Categories
EKSODO

EKSODO 10

Chozizwitsa cha 8: Dzombe

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwaFarao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao;

2 ndi kuti ufotokozere m’makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

3 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;

4 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m’dziko lako;

5 ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo;

6 ndipo lidzadzaza m’nyumba zako, ndi m’nyumba za anyamata ako onse, ndi m’nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.

7 Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?

8 Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo yani?

9 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng’ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.

10 Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana aang’ono anu mumuke; chenjerani pakuti pali choipa pamaso panu.

11 Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna aakulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao.

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako padziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere padziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m’dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.

13 Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum’mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum’mawa inadza nalo dzombe.

14 Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.

15 Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m’dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsale chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba zakuthengo, m’dziko lonse la Ejipito.

16 Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.

17 Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi ino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa ino yokha.

18 Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova.

19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.

20 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele amuke.

Chozizwitsa cha 9: Mdima

21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima padziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika.

22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m’dziko lonse la Ejipito masiku atatu;

23 sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m’nyumba zao.

24 Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu aang’ononso.

25 Koma Mose anati, Mutipatsenso m’dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu.

26 Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.

27 Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.

28 Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.

29 Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/10-fd3a81d3b2320a4b8f2bd04da4aad980.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 11

Chozizwitsa chakhumi: Imfa ya ana oyamba kubadwa

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengeraFarao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.

2 Lankhula tsopano m’makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasilivandi zagolide.

3 Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m’dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

4 Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka Ine kunka pakati pa Aejipito;

5 ndipo ana oyamba a m’dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

6 Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m’dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere.

7 Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israele ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aejipito ndi Aisraele.

8 Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m’dziko la Ejipito.

10 Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m’dziko lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/11-7657d8605d4477b167ba808b09b09743.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 12

Kuikidwa kwa Paska

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m’dziko la Ejipito, ndi kuti,

2 Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa chaka.

3 Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yensemwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.

4 Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.

5 Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

6 Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.

7 Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m’nyumba zimene adyeramo.

8 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.

9 Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake.

10 Ndipo musasiyako kufikira m’mawa; koma yotsalira kufikira m’mamawayo muipsereze ndi moto.

11 Ndipo muziidya chotero: okwinda m’chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m’dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiyePaskawa Yehova.

12 Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m’dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.

13 Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.

14 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.

15 Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m’nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.

16 Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.

17 Ndipo muzisungachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m’dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m’mibadwo yanu, lemba losatha.

18 Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake.

19 Chisapezeke chotupitsa m’nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m’dziko.

20 Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa.

21 Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.

22 Ndipo muzitenga mpukutu wahisope, ndi kuuviika m’mwazi uli m’mbale, ndi kupaka mwazi uli m’mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m’mawa.

23 Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aejipito; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woononga alowe m’nyumba zanu kukukanthani.

24 Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.

25 Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m’dziko limene Yehova adzakupatsani, monga analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku.

26 Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani?

27 Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.

28 Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.

Ana oyamba kubadwa aphedwa

29 Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m’dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba waFaraowakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam’nsinga ali m’kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.

30 Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu mu Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m’mwemo.

31 Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israele; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.

32 Muka nazoni zoweta zanu zazing’ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso.

33 Ndipo Aejipito anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m’dziko; pakuti anati, Tili akufa tonse.

34 Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m’zovala zao pa mapewa ao.

35 Ndipo ana a Israele anachita monga mwa mau a Mose; napempha Aejipito zokometsera zasiliva, ndi zagolide, ndi zovala.

36 Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito, ndipo sanawakanize. Ndipo anawafunkhira Aejipito.

Ana a Israele atuluka mu Ejipito

37 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.

38 Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng’ombe, zoweta zambirimbiri.

39 Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.

40 Ndipo kukhala kwa ana a Israele anakhala mu Ejipito ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu.

41 Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko la Ejipito.

42 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m’dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao.

Lamulo la Paska

43 Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;

44 koma kapolo wa mwini aliyense, wogula ndi ndalama, utamdula, ndipo adyeko.

45 Mlendo kapena wolembedwa ntchito asadyeko.

46 Audye m’nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake.

47 Gulu lonse la Israele lizichita ichi.

48 Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.

