Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 20

Mpanduko ndi imfa ya Sheba

1 Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.

2 Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira kuYerusalemu.

3 Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi aang’onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m’nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.

4 Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.

5 Chomwecho Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anachedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira.

6 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.

7 Ndipo anatuluka namtsata anthu a Yowabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onse amphamvu; natuluka mu Yerusalemu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.

8 Pamene anafika iwo pamwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m’chimake m’chuuno mwake; ndipo m’kuyenda kwake lidasololoka.

9 Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.

10 Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m’dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m’mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.

11 Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.

12 Ndipo Amasa analikukunkhulira m’mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye.

13 Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.

14 Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso.

15 Ndipo anadza nammangira misasa mu Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mzindawo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse.

16 Pamenepo mkazi wanzeru wa m’mzindamo anafuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yowabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndilankhule nanu.

17 Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva.

18 Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha.

19 Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?

20 Ndipo Yowabu anayankha nati, Iai ndi pang’ono ponse, chikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga.

21 Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka mumzinda muno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga.

22 Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu.

23 Ndipo Yowabu anali woyang’anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang’anira Akereti ndi Apeleti;

24 ndi Adoramu anayang’anira msonkho; ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri;

25 ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe;

26 ndiponso Ira Myairi anali ansembe a Davide.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/20-30d14305c7cf97d8ef2dc1d79a6039de.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 21

Njala m’dziko, chifukwa chake, matsirizidwe ake

1 Ndipo m’masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.

2 Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).

3 Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?

4 Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifunasilivakapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa mu Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.

5 Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife chotionongera kuti tisakhalenso m’malire ali onse a Israele.

6 Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.

7 Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.

8 Koma mfumu inatenga ana aamuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana aamuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola;

9 niwapereka m’manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m’phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m’masiku a kukolola, m’masiku oyamba, poyamba kucheka barele.

10 Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalole mbalame za m’mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo zakuthengo usiku.

11 Ndipo anauza Davide chimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng’ono wa Saulo anachita.

12 Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m’khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;

13 nachotsa kumeneko mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapachikidwa.

14 Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini mu Zela, m’manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo.

Nkhondo zakupha ziphona za Afilisti

15 Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

16 Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.

17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.

18 Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.

19 Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu.

20 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.

21 Ndipo pakutonza Israele iyeyu, Yonatani mwana a Simea mbale wa Davide anamupha.

22 Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/21-dbab99efb488033e27a03ad83fe84c80.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 22

Nyimbo yoyamikira Yehova ya Davide

1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Saulo.

2 Ndipo anati,

Yehova ndiye thanthwe langa,

ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.

3 Mulungu wa thanthwe langa,

Iye ndidzamkhulupirira;

chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa,

nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;

Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.

4 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande;

chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.

5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,

mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine.

6 Zingwe za kumanda zinandizingira;

misampha ya imfa inandifikira ine.

7 M’kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,

inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;

ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake,

ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.

8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.

Maziko a dziko la kumwamba anasunthika.

Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.

9 M’mphuno mwake munatuluka utsi,

ndi moto wotuluka m’kamwa mwake unaononga;

makala anayaka nao.

10 Anaweramitsa miyambanso, natsika;

ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.

11 Ndipo Iye anaberekeka pakerubinauluka;

inde anaoneka pa mapiko a mphepo.

12 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye,

kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga.

13 Cheza cha pamaso pake

makala a moto anayaka.

14 Yehova anagunda kumwamba;

ndipo Wam’mwambamwamba ananena mau ake.

15 Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza;

mphezi, nawaopsa.

16 Pamenepo m’munsi mwa nyanja munaoneka,

maziko a dziko anaonekera poyera,

ndi mtonzo wa Yehova,

ndi mpumo wa mpweya wa m’mphuno mwake.

17 Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga;

Iye ananditulutsa m’madzi aakulu.

18 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,

kwa iwo akudana ndi ine;

pakuti anandiposa mphamvu.

19 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;

koma Yehova anali mchirikizo wanga.

20 Iye ananditulutsanso ku malo aakulu;

Iye anandipulumutsa,

chifukwa akondwera ndi ine.

21 Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;

monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.

22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova,

osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.

23 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga;

ndipo za malemba ake, sindinawapatukire.

24 Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye,

ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.

25 Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;

monga mwa kuyera kwanga pamaso pake.

26 Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo,

ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro.

27 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;

ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.

28 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;

koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.

29 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;

ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.

30 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;

ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.

31 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro;

mau a Yehova anayesedwa;

Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.

32 Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?

Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?

