Mose awadandaulira amvere Malamulo a Mulungu
1 Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.
2 Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kuchotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.
3 Maso anu anapenya chochita Yehova chifukwa cha Baala-Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala-Peori, Yehova Mulungu wanu anawaononga pakati panu.
4 Koma inu amene munamamatira Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo nonsenu lero lomwe.
5 Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.
6 Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo athu anzeru ndi akuzindikira.
7 Pakuti mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene paliponse timaitanira Iye?
8 Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?
9 Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.
10 Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu mu Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo padziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.
11 Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde paphiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.
12 Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako.
13 Pamenepo anakufotokozeranichipanganochake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.
14 Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawachite m’dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanulanu.
15 Potero dzichenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenye mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu mu Horebu, ali pakati pa moto;
16 kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga chifaniziro chilichonse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;
17 mafanidwe a nyama iliyonse ili padziko lapansi, mafanidwe a mbalame iliyonse yamapiko yakuuluka m’mlengalenga,
18 mafanidwe a chinthu chilichonse chokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iliyonse yokhala m’madzi pansi padziko;
19 ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.
20 Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m’ng’anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.
21 Yehova anakwiyanso nane chifukwa cha mau anu, nalumbira kuti sindidzaoloka Yordani ine, ndi kuti sindidzalowa m’dziko lokomali Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu;
22 pakuti ndidzafa m’dziko muno, osaoloka Yordani; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanulanu.
23 Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.
24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.
25 Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikulu m’dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m’chifaniziro cha kanthu kalikonse, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kuutsa mkwiyo wake:
26 ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zichite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kuchotsedwa ku dziko limene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu; masiku anu sadzachuluka pamenepo, koma mudzaonongeka konse.
27 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang’ono mwaamitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.
28 Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.
29 Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
30 Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ake;
31 popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.
32 Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu padziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzake a thambo, ngati chinthu chachikulu chonga ichi chinamveka, kapena kuchitika?
33 Kodi pali mtundu wa anthu udamva mau a mulungu wina akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo?
34 Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?
35 Inu munachiona ichi, kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu; palibe wina wopanda Iye.
36 Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo padziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.
37 Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;
38 kupirikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino.
39 Potero dziwani lero lino nimukumbukire m’mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m’thambo la kumwamba ndi padziko lapansi; palibe wina.
40 Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke padziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.
Mizinda itatu yopulumukirako kum’mawa kwa Yordani
41 Pamenepo Mose anapatula mizinda itatu tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;
42 kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wake dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa mizinda iyi, akhale ndi moyo:
43 ndiyo Bezeri, m’chipululu, m’dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti mu Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, mu Basani, ndiwo wa Amanase.
44 Ndipo ichi ndi chilamulo Mose anachiika pamaso pa ana a Israele;
45 izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo mu Ejipito;
46 tsidya lija la Yordani, m’chigwa cha pandunji pa Betepeori, m’dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo mu Ejipito;
47 ndipo analanda dziko lake, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;
48 kuyambira ku Aroere, ndiwo m’mphepete mwa mtsinje wa Arinoni, kufikira phiri la Sirioni (ndilo Heremoni),
49 ndi chidikha chonse tsidya lija la Yordani kum’mawa, kufikira ku Nyanja ya Araba, pa tsinde lake la Pisiga.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/4-1ffa6ea78092b5e469811c196309d9f2.mp3?version_id=1068—