1 Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,
2 lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;
3 ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;
4 amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,
5 inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa YesuKhristu.
6 Chifukwa kwalembedwa m’lembo,
Taona, ndiika muZiyonimwala wotsiriza wa pangodya,
wosankhika, wa mtengo wake;
ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.
7 Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo osakhulupirira,
Mwala umene omangawo anaukana,
womwewo unayesedwa mutu wa pangodya.
8 Ndipo,
Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa.
Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.
9 Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
10 inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
Za mayendedwe ao pakati pa akunja. Agonje kwa akulu
11 Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;
12 ndipo mayendedwe anu mwaamitunduakhale okoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.
13 Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;
14 kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.
15 Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;
16 monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.
17 Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.
Zoyenera anyamata Akhristu
18 Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.
19 Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.
20 Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.
21 Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;
22 amene sanachite tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;
23 amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;
24 amene anasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
25 Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang’anira wa moyo wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/2-a6a9dc170e2ed5072df95902e5ad68a9.mp3?version_id=1068—