Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 10

Yohane adya buku lochokera Kumwamba

1 Ndipo ndinaonamngelowina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;

2 ndipo anali nako m’dzanja lake kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lake lamanja panyanja, ndi lamanzerelo pamtunda,

3 nafuula ndi mau aakulu, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anafuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao.

4 Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe.

5 Ndipo mngelo amene ndinamuona alikuimirira panyanja ndi pa mtunda, anakweza dzanja lake lamanja kuloza kumwamba,

6 nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m’mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:

7 komatu m’masiku a mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri m’mene iye adzayamba kuomba lipenga, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri.

8 Ndipo mau ndinawamva ochokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalo m’dzanja lamngelowakuimirira panyanja ndi padziko.

9 Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m’mimba mwako, komatu m’kamwa mwako kadzazuna ngati uchi.

10 Ndipo ndinatenga kabuku m’dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m’kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m’mimba mwanga mudawawa.

11 Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/10-255f531b57fa1bcabc3abc98e9957113.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 11

Mboni ziwiri

1 Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.

2 Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwaamitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.

3 Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.

4 Izo ndizo mitengo iwiri yaazitonandi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.

5 Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m’kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.

6 Izo zili nao ulamuliro wakutseka m’mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chao; ndipo ulamuliro zili nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthawi iliyonse zikafuna.

7 Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m’chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa, ndi kupha izo.

8 Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa.

9 Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lake, osalola mitembo yao iikidwe m’manda.

10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.

11 Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chilili; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya.

12 Ndipo anamva mau aakulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kunka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.

13 Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m’chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.

14 Tsoka lachiwiri lachoka; taonani, tsoka lachitatu lidza msanga.

Lipenga lotsiriza

15 Ndipomngelowachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi waKhristuwake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.

16 Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,

17 nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.

18 Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.

19 Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaonekalikasa la chipanganochake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/11-369b3b645521b7535a96648d4c15bfd4.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 12

Za mkazi ndi chinjoka

1 Ndipo chizindikiro chachikulu chinaoneka m’mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;

2 ndipo anali ndi pakati; ndipo afuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.

3 Ndipo chinaoneka chizindikiro china m’mwamba taonani, chinjoka chofiira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri.

4 Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam’mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.

5 Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake.

6 Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

7 Ndipo munali nkhondo m’mwamba. Mikaele ndiangeloake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo;

8 ndipo sichinapambane, ndipo sanapezekenso malo ao m’mwamba.

9 Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndiSatana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.

10 Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro waKhristuwake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.

11 Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi waMwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.

12 Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.

13 Ndipo pamene chinjoka chinaona kuti chinaponyedwa pansi kudziko, chinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.

14 Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.

15 Ndipo njokayo inalavula m’kamwa mwake, madzi ngati mtsinje, potsata mkazi, kuti mkaziyo akakokoleredwe nao.

16 Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m’kamwa mwake, nilinameza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalavula m’kamwa mwake.

17 Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.

18 Ndipo chinjokacho chinakaimirira m’mbali mwa nyanja.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/12-7a0adf1a96d270b2883b6434d6bd04c4.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 13

Chilombo chakutuluka m’nyanja

1 Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja.

Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m’nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.

2 Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.

3 Ndipo umodzi wa mitu yake unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata chilombocho;

4 ndipo analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chilombocho; ndipo analambira chilombo ndi kunena, Afanana ndi chilombo ndani? Ndipo akhoza ndani kumenyana nacho nkhondo?

5 Ndipo anachipatsa icho m’kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.

6 Ndipo chinatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala mu Mwamba.

7 Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwagonjetsa; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.

8 Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m’buku la moyo laMwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.

9 Ngati wina ali nalo khutu, amve.

10 Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.

Chilombo chotuluka pansi

11 Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.

12 Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola.

13 Ndipo chichita zizindikiro zazikulu, kutinso chitsitse moto uchokere m’mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.

14 Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.

15 Ndipo anachipatsa mphamvu yakupatsa fano la chilombo mpweya, kutinso fano la chilombo lilankhule, nilichite kuti onse osalilambira fano la chilombo aphedwe.

16 Ndipo chichita kuti onse, aang’ono ndi aakulu, achuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire chilembo padzanja lao ndi pamphumi pao;

17 ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, ndilo dzina la chilombo, kapena chiwerengero cha dzina lake.

18 Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chilombocho; pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/13-fd25a7479640af12f23e96f9d76dee2a.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 14

Mwanawankhosa ndi oomboledwa ake paphiri la Ziyoni

1 Ndipo ndinapenya, taonani,Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri laZiyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.

2 Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;

3 ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.

4 Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.

5 Ndipo m’kamwa mwao simunapezedwe bodza; ali opanda chilema.

Angelo atatu akulalikiratu ziweruziro za Mulungu

6 Ndipo ndinaonamngelowina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;

7 ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.

8 Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.

9 Ndipo anawatsata mngelo wina, wachitatu, nanena ndi mau aakulu, Ngati wina alambira chilombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pamphumi pake, kapena padzanja lake

10 iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasakaniza m’chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndisulufurepamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa;

11 ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera kunthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chilombocho ndi fano lake, ndi iye aliyense akalandira lemba la dzina lake.

12 Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.

13 Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.

Masika a dzinthu ndi a mphesa

14 Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina mongaMwana wa Munthu, wakukhala naye korona wagolide pamutu pake, ndi m’dzanja lake chisenga chakuthwa.

