Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 20

Satana womangidwa zaka chikwi

1 Ndipo ndinaonamngeloanatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha ku chiphompho chakuya, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.

2 Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndiSatana, nammanga iye zaka chikwi,

3 namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengensoamitundukufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.

4 Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndiKhristuzaka chikwi.

5 Otsala a akufa sanakhalenso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.

6 Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.

Satana amasulidwa naonongeka

7 Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa Satana m’ndende yake;

8 nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mungodya zinai za dziko,Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.

9 Ndipo anakwera nafalikira m’dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mzinda wokondedwawo: ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa.

10 Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndisulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.

Chiweruziro chotsiriza

11 Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m’mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.

12 Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang’ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zao.

13 Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m’menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.

14 Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.

15 Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m’buku la moyo, anaponyedwa m’nyanja yamoto.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/20-d2dbb3211f1a325187873729fa126e49.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 21

Miyamba yatsopano ndi dziko latsopano

1 Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.

2 Ndipo ndinaona mzinda woyerawo,Yerusalemuwatsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.

3 Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;

4 ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.

5 Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.

6 Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndineAlefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe kukasupe wa madzi a moyo kwaulere.

7 Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.

8 Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndisulufure; ndiyo imfa yachiwiri.

Yerusalemu watsopano

9 Ndipo anadza mmodzi waangeloasanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi waMwanawankhosa.

10 Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,

11 ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;

12 nukhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi maina olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israele;

13 kum’mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwera zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu.

14 Ndipo linga la mzinda linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri aatumwikhumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

15 Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nao muyeso, bango lagolide, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake.

16 Ndipo mzinda ukhala waphwamphwa; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.

17 Ndipo anayesa linga lake, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.

18 Ndipo mirimo ya linga lake ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwa golide woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.

19 Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundumitundu; maziko oyamba, ndi yaspi; achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinai, ndi smaragido;

20 achisanu, ndi sardonu; achisanu ndi chimodzi, ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri, ndi krusolito; achisanu ndi chitatu, ndi berulo; achisanu ndi chinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndi achimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri, ndi ametusto.

21 Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse pa chokha cha ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda nla golide woyengeka, ngati mandala openyekera.

22 Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.

23 Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.

24 Ndipoamitunduadzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.

25 Ndipo pazipata zake sipatsekedwa konse usana, (pakuti sikudzakhala usiku komweko);

26 ndipo adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nao momwemo;

27 ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m’buku la moyo la Mwanawankhosa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/21-e05aabe0a210c650c4d57fc8dfb9717c.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 22

1 Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi waMwanawankhosa.

2 Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.

3 Ndipo sipadzakhalanso temberero lililonse; ndipo mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ake adzamtumikira Iye,

4 nadzaona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pao.

5 Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.

Machenjezo ndi malonjezano

6 Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatumamngelowake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga.

7 Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili.

8 Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.

9 Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.

10 Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza chizindikiro mau a chinenero cha buku ili; pakuti nthawi yayandikira.

11 Iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.

12 Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake.

13 Ine ndineAlefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chitsiriziro.

14 Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m’mzinda pazipata.

15 Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.

16 Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi muMipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.

17 Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.

18 Ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mau a chinenero cha buku ili, Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m’bukumu:

19 ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m’mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m’bukumu.

20 Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga.Amen; idzani, Ambuye Yesu.

21 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi oyera mtima onse. Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/22-eef11f66aead73699d219743f5e649f5.mp3?version_id=1068—