Categories
2 MBIRI

2 MBIRI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likamba za mfumu Solomoni ndi mafumu a ku Yuda okha mpaka nthawi ya kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu.

Za mkatimu

Ufumu wa Solomoni

1.1—9.31

a. Zaka zoyamba za ufumu wake

1.1-17

b. Amanga Kachisi wa Yehova

2.1—7.10

c. Zaka zotsiriza za ufumu wake

7.11—9.31

Za mafumu ena a ku Yuda

10.1—36.23

a. Mafumu akumpoto aukira ufumu wa Rehobowamu

10.1-19

b. Mafumu a ku Yuda

11.1—36.12

c. Kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu

36.13-23

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 1

Solomoni apereka nsembe ku Gibiyoni

1 Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa mu ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.

2 Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo.

3 Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunalichihema chokomanakocha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m’chipululu.

4 Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kuchokera ku Kiriyati-Yearimu kunka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema kuYerusalemu.

5 Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezalele mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la chihema cha Yehova; ndipo Solomoni ndi khamulo anafunako.

6 Nakwerako Solomoni ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku chihema chokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza chikwi chimodzi.

Solomoni apempha nzeru kwa Mulungu

7 Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni, nati kwa iye, Pempha chomwe ndikupatse.

8 Nati Solomoni kwa Mulungu, Mwachitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m’malo mwake.

9 Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi.

10 Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?

11 Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,

12 nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.

13 Momwemo Solomoni anadza ku Yerusalemu kuchokera ku msanje uli ku Gibiyoni, ku khomo la chihema chokomanako; ndipo anachita ufumu pa Israele.

Magaleta ndi apakavalo a Solomoni

14 Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo, nakhala nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m’mizinda ya magaleta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.

15 Ndipo mfumu inatero kutisilivandi golide zikhale mu Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza ichuluke ngati mikuyu yokhala kuchidikha.

16 Ndi akavalo amene Solomoni anali nao anafuma ku Ejipito; amalonda a mfumu anawalandira magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake.

17 Ndipo anatenga natuluka nalo galeta ku Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawatulutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/1-05d665a60520b8bf8db3d8daccd4ceb7.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 2

Solomoni apangana ndi Hiramu za mirimo ya Kachisi

1 Ndipo Solomoni anati alimangire dzina la Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.

2 Nawerenga Solomoni amuna zikwi khumi mphambu makumi asanu ndi limodzi osenza mirimo, ndi amuna zikwi makumi asanu ndi atatu otema mitengo m’mapiri, ndi zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kuwayang’anira.

3 Ndipo Solomoni anatumiza kwa Huramu mfumu ya Tiro, ndi kuti, Monga momwe munachitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundichitire ine momwemo.

4 Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m’mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.

5 Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikulu; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkulu woposa milungu yonse.

6 Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam’mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?

7 Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndisiliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine mu Yuda ndi muYerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.

8 Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebanoni; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo mu Lebanoni; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu,

9 ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikulu ndi yodabwitsa.

10 Ndipo taonani, ndidzawapatsa anyamata anu otema akulikha mitengo miyeso ya tirigu wopuntha zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya barele zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikulu ya vinyo zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikulu ya mafuta zikwi makumi awiri.

11 Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomoni, ndi kuti, Powakonda anthu ake Yehova anakulongani mfumu yao.

12 Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.

13 Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala nalo luntha, Huramuabi,

14 ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana aakazi a Dani, ndipo atate wake ndiye munthu wa ku Tiro, wodziwa kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira chopanga chilichonse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.

15 Ndipo tsono tirigu ndi barele, mafuta ndi vinyo, mbuye wanga wanenazi, azitumize kwa anyamata ake;

16 ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.

17 Ndipo Solomoni anawerenga alendo onse okhala m’dziko la Israele, monga mwa mawerengedwe aja atate wake Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.

18 Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m’mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi agwiritse anthu ntchito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/2-52f18f8c617864d08c9a7ee4822fece9.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 3

Mamangidwe a Kachisi

1 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova kuYerusalemu, m’phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.

2 Nayamba kumanga tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri, chaka chachinai cha ufumu wake.

3 Ndipo maziko adawaika Solomoni akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wake, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.

4 Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m’litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m’katimo ndi golide woona.

5 M’nyumba yaikulu tsono anatchinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golide wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.

