Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli likukamba za kusintha kwa zinthu m’dziko la Aisraele, kuchokera pa nthawi ya

Oweruza

kufikira pa nthawi yokhazikitsa ufumu. Nkhani yonse yagona pa anthu atatuwa: Samuele mweruzi omaliza, Saulo mfumu yoyamba, ndiponso Davide ndi zochita zake pa unyamata wake asanalowe ufumu.

Phunziro lopezeka m’bukuli monganso m’mabuku ena osimba mbiri ya Aisraele ndi lakuti, kukhala okhulupirika kwa Mulungu kumabweretsa mtendere ndi madalitso, koma kusamvera ndi kupandukira Mulungu kumadzetsa zoipa. Awa ndi mau amene Yehova adawauza wansembe Eli, “Popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.” (2.30).

Mau ena opezeka m’bukumu aonetsa kuti si Aisraele onse ankafuna kukhala ndi mfumu yowalamulira. Paja Yehova yekha anali ngati mfumu yao yeniyeni; koma chifukwa cha pempho laolo, Yehova adawasankhirabe mfumu. Chinthu chofunika chinali chakuti mfumuyo pamodzi ndi Aisraele onse amvere ulamuliro wa Mulungu ndi kutsata mau ake (2.7-10); akamatero, onse adzakhala pabwino, anthu olemera ndi osauka omwe.

Za mkatimu

Samuele pa ntchito yake yoweruza Aisraele

1.1—7.17

Saulo alowa ufumu

8.10—10.27

Zaka zoyamba za ufumu wa Saulo

11.1—15.35

Saulo ndi Davide

16.1—30.31

Imfa ya Saulo ndi ana ake

31.1-13

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 1

1 Ndipo panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Elikana, mwana wake wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, Mwefuremu.

2 Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.

3 Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m’mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.

4 Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wake, ndi ana ake onse, aamuna ndi aakazi, gawo lao;

5 koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake.

6 Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake.

7 Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.

8 Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?

9 Chomwecho Hana anauka atadya mu Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.

10 Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;

11 nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.

12 Ndipo panali, m’mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake.

13 Koma Hana ananena mu mtima; milomo yake inatukula, koma mau ake sanamveke; chifukwa chake Eli anamuyesa woledzera.

14 Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako.

15 Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwe vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.

16 Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; chifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kuchuluka kwa kudandaula kwanga ndi kuvutika kwanga.

17 Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.

18 Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.

19 Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.

20 Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,

21 Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lake onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya chaka ndi chaka, ndi ya chowinda chake.

22 Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.

23 Ndipo Elikana mwamuna wake anati, Chita chimene chikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ake. Chomwecho mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wake, kufikira anamletsa kuyamwa.

24 Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng’ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng’ono.

25 Ndipo iwo anapha ng’ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli.

26 Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.

27 Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye;

28 chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/1-ef9f15a8491ab620c761f067435b8de5.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 2

Choyamikira cha Hana

1 Ndipo Hana anapemphera, nati,

Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova,

nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova;

pakamwa panga pakula kwa adani anga;

popeza ndikondwera m’chipulumutso chanu.

2 Palibe wina woyera ngati Yehova;

palibe wina koma Inu nokha;

palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

3 Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero;

m’kamwa mwanu musatuluke zolulutsa;

chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru,

ndipo Iye ayesa zochita anthu.

4 Mauta a amphamvu anathyoka,

koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m’chuuno.

5 Amene anakhuta anakasuma chakudya;

koma anjalawo anachira;

inde chumba chabala asanu ndi awiri;

ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.

6 Yehova amapha, napatsa moyo;

Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.

7 Yehova asaukitsa, nalemeretsa;

achepetsa, nakuzanso.

8 Amuutsa waumphawi m’fumbi,

nanyamula wosowa padzala,

kukamkhalitsa kwa akalonga;

ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero.

Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova,

ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.

9 Adzasunga mapazi a okondedwa ake,

koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima;

pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.

