Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 20

Malamulo a kunkhondo

1 Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito, ali ndi inu.

2 Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,

3 nati nao, Tamverani, Israele, muyandikiza kunkhondo lero pa adani anu; musafumuka mitima yanu; musachita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;

4 pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.

5 Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.

6 Ndipo ndani munthuyo anaoka munda wampesa osalawa zipatso zake? Amuke nabwerere kunyumba yake, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zake.

7 Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.

8 Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.

9 Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu.

10 Pamene muyandikiza mzinda kuchita nao nkhondo, muziufuulira ndi mtendere.

11 Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opezeka m’mwemo akhale akapolo anu, nadzakugwirirani ntchito yathangata.

12 Koma ukapanda kuchita zamtendere ndi inu, koma kuchita nkhondo nanu, pamenepo muumangire tsasa.

13 Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m’dzanja lanu, mukanthe amuna ake onse ndi lupanga lakuthwa.

14 Koma akazi ndi ana ndi ng’ombe ndi zonse zili m’mzindamo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

15 Muzitero nayo mizinda yonse yokhala kutalitali ndi inu, yosakhala mizinda yaamitunduawa.

16 Koma za mizinda ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma;

17 koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;

18 kuti angakuphunzitseni kuchita monga mwa zonyansa zao zonse, amazichitira milungu yao; ndipo mungachimwire Yehova Mulungu wanu.

19 Pamene mumangira tsasa mzinda masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yake ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m’munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?

20 Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mzinda wochita nanu nkhondo muumangire machemba, mpaka mukaugonjetsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/20-61ba721a21afa93af53b4e7dd5a27688.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 21

Za wophedwa mosadziwika

1 Akapeza munthu waphedwa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, nagona pamunda, wosadziwika wakumkantha,

2 pamenepo azituluka akulu anu ndi oweruza anu, nayese kumizinda yomzinga wophedwayo;

3 ndipo kudzali kuti mzinda wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akulu a mzinda uwu atenge ng’ombe yaikazi yosagwira ntchito, yosakoka goli;

4 ndipo akulu a mzinda uwu atsike nayo ng’ombeyo ku chigwa choyendako madzi, chosalima ndi chosabzala, nayidula khosi ng’ombeyo m’chigwamo;

5 ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m’dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.

6 Ndipo akulu onse a mzindawo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa ng’ombeyo yodulidwa khosi m’chigwamo;

7 nayankhe nati, Manja athu sanakhetse mwazi uwu, ndi maso athu sanauone.

8 Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo.

9 Chotero mudzichotsere mwazi wosachimwa pakati panu, pakuti wachita choyenera pamaso pa Yehova.

Za akazi otengedwa kunkhondo

10 Pamene mutuluka kunka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m’manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu;

11 mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna mumtenga akhale mkazi wanu;

12 pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake;

13 navule zovala za ukapolo wake, nakhale m’nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mai wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu.

14 Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa chuma, popeza wamchepetsa.

Mphamvu ya oyamba kubadwa

15 Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;

16 pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ake aamuna chuma chake, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.

17 Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.

Za ana opulukira osamvera

18 Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga;

19 azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mzinda wake, ndi ku chipata cha malo ake;

20 ndipo anene kwa akulu a mzinda wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.

21 Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.

Za kuika wophedwa mompachika

22 Munthu akakhala nalo tchimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampachika;

23 mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/21-3d5c8c0c6adbb5762e6062edc3aa4999.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 22

Za zoweta zolowerera

1 Mukapenya ng’ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.

2 Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.

3 Mutero nayenso bulu wake; mutero nachonso chovala chake, mutero nachonso chotayika chilichonse cha mbale wanu, chakumtayikira mukachipeza ndi inu; musamazilekerera.

4 Mukapenya bulu kapena ng’ombe ya mbale wanu, zitagwa m’njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.

Zosayenerana zisaphatikizike

5 Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.

6 Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana;

7 muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke.

8 Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.

9 Musamabzala mbeu zosiyana m’munda wanu wampesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wampesa zomwe.

10 Musamalima ndi bulu ndi ng’ombe zikoke pamodzi.

11 Musamavala nsalu yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.

12 Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho.

