Categories
2 TIMOTEO

2 TIMOTEO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Pafupi mau onse opezeka mu

Kalata yachiwiri ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Timoteo

ndi malangizo opita kwa Timoteo yemweyo. Paulo akufuna kuti mnyamata wakeyo womthandiza pa ntchito yolalika, alimbikire pa udindo wake wochitira Yesu Khristu umboni, atsate mokhulupirika zophunzitsa zoona zopezeka mu Uthenga Wabwino ndiponso mu Chipangano Chakale. Asaleke kulalika ndi kuphunzitsa, ngakhale pakati pa mazunzo ndi zovuta zochokera kwa anthu ena. Azikana “mafunso opusa ndi opanda malango, podziwa kuti abala ndeu.” Koma ayesetse kutsata chitsanzo chomwe iye Paulo adapereka pa moyo wake wonse, pa za kukhulupirira, kuleza mtima, kukonda, kupirira ndi kulimbikira pa nthawi ya masautso.

M’zonsezi, Paulo akukumbutsa Timoteo za m’mene iye mwini anakhalira ngati chitsanzo pa moyo wake ndi cholinga chake, chikhulupiriro chake, kupirira kwake, chikondi chake, ndi m’mene anazunzikira pa nthawi ya masautso.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Mau oyamika ndi olimbitsa mtima 1.3—2.13

Malangizo ndi mau ena ochenjeza 2.14—4.5

Atsate chitsanzo chomwe Paulo amusiyira 4.6-18

Mau omaliza 4.19-22

Categories
2 TIMOTEO

2 TIMOTEO 1

1 PaulomtumwiwaKhristuYesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa mu Khristu Yesu,

2 kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.

Chikondi cha Paulo cha pa Timoteo

3 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m’mapemphero anga,

4 pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndidzazidwe nacho chimwemwe;

5 pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa agogo ako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.

6 Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.

7 Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

8 Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;

9 amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,

10 koma chaonetsedwa tsopano m’maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,

11 umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake.

12 Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.

13 Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.

14 Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.

15 Ichi uchidziwa, kuti onse a mu Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Figelo ndi Heremogene.

16 Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachite manyazi ndi unyolo wanga;

17 komatu pokhala mu Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza.

18 (Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m’zinthu zambiri mu Efeso, uzindikira iwe bwino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TI/1-3817ba401e4e0c6950a071ca38b51a6c.mp3?version_id=1068—

Categories
2 TIMOTEO

2 TIMOTEO 2

1 Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m’chisomo cha mwaKhristuYesu.

2 Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.

3 Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.

4 Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.

5 Koma ngatinso wina ayesana nao m’makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.

6 Wam’munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo.

7 Lingirira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m’zonse.

8 Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m’mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;

9 m’menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.

10 Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.

11 Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso moyo ndi Iye:

12 ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:

13 ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.

Umo azichita ndi osochera

14 Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.

15 Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

16 Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo,

17 ndipo mau ao adzanyeka chilonda; a iwo ali Himeneo ndi Fileto;

18 ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.

19 Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.

20 Koma m’nyumba yaikulu simuli zotengera za golide ndisilivazokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.

21 Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.

22 Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

23 Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.

24 Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,

25 wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,

26 ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m’mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TI/2-f999249bd350206181f893226ccd5431.mp3?version_id=1068—

Categories
2 TIMOTEO

2 TIMOTEO 3

Zoipa zoopsa masiku otsiriza

1 Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.

2 Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,

3 osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,

4 achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;

5 akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.

6 Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m’nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu:

7 ophunzira nthawi zonse, koma sangathe konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi.

8 Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.

9 Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.

Timoteo alimbike kutsata ziphunzitso zokoma, ndi kulalikira nthawi zonse

10 Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,

11 mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m’zonsezi Ambuye anandilanditsa.

12 Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwaKhristuYesu, adzamva mazunzo.

13 Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.

14 Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa;

15 ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

16 Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo:

17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TI/3-efb88345e68f2a513c14933713db81e2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 TIMOTEO

2 TIMOTEO 4

1 Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndiKhristuYesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake;

2 lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.

3 Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:

4 ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.

5 Koma iwe, khala maso m’zonse, imva zowawa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.

Paulo azindikira kuti imfa yake mpafupi. Aitana Timoteo amzonde. Mbiri ya Dema ndi ena

6 Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.

7 Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:

8 chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.

9 Tayesetsa kudza kwa ine msanga:

10 pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.

11 Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.

12 Koma Tikiko ndamtuma ku Efeso.

13 Chofunda chija ndinachisiya ku Troasi kwa Karpo, udze nacho pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa.

14 Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;

15 ameneyo iwenso uchenjere naye; pakuti anatsutsana nao mau athu.

16 Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.

17 Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndiamitunduonse amve; ndipo ndinalanditsidwa m’kamwa mwa mkango.

18 Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi.Amen.

19 Pereka moni kwa Prisika ndi Akwila, ndi banja la Onesifore.

20 Erasto anakhalira mu Korinto; koma Trofimo ndamsiya wodwala ku Mileto.

21 Tayesetsa kudza isanadze nyengo yachisanu. Akukupatsa moni Yubulo, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudia, ndi abale onse.

22 Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale nanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TI/4-be63e4433deaf08f0df54ae0ced4d8e1.mp3?version_id=1068—