10 Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika;

kumwamba Iye adzagunda pa iwo;

Yehova adzaweruza malekezero a dziko.

Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake,

nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.

11 Ndipo Elikana ananka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo.

Kuchimwa kwa ana a Eli

12 Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.

13 Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m’dzanja lake;

14 nachipisa m’chimphuli, kapena mumkhate, kapena m’nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko.

15 Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.

16 Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

17 Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.

18 Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m’chuuno ndiefodiwabafuta.

19 Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung’ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka.

20 Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m’malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.

21 Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.

22 Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo lachihema chokomanako.

23 Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.

24 Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.

25 Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.

26 Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.

Mneneri aneneratu za kupasuka kwa banja la Eli

27 Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali mu Ejipito, m’nyumba yaFarao?

28 Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?

29 Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m’mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?

30 Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.

31 Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m’banja lako musakhalenso nkhalamba.

32 Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m’malo mwa zabwino zonse Iye akadachitira Israele. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba chikhalire.

33 Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha paguwa langa la nsembe, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m’banja lako adzamwalira akali biriwiri.

34 Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.

35 Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m’chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.

36 Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m’banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaone kakudya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/2-1a14a420767e8e6bd79f3928cafb4269.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 3

Masomphenya a Samuele

1 Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.

2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m’malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);

3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m’mene munali likasa la Mulungu.

4 Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano.

5 Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitane, kagone. Napita iye, nagona.

6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.

7 Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

8 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.

9 Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m’malo mwake.

10 Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.

12 Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.

13 Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.

14 Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

Samuele awulula kwa Eli

15 Ndipo Samuele anagona kufikira m’mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.

16 Pamenepo Eli anaitana Samuele, nati, Mwana wanga, Samuele. Nati iye, Ndine.

17 Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.

18 Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.

19 Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe.

20 Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhalemneneriwa Yehova.

21 Ndipo Yehova anaonekanso mu Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/3-14d33f035d75dac34878bfdce1045d58.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 4

Afilisti akantha Aisraele

1 Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.

2 Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.

Likasa lilandidwa, Hofeni ndi Finehasi aphedwa

3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengerelikasa la chipanganola Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m’dzanja la adani athu.

4 Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati paakerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.

5 Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi.

6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n’lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.

7 Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza nkale lonse panalibe chinthu chotere.

8 Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m’manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m’chipululu ndi yomweyi.

9 Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao.

10 Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi.

11 Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.

12 Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong’ambika, ndi dothi pamutu pake.

Imfa ya Eli

13 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m’mbali mwa njira, alikuyang’anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m’mzindamo, nanena izi, a m’mzinda monse analira.

14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.

15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong’o osapenya.

16 Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga?

17 Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa.

18 Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai.

19 Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera.

20 Ndipo pamene adati amwalire, anthu aakazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira.

21 Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.

22 Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/4-f29df2c77837670517c8d4370cb4933d.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 5

Likasa la Mulungu kunyumba ya Dagoni

1 Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.

2 Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni.

3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m’malo mwake.

4 Ndipo m’mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha.

5 Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m’nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino.

Masauko a Afilisti chifukwa cha likasa

6 Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m’midzi yake.

7 Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.

8 Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko.

9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang’ono; ndi mafundo anawabuka.

10 Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu.

11 Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m’mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.

12 Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mzindawo kunakwera kumwamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/5-69ecef3fa6842f65ed3044ac708e7ad6.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 6

Afilisti abweza likasa ku dziko la Aisraele

1 Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.

2 Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.

3 Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israele, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yopalamula, mukatero mudzachiritsidwa, ndi kudziwa chifukwa chake dzanja lake lili pa inu losachoka.

4 Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.

5 Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.

6 Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndiFaraoanaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?

7 Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng’ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng’ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;

8 ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m’bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.

9 Ndipo muyang’anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.

10 Ndipo anthuwo anatero; natenga ng’ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao;

11 naika likasa la Yehova pagaletapo, ndi bokosi m’mene munali mbewa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.

12 Ndipo ng’ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.

13 Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m’chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona.

