Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 20

Yehosafati apempha Yehova pa Amowabu ndi Aamoni

1 Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.

2 Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.

3 Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.

4 Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumizinda yonse ya Yuda kufuna Yehova.

5 Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a kuYerusalemu, kunyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;

6 nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa mu Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse aamitundukodi? Ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.

7 Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m’dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?

8 Nakhala m’mwemo iwowa, nakumangirani m’mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,

9 Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m’nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m’kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.

10 Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m’dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;

11 tapenyani, m’mene atibwezera, kudzatiinga m’cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.

12 Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.

13 Ndipo Ayuda onse anakhala chilili pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.

14 Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahaziele mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano;

15 nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala mu Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.

16 Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera chigwa chakuno cha chipululu cha Yeruwele.

17 Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chilimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.

18 Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala mu Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.

19 Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israele ndi mau omveketsa.

Amowabu ndi Aamoni akanthidwa

20 Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala mu Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.

21 Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.

22 Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m’phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.

23 Pakuti ana a Amoni, ndi a Mowabu, anaukira okhala m’phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala mu Seiri, anasandulikirana kuonongana.

24 Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kuchipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo ili ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.

25 Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.

26 Ndi tsiku lachinai anasonkhana m’chigwa cha Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Beraka, mpaka lero lino.

27 Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kunka ku Yerusalemu ndi chimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.

28 Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.

29 Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m’maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israele.

30 Nuchita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wake anampumulitsira pozungulirapo.

31 Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la make ndiye Azuba mwana wa Sili.

32 Ndipo anayenda m’njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.

33 Komatu misanje siinachotsedwe; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.

34 Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m’buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m’buku la mafumu a Israele.

35 Zitatha izi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israele, yemweyo anachita moipitsitsa;

36 naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisisi, nazipanga zombozo mu Eziyoni-Gebere.

37 Pamenepo Eliyezere mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula ntchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisisi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/20-17ccf1fae3bb491409f9a51e8fe3e07c.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 21

Yehoramu mfumu yoipitsitsa ya Yuda

1 Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

2 Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.

3 Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi mizinda yamalinga mu Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba.

4 Atauka tsono Yehoramu mu ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.

5 Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu muYerusalemuzaka zisanu ndi zitatu.

6 Nayenda m’njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.

7 Koma Yehova sanafune kuononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano adalichita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ake nyali nthawi zonse.

8 Masiku ake Aedomu anapanduka kuchoka m’dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.

9 Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ake, ndi magaleta ake onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magaleta.

10 Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m’dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m’dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.

11 Anamanganso misanje m’mapiri a Yuda, nachititsa okhala mu Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.

12 Ndipo anamdzera kalata yofuma kwa Eliyamneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayende m’njira za Yehosafati atate wanu, kapena m’njira za Asa mfumu ya Yuda,

13 koma mwayenda m’njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;

14 taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi chuma chanu chonse, makanthidwe aakulu;

15 ndipo mudzadwala kwakukulu nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzatuluka chifukwa cha nthendayi tsiku ndi tsiku.

16 Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;

17 ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m’nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Ahaziya yekha mwana wake wamng’ono.

18 Ndi pambuyo pake pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m’matumbo ake ndi nthenda yosachira nayo.

19 Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pake pa zaka ziwiri, anatuluka matumbo ake mwa nthenda yake namwalira nazo nthenda zoipa. Ndipo anthu ake sanampserezere zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ake.

20 Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m’mzinda wa Davide, koma si m’manda a mafumu ai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/21-69c50655e269ccdcaaf9d498f3d449b9.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 22

Ahaziya mfumu ya Yuda aphedwa ndi Yehu

1 Ndipo okhala muYerusalemuanamlonga Ahaziya mwana wake wamng’ono akhale mfumu m’malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.

2 Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi; ndi dzina la make ndiye Ataliya mwana wa Omuri.

3 Iyenso anayenda m’njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.

4 Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko.

5 Anayendanso m’kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.

6 Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, popeza anadwala.

7 Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

8 Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Yuda, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.

9 Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala mu Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.

Ataliya apha achifumu onse, Yowasi apulumuka

10 Pamene Ataliya mai wake wa Ahaziya anaona kuti mwana wake adafa, anauka, naononga mbeu yonse yachifumu ya nyumba ya Yuda.

11 Koma Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wake m’chipinda chogonamo. Momwemo Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wake wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.

