Categories
EKSODO

EKSODO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Dzina lakuti

Eksodo

limatanthauza “kutuluka”, ndipo limafotokoza za chinthu chofunikira kwambiri mu mbiri ya Aisraele. Chinthu chimenechi ndicho kusamuka kwa Aisraele kuchokera ku Ejipito kumene anali akapolo. Bukuli lili ndi magawo anai: Gawo loyamba ndilo kumasuka kwa Aisraele ku ukapolo; lachiwiri ndilo ulendo wao kupita kuphiri la Sinai; lachitatu ndi chipangano cha Mulungu ndi anthu ake paphiri la Sinai, pamene anawapatsa malamulo okhudzana ndi chikhalidwe, kayendetse ka dziko komanso chipembedzo; ndipo gawo lachinai ndilo mamangidwe ndi makonzedwe a malo opembedzerapo Aisraele, ndiponso malamulo okhudzana ndi ansembe komanso chipembedzo.

Kwenikweni bukuli likulongosola zimene Mulungu anachita pamene anawamasula anthu ake ku ukapolo ndi kuwasandutsa kukhala mtundu wa anthu okhala ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino.

Mwininkhani mu bukuli ndiye Mose, amene Mulungu anamusankha kuti atsogolere anthu ake kuchokera ku Ejipito. Gawo lodziwika bwino la bukuli ndilo Malamulo Khumi (20.1-17).

Za mkatimu

Aisraele apulumuka ku ukapolo wa ku Ejipito

1.1—15.21

a. Akapolo ku Ejipito

1.1-22

b. Kubadwa kwa Mose ndi ubwana wake

2.1—4.31

c. Mose ndi Aroni akumana ndi mfumu ya Ejipito

5.1—11.10

d. Aisraele achita Paska nachoka ku Ejipito

12.1—15.21

Kuchokera ku Nyanja Yofiira mpaka kuphiri la Sinai

15.22—18.27

Kuperekedwa kwa Malamulo ndi chipangano

19.1—24.18

Malo Opatulika ndi malangizo a chipembedzo

25.1—40.38

Categories
EKSODO

EKSODO 1

Masautso a ana a Israele mu Ejipito

1 Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

2 Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda;

3 Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;

4 Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere.

5 Ndipo amoyo onse amene anatuluka m’chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali mu Ejipito.

6 Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse.

7 Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.

8 Pamenepo inalowa mfumu yatsopano mu ufumu wa Ejipito, imene siinadziwe Yosefe.

9 Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.

10 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m’dzikomo.

11 Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangiraFaraomizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.

12 Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.

13 Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa;

14 nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

Anamwino samvera mfumu

15 Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;

16 ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.

17 Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.

18 Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo?

19 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.

20 Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.

21 Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja.

22 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m’mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/1-c487543f057e15449b0be3dbe8f0e5cb.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 2

Kubadwa kwa Mose

1 Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi.

2 Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m’mene anamuona kuti ali wokoma, anam’bisa miyezi itatu.

3 Koma pamene sanathe kum’bisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m’mbali mwa mtsinje.

4 Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira.

5 Ndipo mwana wamkazi waFaraoanatsikira kukasamba m’mtsinje; ndipo atsikana ake anayendayenda m’mbali mwa mtsinje; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.

6 Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.

7 Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?

8 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo.

9 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa.

10 Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m’madzi.

11 Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake.

12 Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha Mwejipito, namfotsera mumchenga.

13 M’mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikumenyana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?

14 Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.

15 Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m’dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.

16 Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.

17 Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

18 M’mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

19 Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m’manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

20 Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya.

21 Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.

22 Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m’dziko la eni.

23 Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.

24 Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukirachipanganochake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.

25 Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/2-90f4e1f8f67f6d2dfd269f428923e43c.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 3

Kuitanidwa kwa Mose

1 Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m’tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.

2 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m’chilangali chamoto chotuluka m’kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.

3 Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji.

4 Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m’kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.

5 Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.

6 Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang’ana Mulungu.

7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

8 ndipo ndatsikira kuwalanditsa m’manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m’dziko lija akwere nalowe m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

9 Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.

10 Tiye tsopano, ndikutuma kwaFarao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israele mu Ejipito.

11 Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?

