Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Timoteo anali Mkhristu wachinyamata wa ku Asiya, mai wake anali Myuda koma bambo wake anali Mgriki. Paulo adamtenga kuti amperekeze pa maulendo ake ndi kumthandiza pa ntchito yolalika. Pomulembera kalatayi, Paulo afuna kumchenjeza pa zophunzitsa zina zabodza zimene zikusokoneza mpingo. Anthu ena ophatikiza nzeru zina zachiyuda ndi zina zachikunja ankati dziko lapansi monga lilirimu nloipa, ndipo palibe munthu angapulumuke akapanda kuphunzira nzeru zina zobisika ndi kutsata miyambo ina, monga kusala zakudya zina ndi zina ndi kuletsa maukwati. Paulo akuperekanso malangizo pa chipembedzo, za kayendetsedwe ka mpingo ndi za makhalidwe ofunika kwa atsogoleri. Akumuuzanso kuti iye ayesetse kukhala mtumiki wokhulupirika pa udindo wake woyang’anira magulu onse a Akhristu.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Malangizo okhudza mpingo ndi atsogoleri ake 1.3—3.16

Malangizo kwa Timoteo pa ntchito yake 4.1—6.21

Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 1

Paulo alangiza Timoteo

1 Paulo,mtumwiwaKhristuYesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu:

2 kwa Timoteo mwana wanga weniweni m’chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

3 Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

4 kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m’chikhulupiriro;

5 koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m’chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;

6 zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pake;

7 pofuna kukhalaaphunzitsi a malamulongakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.

8 Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo,

9 podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,

10 achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;

11 monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.

12 Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,

13 ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;

14 koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.

15 Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

16 komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m’tsogolo kufikira moyo wosatha.

17 Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi.Amen.

18 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;

19 ndi kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chao chidatayika;

20 a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwaSatana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/1-418795448bb20cbb901172483ea6df2b.mp3?version_id=1068—

Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 2

Pemphero la kwa anthu onse

1 Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;

2 chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekezeka monse.

3 Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;

4 amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.

5 Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu,KhristuYesu,

6 amene anadzipereka yekha chiombolo m’malo mwa onse; umboni m’nyengo zake;

7 umene anandiika ine mlaliki wake ndimtumwi(ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi waamitundum’chikhulupiriro ndi choonadi.

8 Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.

Zoyenera akazi

9 Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;

10 komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.

11 Mkazi aphunzire akhale wachete m’kumvera konse.

12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.

13 PakutiAdamuanayamba kulengedwa, pamenepo Heva;

14 ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m’kulakwa;

15 koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/2-0a8170af0d1cfbfedbd854c5012a08a6.mp3?version_id=1068—

Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 3

Zoyenera oyang’anira ndi atumiki

1 Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino.

2 Ndipo kuyenera woyang’anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

3 wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;

4 woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.

5 Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanjiMpingowa Mulungu?

6 Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.

7 Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

8 Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;

9 okhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m’chikumbu mtima choona.

10 Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa.

11 Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m’zonse.

12 Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m’nyumba yao ya iwo okha.

13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m’chikhulupiriro cha mwaKhristuYesu.

14 Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa,

15 kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m’nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.

16 Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m’thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndiangelo, analalikidwa mwaamitundu, wokhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/3-c6233ce223962c42de2485e6178a692f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 4

Chipanduko cha m’masiku otsiriza

1 Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,

2 m’maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m’chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto;

3 a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.

4 Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;

5 pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.

A utumiki akhale okhulupirika ndi achangu

6 Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino waKhristuYesu, woleredwa m’mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;

7 koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;

8 pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.

9 Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse.

10 Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.

11 Lamulira izi, nuziphunzitse.

12 Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m’mau, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.

13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza.

14 Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.

15 Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.

16 Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/4-3ed6b410f224e7cba00a2613b8e541d9.mp3?version_id=1068—

Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 5

Za okalamba ndi amasiye

1 Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;

2 akazi aakulu ngati amai; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.

3 Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.

4 Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.

5 Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m’mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.

6 Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo.

7 Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda chilema.

8 Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

9 Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,

10 wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.

11 Koma amasiye aang’ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitiraKhristuchipongwe afuna kukwatiwa;

12 pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chao choyamba.

13 Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.

14 Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang’ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;

15 pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsataSatana.

16 Ngati mkazi wina wokhulupirira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipoMpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.

Ulamuliro wa aphunzitsi. Malangizo ena

17 Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mau ndi m’chiphunzitso.

18 Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng’ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.

19 Pa mkulu usalandire chomnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.

20 Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo achite mantha.

21 Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndiangeloosankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.

22 Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.

23 Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang’ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.

24 Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata.

25 Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/5-a4e24bb3ba389691c6e20949cae9d8a4.mp3?version_id=1068—

Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 6

Zoyenera akapolo

1 Onse amene ali akapolo a m’goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.

2 Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.

Zochenjeza zina

3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu YesuKhristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:

4 iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;

5 makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.

6 Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu;

7 pakuti sitinatenge kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitingathe kupita nako kanthu pochoka pano;

8 koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimene zitikwanire.

9 Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chionongeko ndi chitayiko.

10 Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

11 Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.

12 Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

13 Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato;

14 kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu;

15 limene adzalionetsa m’nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;

16 amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m’kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha.Amen.

17 Lamulira iwo achuma m’nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;

18 kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;

19 nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.

20 Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama;

21 chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro. Chisomo chikhale nanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/6-a789bb02dcbaf3472b214cc55a04588e.mp3?version_id=1068—