Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 10

Ufumu ugawanika pakati. Rehobowamu mfumu ya Yuda, Yerobowamu ya Israele

1 Ndipo Rehobowamu anamuka ku Sekemu; pakuti Aisraele onse adadza ku Sekemu kumlonga ufumu.

2 Ndipo kunali, atamva Yerobowamu mwana wa Nebati (popeza anali mu Ejipito kumene adathawira, kuthawa Solomoni mfumu), Yerobowamu anabwera kuchoka ku Ejipito.

3 Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobowamu ndi Aisraele onse, nalankhula ndi Rehobowamu, ndi kuti,

4 Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko ntchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lake lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.

5 Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nachoka anthu.

6 Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?

7 Ndipo ananena naye, kuti, Mukawachitira chokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha.

8 Koma analeka uphungu wa akuluakuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pake.

9 Nati nao, Mundipangire bwanji inu, kuti tibwezere mau anthu awa ananena nanewo, ndi kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenzetsa ife?

10 Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m’chuuno mwa atate wanga.

11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

12 Tsono Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu.

13 Ndipo mfumu inawayankha mokalipa, popeza mfumu Rehobowamu analeka uphungu wa akuluakulu,

14 nalankhula nao monga umo anampangira achinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

15 Momwemo mfumu siinamvere anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ake, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.

16 Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvere anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m’mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang’anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao.

17 Koma za ana a Israele okhala m’mizinda ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao.

18 Pamenepo Rehobowamu mfumu inatuma Hadoramu woyang’anira thangata; koma ana a Israele anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehobowamu mfumu anafulumira kukwera pa galeta wake kuthawira kuYerusalemu.

19 Motero Israele anapandukana nayo nyumba ya Davide mpaka lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/10-84402dd3a662ac7b20669d9c9373b326.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 11

Mulungu aletsa nkhondo pakati pa Yuda ndi Israele

1 Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.

2 Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,

3 Lankhula ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,

4 Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu.

5 Ndipo Rehobowamu anakhala mu Yerusalemu, namanga mizinda yolimbikiramo mu Yuda.

6 Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa,

7 ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,

8 ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,

9 ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,

10 ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo mizinda yamalinga ya mu Yuda ndi Benjamini.

11 Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo.

12 Ndi m’mizinda iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.

Alevi ndi Aisraele ambiri afika ku Yerusalemu

13 Ndipo ansembe ndi Alevi okhala mu Israele yense anadziphatikiza kwa iye, ochokera m’malire ao onse.

14 Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;

15 nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang’ombe adawapanga.

16 Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m’mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.

17 Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehobowamu, mwana wa Solomoni zaka zitatu; pakuti anayenda m’njira ya Davide ndi Solomoni zaka zitatu.

18 Ndipo Rehobowamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Yese;

19 ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.

20 Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.

21 Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake aang’ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang’ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana aamuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana aakazi makumi asanu ndi limodzi).

22 Ndipo Rehobowamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkulu, kalonga mwa abale ake; ndiko kuti adzamlonga ufumu.

23 Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake aamuna onse m’maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumizinda yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/11-0d2091f6ae9a6736539be83cc44f2d27.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 12

Sisake wa ku Ejipito athira nkhondo Rehobowamu

1 Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.

2 Ndipo Rehobowamu atakhala mfumu zaka zinai, Sisake mfumu ya ku Ejipito anakwereraYerusalemu, popeza iwo adalakwira Yehova.

3 Anakwera ndi magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kutuluka mu Ejipito ngosawerengeka, Alibiya, Asuki, ndi Akusi.

4 Ndipo analanda mizinda yamalinga yokhala ya Yuda, nadza ku Yerusalemu.

5 Pamenepo Semayamnenerianadza kwa Rehobowamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m’dzanja la Sisake.

6 Pamenepo akalonga a Israele ndi mfumu anadzichepetsa, nati, Yehova ali wolungama.

7 Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake.

8 Koma adzakhala akapolo ake, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko.

Sisake alanda chuma cha Kachisi ndi cha nyumba ya mfumu

9 Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.

10 Ndipo Rehobowamu mfumu anapanga m’malo mwa izi zikopa zamkuwa, nazipereka m’manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

11 Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m’nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku chipinda cha olindirira.

12 Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma mu Yuda.

13 Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu mu Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, ndiwo mzinda Yehova adausankha m’mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.

14 Koma anachita choipa, popeza sanalunjikitse mtima wake kufuna Yehova.

15 Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.

16 Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa m’mzinda wa Davide; ndipo Abiya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/12-922e6211e9852a9882ef392494f0b7a4.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 13

Abiya ndi Yerobowamu amenyana nkhondo, Israele akanthidwa

1 Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yerobowamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.

2 Anakhala mfumu m’Yerusalemuzaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.

3 Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.

4 Ndipo Abiya anaimirira paphiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efuremu, nati, Mundimvere Yerobowamu ndi Aisraele onse;

5 simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israele anapereka chiperekere ufumu wa Israele kwa Davide, kwa iye ndi ana ake, ndi pangano lamchere?