12 Ndipo iye anali nao wobisika m’nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi chimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/22-c047fc9323b89776a91a4b5ddf9abeca.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 23

Yehoyada adzoza Yowasi akhale mfumu

1 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.

2 Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m’mizinda yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele; nadza iwo kuYerusalemu.

3 Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m’nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.

4 Chimene muzichita ndi ichi: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera tsiku laSabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;

5 ndi limodzi la magawo atatu likhale kunyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku Chipata cha Maziko; ndi anthu onse akhale m’mabwalo a nyumba ya Yehova.

6 Koma asalowe mmodzi m’nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.

7 Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zake m’dzanja mwake; ndipo aliyense wolowa m’nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakutuluka iye.

8 Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo.

9 Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi malaya achitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m’nyumba ya Mulungu.

10 Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m’dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba.

11 Pamenepo anatulutsa mwana wa mfumu, namveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ake anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.

Aphedwa Ataliya

12 Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m’nyumba ya Yehova;

13 napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m’dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang’amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.

14 Koma Yehoyada wansembe anatuluka nao atsogoleri a mazana akuyang’anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mtulutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo aliyense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m’nyumba ya Yehova.

15 Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku Chipata cha Akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.

Pangano la Yehoyada wansembe

16 Ndipo Yehoyada anachita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.

17 Ndi anthu onse anamuka kunyumba yaBaala, naipasula, naphwanya maguwa ake a nsembe, ndi mafano ake; namupha Matani wansembe wa Baala kumaguwa a nsembe.

18 Ndipo Yehoyada anaika mayang’aniro a nyumba ya Yehova m’dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang’anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m’chilamulo cha Mose, ndi kukondwera ndi kuimbira, monga mwa chilangizo cha Davide.

19 Ndipo anaika odikira kumakomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kalikonse asalowemo.

20 Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m’dziko, natsika ndi mfumu kunyumba ya Yehova; nalowera pa chipata cha kumtunda m’nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.

21 Ndipo anthu onse a m’dziko anakondwera; ndi m’mzinda munali chete, atamupha Ataliya ndi lupanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/23-0620229be82c1bca9e3ee495dce24e59.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 24

Yowasi akonzanso Kachisi

1 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi anai; ndi dzina la make ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

2 Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.

3 Ndipo Yehoyada anamtengera akazi awiri, nabala ana aamuna ndi aakazi.

4 Ndipo pambuyo pake mumtima mwa Yowasi munali chofuna kukonzanso nyumba ya Yehova.

5 Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Mutuluke kunka kumizinda ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisraele onse ndalama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka; ndipo inu fulumirani nayo ntchitoyi. Koma Alevi sanafulumire nayo.

6 Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera mu Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?

7 Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwaBaala.

8 Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja kuchipata cha nyumba ya Yehova.

9 Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisraele m’chipululu.

10 Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m’bokosi mpaka atatha.

11 Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m’bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka.

12 Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira ntchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akuchita ndi chitsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.

13 Momwemo anachita ogwira ntchito, nikula ntchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ake, nailimbitsa.

14 Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndisiliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m’nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.

Anthu apatukira mafano

15 Koma Yehoyada anakalamba, nachuluka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.

16 Ndipo anamuika m’mzinda wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino mu Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.

17 Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.

18 Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwao kumene.

19 Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawachitira umboni; koma sanawamvere.

Zekariya adzudzula anthu naphedwa

20 Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.

21 Koma anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m’bwalo la nyumba ya Yehova.

22 Motero mfumu Yowasi sanakumbukire zokoma anamchitirazi Yehoyada atate wake, koma anapha mwana wake; ndiye pomwalira anati, Yehova achipenye, nachifunse.

23 Ndipo kunachitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.

24 Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m’dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga.

25 Ndipo atamchokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikulu), anyamata ake anamchitira chiwembu, chifukwa cha mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pake, namwalira iye; ndipo anamuika m’mzinda wa Davide, koma osamuika m’manda a mafumu.

26 Omchitira chiwembu ndi awa: Zabadi, mwana wa Simeati wamkazi Mwamoni; ndi Yehozabadi, mwana wa Simiriti wamkazi Mmowabu.

27 Za ana ake tsono, ndi katundu wamkulu anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m’buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/24-891642533ed3e6414263cac0c605a0f8.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 25

Amaziya agonjetsa Aedomu

1 Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.

2 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro.

