Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 20

1 Ndipo kunali, pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Yowabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala kuYerusalemu. Ndipo Yowabu anakantha Raba, naupasula.

2 Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumchotsa pamutu pake, napeza kulemera kwake talente wa golide; panalinso miyala ya mtengo wake pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, natulutsa zankhondo za m’mzindamo zambiri ndithu.

3 Natulutsanso anthu anali m’mwemo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi zipangizo zochekera zachitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.

Abwereza kukantha Afilisti

4 Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezere ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Sipai wa ana a chimphona; ndipo anawagonjetsa.

5 Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliyati Mgiti, amene luti la mkondo wake linanga mtanda woombera nsalu.

6 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene zala zake za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi chimodzi ku dzanja lililonse, ndi zisanu ndi chimodzi ku phazi lililonse; nayenso anabadwa mwa chimphonacho.

7 Ndipo potonza Israele iyeyu Yonatani mwana wa Simea mbale wake wa Davide anamkantha.

8 Awa anabadwa mwa chimphonacho ku Gati, koma anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/20-1a6920d4244cba0897aec2a6b17e5b50.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 21

Davide awerenga anthu, mliri ugwera Israele

1 PamenepoSatanaanaukira Israele, nasonkhezera Davide awerenge Israele.

2 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa akulu a anthu, Kawerengeni Israele kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe chiwerengo chao.

3 Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?

4 Koma mau a mfumu anamtsutsa Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza kuYerusalemu.

5 Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.

6 Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.

7 Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele.

8 Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndachimwa kwakukulu ndi kuchita chinthu ichi; koma tsopano, muchotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndachita kopusa ndithu.

9 Ndipo Yehova ananena ndi Gadi mlauli wa Davide, ndi kuti,

10 Kanene kwa Davide kuti, Atero Yehova, Ndikuikira zitatu; dzisankhireko chimodzi ndikuchitire ichi.

11 Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko;

12 kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m’dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine?

13 Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m’dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m’dzanja la munthu.

14 Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israele; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israele.

Davide amangira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani

15 Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.

16 Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m’dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.

17 Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.

18 Pamenepo mthenga wa Yehova analamula Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi.

19 Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m’dzina la Yehova.

20 Pocheuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ake aamuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu.

21 Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, natuluka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yake pansi.

22 Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.

23 Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu ichite chomkomera m’maso mwake; taonani, ndikupatsani ng’ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.

24 Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, Iai, koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse; pakuti sindidzatengera Yehova chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake.

25 Momwemo Davide anapatsa Orinani chogulira malowa golide wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwake.

26 Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m’mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.

27 Ndipo Yehova analamula wamthenga kuti abweze lupanga lake m’chimake.

28 Nthawi yomweyi, pakuona Davide kuti Yehova anamvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo.

29 Pakuti chihema cha Yehova amene Mose anapanga m’chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi.

30 Koma Davide sanathe kumuka kukhomo kwake kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/21-f0149d4cadfbfa1c2401749a06460bed.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 22

Davide akonzeratu mirimo yakumanga Kachisi

1 Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.

2 Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m’dziko la Israele; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.

3 Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake;

4 ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Atiro anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yochuluka.

5 Ndipo Davide anati, Solomoni mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakhwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikulu yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mochuluka asanamwalire.

Davide amlangiza Solomoni ammangire Yehova nyumba

6 Pamenepo iye anaitana Solomoni mwana wake, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

7 Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.

8 Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wochuluka, popeza wachita nkhondo zazikulu; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;

9 taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phee; ndipo ndidzampumulitsira adani ake onse pozungulirapo, pakuti dzina lake lidzakhala Solomoni; ndipo ndidzapatsa Israele mtendere ndi bata masiku ake;

10 iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wake; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wake pa Israele, kosalekeza.

11 Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe.

12 Chokhachi, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israele, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.

13 Momwemo udzalemerera, ukasamalira kuchita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israele; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.

