Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 10

Yehu aononga mbumba ya Ahabu

1 Ndipo Ahabu anali nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri mu Samariya. Nalemba makalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

2 Tsono ikakufikani inu kalata iyi, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mizinda yalinga, ndi zida,

3 musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.

4 Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji?

5 Ndipo iye wakuyang’anira nyumba, ndi iye wakuyang’anira mzinda, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani.

6 Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m’mzinda, amene anawalera.

7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m’madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele.

8 Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu ya ana a mfumu. Nati iye, Muiunjike miulu iwiri polowera pa chipata kufikira m’mawa.

9 Ndipo kunali m’mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?

10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya.

11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.

12 Pamenepo ananyamuka, nachoka, namuka ku Samariya. Ndipo pokhala kunyumba yosengera ya abusa panjira,

13 Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tilikutsika kulonjera ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikulu.

14 Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiye ndi mmodzi yense.

Aphedwa aneneri a Baala

15 Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta.

16 Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M’mwemo anamuyendetsa m’galeta wake.

17 Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu mu Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.

18 Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikiraBaalapang’ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.

19 Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.

20 Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.

21 Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m’nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa.

22 Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala.

23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m’nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

24 Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m’manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake.

25 Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumzinda wa nyumba ya Baala.

26 Natulutsa zoimiritsa zija zinali m’nyumba ya Baala, nazitentha.

27 Nagamula fano la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.

28 Momwemo Yehu anaononga Baala mu Israele.

Yehu apembedza mafano

29 Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang’ombe agolide okhala mu Betele ndi mu Dani.

30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m’mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.

31 Koma Yehu sanasamalire kuyenda m’chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.

32 Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m’malire onse a Israele,

33 kuyambira ku Yordani kum’mawa, dziko lonse la Giliyadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroere, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Giliyadi ndi Basani.

34 Ndipo machitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazichita, ndi mphambu yake yonse, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

35 Nagona Yehu ndi makolo ake, namuika mu Samariya. Ndi Yehowahazi mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

36 Ndipo masiku ake akukhala Yehu mfumu ya Israele mu Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/10-d1e186fb1aa681d106f89ab885c7e630.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 11

Ataliya apha achifumu onse, Yowasi apulumuka

1 Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.

2 Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m’chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.

3 Nakhala naye wobisika m’nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.

4 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m’nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.

5 Nawalamulira, kuti, Chochita inu ndi ichi: limodzi la magawo atatu la inu olowa paSabatalizilindira nyumba ya mfumu,

6 ndi lina lizikhala ku chipata cha Suri, ndi lina ku chipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuitchinjiriza.

7 Ndipo magawo awiri a inu, ndiwo onse otulukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu.

8 Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m’manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye.

9 Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

10 Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m’nyumba ya Yehova.

11 Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m’manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

12 Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m’manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.

13 Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m’nyumba ya Yehova;

14 napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m’dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang’amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu.

15 Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang’anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m’nyumba ya Yehova.

16 Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo kunyumba ya mfumu, namupha pomwepo.

Pangano la Yehoyada wansembe

17 Ndipo Yehoyada anachitachipanganopakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.

18 Namuka anthu onse a m’dzikomo kunyumba yaBaala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang’anira nyumba ya Yehova.

19 Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m’dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu kunyumba ya Yehova, nadzera njira ya chipata cha otumikira, kunka kunyumba ya mfumu. Nakhala iye pa chimpando cha mafumu.

20 Nakondwerera anthu onse a m’dziko, ndi m’mzinda munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu.

21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/11-4ba17fef3ffb7bf5dbcc293ffc28e9b5.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 12

Yowasi akonza Kachisi

1 Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

2 Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m’mene anamlangizira wansembe Yehoyada.

3 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.

4 Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m’mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.

5 Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, paliponse akapeza pogamuka.

6 Koma kunali, chaka cha makumi awiri mphambu zitatu cha mfumu Yowasi, ansembe sanathe kukonza mogamuka nyumba.

7 Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.

8 Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba.

9 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi paguwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova.

10 Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m’bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m’matumba, naziyesa ndalama zopereka m’nyumba ya Yehova.

11 Napereka ndalama zoyesedwa m’manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang’anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova,

12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.

13 Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;

14 pakuti anazipereka kwa iwo akugwira ntchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova.

15 Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m’manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.

16 Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.

Yowasi agonja kwa Hazaele mfumu ya Aramu

17 Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.