33 Mulungu ndiye linga langa lamphamvu;

ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake.

34 Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala;

nandiika pa misanje yanga.

35 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;

kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.

36 Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;

ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.

37 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,

ndi mapazi anga sanaterereke.

38 Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga;

ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha.

39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka,

inde anagwa pansi pa mapazi anga.

40 Pakuti Inu munandimanga m’chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo;

munandigonjetsera akundiukira.

41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,

kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.

42 Anayang’ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;

ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe.

43 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko,

ndinawapondereza ngati dothi la m’makwalala.

44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;

munandisunga ndikhale mutu waamitundu;

Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.

45 Alendo adzandigonjera ine,

pakumva za ine, adzandimvera pomwepo.

46 Alendo adzafota,

nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.

47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;

ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa;

48 inde Mulungu wakundibwezera chilango ine,

ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.

49 Amene anditulutsa kwa adani anga;

inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;

mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.

50 Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,

ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.

51 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu;

naonetsera chifundo wodzozedwa wake,

kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/22-06f0c38dcd56c1f96249c9363cdb4311.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 23

Nyimbo yotsiriza ya Davide

1 Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:

Atero Davide mwana wa Yese,

atero munthu wokwezedwa,

ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,

ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.

2 Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,

ndi mau ake anali pa lilime langa.

3 Mulungu wa Israele anati,

Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine;

kudzakhala woweruza anthu molungama;

woweruza m’kuopa Mulungu.

4 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m’mawa,

potuluka dzuwa, M’mawa mopanda mitambo;

pamene msipu uphuka kutuluka pansi,

chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.

5 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu;

koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha,

lolongosoka mwa zonse ndi losungika;

pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse,

ndi kufuma kwanga konse,

kodi sadzachimeretsa?

6 Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,

pakuti siigwiridwa ndi dzanja;

7 koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo;

ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m’malo mwao.

Angwazi a Davide

8 Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.

9 Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;

10 iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m’mbuyo mwake kukafunkha kokha.

11 Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12 Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu.

13 Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m’phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m’chigwa cha Refaimu.

14 Pamenepo Davide anali m’linga, ndi boma la Afilisti linali mu Betelehemu.

15 Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! Wina akadandipatsa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chili pachipatapo!

16 Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, ndipo zinatunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.

17 Nati, Ndisachite ichi ndi pang’ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi.

18 Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19 Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikane ndi atatu oyamba.

20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m’mbuna nyengo ya chipale chofewa;

21 ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m’dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m’dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22 Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23 Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikane ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang’anira olindirira ake.

24 Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;

25 Sama Mharodi, Elika Mharodi;

26 Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekowa.

27 Abiyezere Mwanatoti, Mebunai Muhusa;

28 Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa;

29 Helebi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea wa ana a Benjamini;

30 Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi;

31 Abiyaliboni Mwarabati, Azimaveti Mbahurimi;

32 Eliyaba Msaaliboni wa ana a Yaseni, Yonatani;

33 Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari;

34 Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele Mgiloni;

35 Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba;

36 Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi;

37 Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya;

38 Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri;

39 Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/23-8ccdfe58f58a58338ec50c7f9a340fd8.mp3?version_id=1068—

Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 24

Kuwerengedwa kwa anthu kuwatengera chilango cha Mulungu

1 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.

2 Ndipo mfumu inanena ndi Yowabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israele, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kuchuluka kwao kwa anthu.

3 Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?

4 Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele.

5 Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mzinda uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere;

6 nafika ku Giliyadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Yaana ndi kuzungulira, kufikira ku Sidoni,

7 nafika ku linga la Tiro ndi kumizinda yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.

8 Chomwecho pamene atayenda dziko lonse anafika kuYerusalemupakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri.

9 Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.

10 Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu.

11 Ndipo pouka Davide m’mawa mau a Yehova anafika kwamneneriGadi, mlauli wa Davide, kuti,

12 Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha chimodzi cha izo, ndikakuchitire chimenecho.

13 Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m’dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m’dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.

14 Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m’dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m’dzanja la munthu.

15 Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m’mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

16 Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi.

17 Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.

Davide ammangira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna

18 Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi.

19 Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova.

20 Ndipo Arauna anayang’ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.

21 Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide, anati, Kugula dwale lako ili, kuti ndimangirepo Yehova guwa la nsembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.

22 Arauna nati kwa Davide Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe chomkomera; siizi ng’ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng’ombe zikhale nkhuni;

23 zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni.

24 Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng’ombezo naperekapo masekeli makumi asanu asiliva.

25 Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/24-3df6d82f8de8a94f993c4f0eabb7d533.mp3?version_id=1068—