6 Koma Yerobowamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomoni mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wake.

7 Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwapambana.

8 Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m’dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang’ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.

9 Simunapirikitse kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m’maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang’ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.

10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m’ntchito mwao,

11 nafukizira Yehova nsembe zopsereza m’mawa ndi m’mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.

12 Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ake, ndi malipenga oliza nao chokweza, kukulizirani inu chokweza. Ana a Israele inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.

13 Koma Yerobowamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.

14 Ndipo pocheuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; nafuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.

15 Pamenepo amuna a Yuda anafuula chokweza; ndipo pofuula amuna a Yuda, kunachitika kuti Mulungu anakantha Yerobowamu ndi Aisraele onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.

16 Ndipo ana a Israele anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m’dzanja lao.

17 Ndipo Abiya ndi anthu ake anawakantha makanthidwe aakulu; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazana asanu a Israele.

18 Momwemo anachepetsedwa ana a Israele nthawi ija, napambana ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.

19 Ndipo Abiya analondola Yerobowamu, namlanda mizinda yake, Betele ndi midzi yake, ndi Yesana ndi midzi yake, ndi Efuroni ndi midzi yake.

20 Ndi Yerobowamu sanaonenso mphamvu m’masiku a Abiya, namkantha Yehova, nafa iye.

21 Koma Abiya anakula mphamvu, nadzitengera akazi khumi ndi anai, nabala ana aamuna makumi awiri mphambu awiri, ndi ana aakazi khumi mphamvu asanu ndi mmodzi.

22 Machitidwe ena tsono a Abiya, ndi mayendedwe ake, ndi mau ake, alembedwa m’buku lomasulira lamneneriIdo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/13-ca48a2011359c95b8f8c3ef6deef8494.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 14

Asa akantha Akusi

1 Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m’mzinda wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake; m’masiku ake dziko linaona bata zaka khumi.

2 Ndipo Asa anachita chokoma ndi choyenera m’maso mwa Yehova Mulungu wake,

3 nachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,

4 nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kuchita chilamulo ndi chowauza Iye.

5 Anachotsanso m’mizinda yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unachita bata pamaso pake.

6 Ndipo anamanga mizinda yamalinga mu Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.

7 Ndipo anati kwa Yuda, Timange mizinda iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika.

8 Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.

9 Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

10 Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m’chigwa cha Zefati ku Maresa.

11 Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m’dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.

12 Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.

13 Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri.

14 Ndipo anakantha mizinda yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m’mizinda monse, pakuti mudachuluka zofunkha m’menemo.

15 Anakanthanso a m’mahema a ng’ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndingamira; nabwerera kunka kuYerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/14-60d7db5b8d612448ac8e7007a9492ae2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 15

Asa achotsa mafano nabwereza chipangano ndi Mulungu

1 Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi,

2 ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.

3 Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;

4 koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele m’kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza.

5 Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m’maikomo.

6 Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzake, ndi mzinda kupasula mzinda; pakuti Mulungu anawavuta ndi masautso ali onse.

7 Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho.

8 Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi chinenero cha Odedimneneriyo, analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m’dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m’mizinda adailanda ku mapiri a Efuremu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pachipinda cholowera cha nyumba ya Yehova.

9 Namemeza onse a mu Yuda ndi mu Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye.

10 Ndipo anasonkhana kuYerusalemumwezi wachitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai.

11 Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng’ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.

12 Nalowachipanganochakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;

13 ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng’ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.

14 Ndipo analumbira kwa Yehova ndi mau aakulu, ndi kufuula ndi mphalasa ndi malipenga.

15 Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi khumbo lao lonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.

16 Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni.

17 Chinkana misanje siinachotsedwe mu Israele, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ake onse.

18 Ndipo analowa nazo zopatulika za atate wake, ndi zopatulika zakezake, kunyumba ya Mulungu; ndizosiliva, ndi golide, ndi zipangizo.

19 Ndipo panalibenso nkhondo mpaka Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zinai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/15-78dc5fd3a6e10dad03f0a6ca1f6d54f5.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 16

Asa apangana ndi Benihadadi, nalimbana ndi Israele

1 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

2 Pamenepo Asa anatulutsasilivandi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,

3 Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golide; mukani, pasulani pangano lanu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.

4 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi mizinda ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi mizinda yonse ya chuma ya Nafutali.

5 Ndipo kunali, pakumva ichi Baasa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa ntchito yake.

6 Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yake, imene Baasa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.

Hanani mlauli adzudzula Asa

7 Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m’dzanja lanu.

8 Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m’dzanja mwanu?

9 Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m’menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.

10 Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m’kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.

11 Ndipo taonani, zochita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

12 Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafune Yehova, koma asing’anga.

13 Nagona Asa ndi makolo ake, namwalira atakhala mfumu zaka makumi anai.

14 Ndipo anamuika m’manda ake adadzisemerawo m’mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/16-f8b7e7e6c2d74b44ff18accd71bbe43a.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 17

Ukoma ndi ukulu wa Yehosafati

1 Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele.

