Categories
AROMA

AROMA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata ya Paulo kwa Aroma

inalembedwa pofuna kukonzekera za ulendo wa Paulo wopita ku mpingo wa ku Roma. Cholinga chake chinali chakuti akagwire ntchito ndi Akhristu a kumeneko kwa kanthawi, kenaka mothandizidwa ndi iwo, akapitirire mpaka ku dziko la Speini. Iye analemba kalatayi pofuna kufotokozera za m’mene iye amachidziwira Chikhristu komanso m’mene Chikhristucho chimayenera kuwongolera moyo okhulupirira. Uthenga wonse umene Paulo amalalikira ukupezeka mu bukuli.

Atatha kuwalonjera anthu a ku mpingo wa ku Roma ndi kuwapempherera, Paulo akunena za mutu wa kalatayi umene uli woti, “Pakuti m’menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro” (1.17).

Kenaka Paulo akutambasula mutu wake wa nkhani. Anthu onse, Ayuda ndi akunja omwe, afunika kuti alungamitsidwe ndi Mulungu, popeza onse ali pansi pa mphamvu ya uchimo. Anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu kudzera mu kukhulupirira Yesu Khristu. Kenaka Paulo akulongosola za moyo watsopano umene upezeka polumikizana ndi Yesu. Izi zimachokera mu ubale watsopano ndi Mulungu umene munthu amakhala nao. Okhulupirira ali ndi mtendere ndi Mulungu ndipo Mzimu wa Mulungu amawamasula kuchokera ku mphamvu ya uchimo ndi ya imfa. Mu mutu 5—8 Paulo akunena za cholinga cha lamulo la Mulungu ndi mphamvu ya Mzimu wa Mulungu pa moyo wa okhulupirira. Kenaka mtumwiyu akulimbana ndi funso lakuti kodi Ayuda ndi akunja akulowa bwanji mu cholinga cha Mulungu pa anthu onse. Kenaka akumaliza ponena kuti zimene adachita Ayuda pomukana Yesu chinali chikonzero cha Mulungu pofuna kuti anthu ena onse alandire chisomo cha Mulungu chimene chipezeka mwa Khristu Yesu, ndipo iye akukhulupirira kuti Ayuda sadzakana Khristu mpaka kalekale. Potsiriza penipeni, Paulo akulemba za makhalidwe abwino a Chikhristu, makamaka za kukondana wina ndi mnzake. Akulembanso za mitu ina monga kutumikira Mulungu, udindo wa Akhristu m’dziko lao komanso kwa anzao, ndi nkhani yokhudza chikumbumtima. Iye akumaliza kalata yakeyo ndi uthenga wolembera anzake komanso mau oyamika Mulungu.

Za mkatimu

Mau oyamba komanso mutu wa kalata 1.1-17

Kufunikira kwa chipulumutso 1.18—3.20

Njira ya Mulungu ya chipulumutso 3.21—4.25

Moyo watsopano mwa Khristu 5.1—8.39

Cholinga cha Mulungu pa fuko la Israele 9.1—11.36

Makhalidwe abwino a Chikhristu 12.1—15.13

Mau omaliza komanso malonje 15.14—16.27

Categories
AROMA

AROMA 1

1 Paulo, kapolo wa YesuKhristu,mtumwiwoitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,

2 umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m’malembo oyera,

3 wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,

4 amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;

5 amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;

6 mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Khristu;

7 kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Paulo ayamika Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro cha Aroma. Afuna kucheza nao

8 Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.

9 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,

10 ndi kupempha masiku onse m’mapemphero anga, ngati nkutheka tsopano mwa chifuniro cha Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.

11 Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;

12 ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.

13 Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthuamitunduena.

Uthenga wake wa Paulo wakuti anthu ayesedwa olungama mwa chikhulupiriro

14 Ine ndili wamangawa wa Agriki ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.

15 Chotero, momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.

16 Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.

17 Pakuti m’menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.

Kuipitsitsa kwa anthu

18 Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m’chosalungama chao;

19 chifukwa chodziwika cha Mulungu chaonekera m’kati mwao; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo.

20 Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

21 chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m’maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.

22 Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

23 nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

24 Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m’zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;

25 amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha.Amen.

26 Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe:

27 ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.

28 Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m’chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;

29 anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;

30 akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,

31 opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;

32 amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/1-8b6387114411c45a4e1acbb8af72c150.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 2

Kusamvera kwa Ayuda

1 Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m’mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.

2 Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere.

3 Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu?

4 Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?

5 Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;

6 amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake;

7 kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;

8 koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,

9 nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mgriki;

10 koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki;

11 pakuti Mulungu alibe tsankho.

12 Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;

13 pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.

14 Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;

15 popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m’mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana;

16 tsiku limene Mulungu adzaweruza ndiKhristuYesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.

