Categories
AGALATIYA

AGALATIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Pamene uthenga wabwino wonena za Yesu unayamba kulalikidwa ndi kulandiridwa pakati pa anthu amene sanali Ayuda, funso lalikulu limene limafunsidwa linali lakuti:

Kodi ndikoyenera kuti munthu atsatire Malamulo a Mose ngati akufuna kukhala Mkhristu?

Paulo ananena kuti izi sizinali zoyenera. Iye anatinso chofunika pa moyo wotsatira Khristu ndi ndicho chakuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhulupirira Khristu basi. Komabe pakati pa mipingo ya ku Galatiya, limene linali dera la ku Asiya, panali anthu amene anabwera ndi kumasutsana ndi Paulo ponena kuti munthu ayenera kutsata Malamulo a Mose ngati akufuna alungamitsidwe ndi Mulungu.

Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Agalatiya

inalembedwa pofuna kukonza chiphunzitso cholakwikachi chimene ena anabweretsa ndi kupotoza nacho anthu anzao. Paulo anayamba pa kuteteza udindo wake monga mtumwi wa Yesu Khristu. Iye anatsindika mfundo yakuti maitanidwe ake kukhala mtumwi anachokera kwa Mulungu, osati kwa munthu, ndiponso kuti utumiki wake unali wa kwa anthu sanali Ayuda. Kenaka akufotokoza kuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhapokha pamene akhulupirira. Mu mitu yomalizira, Paulo akutionetsa kuti khalidwe labwino la Chikhristu limachokera ku chikondi chimene chimapezeka pamene munthu wakhulupirira Yesu.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-10

Ulamuliro wa Paulo pokhala mtumwi 1.11—2.21

Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu 3.1—4.31

Ufulu ndi udindo wa Mkhristu 5.1—6.10

Mau omaliza 6.11-18

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 1

1 Paulo,mtumwi(wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa YesuKhristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),

2 ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwaMipingoya ku Galatiya:

3 Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,

4 amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m’nyengo ya pansi pano ino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;

5 yemweyo akhale nao ulemerero kunthawi za nthawi.Amen.

Kupatuka kwa Agalatiya. Utumiki wa Paulo uchokera kwa Mulungu

6 Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m’chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina;

7 umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.

8 Koma ngakhale ife, kapenamngelowochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.

9 Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.

10 Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.

11 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.

12 Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa vumbulutso la Yesu Khristu.

13 Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,

14 ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.

15 Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,

16 kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwaamitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi:

17 kapena kukwera kunka kuYerusalemusindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.

18 Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.

19 Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

20 Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.

21 Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.

22 Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu;

23 koma analinkumva kokha, kuti, Iye wakutilondalonda ife kale, tsopano alalikira chikhulupirirocho adachipasula kale;

24 ndipo analemekeza Mulungu mwa ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/1-2989d8251c665c21feacbd381510f64b.mp3?version_id=1068—

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 2

1 Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka kuYerusalemupamodzi ndi Barnabasi, ndinamtenganso Tito andiperekeze.

2 Koma ndinakwera kunkako movumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwaamitundu; koma m’tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga chabe.

3 Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mgriki, sanamkakamize adulidwe;

4 ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m’tseri, amene analowa m’tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwaKhristuYesu, kuti akatichititse ukapolo.

5 Koma sitidawafumukire mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi inu.

6 Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezere ine kanthu;

7 koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe

8 (pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);

9 ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;

10 pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.

11 Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa.

12 Pakuti asanafike ena ochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.

13 Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m’maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m’maso kwao.

14 Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?

15 Ife ndife Ayuda pachibadwidwe, ndipo sitili ochimwa a kwa amitundu;

16 koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.

17 Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Khristu, tipezedwanso tili ochimwa tokha, kodi Khristu ali mtumiki wa uchimo chifukwa chake? Msatero ai.