6 Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wake; ndi golide wake ndiye golide wa Paravaimu.

7 Anamamatizanso Kachisi, mitanda, ziundo, ndi makoma ake, ndi zitseko zake, ndi golide; nalembaakerubipamakoma.

8 Ndipo anamanga malo opatulika kwambiri, m’litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; naikuta ndi golide wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.

9 Ndi kulemera kwake kwa misomali ndiko masekeli makumi asanu a golide. Ndipo anazikuta ndi golide zipinda zosanjikizana.

10 Ndipo m’malo opatulika kwambiri anapanga akerubi awiri, anachita osema, nawakuta ndi golide.

11 Ndi mapiko a akerubi m’litali mwake ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzake mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.

12 Ndi phiko la kerubi wina mikono isanu lojima khoma la nyumba, ndi phiko linzake mikono isanu lolumikizana ndi phiko la kerubi wina.

13 Mapiko a akerubi awa anafunyululika mikono makumi awiri; ndipo anaima ndi mapazi ao, ndi nkhope zao zinaloza kukhomo.

14 Ndipo anaomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiira, ndi lofiirira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi.

15 Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iliyonse ndiwo mikono isanu.

16 Napanga maunyolo a m’chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.

17 Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kachisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzake ku dzanja lamanzere; nalitcha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Bowazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/3-0d1ae3980a50b2e8282ecb090333d1c7.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 4

Guwa la nsembe ndi thawale lamkuwa ndi zipangizo zina zonse

1 Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m’litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi.

2 Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.

3 Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng’ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng’ombe zinali m’mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.

4 Linasanjikika pa ng’ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum’mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi mbuyo zao zinayang’anana.

5 Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati duwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu.

6 Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m’menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.

7 Ndipo anapanga zoikaponyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika mu Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.

8 Anapanganso magome khumi, nawaika mu Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide.

9 Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa.

10 Ndipo anaika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum’mawa chakumwera.

11 Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m’nyumba ya Mulungu:

12 nsanamira ziwiri, ndi zikhozo, ndi mitu iwiri inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi maukonde awiri akukuta zikho ziwiri za mitu ili pamwamba pa nsanamirazo,

13 ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uliwonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo.

14 Anapanganso maphaka, napanga mbiya zaphwamphwa khumi pamwamba pa maphaka;

15 thawale limodzi ndi ng’ombe khumi ndi ziwiri pansi pake.

16 Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.

17 Mfumuyi inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m’dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.

18 Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseke.

19 Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m’nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;

20 ndi zoikaponyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati;

21 ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolide, ndiwo golide wangwiro;

22 ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m’nyumba, zitseko zake za m’katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/4-10ddfe45835739dd3b18e7071055c0f2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 5

Aika likasa mu Kachisi

1 Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziikasiliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m’chuma cha nyumba ya Mulungu.

Kuperekedwa kwa Kachisi

2 Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, kuYerusalemu, kukatengalikasa la chipanganocha Yehova kumzinda wa Davide ndiwoZiyoni.

3 Ndipo amuna onse a Israele anasonkhana kwa mfumu kumadyerero anachitikawo, m’mwezi wachisanu ndi chiwiri.

4 Nadza akuluakulu onse a Israele, nanyamula likasalo Alevi.

5 Ndipo anakwera nalo likasa, ndichihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m’chihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.

6 Ndi mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng’ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.

7 Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m’chipinda chamkati mwa Kachisi, m’malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko aakerubi.

8 Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pamalo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zake pamwamba pake.

9 Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino.

10 Munalibe kanthu kena m’likasa, koma magome awiri Mose anawaika m’mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo mu Ejipito.

11 Ndipo ansembe anatuluka m’malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;

12 Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum’mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.

13 Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;

14 ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/5-38eb7d8c257d9e000ebb9a24d68f7d32.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 6

Chonena Solomoni ndi pemphero lake popereka Kachisi

1 Pamenepo Solomoni anati, Yehova anati kuti adzakhala mu mdima wandiweyani.

2 Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.

3 Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yake, nidalitsa khamu lonse la Israele; ndi khamu lonse la Israele linaimirira.