Za akazi onenezedwa

13 Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,

14 namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeze zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu;

15 pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mzinda kuchipata;

16 ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda;

17 ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeze zizindikiro za unamwali wake m’mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mzindawo.

18 Pamenepo akulu a mzindawo azitenga munthuyu ndi kumkwapula;

19 ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi asiliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sangathe kumchotsa masiku ake onse.

20 Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo;

21 pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m’nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.

Zoyanjana zosaloledwa

22 Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.

23 Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m’mzinda mwamuna, nagona naye;

24 muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mzinda uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m’mzinda; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.

25 Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye;

26 koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha;

27 pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anafuula, koma panalibe wompulumutsa.

28 Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo,

29 pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse.

30 Munthu asatenge mkazi wa atate wake, kapena kuvula atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/22-7f10dc81e1fe53d6038aa66ae9435545.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 23

Oletsedwa ku msonkhano wa Yehova

1 Munthu wofulika kapena woduka chiwalo chaumuna, asalowe m’msonkhano wa Yehova.

2 Mwana wa m’chigololo asalowe m’msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m’msonkhano wa Yehova.

3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m’msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m’msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;

4 popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m’njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.

5 Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.

6 Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.

7 Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m’dziko lake.

8 Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m’msonkhano wa Yehova.

9 Nkhondo yanu ikatuluka pa adani anu, mudzisunge kusachita choipa chilichonse.

10 Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono;

11 koma kudzali pofika madzulo, asambe m’madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono.

12 Mukhale nao malo kunja kwa chigono kumene muzimukako kuthengo;

13 nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho;

14 popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.

Za akapolo opulumuka, za achigololo, za okongoletsa mopindulitsa

15 Musamapereka kwa mbuye wake kapolo wopulumuka kwa mbuye wake kuthawira kwa inu;

16 akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m’mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.

17 Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana aakazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana aamuna a Israele.

18 Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m’nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

19 Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa.

20 Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m’dziko limene mulowamo kulilandira.

21 Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.

22 Koma mukapanda kulonjeza chowinda, mulibe kuchimwa.

23 Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu.

24 Mukalowa m’munda wampesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m’chotengera chanu.

25 Mukalowa m’tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/23-fce006c3bc394350bd23b083770edc37.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 24

Za kalata ya chilekaniro, chikole, kuba munthu, khate

1 Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m’dzanja lake, ndi kumtulutsa m’nyumba mwake.

2 Ndipo atatuluka m’nyumba mwake, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina.

3 Ndipo akamuda mwamuna wachiwiriyo, nakamlemberanso kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m’dzanja lake, nakamtulutsa m’nyumba mwake; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wake;

4 pamenepo mwamuna woyamba anamchotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wake, atadetsedwa iye; pakuti ichi ndi chonyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamachimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.

5 Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke ku nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.

6 Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu.

7 Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu.

8 Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita.

9 Kumbukirani chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriyamu panjira, potuluka inu m’dziko la Ejipito.

Za kukongoletsa

10 Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iliyonse, musamalowa m’nyumba mwake kudzitengera chikole chake.

11 Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituluka nacho chikolecho kwa inu muli pabwalo.

12 Ndipo akakhala munthu waumphawi musagone muli nacho chikole chake;

13 polowa dzuwa mumbwezeretu chikolecho, kuti agone m’chovala chake, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Zachifundo pa antchito aumphawi, alendo ndi amasiye

14 Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m’dziko mwanu, m’midzi mwanu.

15 Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.

16 Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.

17 Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;

18 koma muzikumbukira kuti munali akapolo mu Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.

19 Mutasenga dzinthu zanu m’munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m’mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m’ntchito zonse za manja anu.

20 Mutagwedeza mtengo wanu waazitonamusayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye.

21 Mutatchera m’munda wanu wampesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye.

22 Ndipo muzikumbukira kuti munali akapolo m’dziko la Ejipito; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/24-132d4a323cbbc85ca8a5a33a5edf2133.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 25

Za makwapulidwe a wolakwa

1 Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.

2 Ndipo kudzali, wochita choipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pake, amwerengere zofikira choipa chake.

3 Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.

4 Musamapunamiza ng’ombe popuntha tirigu.

Za kukwatibwa mkazi ndi mlamu wake

5 Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake.

6 Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lake la mbale wake wakufayo, kuti dzina lake lisafafanizidwe mu Israele.

