Categories
AFILIPI

AFILIPI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Afilipi

inalembedwa ku mpingo woyamba umene Paulo anakhazikitsa ku Ulaya. Kalatayi inalembedwa pamene mtumwiyo anali m’ndende, ndipo pamene amavutitsidwa ndi Akhristu ena amene amatsutsana ndi Paulo ndipo iye anakhumudwa chifukwa cha chiphunzitso chonyenga mu mpingo wa Filipi. Komabe m’kalatayi muli chimwemwe ndi kutsimikizika mtima kumene kukupezeka chifukwa cha chikhulupiriro chozama mwa Yesu Khristu chimene Paulo anali nacho.

Chifukwa choyambirira cholembera kalatayi chinali kuwathokoza Akhristu a ku Filipi chifukwa cha mphatso imene iwo anatumiza kuti imuthandize panthawi imene iye anali kusowa. Tsono Pauloyo anagwiritsa ntchito mwayiwu pofuna kuwatsimikizira kuti iwo alimbike mtima ndi kuchilimika ngakhale iye anali pa mavuto amene anali mavuto awonso. Iye akuwadandaulira kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa ngati wa Yesu, m’malo mokhala moyo wodzikonda ndi wodzitukumula. Iye akuwakumbutsa kuti umodzi wao ndi Khristu ndi mphatso ya chisomo cha Mulungu chimene iwo analandira mwa chikhulupiriro, osati kudzera mu kumvera miyambo ya malamulo a Chiyuda. Iye akulemba za chimwemwe ndi mtendere zimene Mulungu amapereka kwa iwo amene amakhala moyanjana ndi Khristu.

Kalatayi imadziwika bwino chifukwa cha kutsindika pa mfundo ya chimwemwe, kudzidalira, umodzi, kupirira pa moyo wa Chikhristu. Ikuonetsanso chikondi chimene Paulo anali nacho pa mpingo wa ku Filipi.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-11

Zimene Paulo anakumana nazo 1.12-26

Moyo mwa Khristu 1.27—2.18

Chikonzero cha Paulo pa Timoteo ndi Epafrodito 2.19-30

Machenjezo pa adani komanso zoopsa 3.1—4.9

Paulo ndi anzake a ku Filipi 4.10-20

Mau omaliza 4.21-23

Categories
AFILIPI

AFILIPI 1

1 Paulo ndi Timoteo, akapolo a YesuKhristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang’anira ndi atumiki:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chikondi cha Paulo cha pa Afilipi. Zipatso za undende wake

3 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;

4 nthawi zonse m’pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,

5 chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

6 pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

7 monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m’mtima mwanga, kuti inu m’zomangira zanga, ndipo m’chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m’chisomo.

8 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m’phamphu la mwa Khristu Yesu.

9 Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m’chidziwitso, ndi kuzindikira konse;

10 kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;

11 odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

12 Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;

13 kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m’bwalo lonse la alonda, ndi kwa ena onse;

14 ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.

15 Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndeu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima;

16 ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino;

17 koma ena alalikira Khristu mochokera m’chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m’zomangira zanga.

18 Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m’choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m’menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

19 Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;

20 monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m’thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.

21 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula.

22 Koma ngati kukhala ndi moyo m’thupi ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha.

23 Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;

24 koma kukhalabe m’thupi ndiko kufunika koposa, chifukwa cha inu.

25 Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu;

26 kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke mu Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.

Akhristu alimbike, ayanjane, adzichepetse, atsate kuyeramtima

27 Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

28 osaopa adani m’kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

29 kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye,

30 ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/1-dd656493ec3aca52a10af61b5e35bb07.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI 2

1 Ngati tsono muli chitonthozo mwaKhristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,

2 kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;

3 musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

4 munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

5 Mukhale nao mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu,

6 ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu,

7 koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu;

8 ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

9 Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,

10 kuti m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,

11 ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.

12 Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;

13 pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.

14 Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani,

15 kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m’dziko lapansi,

16 akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m’tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.

17 Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

18 momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

Paulo atamula Timoteo ndi Epafrodito amithenga ake a kwa Afilipi

19 Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.

20 Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona.

21 Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Khristu.

22 Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.

23 Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posachedwa m’mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani;

24 koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.

25 Koma ndinayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiyemtumwiwanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;

26 popeza anali wolakalaka inu nonse, navutika mtima chifukwa mudamva kuti anadwala.

27 Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.

28 Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso chindichepere chisoni.

29 Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa;

30 pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/2-e415894e19e698ab75291549413459ec.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI 3

Awachenjeza asatsate atumwi onyenga. Aonetsere zipatso za Mzimu

1 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.

2 Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula;

3 pakuti ife ndifemdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwaKhristuYesu, osakhulupirira m’thupi;

4 ndingakhale inenso ndili nako kakukhulupirira m’thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m’thupi, makamaka ineyu;

5 wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo,Mfarisi;

6 monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m’lamulo wokhala wosalakwa ine.

7 Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu.

8 Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,

9 ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;

10 kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;

11 ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.

12 Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.

13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo,

14 ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

15 Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu;

16 chokhachi, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.

17 Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang’anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.

18 Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;

19 chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m’manyazi ao, amene alingirira za padziko.

20 Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;

21 amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/3-6660fa076a251e637ea74e6e52140887.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI 4

1 Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.

2 Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.

3 Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m’goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m’buku la Moyo.

4 Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

6 Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

7 Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwaKhristuYesu.

8 Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

9 Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.

Paulo ayamika Afilipi popeza adamtumiza zomthandizira

10 Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.

11 Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.

12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

13 Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

14 Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m’chisautso changa.

15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m’chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane naneMpingoumodzi wonse m’makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;

16 pakuti mu Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.

17 Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.

18 Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.

19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi,Amen.

21 Perekani moni kwa woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine akupatsani moni.

22 Oyera mtima onse akupatsani inu moni, koma makamaka iwo a banja laKaisara.

23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/4-407964e8d6b92417e3642b890fa40bbe.mp3?version_id=1068—