2 Naika ankhondo m’mizinda yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m’dziko la Yuda, ndi m’mizinda ya Efuremu, imene adailanda Asa atate wake.

3 Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m’njira zake zoyamba za kholo lake Davide, osafuna Abaala;

4 koma anafuna Mulungu wa kholo lake nayenda m’malamulo ake, osatsata machitidwe a Israele.

5 Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m’dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu.

6 Ndi mtima wake unakwezeka m’njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo mu Yuda.

7 Chaka chachitatu cha ufumu wake anatuma akalonga ake, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netanele, ndi Mikaya, aphunzitse m’mizinda ya Yuda;

8 ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asahele, ndi Semiramoti, ndi Yehonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yehoramu, ansembe.

9 Ndipo anaphunzitsa mu Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m’mizinda yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.

10 Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati.

11 Ndipo Afilisti ena anabwera nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.

12 Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.

13 Nakhala nazo ntchito zambiri m’mizinda ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu muYerusalemu.

14 Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;

15 ndi wotsatana naye mkulu Yehohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;

16 ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikiri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri;

17 ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;

18 wotsatana naye Yehozabadi, ndi pamodzi ndi iye okonzekeratu kunkhondo zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.

19 Ndiwo amene analindirira mfumu, osawerenga iwo aja mfumu adawaika m’mizinda yamalinga mu Yuda monse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/17-fbc2893605d2a4d8c5683c10e6df1395.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 18

Pangano pakati pa Yehosafati ndi Ahabu; afunsira kwa aneneri

1 Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.

2 Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng’ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.

3 Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.

4 Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.

5 Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri aamuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m’dzanja la mfumu.

6 Koma Yehosafati anati, Kulibenso kunomneneriwa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?

7 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.

8 Pamenepo mfumu ya Israele inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Imila.

9 Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.

10 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adzatha psiti.

11 Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m’dzanja la mfumu.

Mikaya anenera motsutsana nao

12 Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m’kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.

13 Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.

14 Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Giliyadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzachita mwai; ndipo adzaperekedwa m’dzanja lanu.

15 Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane choonadi chokhachokha m’dzina la Yehova?

16 Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense kunyumba yake mumtendere.

17 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Sindinakuuzeni kuti sadzandinenera zabwino koma zoipa?

18 Nati iye, Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lilikuima padzanja lake lamanja, ndi padzanja lake lamanzere.

19 Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israele ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Giliyadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti.

20 Ndipo unatuluka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi chiyani?

21 Nuti uwu, Ndidzatuluka ndi kukhala mzimu wonama m’kamwa mwa aneneri ake onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; tuluka, ukatero kumene.

22 Ndipo tsono taonani, Yehova analonga mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anu awa, nakunenetserani choipa Yehova.

23 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji kulankhula ndi iwe?

24 Nati Mikaya, Tapenya, udzaona tsiku lolowa iwe m’chipinda cham’kati kubisala.

25 Ndipo mfumu ya Israele inati, Mumtenge Mikaya, mukambweze kwa Amoni kazembe wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu;

26 nimuziti, Itero mfumu, Mumuike uyu m’kaidi, ndi kumdyetsa chakudya chomsautsa, ndi kumwetsa madzi omsautsa, mpaka ndikabwera mumtendere.

27 Nati Mikaya, Mukakabwera ndi mtendere konse, Yehova sananene mwa ine. Nati iye, Tamverani, anthu inu nonsenu.

Nkhondo iwakanika naphedwa Ahabu

28 Momwemo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera kunka ku Ramoti Giliyadi.

29 Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo.

30 Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magaleta ake, ndi kuti, Musayambana ndi ang’ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yekha.

31 Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.

32 Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona kuti sanali mfumu ya Israele anabwerera osamtsatanso.

33 Ndipo munthu anaponya muvi wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israeleyo pakati pa maluma a malaya ake achitsulo. Potero anati kwa woyendetsa galetayo, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kukhamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.

34 Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israele inagwirizizika m’galeta wake popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/18-c3842ca5326a85b5ec4007925e6d2611.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 19

Mneneri Yehu adzudzula Yehosafati

1 Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera kunyumba yake kuYerusalemumumtendere.

2 Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.

3 Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m’dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.

4 Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, natulukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efuremu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao.

5 Naika oweruza m’dziko, m’mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda, mzinda ndi mzinda;

6 nati kwa oweruza, Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.

7 Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.

8 Yehosafati anaikanso mu Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele, aweruzire Yehova, nanena milandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.

9 Ndipo anawalangiza, ndi kuti, Muzitero ndi kuopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro.

10 Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m’mizinda mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.

11 Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkulu, ndiye mkulu wanu m’milandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismaele, wolamulira nyumba ya Yuda, m’milandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Chitani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/19-de332828a0c67998289e8cb89d43359c.mp3?version_id=1068—