49 Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.

50 Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.

51 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m’dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/12-90a3e3ea3dfeac75a69656724a3a3d4e.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 13

Ana oyamba kubadwa apatulidwira Yehova

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti,

2 Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.

3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m’nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.

4 Mutuluka lero lino mwezi wa Abibu.

5 Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m’dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.

6 Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova;

7 Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisaoneke kwanu m’malire ako onse.

8 Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.

9 Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m’kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.

10 Chifukwa chake uzikasunga lemba ili pa nyengo yake chaka ndi chaka.

11 Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m’dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo,

12 kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.

13 Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndimwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.

14 Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m’nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;

15 ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m’dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.

16 Ndipo chizikhala ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chapamphumi pakati pamaso ako; pakuti Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.

Ulendo wonka ku Nyanja Yofiira

17 Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m’mbuyo kunka ku Ejipito.

18 Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m’dziko la Ejipito okonzeka.

19 Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israele ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawasiya kuno.

20 Ndipo anachokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a chipululu.

21 Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m’njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;

22 sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/13-2900ce8a6a33b640315e7c160fc7c743.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 14

Farao alondola Aisraele

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti,

2 Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m’mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.

3 NdipoFaraoadzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera.

4 Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.

5 Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?

6 Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake;

7 napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse.

8 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.

9 Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.

10 Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.

11 Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m’chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?

12 Si awa mauwo tinalankhula nanu mu Ejipito ndi kuti, Tilekeni, kuti tigwirire ntchito Aejipito? Pakuti kutumikira Aejipito kutikomera si kufa m’chipululu ai.

13 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.

14 Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.

Aisraele aoloka pouma

15 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.

16 Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.

17 Ndipo Ine, taonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aejipito, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.

18 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.

19 Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;

20 nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizane ndi unzake usiku wonse.

21 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.

22 Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

23 Ndipo Aejipito anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magaleta ake, ndi apakavalo ake.

24 Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m’moto ndi m’mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.

25 Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.

Aejipito amizidwa m’nyanja

26 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aejipito, magaleta ao, ndi apakavalo ao.

27 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m’mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m’kati mwa nyanja.

28 Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m’nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.

29 Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.

30 Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m’manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m’mphepete mwa nyanja.

31 Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/14-b37eeef7335ffce47cc6c0b169cd0ccb.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 15

Nyimbo yolemekeza Mulungu

1 Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti,

Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu;

kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja.

2 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga,

ndipo wakhala chipulumutso changa;

ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza;

ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.

3 Yehova ndiye wankhondo;

dzina lake ndiye Yehova.

4 Magaleta aFaraondi nkhondo yake anawaponya m’nyanja;

ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.

5 Nyanja inawamiza;

anamira mozama ngati mwala.

6 Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,

dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.

7 Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu;

mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.

8 Ndipo ndi mpumo wa m’mphuno mwanu madzi anaunjikika,

mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu;

zozama zinalimba m’kati mwa nyanja.

9 Mdani anati,

Ndiwalondola, ndiwapeza,

ndidzagawa zofunkha;

ndidzakhuta nao mtima;

ndidzasolola lupanga langa,

dzanja langa lidzawaononga.

10 Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;

anamira m’madzi aakulu ngati mtovu.

11 Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?

Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera,

woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?

12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja,

nthaka inawameza.

13 Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola;

mwamphamvu yanu mudawalondolera

njira yakunka pokhala panu poyera.

14 Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira;

kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya.

15 Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa;

agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu;

okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.

16 Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera;

padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala;

kufikira apita anthu anu, Yehova,

kufikira apita anthu amene mudawaombola.

17 Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu,

pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova,

malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.

18 Yehova adzachita ufumu nthawi yonka muyaya.

19 Pakuti akavalo a Farao analowa m’nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m’nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja.

20 Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m’dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang’ombe.

21 Ndipo Miriyamu anawayankha,

Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu;

kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja.

Madzi a ku Mara

22 Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m’chipululu cha Suri; nayenda m’chipululu masiku atatu, osapeza madzi.

23 Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a pa Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara.

24 Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani?

25 Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m’madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;

26 ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.

