Categories
2 PETRO

2 PETRO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yachiwiri ya Petro

kwa gulu lalikulu la Akhristu oyambirira. Cholinga chenicheni cha kalatayi ndicho kulimbana ndi zonena za aphunzitsi onyenga ndi makhalidwe oipa amene amabwera chifukwa cha chiphunzitsochi. Yankho lake la mavutowa lipezeka pogwiritsitsa chidziwitso chenicheni cha Mulungu ndi cha Ambuye Yesu Khristu. Chidziwitso chimenechi chinaperekedwa ndi anthu amene iwo eni adamuona Yesu chamaso namumva iye akulalikira. Wolembayo akukhudzidwa makamaka ndi chiphunzitso chakuti Khristu sadzabweranso. Iye akunena kuti kuchedwa kubweranso kwa Khristu ndi chifukwa chakuti, “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (3.9)

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Maitanidwe a Chikhristu 1.3-21

Aphunzitsi onyenga 2.1-22

Kubweranso komaliza kwa Khristu 3.1-18

Categories
2 PETRO

2 PETRO 1

1 Simoni Petro, kapolo ndimtumwiwa YesuKhristukwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m’chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m’chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.

Atsate zokoma za Chikhristu

3 Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha;

4 mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m’chilakolako.

5 Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso;

6 ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo;

7 ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.

8 Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.

9 Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woiwala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale.

10 Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;

11 pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.

12 Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m’choonadi chili ndi inu.

13 Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m’msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;

14 podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.

15 Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi.

16 Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake.

17 Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;

18 ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.

19 Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;

20 ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha,

21 pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2PE/1-71295bbdadf2fa4c414f5949746af942.mp3?version_id=1068—

Categories
2 PETRO

2 PETRO 2

Za aphunzitsi onyenga

1 Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m’tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.

2 Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.

3 Ndipo m’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.

4 Pakuti ngati Mulungu sanalekerereangeloadachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;

5 ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;

6 ndipo pakuisandutsa makala mizinda ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza;

7 ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja

8 (pakuti wolungamayo pokhala pakati pao. Ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zao zosaweruzika).

9 Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;

10 koma makamaka iwo akutsata za thupi, m’chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;

11 popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano.

12 Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m’kuononga kwao,

13 ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m’madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu;

14 okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;

15 posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;

16 koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwamneneriyo.

17 Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.

18 Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;

19 ndi kuwalonjeza ufulu, pamene iwo eni ali akapolo a chivundi; pakuti chimene munthu agonjetsedwa nacho, adzakhala kapolo wa chimenecho.

20 Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi YesuKhristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.

21 Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.

22 Chidawachitikira iwo monga mwa mwambi woona uja, Galu wabwerera kumasanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2PE/2-b4724893991f11df8bd263118d252f55.mp3?version_id=1068—

Categories
2 PETRO

2 PETRO 3

Kubwera kwa Ambuye

1 Okondedwa, iyi ndiye kalata yachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;

2 kuti mukumbukire mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwaatumwianu;

3 ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,

4 ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.

5 Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;

6 mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;

7 koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.

8 Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.

9 Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m’mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.

11 Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo,

12 akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m’menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.

13 Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.

14 Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.

15 Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani;

16 monganso m’makalata ake onse pokamba momwemo za izi; m’menemo muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni.

17 Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.

18 Koma kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi YesuKhristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2PE/3-4a10fa243ba5b8877a15dcc5d114703e.mp3?version_id=1068—