Categories
2 ATESALONIKA

2 ATESALONIKA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Ngakhale Paulo awalembera kalata ija, Atesalonika adakhala akutsutsanabe pa za kubweranso kwa Ambuye, mwakuti panali chisokonezo. Ena mwa iwo ankati tsiku la kubwera kwa Khristu lafika kale. Tsono Paulo awalembera kalata yachiwiri, kuwadziwitsa kuti Khristu asanabwere, zinthu zidzaipiratu, pakuti padzafika wina wake wotchedwa “Woipitsitsa uja” amene adzalimbane ndi Khristu, mwakuti zoipa zija zidzafika pake penipeni.

Nchifukwa chake Paulo akuwauza Akhristu kuti asaope zovuta ndi mazunzo, koma akhale ndi chikhulupiriro cholimba, abagwira ntchito kuti apeze chakudya, monga momwe iye ndi anzake amachitira, ndipo apitirize kuchita zabwino.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Ayamikira chikhulupiriro chao ndipo awachenjeza 1.3-13

Za kubwera kwa Woipitsitsa uja 2.1-17

Malangizo okhudza moyo wao wa Chikhristu 3.1-15

Mau omaliza 3.16-18

Categories
2 ATESALONIKA

2 ATESALONIKA 1

1 Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwaMpingowa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye YesuKhristu:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.

Kulimbika kwa Atesalonika nkana asautsidwa

3 Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;

4 kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu mu Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m’mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;

5 ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;

6 popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso,

7 ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndiangeloa mphamvu yake,

8 m’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;

9 amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake,

10 pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m’tsiku lija.

11 Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse chomkomera chonse, ndi ntchito ya chikhulupiriro mumphamvu;

12 kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TH/1-88a7a3123a92052778e6f5ac706ac145.mp3?version_id=1068—

Categories
2 ATESALONIKA

2 ATESALONIKA 2

Asanabwere Khristu adzaoneka wokana Khristu

1 Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu YesuKhristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye;

2 kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;

3 munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,

4 amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.

5 Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani izi?

6 Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akavumbulitsidwe iye m’nyengo yake ya iye yekha.

7 Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati.

8 Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;

9 ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama;

10 ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandire, kuti akapulumutsidwe iwo.

11 Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;

12 kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.

13 Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;

14 kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

15 Chifukwa chake tsono, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata yathu.

16 Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,

17 asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mau onse abwino.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TH/2-e10666c7e66dd6df1a9b3491200613b5.mp3?version_id=1068—

Categories
2 ATESALONIKA

2 ATESALONIKA 3

Zowachenjeza ndi malankhulano

1 Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;

2 ndi kuti tilanditsidwe m’manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si onse ali nacho chikhulupiriro.

3 Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

4 koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani.

5 Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m’chikondi cha mulungu ndi m’chipiriro chaKhristu.

6 Ndipo tikulamulirani, abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.

7 Pakuti mudziwa nokha m’mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhale dwakedwake mwa inu;

8 kapena sitinadye mkate chabe padzanja la munthu aliyense, komatu m’chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;

9 si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.

10 Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.

11 Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwakedwake, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina.

12 Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.

13 Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.

14 Koma ngati wina samvera mau athu m’kalata iyi, yang’anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.

15 Koma musamuyese mdani, koma mumuyambirire ngati mbale.

16 Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.

17 Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m’kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga.

18 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TH/3-277890d7aec07ad5224ae5b2f0a34718.mp3?version_id=1068—