12 Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.

13 Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani?

14 Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.

15 Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.

16 Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;

17 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m’mazunzo a Aejipito, kukulowezani m’dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

18 Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m’chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.

19 Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.

20 Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.

21 Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu;

22 koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m’nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/3-5525bed4c5ed59506c9457c932d08062.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 4

Mose alandira mphamvu yakuchita zodabwitsa

1 Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekere iwe.

2 Ndipo Yehova ananena naye, Icho nchiyani m’dzanja lako? Nati, Ndodo.

3 Ndipo ananena Iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa.

4 Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumchira; ndipo anatambasula dzanja lake, naigwira, nikhalanso ndodo m’dzanja lake;

5 kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.

6 Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa.

7 Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale.

8 Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi.

9 Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda.

10 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m’kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.

11 Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m’kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?

12 Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m’kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.

13 Koma anati, Mverani, Ambuye, tumizani padzanja la iye amene mudzamtuma.

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m’mtima mwake.

15 Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m’kamwa mwako, ndi m’kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.

16 Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m’kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.

17 Ndipo ukaigwire m’dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo.

18 Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali mu Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.

19 Ndipo Yehova ananena ndi Mose mu Midiyani, Muka, bwerera kunka ku Ejipito; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako.

20 Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m’dzanja lake.

21 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m’dzanja lako, pamaso paFarao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.

22 Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.

23 Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.

24 Ndipo kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.

25 Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka.

26 Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa chamdulidwe.

Mose akomana ndi Aroni

27 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.

28 Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira.

29 Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akulu onse a ana a Israele;

30 ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nachita zizindikiro zija pamaso pa anthu.

31 Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/4-690f5e15632697e05fe248246069df29.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 5

Kupempha kwa Mose ndi Aroni kuipsa mlandu wa Aisraele

1 Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndiFarao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m’chipululu.

2 Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.

3 Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m’chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga.

4 Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu.

5 Farao anatinso, Taonani, anthu a m’dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao.

6 Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,

7 Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu.

8 Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita ulesi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.

9 Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza.

10 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.

11 Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu.

12 Pamenepo anthuwo anabalalika m’dziko lonse la Ejipito kufuna chiputu ngati udzu.

13 Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.

14 Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsirize bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?

15 Pamenepo akapitao a ana a Israele anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu?

16 Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.

17 Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.

18 Mukani tsopano, gwirani ntchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse chiwerengero chake cha njerwa.

19 Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake.

20 Ndipo potuluka kwa Farao iwo anakomana ndi Mose ndi Aroni, alikuima popenyana nao;

21 ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m’dzanja lao kutipha nalo.

Mulungu alonjeza kupulumutsa anthu ake

22 Pamenepo Mose anabwerera nanka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji?

23 Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m’dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditse anthu anu konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/5-5ac7b77ff7f2c8cb8ea7a6763c30da99.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 6

1 Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitiraFarao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m’dziko lake.

2 Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA:

3 ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.

4 Ndipo ndinakhazikitsanso naochipanganochanga, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m’mwemo.

5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa.

6 Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;

7 ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.

8 Ndipo ndidzakulowetsani m’dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.

9 Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.

10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

11 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m’dziko lake.

12 Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?

13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m’dziko la Ejipito.

Chibadwidwe cha Mose ndi Aroni

14 Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.

15 Ndi ana aamuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amenewo ndiwo mabanja a Simeoni.

16 Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.

17 Ana aamuna a Geresoni ndiwo: Libini ndi Simei, mwa mabanja ao.

18 Ndi ana aamuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu.

19 Ndipo ana aamuna a Merari ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao.

20 Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.

21 Ndi ana aamuna a Izihara ndiwo: Kora ndi Nefegi, ndi Zikiri.

22 Ndi ana aamuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri.

23 Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.

24 Ndipo ana aamuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.

25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.

26 Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m’dziko la Ejipito mwa makamu ao.

27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele mu Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.

Mulungu ampangira Mose

28 Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m’dziko la Ejipito,

29 Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe.

30 Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/6-9143a82f0a77e8e383912e21abcd6d68.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 7

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwaFarao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako.

2 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m’dziko lake.

3 Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m’dziko la Ejipito.