18 Pakuti ngati izi zomwezi ndazigumula ndidzimanganso, ndidzitsimikizira ndekha ndili wolakwa.

19 Pakuti ine mwa lamulo ndafa kulamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.

20 Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m’thupi, ndili nao m’chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

21 Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/2-385591379d34146934138156cddba972.mp3?version_id=1068—

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 3

Chilamulo sichingathe kupulumutsa; chititsogolera kutifikitsa kwa Khristu

1 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene YesuKhristuanaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?

2 Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?

3 Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?

4 Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwachabe? Ngatitu kwachabe.

5 Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?

6 Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye chilungamo,

7 chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.

8 Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungamaamitundundi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.

9 Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.

10 Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa,

Wotembereredwa aliyense

wosakhala m’zonse zolembedwa

m’buku la chilamulo, kuzichita izi.

11 Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro;

12 koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.

13 Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu; pakuti kwalembedwa,

Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.

14 Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.

15 Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.

16 Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.

17 Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.

18 Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.

19 Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndiangelom’dzanja la nkhoswe.

20 Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.

21 Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.

22 Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.

23 Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwinobwino.

24 Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.

25 Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.

26 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

27 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

28 Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.

29 Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/3-93bca78fb47160ab321381a8bdc8b7c3.mp3?version_id=1068—

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 4

Uthenga Wabwino utimasula kuchilamulo

1 Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse;

2 komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wake.

3 Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;

4 koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,

5 kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.

6 Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m’mitima yathu, wofuulaAbba!Atate!

7 Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.

8 Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m’chibadwidwe chao;

9 koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?

10 Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka.

11 Ndiopera inu, kuti kapena ndadzivutitsa ndi inu chabe.

12 Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitire choipa ine;

13 koma mudziwa kuti m’kufooka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba:

14 ndipo chija cha m’thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputse, kapena sichinakunyansireni, komatu munandilandira ine mongamngelowa Mulungu, mongaKhristuYesu mwini.

15 Pamenepo thamo lanu lili kuti? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.

16 Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?

17 Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.

18 Koma nkwabwino kuchita changu m’zabwino nthawi zonse, si pokhapokha pokhala nanu pamodzi ine.

19 Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,

20 koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; chifukwa ndisinkhasinkha nanu.

Sara ndi Hagara atifanizira mapangano awiriwo

21 Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo?

22 Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana aamuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.

23 Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa;

24 pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.

25 Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, mu Arabiya, nafanana ndiYerusalemuwa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake.

26 Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.

27 Pakuti kwalembedwa,

Kondwera, chumba iwe wosabala;

imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala;

pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka

koposa ana a iye ali naye mwamuna.

28 Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano.

29 Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano.

30 Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.

31 Chifukwa chake, abale, sitili ana a mdzakazi, komatu a mfulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/4-08a091e377d42d53ad74a50678e5b0ac.mp3?version_id=1068—

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 5

Asunge ufulu wa Chikhristu

1 Khristuanatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

2 Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu.

3 Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.

4 Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.

5 Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m’chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.

6 Pakuti mwa Khristu Yesu kapenamdulidwekapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.

7 Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?

8 Kukopa kumene sikuchokera kwa Iye anakuitanani.

9 Chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse.

10 Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake.

11 Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha.

12 Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.

13 Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

14 Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

15 Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.

Ntchito za thupi ndi zipatso za Mzimu

16 Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.

17 Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.

18 Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.

19 Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,

20 kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,

21 njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

22 Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

23 chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

24 Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.

25 Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

26 Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/5-6874a9a58b60e6c51c47ab4708aedf46.mp3?version_id=1068—

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 6

Malangizo otsiriza, kulawirana

1 Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

2 Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo chaKhristu.

3 Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.

4 Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.

5 Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.

6 Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m’zonse zabwino.

7 Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

8 Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

9 Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

10 Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.

11 Taonani, malembedwe aakuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.

12 Onse amene afuna kuonekera okoma m’thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu.

13 Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m’thupi lanu.

14 Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.

15 Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.

16 Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.

17 Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m’thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.

18 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/6-33f06d7807d214f1000b3d38fa06dd0c.mp3?version_id=1068—