14 Taona tsono, m’kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi asiliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.

15 Uli naonso antchito ochuluka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akuchita ntchito zilizonse;

16 golide, ndisiliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nuchite, Yehova akhale nawe.

17 Davide analangizanso akalonga a Israele athandize Solomoni mwana wake, ndi kuti,

18 Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Sanakupumulitseni pambali ponse? Pakuti anapereka nzika za m’dziko m’dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ake.

19 Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalolikasa la chipanganola Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/22-bbf39644313853c55d837a0dfbbc15d4.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 23

Davide alonga Solomoni mu ufumu, nakonza chigawo cha Alevi

1 Atakalamba tsono Davide ndi kuchuluka masiku, iye analonga mwana wake Solomoni akhale mfumu ya Israele.

2 Ndipo anasonkhanitsa akulu onse a Israele, ndi ansembe ndi Alevi.

3 Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.

4 A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang’anira ntchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi chimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,

5 ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.

6 Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.

7 A Ageresoni: Ladani ndi Simei.

8 Ana a Ladani: wamkulu ndi Yehiyele, ndi Zetamu, ndi Yowele; atatu.

9 Ana a Simei: Selomoti, ndi Haziyele, ndi Harani; atatu. Ndiwo akulu a nyumba za makolo a Ladani.

10 Ndi ana a Simei: Yahati, Zina, ndi Yeusi, ndi Beriya. Awa anai ndiwo ana a Simei.

11 Wamkulu wa iwo ndi Yahati, mnzake ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.

12 Ana a Kohati: Amuramu, Izihara, Hebroni, ndi Uziyele; anai.

13 Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m’dzina lake kosatha.

14 Kunena za Mose munthu wa Mulunguyo, ana ake anatchulidwa mwa fuko la Levi.

15 Ana a Mose: Geresomo, ndi Eliyezere.

16 Ana a Geresomo: wamkulu ndi Sebuele.

17 Ndi ana a Eliyezere: wamkulu ndi Rehabiya. Ndipo Eliyezere analibe ana ena, koma ana a Rehabiya anachuluka kwambiri.

18 Ana a Izihara: wamkulu ndiye Selomiti.

19 Ana a Hebroni: wamkulu ndi Yeriya, wachiwiri ndi Amariya, wachitatu ndi Yahaziele, wachinai ndi Yekameamu.

20 Ana a Uziyele: wamkulu ndi Mika, wachiwiri ndi Isiya.

21 Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi ana a Mali: Eleazara ndi Kisi.

22 Nafa Eleazara wopanda ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.

23 Ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yeremoti; atatu.

24 Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

25 Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israele wapumulitsa anthu ake; ndipo akhala muYerusalemukosatha;

26 ndiponso Alevi asasenzenso chihema ndi zipangizo zake zonse za utumiki wake.

27 Pakuti monga mwa mau ake otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

28 Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m’nyumba ya Yehova, m’mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;

29 ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda chotupitsa, ndi ya chiwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iliyonse;

30 ndi kuimirira m’mawa ndi m’mawa kuyamika ndi kulemekeza Yehova, momwemonso madzulo;

31 ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwake monga mwa lemba lake, kosalekeza pamaso pa Yehova;

32 ndi kuti asunge udikiro wachihema chokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/23-22b1f9447a234b43cf6aa6934599721a.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 24

Magawo 24 a ansembe

1 Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

2 Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe.

3 Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao mu utumiki wao.

4 Ndipo anapeza kuti amuna aakulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.

5 Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.

6 Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.