7 Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina mu Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.

8 Pamenepo akulu a mzinda wake amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;

9 pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake.

10 Ndipo azimutcha dzina lake mu Israele, Nyumba ya uje anamchotsa nsapato.

11 Akalimbana wina ndi mnzake, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wake m’dzanja la wompandayo, nakatulutsa dzanja lake, ndi kumgwira kudzivalo;

12 pamenepo muzidula dzanja lake; diso lanu lisamchitire chifundo.

13 Musamakhala nayo m’thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukulu ndi waung’ono.

14 Musamakhala nayo m’nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukulu ndi waung’ono.

15 Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu achuluke m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

16 Pakuti onse akuchita zinthu izi, onse akuchita chisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

Amaleke afafanizike

17 Kumbukirani chochitira inu Amaleke panjira, potuluka inu mu Ejipito;

18 kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m’mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu.

19 Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu, kuti muzifafaniza chikumbutso cha Amaleke pansi pa thambo; musamaiwala.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/25-ea713d769bfa1dc310612fe6ab3579d2.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 26

Chopereka cha zipatso zoyamba

1 Ndipo kudzali, utakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, ndipo mwachilandira ndi kukhala m’mwemo;

2 kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.

3 Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m’masiku awa, ndi kunena naye, Ndivomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili.

4 Ndipo wansembe alandire dengu m’manja mwanu, ndi kuuika paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu.

5 Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang’ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;

6 koma Aejipito anatichitira choipa, natizunza, natisenza ntchito yolimba.

7 Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi ntchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;

8 ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa;

9 ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

10 Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu;

11 ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.

Limodzi la magawo khumi chaka chachitatu

12 Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m’midzi mwanu, ndi kukhuta.

13 Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndachotsa zopatulika m’nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwire malamulo anu, kapena kuwaiwala.

14 Sindinadyeko m’chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine.

15 Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m’mwamba, ndipo dalitsani anthu anu Israele, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

16 Lero lino Yehova Mulungu wanu akulamulirani kuchita malemba ndi maweruzo awa; potero muzimvera ndi kuwachita ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

17 Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m’njira zake, ndi kusunga malemba ake, ndi malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi kumvera mau ake.

18 Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu akeake a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ake onse;

19 kuti akukulitseni koposaamitunduonse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/26-55cecf4c552c358fdb670636916d9f18.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 27

Za kuutsa miyala ya chikumbutso ataoloka Yordani

1 Ndipo Mose ndi akulu a Israele anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero.

2 Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikulu, ndi kuimata ndi njeresa;

3 ndipo mulemberepo mau onse a chilamulo ichi, mutaoloka; kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.

4 Ndipo kudzali, mutaoloka Yordani, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m’phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa.

5 Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo pangizo chachitsulo.

6 Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;

7 ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

8 Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a chilamulo ichi mopenyeka bwino.

9 Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.

10 Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.

Mdalitso ndi temberero ku Gerizimu ndi Ebala

11 Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,

12 Aimirire awa paphiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.

13 Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.

14 Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israele, ndi mau omveka.

15 Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m’malo a m’tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti,Amen.

16 Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

17 Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

18 Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m’njira. Ndi anthu onse anene, Amen.

19 Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.

20 Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

21 Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iliyonse. Ndi anthu onse anene, Amen.

22 Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen.

23 Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

24 Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m’tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.

25 Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.

26 Wotembereredwa iye wosavomereza mau a chilamulo ichi kuwachita. Ndi anthu onse anene, Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/27-b29c8c4ac6a5289845274072baee4c4c.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 28

Madalitso pa kumvera kwao

1 Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi;

2 ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

3 Mudzakhala odala m’mzinda, ndi odala kubwalo.

4 Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

5 Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu.

6 Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.

7 Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.

8 Yehova adzakulamulirani dalitso m’nkhokwe zanu, ndi m’zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

9 Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira zake.

10 Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.

11 Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m’zipatso za thupi lanu, ndi m’zipatso za zoweta zanu, ndi m’zipatso za nthaka yanu, m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.

12 Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m’nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

13 Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;

14 osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.

Matemberero pa kusamvera kwao

15 Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.

16 Mudzakhala otembereredwa m’mzinda, ndi otembereredwa pabwalo.

17 Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu.