18 Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.

19 Machitidwe ena tsono a Yowasi ndi zonse adazichita sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

20 Ndipo anyamata ake ananyamuka, napangana, nakantha Yowasi kunyumba ya Milo potsikira ku Sila.

21 Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m’mzinda wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/12-13d6fb3e643593576c6027b830fdf6f2.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 13

Yehowahazi mfumu ya Israele

1 Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.

3 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m’dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m’dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo.

4 Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m’mene mfumu ya Aramu inawapsinja.

5 Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi padzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m’mahema mwao monga kale.

6 Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m’mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya.

7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.

8 Machitidwe ena tsono a Yehowahazi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

9 Ndipo Yehowahazi anagona ndi makolo ake, namuika mu Samariya; nakhala mfumu m’malo mwake Yowasi mwana wake.

Yehowasi mfumu ya Israele

10 Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi.

11 Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.

12 Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

13 Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele.

Kumwalira kwa Elisa

14 Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!

15 Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mivi; nadzitengera uta ndi mivi.

16 Nati kwa mfumu ya Israele, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ake pa manja a mfumu.

17 Nati, Tsegulani zenera la kum’mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu mu Afeki mpaka mudzawatha.

18 Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

19 Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.

20 Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amowabu analowa m’dziko poyambira chaka.

21 Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m’manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.

22 Ndipo Hazaele mfumu ya Aramu anapsinja Israele masiku onse a Yehowahazi.

23 Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa chachipanganochake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.

24 Nafa Hazaele mfumu ya Aramu, nakhala mfumu m’malo mwake Benihadadi mwana wake.

25 Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m’dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele mizinda ija adailanda m’dzanja la Yehowahazi atate wake ndi nkhondo. Yehowasi anamkantha katatu, naibweza mizinda ya Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/13-7fec170b86d17c24e561a8f820d8ac0d.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 14

Amaziya mfumu ya Yuda ndi Yehowasi mfumu ya Israele

1 Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai muYerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.

3 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.

4 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5 Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m’dzanja lake, anakantha anyamata ake amene adakantha mfumu atate wake;

6 koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, m’mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.

7 Anapha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.

8 Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso.

9 Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama yakuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.

10 Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;

11 Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.

12 Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawira yense kuhema kwake.

13 Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.

14 Natenga golide ndisilivayense, ndi zotengera zonse anazipeza m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m’nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya.

15 Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

16 Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m’malo mwake Yerobowamu mwana wake.

17 Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu.

18 Machitidwe ena tsono a Amaziya, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

19 Ndipo anamchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.

20 Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide.

21 Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m’malo mwa atate wake Amaziya.

22 Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.

Yerobowamu wachiwiri mfumu ya Israele

23 Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.

24 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

25 Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitaimneneriyo, ndiye wa Gatihefere.

26 Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.

27 Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.

28 Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

29 Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m’malo mwake Zekariya mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/14-9f68ca5a021fc518427088ea3b7a8904.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 15

Azariya mfumu ya Yuda

1 Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.

3 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.

4 Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5 Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhatempaka tsiku la imfa yake, nakhala m’nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang’anira banja la mfumu, naweruza anthu a m’dziko.

6 Machitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

7 Nagona Azariya ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m’mzinda wa Davide; nakhala mfumu m’malo mwake Yotamu mwana wake.

Zekariya mfumu ya Israele

8 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele mu Samariya miyezi isanu ndi umodzi.

9 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

10 Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m’malo mwake.

11 Machitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

12 Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.

Salumu mfumu ya Israele

13 Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi mu Samariya.

14 Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi mu Samariya, namupha; nakhala mfumu m’malo mwake.

15 Machitidwe ena tsono a Salumu ndi chiwembu chake anachichita, taonani, zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

Menahemu mfumu ya Israele

16 Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m’mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m’mwemo.

17 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi mu Samariya.

18 Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

19 Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente asilivachikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m’dzanja lake.

20 Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israele ndalamazi, nasonkhetsa achuma, yense masekeli makumi asanu a siliva, kuti azipereke kwa mfumu ya Asiriya. Nabwerera mfumu ya Asiriya osakhala m’dzikomo.

21 Machitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

22 Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m’malo mwake Pekahiya mwana wake.

Pekahiya mfumu ya Israele

23 Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.

24 Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

25 Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye mu Samariya, m’nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m’malo mwake.

26 Machitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazichita, taonani zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

Peka mfumu ya Israele

27 Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.

28 Nachita choipa pamaso pa Yehova, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

29 Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.

