Mulungu alonjeza kuwalanditsa akalapa atachimwa
1 Ndipo kudzakhala, zikakugwerani zonsezi, mdalitso ndi temberero, ndinaikazi pamaso panu, ndipo mukazikumbukira mumtima mwanu mwaamitunduonse, amene Yehova Mulungu wanu anakupirikitsiraniko;
2 nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse;
3 pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.
4 Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;
5 ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m’dziko lidakhala laolao la makolo anu, nilidzakhala lanulanu; ndipo adzakuchitirani zokoma, ndi kukuchulukitsani koposa makolo anu.
6 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.
7 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.
8 Pamenepo mutembenuke ndi kumvera mau a Yehova, ndi kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino.
9 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakuchulukitsirani ntchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukuchitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;
10 ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ake ndi malemba ake olembedwa m’buku la chilamulo ichi; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
11 Pakuti lamulo ili ndikuuzani lero lino, silikukanikani kulizindikira, kapena silikhala kutali.
12 Silikhala m’mwamba, kuti mukati, Adzatikwerera m’mwamba ndani, ndi kubwera nalo kwa ife, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite?
13 Ndipo silikhala tsidya la nyanja, kuti mukati, Adzatiolokera ndani tsidya la nyanja, ndi kutitengera ili, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite?
14 Pakuti mauwa ali pafupifupi ndi inu, m’kamwa mwanu, ndi m’mtima mwanu, kuwachita.
15 Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa;
16 popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m’dziko limene mulowako kulilandira.
17 Koma mukatembenukira mtima wanu, osamvera inu, nimukacheteka, ndi kugwadira milungu ina ndi kuitumikira;
18 ndikulalikirani inu lero, kuti mudzatayika ndithu, masiku anu sadzachuluka m’dziko limene muolokera Yordani kulowamo kulilandira.
19 Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;
20 kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/30-e69e4a14f58e9ffff03c49e146de16af.mp3?version_id=1068—