Categories
AHEBRI

AHEBRI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mlembi wa

Kalata yolembera kwa Ahebri

akufuna kuwalimbitsa mtima Akhristu ena okhala pakati pa anthu ena amene amawavutitsa, kuti asafooke pa chikhulupiriro chao, kuwopa kuti angasiye Chikhristu. Awaonetsa kuti chikhulupiriro choona maziko ake ndi Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Wansembe wamuyaya, amene apulumutsa omkhulupirira pakuwayanjanitsa ndi Mulungu.

Iye yekha pokhala Mkulu wa ansembe atha kupulumutsa anthu okhulupirira kumachimo, mantha ndi imfa; nsembe zakale zija zinkangofanizira nsembe yeniyeni yomwe Yesu adaipereka pakufera anthu onse.

Mau aakulu mu buku limeneli ali pa 5.8-9 pamene akunena za Yesu kuti, “angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”

Pa mutu 11 iye akupereka zitsanzo za chikhulupiriro cha Aisraele ena otchuka, ndipo akuwauza awerengi ake kuti akhalebe okhulupirika. Pa mutu 12, akuwauzanso kuti akhalebe wokhulupirika mpaka mapeto, nakhazike maso ao pa Yesu, ndi kupirira pamene akumana ndi mazunzo kapena masautso. Bukuli likumaliza ndi malangizo komanso machenjezo.

Za mkatimu

Mulungu adziwululira chonse kudzera mwa Khristu 1.1-3

Za ukulu wake wa Khristu, Mwana wa Mulungu 1.4—4.13

Aposa angelo 1.4-14

Khristu mtsogoleri wa chipulumutso 2.1-18

Aposa Mose yemwe 3.1—4.13

Za ukulu wa unsembe wa Khristu 4.14—10.39

Unsembe wake ndi wamuyaya, apambana Melkizedeki 4.14—7.28

Ukulu wa chipangano chake 8.1—9.28

Ukulu wa nsembe yake 10.1-38

Za chikhulupiriro cha anthu ake 11.1-40

Za chitsanzo cha Yesu Khristu 12.1-29

Mau otsiriza: za m’mene tingakondweretsere Mulungu 13.1-25

Categories
AHEBRI

AHEBRI 1

Khristu Mwana wa Mulungu aposatu angelo

1 Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,

2 koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am’mwamba omwe;

3 ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m’mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,

4 atakhala wakuposaangelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.

5 Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse,

Iwe ndiwe Mwana wanga,

lero Ine ndakubala Iwe?

Ndiponso,

Ine ndidzakhala kwa Iye Atate,

ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?

6 Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m’dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.

7 Ndipo za angelo anenadi,

Amene ayesa angelo ake mizimu,

ndi omtumikira Iye akhale malawi amoto.

8 Koma ponena za Mwana, ati,

Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi;

ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

9 Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa;

mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani

ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.

10 Ndipo,

Inu, Ambuye, pachiyambipo munaika maziko ake a dziko,

ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu.

11 Iyo idzataika; komatu mukhalitsa;

ndipo iyo yonse idzasuka monga malaya;

12 ndi monga chofunda mudzaipinda

monga malaya, ndipo idzasanduka;

koma Inu ndinu yemweyo,

ndipo zaka zanu sizidzatha.

13 Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?

14 Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/1-23bb154486015fdb374ae1f4924c7f6c.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 2

Yesu Khristu Nkhoswe yathu yakuposa angelo akhoza kumva nafe chifundo

1 Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.

2 Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndiangeloadakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama,

3 tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;

4 pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

5 Pakuti sanagonjetsere angelo dziko lilinkudza limene tinenali.

6 Koma wina anachita umboni pena, nati,

Munthu nchiyani kuti mumkumbukira iye?

Kapena mwana wa munthu kuti mucheza naye?

7 Munamchepsa pang’ono ndi angelo,

mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu,

ndipo mudamuika iye woyang’anira ntchito za manja anu;

8 mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake.

Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyepo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayambe tsopano apa kuona zonse zimgonjera.

9 Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang’ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.

10 Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.

11 Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.

12 Ndi kuti,

Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,

pakati paMpingondidzakuimbirani.

13 Ndiponso,

Ndidzamtama Iye.

Ndiponso,

Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.

14 Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;

15 nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m’moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

16 Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.

17 Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m’zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

18 Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/2-fc1a794c8b98ac9014c20c24cf8d9571.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 3

Khristu ali wamkulu woposa Mose. Awachenjeza amkhulupirire

1 Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani zaMtumwindi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;

2 amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m’nyumba yake yonse.

3 Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.

4 Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.

5 Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m’nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;

6 komaKhristumonga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.

7 Momwemo, monga anena Mzimu Woyera,

Lero ngati mudzamva mau ake,

8 musaumitse mitima yanu, monga m’kupsetsa mtimamo,

monga muja tsiku la chiyesero m’chipululu,

9 chimene makolo anu anandiyesa nacho,

ndi kundivomereza,

naona ntchito zanga zaka makumi anai.

10 Momwemo ndinakwiya nao mbadwo uwu,

ndipo ndinati, Nthawi zonse amasochera mumtima;

koma sanazindikire njira zanga iwowa;

11 Monga ndinalumbira mu ukali wanga:

Ngati adzalowa mpumulo wanga!

12 Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;

13 komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;

14 pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;

15 umo anenamo,

Lero ngati mudzamva mau ake,

musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.

16 Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka mu Ejipito ndi Mose?

17 Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m’chipululu?