30 Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m’malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.

31 Machitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazichita, taonani, zalembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

Yotamu mfumu ya Yuda

32 Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

33 Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndipo dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

34 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya.

35 Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.

36 Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

37 Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye.

38 Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m’malo mwake Ahazi mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/15-05ab450120faa7f323cd084ad9302a92.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 16

Ahazi mfumu ya Yuda

1 Chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi muYerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake;

3 popeza anayenda m’njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa zaamitunduamene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.

4 Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.

5 Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa.

6 Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napirikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komwemo kufikira lero lino.

7 Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m’dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m’dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo.

8 Natenga Ahazisilivandi golide wopezeka m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya.

9 Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.

Guwa la nsembe la ku Damasiko

10 Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse.

11 Ndipo Uriya wansembe anamanga guwa la nsembelo, monga mwa zonse anazitumiza mfumu Ahazi zochokera ku Damasiko; momwemo Uriya wansembe analimanga asanabwere mfumu ku Damasiko.

12 Atafika mfumu kuchokera ku Damasiko, anapenya mfumu guwa la nsembelo, nayandikiza mfumu ku guwa la nsembelo, napereka nsembe pomwepo.

13 Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere paguwa la nsembelo.

14 Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati paguwa lake la nsembe ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa lake la nsembe.

15 Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Paguwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam’mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m’dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.

16 Nachita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi.

17 Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng’ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala.

18 Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a paSabataadawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya.

19 Machitidwe ena tsono adawachita Ahazi, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

20 Nagona Ahazi ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m’mzinda wa Davide; nakhala mfumu m’malo mwake Hezekiya mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/16-728cf72d15365473b82eb1ea97f1cf0c.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 17

Hoseya mfumu yotsiriza ya Israele

1 Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.

2 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye.

3 Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.

4 Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m’kaidi.

Asiriya apasula Samariya, Aisraele natengedwa ukapolo

5 Pamenepo mfumu ya Asiriya anakwera m’dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.

6 Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m’mizinda ya Amedi.

7 Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m’dziko la Ejipito pansi padzanja laFaraomfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,

8 nayenda m’miyambo yaamitunduamene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m’miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.

9 Ndipo ana a Israele anachita m’tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m’mizinda mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumzinda walinga komwe.

10 Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;

11 nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;

12 natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musachita ichi.

13 Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja lamnenerialiyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.

14 Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao.

15 Ndipo anakaniza malemba ake, ndichipanganoanachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa.

16 Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang’ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikiraBaala.

17 Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.

18 Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha.

19 Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m’malemba a Israele amene adawaika.

20 Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m’dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake.

21 Pakuti anang’amba Israele, kumchotsa kunyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati; Yerobowamu naingitsa Israele asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukulu.

22 Nayenda ana a Israele m’zolakwa zonse za Yerobowamu, zimene anazichita osazileka;

23 mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m’dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.

Mfumu ya Asiriya amangitsa alendo m’midzi ya Samariya

24 Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m’mizinda ya Samariya, m’malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m’mizinda mwake.

25 Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaope Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.

26 Motero ananena ndi mfumu ya Asiriya, kuti, Amitundu aja mudawachotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m’mizinda ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; chifukwa chake anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, ilikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.

27 Pamenepo mfumu ya Asiriya analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawachotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.

28 Nadza wina wa ansembewo adawachotsa ku Samariya, nakhala ku Betele, nawalangiza m’mene azimuopera Yehova.

29 Koma a mtundu uliwonse anapanga milungu yaoyao, naiika m’nyumba za misanje adazimangaAsamariya, a mtundu uliwonse m’mizinda mwao mokhala iwo.

30 Ndipo anthu a Babiloni anapanga Sukoti-Benoti, ndi anthu a Kuta anapanga Neregali, ndi anthu a Hamati anapanga Ashima,

31 ndi Aavi anapanga Nibihazi ndi Taritaki; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m’moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.

32 Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m’nyumba za misanje.

33 Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawachotsako.

34 Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele,

35 ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu ina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;

36 koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;

37 ndi malemba, ndi maweruzo, ndi chilamulo, ndi choikika anakulemberani muzisamalira kuzichita masiku onse, nimusamaopa milungu ina;

38 ndi chipangano ndinachichita nanu musamachiiwala, kapena kuopa milungu ina iai;

39 koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m’dzanja la adani anu onse.

40 Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba.