4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m’dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.

5 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.

6 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.

7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.

Mose ndi amatsenga

8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,

9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka.

10 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.

11 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.

12 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao.

13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.

Chozizwitsa choyamba: Madzi asanduka mwazi

14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite.

15 Muka kwa Farao m’mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m’mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m’dzanja lako.

16 Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m’chipululu; koma, taona, sunamvere ndi pano.

17 Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m’mtsinje ndi ndodo ili m’dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.

18 Ndi nsomba zili m’mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m’mtsinjemo.

19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m’dziko lonse la Ejipito, m’zotengera zamtengo, ndi zamwala.

20 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m’mtsinjemo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m’mtsinjemo anasanduka mwazi.

21 Ndi nsomba za m’mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m’mtsinjemo; ndipo munali mwazi m’dziko lonse la Ejipito.

22 Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.

23 Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m’nyumba yake, osasamalira ichi chomwe mumtima mwake.

24 Koma Aejipito onse anakumba m’mphepete mwa mtsinje kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m’mtsinjemo.

25 Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda mtsinje Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/7-d567f6baf72b1042a279266f408e3476.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 8

Chozizwitsa chachiwiri: Achule

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwaFarao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2 Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule;

3 ndipo m’mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m’nyumba mwako, ndi m’chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m’nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m’michembo yanu yootcheramo, ndi m’mbale zanu zoumbiramo.

4 Ndipo achule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse.

5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, pamtsinje, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule padziko la Ejipito.

6 Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pamadzi a mu Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito.

7 Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule padziko la Ejipito.

8 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.

9 Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m’mtsinje mokha?

10 Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.

11 Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m’mtsinje mokha.

12 Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao.

13 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nafa achulewo kuchokera m’zinyumba, ndi m’mabwalo, ndi m’minda.

14 Ndipo anawaola miulumiulu; ndi dziko linanunkha.

15 Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

Chozizwitsa chachitatu: Nsabwe

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m’dziko lonse la Ejipito.

17 Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m’dziko lonse la Ejipito.

18 Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoze; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.

19 Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

Chozizwitsa chachinai: Mizaza

20 Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.

21 Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.

22 Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m’mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.

23 Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.

24 Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m’nyumba ya Farao, ndi m’nyumba za anyamata ake, ndi m’dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.

25 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m’dzikomu.

26 Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aejipito; taonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aejipito pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?

27 Timuke ulendo wa masiku atatu m’chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.

28 Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m’chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.

29 Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.

30 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova.

31 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse.

32 Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/8-9b52f839af4d661081537454e22a4ac2.mp3?version_id=1068—

Categories
EKSODO

EKSODO 9

Chozizwitsa chachisanu: Kalira pa zoweta

1 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwaFarao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2 Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire,

3 taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pangamira, pa ng’ombe, ndi pa zoweta zazing’ono ndi kalira woopsa.

4 Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.

5 Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m’dzikomu.

6 Ndipo m’mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.

7 Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.

Chozizwitsa cha 6: Zilonda pa anthu ndi zoweta

8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng’anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.

9 Ndipo lidzakhala fumbi losalala padziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m’dziko lonse la Ejipito.

10 Ndipo anatenga phulusa la m’ng’anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

11 Ndipo alembi sanathe kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse.

12 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.

Chozizwitsa cha 7: Matalala

13 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mammawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.

14 Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi.

15 Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke padziko lapansi.

16 Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa padziko lonse lapansi.

17 Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?

18 Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.

19 Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m’nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.

20 Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m’zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake;

21 koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zake kubusa.

22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala padziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse zakuthengo, m’dziko la Ejipito.

23 Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala padziko la Ejipito.

24 Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m’dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.

25 Ndipo matalala anapanda m’dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse zakuthengo, nathyola mitengo yonse yakuthengo.

26 M’dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala.

27 Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.

28 Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.

29 Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m’mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.

30 Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu.

31 Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa.

32 Koma tirigu ndi rai sizinayoyoke popeza amabzala m’mbuyo.

33 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m’mzinda nakweza manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko.

34 Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake.

35 Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalole ana a Israele amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/9-c68da97a32252bd8076f42ed69c476b8.mp3?version_id=1068—