18 Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

19 Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu.

20 Yehova adzakutumizirani temberero, chisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika msanga, chifukwa cha zochita inu zoipa, zimene wandisiya nazo.

21 Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.

22 Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.

23 Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko lili pansi panu ngati chitsulo.

24 Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kuchokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.

25 Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.

26 Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi zilombo zonse za padziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.

27 Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.

28 Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima;

29 ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.

30 Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m’mwemo; mudzaoka munda wampesa, osalawa zipatso zake.

31 Adzapha ng’ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.

32 Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m’maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m’dzanja lanu.

33 Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;

34 nimudzakhala oyeruka chifukwa chomwe muchiona ndi maso anu.

35 Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.

36 Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.

37 Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.

38 Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang’ono; popeza dzombe lidzazitha.

39 Mudzaoka m’minda yampesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kutchera mphesa zake, popeza mbozi zidzaidya.

40 Mudzakhala nayo mitengo yaazitonam’malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka.

41 Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.

42 Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe.

43 Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera.

44 Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mchira.

45 Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani;

46 ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthawi zonse.

47 Popeza simunatumikire Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse;

48 chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.

49 Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;

50 mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana;

51 ndipo adzadya zipatso za ng’ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng’ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.

52 Ndipo adzakuzingani m’midzi mwanu monse, kufikira adzagwa malinga anu aatali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m’dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m’midzi mwanu monse, m’dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

53 Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.

54 Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira;

55 osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ake alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu monse.

56 Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi;

57 ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m’tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu.

58 Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m’buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu;

59 Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.

60 Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Ejipito, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.

61 Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m’buku la chilamulo ichi, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.

62 Ndipo mudzatsala anthu pang’ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m’mwamba; popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu.

63 Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.

64 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.

65 Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m’maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.

66 Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.

67 M’mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! Ndi madzulo mudzati, Mwezi utafika m’mawa! Chifukwa cha mantha a m’mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya.

68 Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, panjira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/28-0ef2c8a5fb8f498b65cdcefff9a39fc8.mp3?version_id=1068—

Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 29

Mulungu abwereza kupangana nao

1 Awa ndi mau achipanganochimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m’dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao mu Horebu.

2 Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nati nao, Munapenya inu zonse zimene Yehova anachitiraFarao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse, pamaso panu m’dziko la Ejipito;

3 mayesero aakuluwa maso anu anawapenya, zizindikirozo, ndi zozizwa zazikulu zija;

4 koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.

5 Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m’chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.

6 Simunadye mkate, simunamwe vinyo kapena chakumwa cholimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

7 Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, anatuluka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;

8 ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale cholowa chao cha Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase.

9 Chifukwa chake sungani mau a chipangano ichi ndi kuwachita, kuti muchite mwanzeru m’zonse muzichita.

10 Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mafuko anu, akulu anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israele,

11 makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;

12 kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino;

13 kuti adzikhazikire inu, mtundu wake wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo.

14 Koma sindichita chipangano ichi ndi lumbiro ili ndi inu nokha;

15 komanso ndi iye wakuimirira pano nafe lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndiponso ndi iye wosakhala pano nafe lero lino.

16 Pakuti mudziwa chikhalidwe chathu m’dziko la Ejipito, ndi kuti tinapyola pakati paamitunduamene munawapyola;

17 ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala,silivandi golide, zokhala pakati pao;

18 kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.

19 Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m’mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;

20 Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m’buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.

21 Ndipo Yehova adzamsiyanitsa ndi mafuko onse a Israele ndi kumchitira choipa, monga mwa matemberero onse a chipangano cholembedwa m’buku ili la chilamulo.

22 Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo.

23 Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndisulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m’mkwiyo wake ndi ukali wake;

24 inde amitundu onse adzati, Yehova anachitira dziko ili chotero chifukwa ninji? Nchiyani kupsa mtima kwakukulu kumene?

25 Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m’dziko la Ejipito;

26 napita natumikira milungu ina, naigwadira, milungu imene sanaidziwe, imene sanawagawire;

27 chifukwa chake Yehova anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m’buku ili.

28 Ndipo Yehova anawazula m’nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi mu ukali waukulu, nawaponya m’dziko lina, monga lero lino.

29 Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/29-33f39eda6e94389fa32c2383536aac29.mp3?version_id=1068—