Ayuda atsutsidwa

17 Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu,

18 nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m’chilamulo,

19 nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,

20 wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m’chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi;

21 ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?

22 Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi?

23 Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo?

24 Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.

Mdulidwe woona

25 Pakuti indemdulidweuli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa.

26 Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe?

27 Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?

28 Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo;

29 koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/2-20bf2115e952ec289bbd0355776589b8.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 3

Kuposa kwake kwa Myuda. Mulungu ali wolungama

1 Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapenamdulidweupindulanji?

2 Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.

3 Nanga bwanji ngati ena sanakhulupirire? Kodi kusakhulupirira kwao kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu?

4 Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndipo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa,

Kuti Inu mukayesedwe wolungama m’maneno anu,

ndi kuti mukapambane m’mene muweruzidwa.

5 Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (Ndilankhula umo anenera munthu).

6 Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi?

7 Pakuti ngati choonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa?

8 Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.

Anthu onse agwidwa ndi zoipa

9 Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;

10 monga kwalembedwa,

Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;

11 palibe mmodzi wakudziwitsa,

palibe mmodzi wakulondola Mulungu;

12 onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake;

palibe mmodzi wakuchita zabwino,

inde, palibe mmodzi ndithu.

13 M’mero mwao muli manda apululu;

ndi lilime lao amanyenga;

ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;

14 m’kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;

15 miyendo yao ichita liwiro kukhetsa mwazi;

16 kusakaza ndi kusauka kuli m’njira zao;

17 ndipo njira ya mtendere sanaidziwe;

18 kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.

19 Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;

20 chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.

Tilungamitsidwa mwa kukhulupirira Yesu Khristu

21 Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni;

22 ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa YesuKhristukwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;

23 pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

24 ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu;

25 amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m’mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m’kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;

26 kuti aonetse chilungamo chake m’nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.

27 Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro.

28 Pakuti timuyesa munthu wolungama chifukwa cha chikhulupiriro, wopanda ntchito za lamulo.

29 Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso:

30 ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro.

31 Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/3-4f68932a39b35594dc8e76710c42fc4f.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 4

Abrahamu anayesedwa wolungama ndi chikhulupiriro

1 Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, analandira chiyani?

2 Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai.

3 Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo chinawerengedwa kwa iye chilungamo.

4 Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siiwerengedwa ya chisomo koma ya mangawa.

5 Koma kwa iye amene sachita, koma akhulupirira Iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo.

6 Monganso Davide anena za mdalitso wake wa munthu, amene Mulungu amwerengera chilungamo chopanda ntchito,

7 ndi kuti,

Odala iwo amene akhululukidwa kusaweruzika kwao,

nakwiriridwa machimo ao.

8 Wodala munthu amene Ambuye samwerengera uchimo.

9 Mdalitso umenewu tsono uli kwa odulidwa kodi, kapena kwa osadulidwa omwe? Pakuti timati, Chikhulupiriro chake chinawerengedwa kwa Abrahamu chilungamo.

10 Tsono chinawerengedwa bwanji? M’mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa;

11 iye ndipo analandira chizindikiro cha mdulidwe, ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye anali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupirira, angakhale iwo sanadulidwe, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso;

12 ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe.

13 Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwe kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.

14 Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pake;

15 pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa.

16 Chifukwa chake chilungamo chichokera m’chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;

17 monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.

18 Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere.

19 Ndipo iye osafooka m’chikhulupiriro sanalabadire thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;

20 ndipo poyang’anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,

21 nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.

22 Chifukwa chake ichi chinawerengedwa kwa iye chilungamo.

23 Ndipo ichi sichinalembedwe chifukwa cha iye yekhayekha, kuti chidawerengedwa kwa iye;

24 koma chifukwa cha ifenso, kwa ife amene chidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira Iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu,

25 amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/4-0ca2ce1a9d31c74f0a138130de4ae015.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 5

Zipatso za chikhulupiriro

1 Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu YesuKhristu;

2 amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m’chisomo ichi m’mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.

3 Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m’zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

4 ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

5 ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

6 Pakuti pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Khristu anawafera osapembedza.

7 Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.

8 Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

9 Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.

10 Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.

11 Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.

Uchimo unalowa ndi Adamu, chilungamo ndi Khristu

12 Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.

13 Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo unali m’dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo.

14 Komatu imfa inachita ufumu kuyambira kwaAdamukufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanachimwe monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo.

15 Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Khristu, zinachulukira anthu ambiri.

16 Ndipo mphatso siinadze monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.

17 Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m’moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu.

18 Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.

19 Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.

20 Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;

21 kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/5-96bd378298c85b9755d569d11db7ec9d.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 6

Khristu anatithyolera mphamvu ya zoipa

1 Chifukwa chake tidzatani? Tidzakhalabe mu uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke?

2 Msatero ai. Ife amene tili akufa ku uchimo, tidzakhala bwanji chikhalire m’menemo?

3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwaKhristuYesu; tinabatizidwa mu imfa yake?