18 Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?

19 Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanathe kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/3-1b80048748c76343deb8ff6d48e2b716.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 4

1 Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.

2 Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.

3 Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena,

Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga,

ngati adzalowa mpumulo wanga.

Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.

4 Pakuti wanena pena za tsiku lachisanu ndi chiwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse.

5 Ndipo m’menemonso,

Ngati adzalowa mpumulo wanga.

6 Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowemo chifukwa cha kusamvera,

7 alangizanso tsiku lina, ndi kunena mu Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale,

Lero ngati mudzamva mau ake,

musaumitse mitima yanu.

8 Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m’tsogolomo za tsiku lina.

9 Momwemo utsalira mpumulo waSabatawa kwa anthu a Mulungu.

10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.

11 Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwe cha kusamvera.

12 Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

13 Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Khristu aposa akulu a ansembe

14 Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.

15 Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.

16 Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/4-3149056aa2f36539013e78c49169a9d9.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 5

1 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:

2 akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko;

3 ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m’malo a anthuwo, moteronso m’malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo.

4 Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.

5 KoteronsoKhristusanadzilemekeze yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye,

Mwana wanga ndi Iwe,

lero Ine ndakubala Iwe.

6 Monga anenanso mwina,

Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse

monga mwa dongosolo laMelkizedeki.

7 Ameneyo, m’masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,

8 angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;

9 ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;

10 wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.

11 Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otivuta powatanthauzira, popeza mwagontha m’makutu.

12 Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.

13 Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mau a chilungamo; pakuti ali khanda.

14 Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/5-0baa21da20182abcb79fbe6663f03bb7.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 6

1 Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe chaKhristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,

2 a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.

3 Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.

4 Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,

5 nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza,

6 koma anagwa m’chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.

7 Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:

8 koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang’ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.

9 Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;

10 pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

11 Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro;

12 kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.

13 Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,

14 nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.

15 Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.

16 Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m’chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.

17 Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;

18 kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m’mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;

19 chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m’katikati mwa chophimba;

20 m’mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo laMelkizedeki.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/6-82e75569e42eda650050838c72d7806c.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 7

Mkulu wa ansembe Melkizedeki afanizira Yesu Khristu, Mkulu wa ansembe wosatha

1 PakutiMelkizedekiuyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,

2 amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;

3 wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.

4 Koma tapenyani ukulu wake wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.

5 Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m’chuuno cha Abrahamu;

6 koma iye amene mawerengedwe a chibadwidwe chake sachokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.

7 Ndipo popanda chitsutsano konse wamng’ono adalitsidwa ndi wamkulu.

8 Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo.

9 Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzilimodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi;

10 pakuti pajapo anali m’chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye.

11 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?

12 Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.

13 Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

14 Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.

15 Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melkizedeki,

16 amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;

17 pakuti amchitira umboni,

Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha

monga mwa dongosolo la Melkizedeki.

18 Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufooka kwake, ndi kusapindulitsa kwake,

19 (pakuti chilamulo sichinachitire kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu.

20 Ndipo monga momwe sikudachitike kopanda lumbiro; (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro;

21 koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye,

Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa,

iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).

22 Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

23 Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe;

24 koma Iye chifukwa kuti akhala Iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika,

25 kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.

26 Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;

27 amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.

28 Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/7-9d9ec56309a6379cd9fb8c102a1fc383.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 8

Yesu ali Mkulu wa ansembe wa chipangano chatsopano

1 Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,

2 Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.

3 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka.

4 Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo;

5 amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m’mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m’phiri.

6 Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.

7 Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo.

8 Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena,

Taonani, akudza masiku, anena Ambuye,

Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele,

ndi nyumba ya Yuda,

9 losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao,

tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera

atuluke m’dziko la Ejipito;

kuti iwo sanakhalebe m’pangano langa,

ndipo Ine sindinawasamalire iwo, anena Ambuye.

10 Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele,

atapita masiku ajawa, anena Ambuye:

Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m’nzeru zao,

ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo;

ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu,

ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:

11 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzake,

ndipo yense mbale wake, ndi kuti, Zindikira Ambuye:

Pakuti onse adzadziwa Ine,

kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo.

12 Kuti ndidzachitira chifundo zosalungama zao,

ndipo zoipa zao sindidzazikumbukanso.

13 Pakunena Iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma chimene chilinkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/8-929b266e7ccf7e0442c70f84c3911183.mp3?version_id=1068—

Categories
AHEBRI

AHEBRI 9

Za chipembedzo chapansipano ndi cha Kumwamba

1 Ndipo chingakhalechipanganochoyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a padziko lapansi.

2 Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m’menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.

3 Koma m’kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;

4 okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndilikasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamomana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;

5 ndi pamwamba pakeakerubia ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.

6 Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m’chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;

7 koma kulowa m’chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;

8 Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;

9 ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m’mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.

10 Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.

11 Koma atafikaKhristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,

12 kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.

13 Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, ndi makala a ng’ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi;

14 koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

15 Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.

16 Pakuti pamene pali chopangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo.

17 Pakuti chopangiratu chiona mphamvu atafa mwini wake; popeza chilibe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo;

18 momwemo choyambachonso sichinakonzeke chopanda mwazi.

19 Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang’ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndihisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,

20 nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulani.

21 Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo.

22 Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.

23 Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za mu Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam’mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.

24 Pakuti Khristu sanalowe m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;

25 kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m’malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;

26 chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.

27 Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;

28 kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/9-67a079c898aa703b3583f8198bc625eb.mp3?version_id=1068—