Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Buku la

Chivumbulutso

lidalembedwa pa nthawi ina pamene Akhristu ankazunzidwa chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu kuti Iye ndi Ambuye. Wolemba bukuli akufuna kuwalimbitsa mtima Akhristu onse kuti akhale okhulupirika kwa Ambuye pamene akukumana ndi mavuto komanso mazunzo.

Pafupi mau onse a m’bukuli akamba za zobisika ndi zinsinsi zina ndi zina zimene mlembiyo adazimva ndi kuziwona m’masomphenya; ndipo amazilongosola mwa njira ya mafanizo ndi mau ophiphiritsa, kotero kuti Akhristu okha pa masiku akalewo ankamvetsapo mauwo, chonsecho anzao onse akunja sankatha kutulukira tanthauzo lake lenileni. Mfundo zake za bukuli amazikamba mobwerezabwereza mwa njira zosiyanasiyana, potsata zomwe zija anaziwona m’masomphenya; motero nkwapatali kutanthauzira imodziimodzi mwa nkhani zonsezo movemerezana. Komabe phunziro lalikulu lopezeka m’bukuli nlakuti, lidzafika tsiku lina pamene, kudzera mwa Khristu Ambuye, Mulungu adzagonjetsa kotheratu adani ake onse ndi Satana yemwe; ndipo adzapereka mphotho kwa anthu ake okhulupirika, adzawadalitsa poti adzakonzanso zonse kuti zikhale zatsopano.

Za mkatimu

Yohane apereka moni kwa mipingo isanu ndi iwiri 1.1-8

Aona Khristu m’masomphenya 1.9-20

Makalata olembera mipingo isanu ndi iwiri 2.1—3.22

Za m’mene amapembedzera Kumwamba 4.1-11

Za Mwanawankhosa ndi buku lomatidwa ndi zimatiro 5.1—8.1

Za angelo asanu ndi awiri oliza malipenga 8.2—11.19

Za chinjoka ndi zilombo ziwiri 12.1—13.18

Zina ndi zina zooneka m’masomphenya 14.1—15.8

Za mbale zisanu ndi ziwiri za ukali wa Mulungu 16.1-21

Za kugwa kwa Babiloni ndi kugonjetsedwa kwa Satana 17.1—20.10

Za chiweruzo chotsiriza 20.11-15

Za dziko latsopano ndi Yerusalemu watsopano 21.1—22.5

Mau otsiriza: za kubwera kwa Yesu 22.6-21

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 1

Choneneratu bukuli

1 Chivumbulutso cha YesuKhristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwamngelowake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;

2 amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona.

3 Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.

Mau a kwa Mipingo isanu ndi iwiri ya mu Asiya

4 Yohane kwaMipingoisanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;

5 ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;

6 natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi.Amen.

7 Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu.Amen.

8 Ine ndineAlefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

Yohane pa chisumbu cha Patimosi. Amlembetsa masomphenya

9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m’chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.

10 Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,

11 ndi kuti, Chimene upenya, lemba m’buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.

12 Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;

13 ndipo pakati pa zoikaponyalizo wina wongaMwana wa Munthuatavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.

14 Ndipo tsitsi la pamutu pake linali loyera ngati ubweya woyera, ngati chipale chofewa; ndi maso ake ngati lawi la moto;

15 ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m’ng’anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.

16 Ndipo m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m’kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.

17 Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,

18 ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.

19 Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m’tsogolomo;

20 chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/1-4e3de28f8fa0a8669be5a0559b81fe80.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 2

Kalata ya kwa Mpingo wa ku Efeso

1 KwamngelowaMpingowa ku Efeso lemba:

Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m’dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:

2 Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okhaatumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

3 ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.

4 Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.

5 Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.

6 Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito zaAnikolai, zimene Inenso ndidana nazo.

7 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.

Kalata yachiwiri, ya kwa Mpingo wa ku Smirina

8 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba:

Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:

9 Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatusunagogewaSatana.

10 Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

11 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.

Kalata yachitatu, ya kwa Mpingo wa ku Pergamo

12 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba:

Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse:

13 Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m’masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.

14 Komatu ndili nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.

15 Kotero uli nao akugwira chiphunzitso cha Anikolai momwemonso.

16 Chifukwa chake lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nao nkhondo ndi lupanga la m’kamwa mwanga.

17 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsamanaobisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.

Kalata yachinai, ya kwa Mpingo wa ku Tiatira

18 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba:

Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:

19 Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.

20 Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekhamneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.

21 Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake.

22 Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m’chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake.

23 Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.

24 Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikire zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.

25 Koma chimene muli nacho, gwirani kufikira ndikadza.

26 Ndipo iye amene apambana, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa paamitundu;

27 ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga;

28 ndipo ndidzampatsa iye nthanda.

29 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/2-c768222bb09d3ef2112c268cabf4c83d.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 3

Kalata yachisanu ya kwa Mpingo wa ku Sardi

1 Ndipo kwamngelowaMpingowa ku Sardi lemba:

Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.

2 Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeze ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga.

3 Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.

4 Komatu uli nao maina owerengeka mu Sardi, amene sanadetse zovala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m’zoyera; chifukwa ali oyenera.

5 Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m’buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.

6 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Kalata yachisanu ndi chimodzi, ya kwa Mpingo wa ku Filadelfiya

7 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba:

Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:

8 Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang’ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.