7 Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, wachiwiri Yedaya,

8 wachitatu Harimu, wachinai Seorimu,

9 wachisanu Malikiya, wachisanu ndi chimodzi Miyamini,

10 wachisanu ndi chiwiri Hakozi, wachisanu ndi chitatu Abiya,

11 wachisanu ndi chinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya,

12 wakhumi ndi chimodzi Eliyasibu, wakhumi ndi chiwiri Yakimu,

13 wakhumi ndi chitatu Hupa, wakhumi ndi chinai Yesebeabu,

14 wakhumi ndi chisanu Biliga, wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Imeri,

15 wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Heziri, wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hapizeze,

16 wakhumi ndi chisanu ndi chinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikele,

17 wa makumi awiri ndi chimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi chiwiri Gamuli,

18 wa makumi awiri ndi chitatu Delaya, wa makumi awiri ndi chinai Maaziya.

19 Awa ndi malongosoledwe ao mu utumiki wao kulowa m’nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.

20 Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amuramu, Subaele; wa ana a Subaele, Yedeiya.

21 Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkulu ndi Isiya.

22 Wa Aizihara: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.

23 Ndi wa ana a Hebroni: mkulu ndi Yeriya, wachiwiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameamu.

24 Wa ana a Uziyele, Mika; wa ana a Mika, Samiri.

25 Mbale wa Mika, Isiya; a ana a Isiya, Zekariya.

26 Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno.

27 Ana a Merari: wa Yaziya, Beno, ndi Sohamu, ndi Zakuri, ndi Ibiri.

28 Wa Mali: Eleazara, ndiye wopanda ana.

29 Wa Kisi: mwana wa Kisi, Yerameele.

30 Ndi ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yerimoti. Awa ndi ana a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.

31 Awanso anachita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akulu a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkulu wa nyumba za makolo monga mng’ono wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/24-c16135bcb3b7fc14ae7181383f57417c.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 25

Chigawo cha oimbira nyimbo

1 Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho:

2 a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa chilangizo cha Asafu, wakunenera mwa chilangizo cha mfumu.

3 A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.

4 A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamiti-Ezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahaziyoti;

5 awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m’mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yake. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna khumi ndi anai, ndi ana aakazi atatu.

6 Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m’nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m’nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.

7 Ndipo chiwerengo chao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa aimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.

8 Ndipo anachita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang’ono ndi akulu, mphunzitsi ndi wophunzira.

9 Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; wachiwiri Gedaliya, iye ndi abale ake, ndi ana ake khumi ndi awiri;

10 wachitatu Zakuri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

11 wachinai Iziri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

12 wachisanu Netaniya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

13 wachisanu ndi chimodzi Bukiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

14 wachisanu ndi chiwiri Yesarela, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

15 wachisanu ndi chitatu Yesaya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

16 wachisanu ndi chinai Mataniya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

17 wakhumi Simei, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

18 wakhumi ndi chimodzi Azarele, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

19 wakhumi ndi chiwiri Hasabiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

20 wakhumi ndi chitatu Subaele, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

21 wakhumi ndi chinai Matitiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

22 wakhumi ndi chisanu Yeremoti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

23 wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Hananiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

24 wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Yosibekasa, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

25 wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hanani, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

26 wakhumi ndi chisanu ndi chinai Maloti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

27 wamakumi awiri Eliyata, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

28 wa makumi awiri ndi chimodzi Hotiri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

29 wa makumi awiri ndi chiwiri Gidaliti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

30 wa makumi awiri ndi chitatu Mahaziyoti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri;

31 wa makumi awiri ndi chinai Romamiti-Ezere, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/25-10cfaaf8799697c1e2b944529adc67bf.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 26

Chigawo cha odikira

1 A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu.

2 Ndipo Meselemiya anali ndi ana, woyamba Zekariya, wachiwiri Yediyaele, wachitatu Zebadiya, wachinai Yatiniele,

3 wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani, wachisanu ndi chiwiri Eliehoenai.

4 Ndipo Obededomu anali nao ana, woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele,

5 wachisanu ndi chimodzi Amiyele, wachisanu ndi chiwiri Isakara, wachisanu ndi chitatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa.

