Ayuda anataya chilungamo cha Mulungu
1 Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.
2 Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
3 Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.
4 PakutiKhristuali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa aliyense amene akhulupirira.
5 Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m’lamulo, adzakhala nacho ndi moyo.
6 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? Ndiko, kutsitsako Khristu;
7 kapena, Adzatsikira ndani ku chiphompho chakuya? Ndiko, kukweza Khristu kwa akufa,
8 Koma chitani? Mau ali pafupi ndiwe, m’kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:
9 kuti ngati udzavomereza m’kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:
10 pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m’kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.
11 Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi.
12 Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye;
13 pakuti, aliyense amene adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.
14 Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?
15 Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.
16 Koma sanamvere Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?
17 Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Khristu.
18 Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu,
Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi,
ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.
19 Koma nditi, Kodi Israele alibe kudziwa? Poyamba Mose anena,
Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo
amene sakhala mtundu wa anthu,
ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.
20 Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati,
Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifune;
ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunse.
21 Koma kwa Israele anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/10-314b137f34fede060bc9942c7fb5e0f2.mp3?version_id=1068—