Mapatulidwe a ansembe
1 Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng’ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,
2 ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.
3 Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng’ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.
4 Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo lachihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m’madzi.
5 Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am’kati, ndi mwinjiro waefodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m’chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;
6 ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.
7 Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.
8 Ndipo ubwere nao ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya am’kati.
9 Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m’chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna.
10 Ndipo ubwere nayo ng’ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa ng’ombe yamphongoyo.
11 Nuphe ng’ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako.
12 Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng’ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.
13 Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.
14 Koma nyama ya ng’ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.
15 Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
16 Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira.
17 Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m’ziwalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziwalo zake, ndi pamutu pake.
18 Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.
19 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
20 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.
21 Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.
22 Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam’mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;
23 ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;
24 ndipo uike zonsezi m’manja a Aroni, ndi m’manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
25 Pamenepo uzilandire m’manja mwao, ndi kuzipsereza paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.
26 Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.
27 Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam’mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;
28 ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.
29 Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake aamuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala;
30 mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m’malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m’chihema chokomanako kutumikira m’malo opatulika.
31 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nyama yake m’malo opatulika.
32 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mudengu, pa khomo la chihema chokomanako.
33 Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.
34 Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m’mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi.
35 Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake aamuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.
36 Nukonze ng’ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.
37 Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.
Nsembe ya masiku onse
38 Koma izi ndizo uzikonza paguwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.
39 Mwanawankhosawina ukonze m’mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo;
40 ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.
41 Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m’mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
42 Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.
43 Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.
44 Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.
45 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele, ndi kukhala Mulungu wao.
46 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/29-93258c3d3ed363f80d63cca94d51cbc5.mp3?version_id=1068—