6 Kwa Semaya mwana wake yemwe kunabadwa ana, akulamulira nyumba ya atate wao; pakuti anali ngwazi zamphamvu.

7 Ana a Semaya: Otini, ndi Refaele, ndi Obedi, Elizabadi, amene abale ao ndiwo odziwa mphamvu, Elihu, ndi Semakiya.

8 Onsewa ndiwo a ana a Obededomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obededomu.

9 Ndi Meselemiya anali ndi ana, ndi abale odziwa mphamvu khumi mphambu asanu ndi atatu.

10 Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkulu ndi Simiri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wake anamuyesa wamkulu;

11 wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya, wachinai Zekariya; ana ndi abale onse a Hosa ndiwo khumi ndi atatu.

12 Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akuchita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m’nyumba ya Yehova.

13 Ndipo anachita maere, ang’ono ndi akulu, monga mwa nyumba za makolo ao, kuchitira zipata zonse.

14 Ndi maere a kum’mawa anagwera Selemiya. Ndipo anachitira maere Zekariya mwana wake, phungu wanzeru, ndi maere anamgwera kumpoto;

15 Obededomu kumwera, ndi ana ake nyumba ya akatundu.

16 Supimu ndi Hosa kumadzulo, ku chipata cha Saleketi, ku mseu wokwerapo, udikiro pandunji pa udikiro.

17 Kum’mawa kunali Alevi asanu ndi mmodzi, kumpoto anai tsiku ndi tsiku, kumwera anai tsiku ndi tsiku, ndi a nyumba ya akatundu awiri ndi awiri.

18 Ku Parabara kumadzulo anai kumseu, ndi awiri ku Parabara.

19 Awa ndi magawidwe a odikira; a ana a Akora, ndi a ana a Merari.

Osunga chuma Nyumba ya Mulungu

20 Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang’anira chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi chuma cha zopatulika.

21 Ana a Ladani: ana a Ladani a Ageresoni, akulu a nyumba za makolo a Ladani Mgeresoni, Yehiyeli.

22 Ana a Yehiyeli: Zetamu ndi Yowele mbale wake, oyang’anira chuma cha nyumba ya Yehova.

23 Aamuramu, Aizihara, Ahebroni, Auziyele;

24 ndi Sebuele mwana wa Geresomo, mwana wa Mose, ndiye mkulu woyang’anira zuma.

25 Ndi abale ake a Eliyezere: Rehabiya mwana wake, ndi Yesaya mwana wake ndi Yoramu mwana wake, ndi Zikiri mwana wake, ndi Selomoti mwana wake.

26 Selomoti amene ndi abale ake anayang’anira chuma chonse cha zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akulu a nyumba za akulu, akulu a zikwi ndi mazana, adazipatula.

27 Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova.

28 Ndipo zonse adazipatula Samuele mlauli, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndi Yowabu mwana wa Zeruya; aliyense anapatula kanthu kalikonse, anazisunga Selomoti ndi abale ake.

Akapitao ndi oweruza

29 A Aizihara: Kenaniya ndi ana ake anachita ntchito ya pabwalo ya Israele, akapitao ndi oweruza milandu.

30 A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake odziwa mphamvu chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang’anira Israele tsidya lino la Yordani kumadzulo, kuyang’anira ntchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.

31 Yeriya ndiye mkulu wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Chaka cha makumi anai cha ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazere wa ku Giliyadi.

32 Ndi abale ake ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akulu a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang’anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/26-27d19984d88449b9d10f2e4d21a33cb7.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 27

Ankhondo ndi akazembe ao

1 Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.

2 Woyang’anira chigawo choyamba cha mwezi, woyamba ndiye Yasobeamu mwana wa Zabidiele; m’chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

3 Ndiye wa ana a Perezi, mkulu wa akazembe onse a khamu mwezi woyamba.

4 Woyang’anira chigawo cha mwezi wachiwiri ndiye Dodai Mwahohi ndi chigawo chake; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m’chigawo chake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

5 Kazembe wachitatu wa khamu wa mwezi wachitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkulu; ndi m’chigawo mwake munalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.