4 Chifukwa chake tinaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano.

5 Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake;

6 podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;

7 pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo.

8 Koma ngati ife tinafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye;

9 podziwa kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa Iye.

10 Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

11 Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.

12 Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake:

13 ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

14 Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.

Ife ndife akapolo a Mulungu

15 Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai.

16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?

17 Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho;

18 ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo.

19 Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusaweruzika kuti zichite kusaweruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso.

20 Pakuti pamene inu munali akapolo a uchimo, munali osatumikira chilungamo.

21 Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m’zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa.

22 Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.

23 Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/6-0f1725adfc408b320f4274140008d737.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 7

Okhulupirira akwatiwa ndi Khristu

1 Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulolo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo?

2 Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.

3 Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.

4 Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi laKhristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso.

5 Pakuti pamene tinali m’thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m’ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.

6 Koma tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m’chilembo chakale ai.

Malamulo aonetsa zoipa

7 Pamenepo tidzatani? Kodi chilamulo chili uchimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire;

8 koma uchimo, pamene unapeza chifukwa, unachita m’kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo uchimo uli wakufa.

9 Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.

10 Ndipo lamulo, limene linali lakupatsa moyo, ndinalipeza lakupatsa imfa.

11 Pakuti uchimo, pamene unapeza chifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo.

12 Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.

Kulimbana m’kati mwanga

13 Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo.

14 Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.

15 Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi.

16 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino.

17 Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m’kati mwanga ndiwo.

18 Pakuti ndidziwa kuti m’kati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.

19 Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.

20 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m’kati mwanga ndiwo.

21 Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko.

22 Pakuti monga mwa munthu wa m’kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu:

23 koma ndiona lamulo lina m’ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m’ziwalo zanga.

24 Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?

25 Ndiyamika Mulungu, mwa YesuKhristuAmbuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/7-7bcd7c3c6c367435646a8a25a1011f7a.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 8

Moyo wathu watsopano mwa Khristu

1 Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwaKhristuYesu alibe kutsutsidwa.

2 Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

3 Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m’chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m’thupi;

4 kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.

5 Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:

6 pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.

7 Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.

8 Ndipo iwo amene ali m’thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

9 Koma inu simuli m’thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.

10 Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo.

11 Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.

Ife ndife ana a Mulungu

12 Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi;

13 pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.

14 Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.

15 Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti,Abba!Atate!

16 Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

17 ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.

Zolengedwa zonse zilindira ana a Mulungu

18 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

19 Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu.

20 Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo

21 kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.

22 Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.

23 Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tili nazo zipatso zoyamba za Mzimu, inde ifenso tibuula m’kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu.

24 Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?

25 Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.

26 Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;

27 ndipo Iye amene asanthula m’mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuniro cha Mulungu.

28 Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

29 Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;

30 ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.

Mulungu ali nafe, adzatitsutsa ndani?

31 Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

32 Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

33 Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama;

34 ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso padzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.

35 Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?

36 Monganso kwalembedwa,

Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse;

tinayesedwa monga nkhosa zakupha.

37 Koma m’zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

38 Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhaleangelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,

39 ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/8-89ca632bfc66b85ddf94d2f11f685d49.mp3?version_id=1068—

Categories
AROMA

AROMA 9

Paulo alirira kusamvera kwa Israele

1 Ndinena zoona mwaKhristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,

2 kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.

3 Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;

4 ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;

5 a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse.Amen.

Ulamuliro wa Mulungu wakusankha ena

6 Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;

7 kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.

8 Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.

9 Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.

10 Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;

11 pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,

12 chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.

13 Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.

14 Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.

15 Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.

16 Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.

17 Pakuti lembo linena kwaFarao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe padziko lonse lapansi.

18 Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.

19 Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuniro chake?

20 Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?

21 Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?

22 Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?

23 Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero,

24 ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthuamitundu?

25 Monga atinso mwa Hoseya,

Amene sanakhale anthu anga, ndidzawatcha anthu anga;

ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.

26 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo,

Simuli anthu anga ai,

pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.

27 Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti,

Ungakhale unyinji wa ana a Israele

ukhala monga mchenga wa kunyanja,

chotsalira ndicho chidzapulumuka.

28 Pakuti Ambuye adzachita mau ake padziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule.

29 Ndipo monga Yesaya anati kale,

Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyire ife mbeu,

tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.

30 Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsate chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;

31 koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikile lamulolo.

32 Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsate ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pamwala wokhumudwitsa;

33 monganso kwalembedwa, kuti,

Onani, ndikhazika muZiyonimwala wakukhumudwa nao,

ndi thanthwe lophunthwitsa;

ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/9-2655e52f3220d2f89befdc76f3743a7c.mp3?version_id=1068—