Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yachiwiri ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Akorinto

inalembedwa panthawi imene ubale wake ndi mpingo wa ku Korinto sunali bwino konse. Anthu ena a ku mpingo wa ku Korinto ankamunena Paulo, komabe iye anaonetsa kuti amafunitsitsa kuti ayanjane naonso ndipo izi zitachitika, iye anakondwera kwambiri.

Mu gawo loyamba la kalatayi Paulo akukamba za ubale wake ndi mpingo wa ku Korinto, ndipo akulongosola chifukwa chimene iye anawayankha mokwiya potsata chipongwe chimene iwo anamuchitira komanso za mtsutsano umene unalipo mu mpingowo. Iye akulongosola kuti ali ndi chimwemwe kuti kukwiya kwake kunathandizira kuti iwo alape ndi kuyanjana. Kenaka akuwupempha mpingowo kuti upereke moolowa manja pothandiza Akhristu osowa a ku Yudeya. Mu mitu yomalizira, Paulo akuteteza utumiki wake wa utumwi kwa anthu ochepa a ku Korinto amene adadzikhazikitsa wokha ngati atumwi enieni, namanena kuti Paulo ndi mtumwi wonyenga.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-11

Paulo ndi mpingo wa ku Korinto 1.12—7.16

Chopereka cha Akhristu a ku Yudeya 8.1—9.15

Paulo adziteteza pa udindo wake monga mtumwi 10.1—13.10

Mau omaliza 13.11-14

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 1

1 Paulo,mtumwiwaKhristuYesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwaMpingowa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali muAkayamonse:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chiyamiko pa matonthozo a Mulungu

3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,

4 wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

5 Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.

6 Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.

7 Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.

8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;

9 koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

10 amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;

11 pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.

Chifukwa cha kuchedwa Paulo kudza ku Korinto

12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m’chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m’nzeru ya thupi, koma m’chisomo cha Mulungu tinadzisunga m’dziko lapansi, koma koposa kwa inu.

13 Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso muvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzavomereza kufikira chimaliziro;

14 monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m’tsiku la Ambuye wathu Yesu.

15 Ndipo m’kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri;

16 ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.

17 Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?

18 Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhale eya ndi iai.

19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhale eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.

20 Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa IyeAmen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

21 Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;

22 amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

23 Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.

24 Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/1-082e8bba3815b27435b39e619dbbf640.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 2

1 Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni.

2 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni?

3 Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.

4 Pakuti m’chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa.

5 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititse chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse.

6 Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira;

7 kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.

8 Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.

9 Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m’zonse.

10 Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso paKhristu;

11 kuti asatichenjerereSatana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.

12 Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,

13 ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.

Makhalidwe ndi zipatso za utumiki wa Paulo

14 Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m’chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

15 Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa;

16 koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

17 Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/2-c4b1668cccf3b2bfa834370cbe557c6a.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 3

1 Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?

2 Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;

3 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata yaKhristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome amiyala, koma m’magome a mitima yathupi.

4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu:

5 si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;

6 amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.

7 Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m’miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:

8 koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala mu ulemerero?

9 Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri.

10 Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwe cha ulemerero m’menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo.

11 Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili mu ulemerero.

12 Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,

13 ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang’anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa;

14 koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.

15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao.

16 Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chichotsedwa.

17 Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/3-6a88c6d8f884f0eb8f463b4c541c9820.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 4

Paulo alalikira Yesu yekhayekha

1 Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka;

2 koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.

3 Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;

4 mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero waKhristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.

5 Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma YesuKhristuAmbuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.

6 Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.

7 Koma tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;

8 ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi;

9 olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

10 nthawi zonse tilikusenzasenza m’thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m’thupi mwathu.

11 Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m’thupi lathu lakufa.

12 Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu.

13 Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula;

14 podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.

15 Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.

Chipatso cha kumva zowawa. Zosaoneka zilinganizidwa ndi zooneka

16 Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

17 Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;

18 popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/4-f0cff854b9bf218f95d71864820da0f7.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 5

1 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.

2 Pakutinso m’menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;

3 ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche.

4 Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.

5 Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.

6 Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m’thupi, sitili kwa Ambuye.

7 (Pakuti tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe);

8 koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.

9 Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye.

10 Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza waKhristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.

Utumiki wa chiyanjanitso

11 Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m’zikumbu mtima zanu.

12 Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.

13 Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.

14 Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;

15 ndipo adafera onse kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma mwa Iye amene adawafera iwo, nauka.

16 Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.

17 Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

18 Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;

19 ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.

20 Chifukwa chake tili atumiki m’malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m’malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

21 Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/5-62a841973f31974eb932ff57b097646f.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 6

Kudzikana kwa Paulo mu utumiki wake

1 Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,

2 (pakuti anena,

M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,

ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza.

Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);

3 osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe;

4 koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m’kupirira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja,

5 m’mikwingwirima, m’ndende, m’maphokoso, m’mavutitso, m’madikiro, m’masalo a chakudya;

6 m’mayeredwe, m’chidziwitso, m’chilekerero, m’kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m’chikondi chosanyenga;

7 m’mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,

8 mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;

9 monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;

10 monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Awadandaulira akhale oyera mtima

11 M’kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.

12 Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu.

13 Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.

14 Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?

15 NdipoKhristuavomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

16 Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

17 Chifukwa chake,

Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye,

Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka;

ndipo Ine ndidzalandira inu,

18 ndipo ndidzakhala kwa inu Atate,

ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi,

anena Ambuye Wamphamvuyonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/6-2f305d5fa545ff181abdc72c9d1cce3c.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 7

Paulo akondwera pa kudza kwa Tito, ndi pa zipatso za kalata yake woyamba

1 Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.

2 Tipatseni malo; sitinamchitire munthu chosalungama, sitinaipse munthu, sitinachenjerere munthu.

3 Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.

4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m’chisautso chathu chonse.

5 Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m’katimo mantha.

6 Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;

7 koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene anatonthozedwa nacho mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa.

8 Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata ija, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata ija inakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.

9 Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m’kanthu kalikonse.

10 Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.

11 Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M’zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m’menemo.

12 Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.

13 Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m’chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.

14 Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m’choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.

15 Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.

16 Ndikondwera kuti m’zonse ndilimbika mtima za inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/7-2d8cf32422bf33858840569909690cc8.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 8

Chipereko cha kwa Akhristu aumphawi a ku Yerusalemu

1 Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwaMipingoya ku Masedoniya,

2 kuti m’chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.

3 Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yao,

4 anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;

5 ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.

6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.

7 Koma monga muchulukira m’zonse, m’chikhulupiriro, ndi m’mau, ndi m’chidziwitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m’chisomo ichi.

8 Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.

9 Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu YesuKhristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.

10 Ndipo m’menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.

11 Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m’chimene muli nacho.

12 Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.

13 Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;

14 koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu.

15 Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinamtsalire; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichinamsowe.

16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

17 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake.

18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli mu Mipingo yonse;

19 ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m’chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;

20 ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira;

21 pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

22 Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m’zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu.

23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.

24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/8-6d21823f6abb21f2ae46439c7efd2c04.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 9

1 Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;

2 pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kutiAkayaanakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.

3 Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m’menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;

4 kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m’kulimbika kumene.

5 Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.

6 Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.

7 Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

8 Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m’zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;

9 monga kwalembedwa,

Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka;

chilungamo chake chikhale kunthawi yonse.

10 Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;

11 polemeretsedwa inu m’zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.

12 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;

13 popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino waKhristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;

14 ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.

15 Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/9-5838a978a1e6dc31be2fcc956b07afcf.mp3?version_id=1068—