6 Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang’anira chigawo chake ndi Amizabadi mwana wake.

7 Wachinai wa mwezi wachinai ndiye Asahele mbale wa Yowabu, ndi pambuyo pake Zebadiya mwana wake; ndi m’chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

8 Kazembe wachisanu wa mwezi wachisanu ndiye Samuti Mwizara; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

9 Wachisanu ndi chimodzi wa mwezi wachisanu ndi chimodzi ndiye Ira mwana wa Ikesi Mtekowa; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

10 Wachisanu ndi chiwiri wa mwezi wachisanu ndi chiwiri ndiye Helezi Mpeloni wa ana a Efuremu; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

11 Wachisanu ndi chitatu wa mwezi wachisanu ndi chitatu ndiye Sibekai Muhusa wa Azera; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

12 Wachisanu ndi chinai wa mwezi wachisanu ndi chinai ndiye Abiyezere Mwanatoti wa Abenjamini; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

13 Wakhumi wa mwezi wakhumi ndiye Maharai Mnetofa wa Azera; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

14 Wakhumi ndi chimodzi wa mwezi wakhumi ndi chimodzi ndiye Benaya Mpiratoni wa ana a Efuremu; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

15 Wakhumi ndi chiwiri wa mwezi wakhumi ndi chiwiri ndiye Helidai Mnetofa wa Otiniyele; ndi m’chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.

Oyang’anira mafuko 12 a Israele

16 Koma oyang’anira mafuko a Israele ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliyezere mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;

17 wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemuwele; wa Aroni, Zadoki;

18 wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omuri mwana wa Mikaele;

19 wa Zebuloni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafutali, Yerimoti mwana wa Aziriele;

20 wa ana a Efuremu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa hafu la fuko la Manase, Yowele mwana wa Pedaya;

21 wa hafu la fuko la Manase mu Giliyadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yaasiyele mwana wa Abinere;

22 wa Dani, Azarele mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mafuko a Israele.

23 Koma Davide sanawerenge iwo a zaka makumi awiri ndi ochepapo, pakuti Yehova adati kuti adzachulukitsa Israele ngati nyenyezi za kuthambo.

24 Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwe m’buku la mbiri ya mfumu Davide.

Oyang’anira a zake za Davide

25 Ndipo woyang’anira chuma cha mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyele, ndi woyang’anira wa chuma cha m’minda, m’mizinda ndi m’midzi, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;

26 ndi woyang’anira iwo akugwira ntchito ya m’munda yakulima nthaka ndiye Eziri mwana wa Kelubu;

27 ndi woyang’anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang’anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;

28 ndi woyang’anira mitengo yaazitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala-Hanani Mgederi; ndi woyang’anira zosungiramo mafuta ndiye Yowasi;

29 ndi woyang’anira ng’ombe zakudya mu Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang’anira ng’ombe za m’zigwa ndiye Safati mwana wa Adilai;

30 ndi woyang’anirangamirandiye Obili Mwismaele; ndi woyang’anira abulu ndiye Yedeiya Mmeronoti;

31 ndi woyang’anira zoweta zazing’ono ndiye Yazizi Mhagiri. Onsewa ndiwo akulu a zolemera zake za mfumu Davide.

32 Ndipo Yonatani atate wake wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;

33 ndi Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndi Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu;

34 ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/27-ed4032c8a48689b9bc2d6f17a07224f8.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 28

Davide alangiza akulu onse ndi Solomoni yemwe

1 Pamenepo Davide anasonkhanitsa kuYerusalemuakalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.

2 Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangiralikasa la chipanganola Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.

3 Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.

4 Komatu Yehova Mulungu wa Israele anasankha ine m’nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israele kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m’nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israele yense;

5 ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.