4 Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, wakunena m’kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi manja ake, ndi kuti,

5 Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m’dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m’mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;

6 Koma ndinasankhaYerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.

7 Ndipo Davide atate wanga anafuna mumtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

8 Koma Yehova anati kwa Davide atate wanga, Popeza unafuna mumtima mwako kulimangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti unatero mumtima mwako;

9 koma sudzandimangira nyumba ndiwe, koma mwana wako wakudzatuluka m’chuuno mwako, iyeyo adzalimangira dzina langa nyumbayi.

10 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m’malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi.

11 Ndipo ndalongamo likasa, mulichipanganocha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.

12 Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake.

13 Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m’litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba;

14 nati, Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu ngati Inu, m’mwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;

15 inu amene mwasungira mtumiki wanu Davide atate wanga chija mudamlonjezachi: inde munanena ndi pakamwa panu, ndipo mwachita ndi dzanja lanu, monga momwe muli lero lino.

16 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m’chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.

17 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, achitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.

18 Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m’mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?

19 Chinkana chitero, labadirani pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kufuula ndi kupempha kwake, kumene kapolo wanu apempha pamaso panu;

20 kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.

21 Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israele, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululukire.

22 Munthu akachimwira mnansi wake, ndipo akamuikira lumbiro lakumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira ku guwa lanu la nsembe, m’nyumba ino;

23 pamenepo mumvere mu Mwamba, nimuchite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa chilungamo chake.

24 Ndipo anthu anu Israele akawakantha mdani chifukwa cha kukuchimwirani, nakabwerera iwowa ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m’nyumba ino;

25 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba, nimukhululukire tchimo la anthu anu Israele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

26 Mukatsekeka m’mwamba, mopanda mvula, chifukwa cha kukuchimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa;

27 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba, nimukhululukire tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israele, mutawalangiza njira yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale cholowa chao.

28 Mukakhala njala m’dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m’dziko la mizinda yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;

29 pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu aliyense, kapena ndi anthu anu onse Aisraele, akadziwa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake, nakatambasulira manja ake kuloza kunyumba iyi:

30 pamenepo mumvere mu Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;

31 kuti aope Inu kuyenda m’njira zanu masiku onse akukhala iwo m’dziko limene munapatsa makolo athu.

32 Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israele, akafumira ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono ndi kupemphera kuloza kunyumba iyi;

33 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo, nimumchitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisraele; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi itchedwa ndi dzina lanu.

34 Akatulukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iliyonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza kumzinda uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu;

35 pamenepo mumvere mu Mwamba pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

36 Akachimwira Inu (pakuti palibe munthu wosachimwa), nimukakwiya nao, ndi kuwapereka kwa adani, kuti awatenge andende kunka nao ku dziko lakutali, kapena lapafupi;

37 koma akalingirira m’mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m’dziko la undende wao, ndi kuti, Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita choipa;

38 akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m’dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mzinda mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi;

39 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao; nimukhululukire anthu anu amene anakuchimwirani.

40 Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.

41 Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.

42 Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukire zachifundo za Davide mtumiki wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/6-ddac81d11a49dcff38e9643616b50664.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 7

Chivomerezo cha Yehova mwa moto ndi ulemerero wao wodzaza Kachisi

1 Atatha tsono Solomoni kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi.

2 Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m’nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

3 Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova pa nyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.

4 Pamenepo mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.

5 Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng’ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Mulungu.

6 Naimirira ansembe mu udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense.

7 Ndipo Solomoni anapatula pakati pake pa bwalo lili pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomoni linachepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.

8 Nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisraele onse pamodzi naye, khamu lalikulu ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Ejipito.

9 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu anachita msonkhano woletsa; popeza anachita zakupereka guwa la nsembe masiku asanu ndi awiri, ndi madyerero masiku asanu ndi awiri.

10 Ndipo tsiku la makumi awiri ndi chitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m’mtima mwao chifukwa cha zokoma Yehova adawachitira Davide, ndi Solomoni, ndi Aisraele anthu ake.

Yehova aonekeranso kwa Solomoni

11 Momwemo Solomoni anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo zilizonse zidalowa mumtima mwake mwa Solomoni kuzichita m’nyumba ya Yehova, ndi m’nyumba yakeyake, anachita mosalakwitsa.

12 Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.

13 Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;

14 ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.

15 Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga otchera, pemphero la m’malo ano.

16 Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.