14 Ndipo galetalo linafika m’munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pamwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng’ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.

15 Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m’mene munali zokometsera zagolide, naziika pamwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.

16 Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo.

17 Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi;

18 ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, mizinda ya malinga, ndi midzi yopanda malinga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m’munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.

19 Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m’likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.

Likasa lisungidwa ku Kiriyati-Yearimu

20 Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife?

21 Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/6-9ca9e6ba1aaac566a6452163c956e7f0.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 7

1 Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m’nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.

Afilisti akanthidwa ku Mizipa

2 Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.

3 Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndiAsitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m’manja a Afilisti.

4 Pomwepo ana a Israele anachotsa Abaalandi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.

5 Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.

6 Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa.

7 Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo.

8 Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m’manja a Afilistiwo.

9 Ndipo Samuele anatengamwanawankhosawoyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.

10 Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.

11 Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara.

12 Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.

13 Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele.

14 Ndipo mizinda ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa midzi yao m’manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere;

15 ndipo Samuele anaweruza Israele masiku onse a moyo wake.

16 Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m’malo onse amenewa.

17 Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/7-a0cd6d3c24ae536611a2a58c4d542716.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 8

Aisraele akhumba mfumu

1 Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake aamuna akhale oweruza a Israele.

2 Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba.

3 Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.

4 Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama;

5 nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo muchitidwa m’mitundu yonse ya anthu.

6 Koma chimenechi sichinakondweretse Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.

7 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.

8 Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso.

9 Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.

10 Ndipo Samuele anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova.

11 Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu aamuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;

12 idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.

13 Ndipo idzatenga ana anu aakazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.

14 Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mpesa yanu, ndi minda yaazitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.

15 Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.

16 Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake.

17 Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake.

18 Ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.

19 Koma anthu anakana kumvera mau a Samuele; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;

20 kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kutuluka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu.

21 Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m’makutu a Yehova.

22 Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumzinda wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/8-ba15a571f84f2990e673f761ffe7ad5f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 9

Saulo afuna abulu olowerera a atate wake

1 Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.

2 Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m’chifuwa.

3 Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo.

4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.

5 Pamene anafika ku dziko la Zufu, Saulo anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira abuluwo, ndi kutenga nkhawa chifukwa cha ife.

6 Koma ananena naye, Onatu, m’mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.

7 Ndipo Saulo ananena ndi mnyamata wake, Koma taona, tikapitako timtengere chiyani munthuyo? Popeza mkate udatha m’zotengera zathu, ndiponso tilibe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tili nacho chiyani?

8 Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m’dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wasiliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.

9 Kale mu Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwamnenerimakono ano, anatchedwa mlauli kale.

10 Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguyo.

11 Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?

12 Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m’tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;

13 mutafika m’mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza.

14 Ndipo iwowa anakwera kumzinda; ndipo m’mene analowa m’mzindamo, onani, Samuele anatulukira pali iwo, kuti akakwere kumsanje.

Saulo akomana ndi Samuele

15 Ndipo Yehova anaululiratu m’khutu la Samuele dzulo lake la tsiku limene Saulo anabwera, kuti,

16 Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m’manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

17 Ndipo pamene Samuele anaona Saulo, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! Ameneyu adzaweruza anthu anga.

18 Pomwepo Saulo anayandikira kwa Samuele pakati pa chipata, nati, Mundidziwitse nyumba ya mlauliyo ili kuti.

19 Ndipo Samuele anayankha Saulo nati, Ine ndine mlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m’mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse zili mumtima mwako.

20 Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako?

21 Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling’ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?

22 Ndipo Samuele anatenga Saulo ndi mnyamata wake, napita nao ku chipinda cha alendo, nawakhalitsa pamalo a ulemu pakati pa oitanidwa onse; ndiwo anthu monga makumi atatu.

23 Ndipo Samuele ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe.

24 Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.

25 Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.

26 Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.

27 Ndipo pamene analikutsika polekeza mzinda, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/9-156a4f04714f79d136328efe3c001e4e.mp3?version_id=1068—