6 Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake.

7 Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kosatha, akalimbika kuchita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.

8 Ndipo tsopano, pamaso pa Aisraele onse, khamu la Yehova, ndi m’makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanulanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu cholowa chao kosalekeza.

9 Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.

10 Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite.

Davide apereka kwa Solomoni chifaniziro ndi mirimo ya Kachisi

11 Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m’katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;

12 ndi chifaniziro cha zonse anali nazo mwa mzimu, cha mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi cha zipinda zonse pozungulirapo, cha zosungiramo chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi cha zosungiramo chuma za zinthu zopatulika;

13 ndi cha magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi cha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi cha zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;

14 cha golide woyesedwa kulemera kwake wa zipangizo zagolide, wa zipangizo zonse za ntchito ya mtundu uliwonse; chasilivawa zipangizo zasiliva woyesedwa kulemera kwake, wa zipangizo za ntchito ya mitundumitundu;

15 mwa kulemera kwakenso cha zoikaponyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikaponyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikaponyali chilichonse;

16 ndi golide woyesedwa kulemera kwake wa magome a mkate woonekera, wa gome lililonse; ndi siliva wa magome asiliva,

17 ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golide woona, ndi cha mitsuko yake yagolide, woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse; ndi cha mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse;

18 ndi cha guwa la nsembe lofukizapo la golide woyengetsa woyesedwa kulemera kwake, ndi chifaniziro cha galeta waakerubiagolide akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la chipangano la Yehova.

19 Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.

20 Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.

21 Ndipo taona, pali zigawo za ansembe ndi Alevi, za utumiki wonse wa nyumba ya Mulungu; ndipo pamodzi nawe mu ntchito iliyonse pali onse ofuna eni ake aluso, achite za utumiki uliwonse; akulu omwe ndi anthu onse adzachita monga umo udzanenamo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/28-d7e996a3b65eafb17761aa474ffb4e9e.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 29

Zopereka zaufulu zomangira Kachisi

1 Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu.

2 Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndisilivawa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka.

3 Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;

4 ndicho matalente zikwi zitatu za golide, golide wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi;

5 golide wa zija zagolide, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za ntchito zilizonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero lino?

6 Pamenepo akulu a nyumba za makolo, ndi akulu a mafuko a Israele, ndi akulu a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang’anira ntchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,

7 napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi.

8 Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wake anaipereka ku chuma cha nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehiyele Mgeresoni.

9 Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.

Pemphero la Davide, ndi kumwalira kwake

10 Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.

11 Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.

12 Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m’dzanja lanu.

13 Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.

14 Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.

15 Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.

16 Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu.

17 Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.

18 Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isaki, ndi wa Israele makolo athu, musungitse ichi kosatha m’chilingaliro cha maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,

19 nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.

20 Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.

21 Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m’mawa mwake mwa tsiku lija, ndizo ng’ombe chikwi chimodzi, nkhosa zamphongo chikwi chimodzi, ndi anaankhosa chikwi chimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zochuluka za Aisraele onse:

22 nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi chimwemwe chachikulu. Ndipo analonga ufumu Solomoni mwana wa Davide kachiwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.

23 Momwemo Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Yehova, ndiye mfumu m’malo mwa Davide atate wake, nalemerera, namvera iye Aisraele onse.

24 Ndi akulu onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana aamuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomoni mfumu.

25 Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.

26 Momwemo Davide mwana wa Yese adakhala mfumu ya Aisraele onse.

27 Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israele ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu mu Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu muYerusalemu.

28 Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

29 Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m’buku la mau a Samuele mlauli, ndi m’buku la mau a Natanimneneri, ndi m’buku la mau a Gadi mlauli;

30 pamodzi ndi za ufumu wake wonse, ndi mphamvu yake, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israele, ndi maufumu onse a maiko.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/29-0afaba6d5a6f85450055728b593ab291.mp3?version_id=1068—