Categories
AEFESO

AEFESO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata ya Paulo mtumwi yolembera kwa Aefeso

ikunena za “makonzedwe a Mulungu…ndi makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko”. (1.10) Kalatayi ndi pempho kwa anthu a Mulungu kuti akhale molingana ndi chikonzero chachikuluchi pofuna kuyanjanitsa mtundu wonse wa anthu kudzera mu umodzi umene upezeka mwa Yesu Khristu.

Mu gawo loyamba la buku la

Aefeso

wolembayo akutambasula mutu wa umodzi wa mpingo pamene akukamba za m’mene Mulungu Atate anasankhira anthu ake, ndipo m’mene iwowo amalandira chikhululukiro cha machimo namasulidwa kuchokera kumachimo kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Komanso akukamba za lonjezo lalikulu la Mulungu limene litsimikizidwa ndi Mzimu Woyera. Mu gawo lachiwiri iye akuwadandaulira awerengi ake kuti umodzi wao mwa Khristu uwonekere poyera pa mayendedwe ao ndi pa moyo wao wonse.

M’kalatamu akugwiritsa ntchito zifanizo zingapo pofuna kuonetsa umodzi wa anthu a Mulungu mwa Khristu: mpingo uli ngati thupi, ndipo Khristu ali ngati mutu wake; kapenanso ngati nyumba, ndipo Khristu ndiye mwala wokhala pangodya; kapenanso ngati mkazi, ndipo Khristu ndiye mwamuna wake wa mpingo. Kenaka kalatayi ikufotokoza zinthu zinanso zofunikira pamene wolembayo akunena za chisomo cha Mulungu mwa Khristu. Chilichonse chikuyesedwa molingana ndi chikondi, kudzipereka, kukhululukira machimo, chisomo komanso chiyero cha Khristu.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Khristu ndi mpingo 1.3—3.21

Moyo watsopano mwa Khristu 4.1—6.20

Mau omaliza 6.21-24

Categories
AEFESO

AEFESO 1

1 Paulo,mtumwiwaKhristuYesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali mu Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:

2 Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Madalitso a Mulungu mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu ndi mutu wa Mpingo

3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Khristu;

4 monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m’chikondi.

5 Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,

6 kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.

7 Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,

8 chimene anatichulukitsira ife m’nzeru zonse, ndi chisamaliro.

9 Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,

10 kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.

11 Mwa Iye tinayesedwa akeake olandira cholowa, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake;

12 kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.

13 Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

14 ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.

15 Mwa ichi inenso, m’mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse,

16 sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m’mapemphero anga;

17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;

18 ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,

19 ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba,

20 imene anachititsa mwa Khristu, m’mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa padzanja lake lamanja m’zakumwamba,

21 pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m’nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;

22 ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwaMpingo

23 amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m’zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/1-3c3dca73d1be39222c9363ebbc1a6fcb.mp3?version_id=1068—

Categories
AEFESO

AEFESO 2

Chipulumutso chichokera kuchisomo

1 Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu,

2 zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;

3 amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m’zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;

4 koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,

5 tingakhale tinali akufa m’zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndiKhristu(muli opulumutsidwa ndi chisomo),

6 ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m’zakumwamba mwaKhristuYesu;

7 kuti akaonetsere m’nthawi zilinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m’kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.

8 Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;

9 chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.

10 Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m’menemo.

Ayuda ndi amitundu ayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa mtanda wa Khristu

11 Momwemo kumbukirani, kuti kale inuamitundum’thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwamdulidwem’thupi, umene udachitika ndi manja;

12 kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m’dziko lapansi.

13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Khristu.

14 Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,

15 atachotsa udani m’thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;

16 ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m’thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;

17 ndipo m’mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;

18 kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.

19 Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;

20 omangika pa maziko aatumwindi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;

21 mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye;

22 chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/2-054984f16af14989be1bea8f545f37dd.mp3?version_id=1068—

Categories
AEFESO

AEFESO 3

Chinsinsi cha maitanidwe a amitundu

1 Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende waKhristuYesu chifukwa cha inuamitundu,

2 ngatitu munamva za udindo wa chisomo cha Mulungu chimene anandipatsa ine cha kwa inu;

3 ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso, monga ndinalemba kale mwachidule,

4 chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m’chinsinsi cha Khristu,

5 chimene sanachizindikiritse ana a anthu m’mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwaatumwindi aneneri ake oyera mwa Mzimu,

6 kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,

7 umene anandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene anandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake.

8 Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;

9 ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;

10 kuti muMpingoazindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m’zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,

11 monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:

12 amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.

13 Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m’zisautso zanga chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu.

Paulo apempherera Aefeso

14 Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate,

15 amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina,

16 kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m’kati mwanu,

17 kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m’mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m’chikondi,

18 mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,

19 ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.

20 Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

21 kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/3-a8dfaafbab123e39e8f3ddd04857eb2e.mp3?version_id=1068—

Categories
AEFESO

AEFESO 4

Umodzi wa iwo a chikhulupiriro

1 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,

2 ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;

3 ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.

4 Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m’chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu;

5 Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,

6 Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m’kati mwa zonse.

7 Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso yaKhristu.

8 Chifukwa chake anena,

M’mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,

naninkha zaufulu kwa anthu.

9 Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?

10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.

11 Ndipo Iye anapatsa ena akhaleatumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;

12 kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;

13 kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.

14 Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;

15 koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

16 kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.

Kusiyana kwa kuyera mtima kwa Chikhristu ndi mayendedwe oipa a akunja

17 Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu mongansoamitunduangoyenda, m’chitsiru cha mtima wao,

18 odetsedwa m’nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao;

19 amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.

20 Koma inu simunaphunzire Khristu chotero,

21 ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu;

22 kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;

23 koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,

24 nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.

25 Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.

26 Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,

27 ndiponso musampatse malo mdierekezi.

28 Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.

29 Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.

30 Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

31 Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.

32 Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/4-257090310aea5a1baec5e980b2138c2f.mp3?version_id=1068—

Categories
AEFESO

AEFESO 5

1 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;

2 ndipo yendani m’chikondi mongansoKhristuanakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

3 Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

4 kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.

5 Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

6 Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

7 Chifukwa chake musakhale olandirana nao;

8 pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,

9 pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,

10 kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani;

11 ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;

12 pakuti zochitidwa nao m’tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.

13 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika.

14 Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.

15 Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;

16 akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.

17 Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani.

18 Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

19 ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu;

20 ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

21 ndi kumverana wina ndi mnzake m’kuopa Khristu.

Zoyenera m’banja la munthu

22 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.

23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

24 Komatu monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m’zinthu zonse.

25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m’malo mwake;

26 kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;

27 kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.

28 Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;

29 pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo;

30 pakuti tili ziwalo za thupi lake.

31 Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.

32 Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo.

33 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/5-43f656087d7fb0dd053cc1e9587b607d.mp3?version_id=1068—

Categories
AEFESO

AEFESO 6

1 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino.

2 Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),

3 kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

4 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

5 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwaKhristu;

6 si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;

7 akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai;

8 podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

9 Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.

Zida za Mulungu

10 Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.

11 Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m’zakumwamba.

13 Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

14 Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;

15 ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;

16 koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.

17 Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;

18 mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,

19 ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m’kunditsegulira m’kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino,

20 chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m’menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.

Tikiko apita naye kalatayo

21 Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;

22 amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.

23 Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.

24 Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m’chosaonongeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/6-ee0a8676fc9c50e57912570a3ac98a73.mp3?version_id=1068—