41 Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/17-3e839b1cecdb13f3819915c88e9976da.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 18

Hezekiya wabwino akhazikanso chipembedzo cha Yehova

1 Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Abi mwana wa Zekariya.

3 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake.

4 Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.

5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

6 Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

7 Ndipo Yehova anali naye, nachita iye mwanzeru kulikonse anamukako, napandukira mfumu ya Asiriya osamtumikira.

8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mzinda walinga.

9 Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.

10 Pakutha pake pa zaka zitatu anaulanda, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Israele analanda Samariya.

11 Ndipo mfumu ya Asiriya anachotsa Aisraele kunka nao ku Asiriya, nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m’mizinda ya Amedi;

12 chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwirachipanganochake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita.

Senakeribu amangira Yerusalemu misasa

13 Chaka chakhumi ndi zinai cha Hezekiya Senakeribu mfumu ya Asiriya anakwerera mizinda yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.

14 Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asiriya ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundichokere; chimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asiriya anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu asilivandi matalente makumi atatu a golide.

15 Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu.

16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golide wa pa zitseko za Kachisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asiriya.

17 Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.

18 Ndipo m’mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang’anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.

19 Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Chikhulupiriro ichi nchotani uchikhulupirira?

20 Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?

21 Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzampyoza dzanja lake; ateroFaraomfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye.

22 Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?

23 Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.

24 Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata aang’ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Ejipito akupatse magaleta ndi apakavalo?

25 Ngati ndakwerera malo ano wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu mu Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe mu Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.

27 Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? Si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

28 Naima kazembeyo, nafuula ndi mau aakulu mu Chiyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikulu mfumu ya Asiriya.

29 Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m’dzanja lake;

30 kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mzinda uwu sudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asiriya.

31 Musamvere Hezekiya; pakuti itero mfumu ya Asiriya, Mupangane nane zamtendere, nimutulukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wake, ndi yense ku mkuyu wake, ndi kumwa yense madzi a m’chitsime chake;

32 mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko laazitonandi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.

33 Kodi mulungu uliwonse waamitunduwalanditsa dziko lake m’dzanja la mfumu ya Asiriya ndi kale lonse?

34 Ili kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m’dzanja langa?

35 Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m’dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m’dzanja langa?

36 Koma anthuwo anakhala chete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

37 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang’anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong’ambika, namuuza mau a kazembeyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/18-7287d1aa3800a05d802ca33cdb0cfbe8.mp3?version_id=1068—

Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 19

Nkhawa ya Hezekiya ndi pemphero lake

1 Ndipo kunali, atamva mfumu Hezekiya, anang’amba zovala zake, nafundira chiguduli, nalowa m’nyumba ya Yehova.

2 Natuma Eliyakimu woyang’anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesayamnenerimwana wa Amozi.

3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.

4 Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.

5 Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.

6 Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asiriya anandichitira nao mwano.

7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m’dziko lake.

8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi.

9 Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,

10 Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti,Yerusalemusudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asiriya.

11 Taona, udamva icho mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

12 Kodi milungu yaamitunduinawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?

13 Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?

14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15 Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati paakerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16 Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.

17 Zoona, Yehova, mafumu a Asiriya anapasula amitundu ndi maiko ao,

18 naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; chifukwa chake anaiononga.

19 Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m’dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.

Yesaya amtonthoza mtima Hezekiya

20 Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Chondipempha iwe pa Senakeribu mfumu ya Asiriya ndachimva.

21 Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi waZiyoniakunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.

22 Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m’mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.

23 Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m’ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba.

24 Ndakapa, ndamwa madzi achilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Ejipito.

25 Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula mizinda yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.

26 Chifukwa chake okhalamo ao anali ofooka manja, anaopsedwa, nachita manyazi, ananga udzu wakuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.

27 Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.

28 Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m’makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m’mphuno mwako, ndi cham’kamwa changa m’milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.

29 Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.

30 Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba.

31 Pakuti ku Yerusalemu kudzatuluka otsala, ndi akupulumukawo kuphiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.

32 Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzalowa m’mzinda muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira.

33 Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m’mzinda muno, ati Yehova.

34 Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.

Mthenga wa Yehova awapha Aasiriya

35 Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.

36 Nachoka Senakeribu mfumu ya Asiriya, namuka, nabwerera, nakhala ku Ninive.

37 Ndipo kunali popembedza iye m’nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/19-aea863c5c1572d087d92c2107d71efd2.mp3?version_id=1068—