Chikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, ndi kumuyenera mfumu, ngatinso ndimchititsa kaso, alembe makalata kusintha mau a chiwembu cha Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m’maiko onse a mfumu;

6 pakuti ndidzapirira bwanji pakuchiona choipa chilikudzera a mtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuchiona chionongeko cha fuko langa?

7 Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.

8 Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m’dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata yolembedwa m’dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kuyisintha.

9 Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.

10 Ndipo analembera m’dzina la mfumu Ahasuwero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza makalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro achifumu, obadwa mosankhika;

11 m’menemo mfumu inalola Ayuda okhala mu mzinda uliwonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ao aang’ono, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,

12 tsiku lomwelo, m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.

13 Chitsanzo chake, cha lemboli, chakuti abukitse lamulo m’maiko onse, chinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera chilango adani ao.

14 Natuluka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro achifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m’chinyumba cha ku Susa.

15 Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mzinda wa Susa unafuula ndi kukondwera.

16 Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi chimwemwe, ndi ulemu.

17 Ndi m’maiko monse, ndi m’mizinda yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m’dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/8-9660cb13c0716d9bd2b13721bc40e932.mp3?version_id=1068—

Categories
ESTERE

ESTERE 9

Ayuda awapha adani ao

1 Mwezi wakhumi ndi chiwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, mau a mfumu ndi lamulo lake ali pafupi kuchitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwachitira ufumu, koma chinasinthika; popeza Ayuda anachitira ufumu iwo odana nao;

2 pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m’mizinda mwao, m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.

3 Ndipo akalonga onse a maikowo, ndi akazembe, ndi ziwanga, ndi iwo ochita ntchito ya mfumu, anathandiza Ayuda; popeza kuopsa kwa Mordekai kudawagwera.

4 Pakuti Mordekai anali wamkulu m’nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m’maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.

5 Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna.

6 Ndipo m’chinyumba cha ku Susa Ayuda anakantha, naononga amuna mazana asanu.

7 Napha Parasadata, ndi Dalifoni, ndi Asipata,

8 ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata,

9 ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaizata,

10 ana aamuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande zofunkha.

11 Tsiku lomwelo anabwera nacho kwa mfumu chiwerengo cha iwo ophedwa m’chinyumba cha ku Susa.

12 Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m’chinyumba cha ku Susa, ndi ana aamuna khumi a Hamani; nanga m’maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika.

13 Nati Estere, Chikakomera mfumu, alole Ayuda okhala mu Susa achite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana aamuna khumi a Hamani apachikidwe pamtengo.

14 Ndipo mfumu inati azichita motero, nalamulira mu Susa, napachikidwa ana aamuna khumi a Hamani.

15 Ndipo Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu mu Susa; koma sanalande zofunkha.

16 Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m’maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalande zofunkha.

17 Chinachitika ichi tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana tsiku lakhumi ndi chitatu ndi lakhumi ndi chinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi chisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19 Chifukwa chake Ayuda a kumidzi, okhala m’mizinda yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

Masungidwe a tsiku la Purimu

20 Ndipo Mordekai analembera izi, natumiza makalata kwa Ayuda onse okhala m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, a kufupi ndi a kutali,

21 kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi chinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chisanu lomwe, chaka ndi chaka,

22 ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23 Ndipo Ayuda anavomereza kuchita monga umo adayambira, ndi umo Mordekai adawalembera;

24 popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda chiwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

25 koma pofika mlanduwo kwa mfumu, iye adalamula polemba kalata kuti chiwembu choipa cha Hamani adachipangira Ayuda chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana ake aamuna apachikidwe pamtengo.

26 Chifukwa chake anatcha masikuwaPurimu, ndilo dzina la ulawo. Momwemo, chifukwa cha mau onse a kalatayo, ndi izi adaziona za mlanduwo, ndi ichi chidawadzera,

27 Ayuda anakhazikitsa ichi, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, chingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, chaka ndi chaka;

28 ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mzinda uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.

29 Pamenepo Estere mkazi wamkulu mwana wa Abihaili, ndi Mordekai Myuda, analembera molamulira, kukhazikitsa kalata iyi yachiwiri ya Purimu.

30 Natumiza iye makalata kwa Ayuda onse, kumaiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahasuwero, ndiwo mau a mtendere ndi choonadi;

31 kukhazikitsa masiku awa a Purimu m’nyengo zao, m’mene Mordekai Myuda ndi mkazi wamkulu Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kufuula kwao.

32 Ndipo kunena kwake kwa Estere kunakhazikitsa mau awa a Purimu; ndipo kunalembedwa m’buku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/9-0405c021758e9aec8ee5ce6d062431b6.mp3?version_id=1068—