9 Taona, ndikupatsa ena otuluka m’sunagogewaSatanaakudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

10 Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.

11 Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako.

12 Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, laYerusalemuwatsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.

13 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Kalata yachisanu ndi chiwiri, ya kwa Mpingo wa ku Laodikea

14 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba:

Izi anena Ameni’yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:

15 Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.

16 Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula m’kamwa mwanga.

17 Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;

18 ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m’moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m’maso mwako, kuti ukaone.

19 Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.

20 Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

21 Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.

22 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/3-99f1c67c31d1d9afe245bbaca739967a.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 4

Masomphenya a mpando wachifumu wa Mulungu, akulu makumi awiri ndi anai, ndi zamoyo zinai

1 Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m’tsogolomo.

2 Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wachifumu mu Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;

3 ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.

4 Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide.

5 Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;

6 ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.

7 Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang’ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka.

8 Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m’katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

9 Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,

10 akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,

11 Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/4-84d53023eff90426f63f347aba9f3a83.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 5

Buku losindikizika ndi zosindikiza zisanu ndi ziwiri. Mwanawankhosa yekha ayenera kulitsegula

1 Ndipo ndinaona m’dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m’kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.

2 Ndipo ndinaonamngelowamphamvu wakulalikira ndi mau aakulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?

3 Ndipo sanathe mmodzi mu Mwamba, kapena padziko, kapena pansi padziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya.

4 Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezeke mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;

5 ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m’fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.

6 Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu,Mwanawankhosaali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m’dziko lonse.

7 Ndipo anadza, nalitenga kudzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu.

8 Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.

9 Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,

10 ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.

11 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;

12 akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.

13 Ndipo cholengedwa chilichonse chili m’mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m’nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.

14 Ndipo zamoyo zinai zinati,Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/5-1a3c586f1556b4a4292da3a3a3a6094d.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 6

Atsegula zosindikiza zisanu ndi chimodzi

1 Ndipo ndinaona pameneMwanawankhosaanamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, chikunena, ngati mau a bingu, Idza.

2 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wogonjetsa kuti akagonjetse.

3 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chikunena, Idza.

4 Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.

5 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikunena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m’dzanja lake.

6 Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.

7 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachinai, ndinamva mau a chamoyo chachinai chikunena, Idza.

8 Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.

9 Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao:

10 ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?

11 Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.

12 Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;

13 ndi nyenyezi zam’mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zake zosapsa, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.

14 Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m’malo mwao.

15 Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;

16 nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kumkwiyo wa Mwanawankhosa;

17 chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/6-b2e136da52be9b6e48d3d36a89790b1e.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 7

Aisraele okhulupirika alanditsidwa

1 Zitatha izi ndinaonaangeloanai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse.

2 Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau aakulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,

3 nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.

4 Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele.

5 Mwa fuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro

zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri.

6 Mwa fuko la Asere zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Nafutali zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri.

7 Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.

8 Mwa fuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Benjamini anasindikizidwa chizindikiro

zikwi khumi ndi ziwiri.

Maonekedwe mu ulemerero a iwo amene anaphedwa chifukwa cha Khristu

9 Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso paMwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwao;

10 ndipo afuula ndi mau aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.

11 Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu,

12 ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

13 Ndipo mmodzi wa akulu anayankha, nanena ndi ine, Iwo ovala zovala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti?

14 Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.

15 Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,

16 sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chilichonse;

17 chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/7-f8842cc0f040e91856d1649f1f13074d.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 8

Atsegula chosindikiza chachisanu ndi chiwiri. Angelo asanu ndi awiri, ndi malipenga oyamba anai

1 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete mu Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.

2 Ndipo ndinaonaangeloasanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.

3 Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.

4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m’dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.

5 Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.

6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.

7 Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.

8 Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m’nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;

9 ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m’nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.

10 Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;

11 ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa.

12 Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.

13 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/8-9189d1753cce6e725ef86f55970fabbb.mp3?version_id=1068—

Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 9

Lipenga lachisanu, tsoka loyamba

1 Ndipomngelowachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya.

2 Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m’chiphomphomo, ngati utsi wa ng’anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho.

3 Ndipo mu utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu.

4 Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena chabiriwiri chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pao ndiwo.

5 Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu.

6 Ndipo m’masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.

7 Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.

8 Ndipo anali nalo tsitsi longa tsitsi la akazi, ndipo mano ao anali ngati mano a mikango.

9 Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko ao ngati mkokomo wa agaleta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.

10 Ndipo lili nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola; ndipo m’michira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.

11 Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.

Lipenga lachisanu ndi chimodzi, tsoka lachiwiri

12 Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso matsoka awiri m’tsogolomo.

13 Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu,

14 nanena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pamtsinje waukulu Yufurate.

15 Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu.

16 Ndipo chiwerengero cha nkhondo za apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndinamva chiwerengero chao.

17 Ndipo kotero ndinaona akavalo m’masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndisulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m’kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure.

18 Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulufure, zotuluka m’kamwa mwao.

19 Pakuti mphamvu ya akavalo ili m’kamwa mwao, ndi m’michira yao; pakuti michira yao ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo aipsa nayoyo.

20 Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;

21 ndipo sanalape mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/9-d2dc29ee07a55f3b89f8404ac7b47010.mp3?version_id=1068—