27 Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pamadziwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/15-32bbeed59877acc9f6ceee96ed122791.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 16

Zinziri ndi mana

1 Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m’chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m’dziko la Ejipito.

2 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m’chipululu;

3 nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m’dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m’chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m’chilamulo changa kapena iai.

5 Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi.

6 Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m’dziko la Ejipito;

7 ndi m’mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?

8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m’mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.

9 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.

10 Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12 Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m’mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

13 Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m’mawa padagwa mame pozungulira tsasa.

14 Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang’ono kamphumphu, kakang’ono ngati chipale panthaka.

15 Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.

16 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m’hema mwake.

17 Ndipo ana a Israele anatero, naola wina wambiri, wina pang’ono.

18 Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalire, ndi iye amene adaola pang’ono sunamsowe; yense anaola monga mwa njala yake.

19 Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m’mawa.

20 Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m’mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.

21 Ndipo anauola m’mawa ndi m’mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.

22 Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.

23 Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma,Sabatalopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m’mawa.

24 Ndipo anausunga kufikira m’mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkhe, ndipo sunagwe mphutsi.

25 Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.

26 Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.

27 Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeze.

28 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?

29 Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m’malo mwake munthu asatuluke m’malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.

30 Ndipo anthu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri.

31 Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lakeMana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.

32 Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m’chipululu, muja ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito.

33 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.

34 Monga Yehova analamula Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko.

35 Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.

36 Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/16-0743f611e7db315835126056b1733a3a.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 17

Madzi atuluka m’thanthwe ku Horebu

1 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m’chipululu cha Sini, M’zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.

2 Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?

3 Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?

4 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang’ono kundiponya miyala.

5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israele; nutenge m’dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo mtsinje, numuke.

6 Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe mu Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele.

7 Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?

Aisraele apambana Amaleke

8 Pamenepo anadza Amaleke, nayambana ndi Israele mu Refidimu.

9 Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m’dzanja langa.

10 Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda.

11 Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele anapambana; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke anapambana.

12 Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.

13 Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ukali wa lupanga.

14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m’buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.

15 Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi:

16 nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleke m’mibadwomibadwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/17-92eaaa534550f75ff29d6bd97d170169.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 18

Yetero azonda Mose nampangira

1 Ndipo Yetero, wansembe wa Midiyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israele anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israele mu Ejipito.

2 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ake awiri;

3 dzina la winayo ndiye Geresomo, pakuti anati, Ndakhala mlendo m’dziko lachilendo;

4 ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga laFarao.

5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, paphiri la Mulungu;

6 nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ake omwe awiri.

7 Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m’hema.

8 Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.

9 Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m’dzanja la Aejipito.

10 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m’dzanja la Aejipito, ndi m’dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi padzanja la Aejipito.

11 Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.

12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

13 Ndipo kunatero kuti m’mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m’mawa kufikira madzulo.

14 Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m’mawa kufikira madzulo?

15 Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;

16 akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake.

17 Koma mpongozi wa Mose ananena naye, Chinthu uchitachi sichili chabwino ai.

18 Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha.

19 Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m’malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;

20 nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.

21 Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;

22 ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing’ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.

23 Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere.

24 Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wake, nachita zonse adazinena.

25 Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.

26 Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing’ono yonse amaweruza okha.

27 Ndipo Mose analola mpongozi wake amuke; ndipo anachoka kunka ku dziko lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/18-a21f16efc489b3414e3c459b26a51257.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 19

Mulungu alamulira anthu za ku Sinai

1 Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m’dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m’chipululu cha Sinai.

2 Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m’chipululu cha Sinai, namanga tsasa m’chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji paphirilo.

3 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m’phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,

4 Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.

5 Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusungachipanganochanga, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;

6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.

7 Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.

8 Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.

11 Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.

12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m’phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

13 dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m’phirimo.

14 Ndipo Mose anatsika m’phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.

15 Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.

16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m’mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.

17 Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde paphiri.

18 Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m’moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m’ng’anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.

19 Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.

20 Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.

21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.

22 Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova.

23 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m’phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m’phirimo, ndi kulipatula.

24 Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.

25 Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/19-7b37211ef39c25bbca9628a4716d8952.mp3?version_id=1068—