17 Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga monga umo anayendera Davide atate wako, nukachita monga mwa zonse ndakulamulira iwe, nukasunga malemba anga ndi maweruzo anga;

18 pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu mu Israele.

19 Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuilambira;

20 pamenepo ndidzawazula m’dziko langa limene ndinawapatsa; ndi nyumba ino ndinaipatulira dzina langa ndidzaitaya, osaionanso, ndi kuiyesa mwambi ndi mnyozo mwa mitundu yonse ya anthu.

21 Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yehova anatero ndi dziko lino ndi nyumba ino chifukwa ninji?

22 Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawatulutsa m’dziko la Ejipito, nagwira milungu ina, nailambira ndi kuitumikira; chifukwa chake anawagwetsera choipa ichi chonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/7-fea45a46c8ae378a7ac174adb2cefff9.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 8

Solomoni amanga midzi ina

1 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m’mene Solomoni anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yakeyake,

2 Solomoni anamanga mizinda imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israele.

3 Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa.

4 Ndipo anamanga Tadimori m’chipululu, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anaimanga mu Hamati.

5 Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, mizinda ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;

6 ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa muYerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m’dziko lonse la ufumu wake.

7 Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisraele,

8 mwa ana ao otsala m’dziko pambuyo pao, amene ana a Israele sanawathe, mwa iwowa Solomoni anawachititsa thangata mpaka lero lino.

9 Koma mwa ana a Israele Solomoni sanawayese akapolo omgwirira ntchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ake aakulu, ndi akulu a magaleta ake, ndi apakavalo ake.

10 Amenewa anali akulu a akapitao a mfumu Solomoni, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.

11 Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi waFaraom’mzinda wa Davide, alowe m’nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m’nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.

Malongosoledwe a chipembedzo ndi nsembezo

12 Pamenepo Solomoni anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova paguwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo pachipinda cholowera,

13 monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m’chaka: pachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.

14 Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.

15 Ndipo sanapatuke pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kalikonse, kapena za chumachi.

16 Momwemo ntchito yonse ya Solomoni inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.

17 Pamenepo Solomoni anamuka ku Eziyoni-Gebere, ndi ku Eloti m’mphepete mwa nyanja, m’dziko la Edomu.

18 Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m’nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/8-239af38835dd1bb3b318f2340ff7b589.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 9

Mfumu yaikazi ya ku Sheba acheza ndi Solomoni

1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa kuYerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndingamirazosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m’mtima mwake.

2 Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire.

3 Ndipo mfumu yaikazi ya ku Sheba ataiona nzeru ya Solomoni, ndi nyumba adaimanga,

4 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.

5 Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m’dziko langa, ya machitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.

6 Koma sindinakhulupirire mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva.

7 Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima chiimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu.

8 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.

9 Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.

10 Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomoni otenga golide ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.

11 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oimbira; sizinaoneke zotere ndi kale lonse m’dziko la Yuda.

12 Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake.

Chuma ndi ulemerero wa Solomoni

13 Kulemera kwake tsono kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide;

14 osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndisilivakwa Solomoni.

15 Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri.

16 Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

17 Mfumu inapanganso mpando wachifumu waukulu wa minyanga, naukuta ndi golide woona.

18 Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m’mbali mwa manjawo.

19 Ndi mikango khumi ndi iwiri inaimirirapo, mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwe wotere mu ufumu uliwonse.

20 Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zipangizo zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali za golide woona; siliva sanayesedwe kanthu m’masiku a Solomoni.

21 Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golide, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.

22 Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a padziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.

23 Ndipo mafumu onse a padziko lapansi anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake Mulungu adazilonga m’mtima mwake.

24 Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndimure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.

25 Ndipo Solomoni anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magaleta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m’mizinda ya magaleta, ndi mu Yerusalemu kwa mfumu.

26 Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Ejipito.

27 Ndipo mfumu inachulukitsa siliva mu Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu ili kumadambo kuchuluka kwake.

28 Ndipo anakamtengera Solomoni akavalo ku Ejipito, ndi ku maiko onse.

Kumwalira kwa Solomoni

29 Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwe kodi m’buku la mau a Natanimnenerindi m’zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m’masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?

30 Ndipo Solomoni anakhala mfumu ya Israele yense mu Yerusalemu zaka makumi anai.

31 Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m’mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/9-190dc855d9078110cc5e389d48e0a5f8.mp3?version_id=1068—