15 Ndipo mngelo wina anatuluka mu Kachisi, wofuula ndi mau aakulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.

16 Ndipo Iye wokhala pamtambo anaponya chisenga chake padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.

17 Ndipo mngelo wina anatuluka mu Kachisi ali mu Mwamba, nakhala nacho chisenga chakuthwa nayenso.

18 Ndipo mngelo wina anatuluka paguwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau aakulu kwa iye wakukhala nacho chisenga chakuthwa, nanena, Tumiza chisenga chako chakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m’dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu.

19 Ndipo mngelo anaponya chisenga chake kudziko nadula mphesa za m’munda wa m’dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.

20 Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/14-114c101bc2f6c7d2431439e2cb3475c9.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 15

Angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri

1 Ndipo ndinaona chizindikiro china m’mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa,angeloasanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.

2 Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosakaniza ndi moto; ndipo iwo amene anachigonjetsa chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.

3 Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo yaMwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.

4 Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

5 Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kachisi wa chihema cha umboni mu Mwamba:

6 ndipo anatuluka mu Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao.

7 Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.

8 Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa mu Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/15-7a246e65a78609aef73c4c7b21eff11b.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 16

1 Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku Kachisi, akunena kwaangeloasanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.

2 Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake.

3 Ndipo wachiwiri anatsanulira mbale yake m’nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m’nyanja zidafa.

4 Ndipo wachitatu anatsanulira mbale yake kumitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi.

5 Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero;

6 popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.

7 Ndipo ndinamva wa paguwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.

8 Ndipo wachinai anatsanulira mbale yake padzuwa; ndipo analipatsa ilo litenthe anthu ndi moto.

9 Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.

10 Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake,

11 nachitira mwano Mulungu wa mu Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalape ntchito zao.

12 Ndipo wachisanu ndi chimodzi anatsanulira mbale yake pamtsinje waukulu Yufurate; ndi madzi ake anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuwa.

13 Ndipo ndinaona motuluka m’kamwa mwa chinjoka, ndi m’kamwa mwa chilombo, ndi m’kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule;

14 pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.

15 (Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)

16 Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa mu Chihebri Armagedoni.

17 Ndipo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mumlengalenga; ndipo mu Kachisimo mudatuluka mau aakulu, ochokera kumpando wachifumu ndi kunena, Chachitika;

18 ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.

19 Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda yaamitunduinagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.

20 Ndipo zisumbu zonse zidathawa, ndi mapiri sanapezeke.

21 Ndipo anatsika kumwamba matalala aakulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/16-4a7c5fa8f0384b99d887d442e00a631e.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 17

Kupasuka kwa Babiloni. Chilombo chisokeretsa mkazi wachigololo

1 Ndipo anadza mmodzi mwaangeloasanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,

2 amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.

3 Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

4 Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golide, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m’dzanja lake chikho chagolide chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake,

5 ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.

6 Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.

7 Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa chifukwa ninji? Ine ndidzakuuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chilombo chakumbereka iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

8 Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m’chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m’buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.

9 Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;

10 ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi.

11 Ndipo chilombo chinalicho, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili mwa zisanu ndi ziwirizo, ndipo chinamuka kuchitayiko.

12 Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo.

13 Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chilombo.

14 Iwo adzachita nkhondo paMwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.

15 Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.

16 Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, ndipo zidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, ndi kudya nyama yake, ndipo zidzampsereza ndi moto.

17 Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m’mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.

18 Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mzinda waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/17-735b95cfeb77cef4200236e3a1edfea1.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 18

Kupasula kwa Babiloni. Maliro padziko lapansi

1 Zitatha izi ndinaonamngelowina wakutsika mu Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake.

2 Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

3 Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.

4 Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;

5 pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira mu Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.

6 Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa ntchito zake; m’chikhomo unathiramo, muuthirire chowirikiza.

7 Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.

8 Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.

9 Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,

10 chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.

11 Ndipo ochita malonda a m’dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

12 malonda a golide, ndi asiliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;

13 ndi sinamoni ndi amomo, ndi zofukiza, ndimure, ndilubani, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng’ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magaleta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.

14 Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakuchokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.

15 Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali chifukwa cha kuopa chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo;

16 nadzanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golide ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale!

17 Pakuti mu ora limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere. Ndipo watsigiro aliyense, ndi yense wakupita panyanja pakutipakuti, ndi amalinyero, ndi onse amene amachita kunyanja, anaima patali,

18 nafuula poona utsi wa kutentha kwake, nanena, Mzinda uti ufanana ndi mzinda waukuluwo?

19 Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti mu ora limodzi unasanduka bwinja.

20 Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndiatumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.

21 Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.

22 Ndipo mau a anthu oimba zeze, ndi a oimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo mmisiri aliyense wa machitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;

23 ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m’dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.

24 Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/18-4b99d1333b3a26bf8e11e48fdb615898.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 19

Kupasula kwa Babiloni. Chimwemwe ndi mayamiko mu Mwamba

1 Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena,Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;

2 pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.

3 Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.

4 Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kunena,Amen; Aleluya.

5 Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang’ono ndi aakulu.

6 Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

7 Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati waMwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.

8 Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

9 Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10 Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.

Khristu agonjetsa chilombo ndi mneneri wonyenga

11 Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.

12 Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha.

13 Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu.

14 Ndipo magulu a nkhondo okhala mu Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu.

15 Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.

16 Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.

17 Ndipo ndinaonamngeloalikuima m’dzuwa; ndipo anafuula ndi mau aakulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu,

18 kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi aang’ono ndi aakulu.

19 Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.

20 Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m’nyanja yamoto yakutentha ndisulufure:

21 ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m’kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/19-c254fa4c315d4a9d42a4f1ec2b47773e.mp3?version_id=1068—