3 Kunachitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ake amene adapha mfumu atate wake.

4 Koma sanaphe ana ao, koma anachita monga umo mulembedwa m’chilamulo, m’buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere tchimo lakelake.

5 Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa.

6 Analemberanso ngwazi zamphamvu za mu Israele zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente asilivazana limodzi.

7 Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israele lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israele, sakhala ndi ana onse a Efuremu.

8 Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.

9 Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israele? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.

10 Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kuchokera ku Efuremu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.

11 Nalimbika mtima Amaziya. Natsogolera anthu ake, namuka ku Chigwa cha Mchere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.

12 Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.

13 Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera mizinda ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betehoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.

Amaziya alangidwa popembedza mafano

14 Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yake, naigwadira, naifukizira.

15 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya, ndipo anamtumiramneneriamene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditse anthu ao m’dzanja lanu?

16 Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.

17 Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani, tionane maso.

18 Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi.

19 Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.

20 Koma wosamvera Amaziya, pakuti ncha Mulungu ichi kuti awapereke m’dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.

21 Motero anakwera Yowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.

22 Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawa yense kuhema kwake.

23 Ndipo Yowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Yehowahazi, ku Betesemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.

24 Natenga golide ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m’nyumba ya Mulungu kwa Obededomu, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwerera kunka ku Samariya.

25 Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu.

26 Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwe kodi m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele?

27 Ndipo chipatukire Amaziya kusatsata Yehova, namchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.

28 Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Yuda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/25-4ae1933dd7914293544961a4e41872b0.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 26

Uziya agonjetsa adani ambiri

1 Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m’malo mwa atate wake Amaziya.

2 Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.

3 Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.

4 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.

5 Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;

6 popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga mizinda m’dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.

7 Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala mu Guribaala, ndi Ameuni.

8 Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lake linabuka mpaka polowera ku Ejipito; pakuti analimbika chilimbikire.

9 Uziya anamanganso nsanja mu Yerusalemu pa Chipata cha Kungodya, ndi pa Chipata cha ku Chigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.

10 Namanga nsanja m’chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.

11 Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, otuluka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeiyele, ndi kapitao Maaseiya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.

12 Chiwerengo chonse cha akulu a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndicho zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.

13 Ndipo m’dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.

14 Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zachitsulo, ndi malaya achitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.

15 Napanga mu Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungodya, aponye nao mivi ndi miyala yaikulu. Ndi dzina lake linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwitsa, mpaka analimbikatu.

Uziya alakwa ku Kachisi nasanduka wakhate

16 Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa mu Kachisi wa Yehova kufukiza paguwa la nsembe la chofukiza.

17 Ndipo Azariya wansembe analowa pambuyo pake, ndi pamodzi naye ansembe a Yehova makumi asanu ndi atatu, ndiwo olimba mtima;

18 natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m’malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.

19 Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza ili m’dzanja lake kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe,khatelinabuka pamphumi pake, pamaso pa ansembe m’nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.

20 Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pake namkankhira msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kutulukako, pakuti Yehova adamkantha.

21 Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m’nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang’anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m’dziko.

22 Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesayamnenerimwana wa Amozi.

23 Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/26-548ef05fd35b385bb0ec854f9da87dd0.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 27

Yotamu mfumu ya Yuda

1 Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

2 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe mu Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda.

3 Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu.

4 Namanga mizinda m’mapiri a Yuda, ndi m’nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.

5 Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente asilivazana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe.

6 Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.

7 Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m’buku la mafumu a Israele ndi Yuda.

8 Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi.

9 Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ake, namuika m’mzinda wa Davide; ndi Ahazi mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 28

Ahazi mfumu yoipitsitsa ya Yuda

1 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake,

2 koma anayenda m’njira za mafumu a Israele, napangiranso Abaalamafano oyenga.

3 Nafukizanso yekha m’chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m’moto, monga mwa zonyansa zaamitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.

4 Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.

5 Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m’dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m’dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe aakulu.

6 Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao.

7 Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efuremu anapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu woyang’anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.

8 Ndipo ana a Israele anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana aamuna ndi aakazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya.

9 Koma panalimneneriwa Yehova pomwepo, dzina lake Odedi; natuluka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m’dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.

10 Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi milandu yopalamula kwa Yehova Mulungu wanu?

11 Mundimvere tsono, bwezani andende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu.

12 Pamenepo akulu ena a ana a Efuremu, Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo,

13 nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutipalamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa machimo athu ndi zopalamula zathu; pakuti tapalamula kwakukulu, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israele.

14 Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga msonkhano wonse.

15 Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mzinda wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.

16 Nthawi yomweyo mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asiriya amthandize.

17 Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.

18 Afilisti omwe adagwa m’mizinda ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi midzi yake, ndi Timna ndi midzi yake, ndi Gimizo ndi midzi yake; nakhala iwo komweko.

19 Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.

20 Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.

21 Pakuti Ahazi analandako za m’nyumba ya Yehova ndi za m’nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo.

22 Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.

23 Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse.

24 Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m’nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m’nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m’ngodya zilizonse za Yerusalemu.

25 Ndi mu mzinda uliwonse wa Yuda anamanga misanje ya kufukizira milungu ina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ake.

26 Machitidwe ena tsono, ndi njira zake zonse, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

27 Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m’mzinda wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/28-191073d70246bd322224cec858e35be3.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 29

Hezekiya mfumu ya Yuda

1 Hezekiya analowa ufumu wake ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Abiya mwana wa Zekariya.

2 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adachitira Davide kholo lake.

3 Chaka choyamba cha ufumu wake, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso.

4 Nalowetsa ansembe ndi Alevi, nawasonkhanitsa pamalo poyera kum’mawa,

5 nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kuchotsa zoipsa m’malo opatulika.

6 Pakuti analakwa makolo athu, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya chokhalamo Yehova, namfulatira.

7 Anatsekanso pa khomo chipinda cholowera, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m’malo opatulika kwa Mulungu wa Israele.

8 Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale chodabwitsa ndi chotsonyetsa, monga umo muonera m’maso mwanu.

9 Pakuti taonani, makolo athu adagwa ndi lupanga, ndi ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali andende chifukwa cha ichi.

10 Tsono mumtima mwanga nditi ndichitechipanganondi Yehova Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kutichokera.

11 Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.

Alevi ayeretsa Kachisi

12 Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yowele mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; ndi a Ageresoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;

13 ndi a ana a Elizafani, Simiri ndi Yeuwele; ndi a ana a Asafu, Zekariya ndi Mataniya;

14 ndi a ana a Hemani, Yehuwele ndi Simei; ndi a ana a Yedutuni, Semaya ndi Uziyele.

15 Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova.

16 Ndipo ansembe analowa m’kati mwake mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, natulutsira kubwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza mu Kachisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuzitulutsira kunja kumtsinje wa Kidroni.

17 Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira kuchipinda cholowera cha nyumba ya Yehova tsiku lachisanu ndi chitatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m’masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi.

18 Pamenepo analowa m’katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zake zonse.

19 Zipangizo zonse zomwe adazitaya mfumu Ahazi mu ufumu wake m’kulakwa kwake kuja, tazikonza, ndi kuzipatula; ndipo taonani, zili kuguwa la nsembe la Yehova.

Hezekiya aikanso chipembedzo cha Yehova

20 Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m’mzinda, nakwera kunka kunyumba ya Yehova.

21 Ndipo anabwera nazo ng’ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi anaankhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yauchimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke paguwa la nsembe la Yehova.

22 Momwemo anapha ng’ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza paguwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi paguwa la nsembe; anaphanso anaankhosa aja, nawaza mwazi paguwa la nsembe.

23 Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yauchimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao,

24 ndi ansembewo anawapha, nachita nsembe yauchimo ndi mwazi wao paguwa la nsembe, kuchita chotetezera Aisraele onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yauchimo zikhale za Aisraele onse.

25 Ndipo anaika Alevi m’nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natanimneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.

26 Alevi tsono anaimirira ndi zoimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga.

27 Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza paguwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoimbira za Davideyo mfumu ya Israele.

28 Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza.

29 Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.

30 Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.

31 Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.

32 Ndi kuwerenga kwake kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng’ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi anaankhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.

33 Ndi zinthu zopatulika zinafikira ng’ombe mazana asanu ndi limodzi, ndi nkhosa zikwi zitatu.

34 Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m’mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha ntchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m’kuongoka mtima kwao kudzipatula.

35 Ndiponso zidachuluka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iliyonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka.

36 Nakondwera Hezekiya ndi anthu onse pa ichi Mulungu adakonzeratu; pakuti chinthuchi chidachitika modzidzimutsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/29-4d3225dc34351c23330033cb2bb7f14a.mp3?version_id=1068—