1 Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, naliika pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu.
2 Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m’dzina la Yehova.
3 Nagwira aliyense wa Israele, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa zouma.
4 Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele.
5 Asafu ndiye mkulu wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeiyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Matitiya, ndi Eliyabu, ndi Benaya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;
6 ndi Benaya ndi Yahaziele ansembe ndi malipenga kosalekeza, kulikasa la chipanganola Mulungu.
Salimo la Davide
7 Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ochita ndiwo Asafu ndi abale ake.
8 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye.
9 Muimbireni, muimbireni zomlemekeza;
fotokozerani zodabwitsa zake zonse.
10 Mudzitamandire ndi dzina lake lopatulika;
mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.
11 Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake;
funani nkhope yake nthawi zonse.
12 Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita,
zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.
13 Inu mbeu ya Israele mtumiki wake,
inu ana a Yakobo, osankhika ake.
14 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
maweruzo ake akhala padziko lonse lapansi.
15 Kumbukirani chipangano chake kosatha,
mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;
16 chipanganocho anapangana ndi Abrahamu,
ndi lumbiro lake ndi Isaki;
17 ndipo anachitsimikizira kwa Yakobo chikhale malemba,
chikhale chipangano chosatha kwa Israele;
18 ndi kunena kuti,
Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,
gawo la cholowa chako.
19 Pokhala inu anthu owerengeka,
inde anthu pang’ono, ndi alendo m’mwemo;
20 nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina,
kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena.
21 Sanalole munthu awasautse;
ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa;
22 ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga,
musamachitira choipa aneneri anga.
23 Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi,
lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
24 Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu,
zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.
25 Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;
ayenera amuope koposa milungu yonse.
26 Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano;
koma Yehova analenga zakumwamba.
27 Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu,
m’malo mwake muli mphamvu ndi chimwemwe.
28 Mchitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu,
mchitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu.
29 Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake;
bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake;
lambirani Yehova m’chiyero chokometsetsa.
30 Njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi,
dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.
31 Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere;
anene mwa amitundu, Yehova achita ufumu.
32 Nyanja ikukume m’kudzala kwake,
munda ukondwerere, ndi zonse zili m’mwemo.
33 Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango
idzafuula mokondwera pamaso pa Yehova;
pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi.
34 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;
pakuti chifundo chake nchosatha.
35 Nimunene, Tipulumutseni,
Mulungu wa chipulumutso chathu;
mutisokolotse ndi kutilanditsa kwaamitundu,
kuti tiyamike dzina lanu loyera,
ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.
36 Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele,
kuyambira kosayamba kufikira kosatha.
Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.
37 Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;
38 ndi Obededomu, ndi abale ake makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obededomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira;
39 ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku chihema cha Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;
40 kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova paguwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m’mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m’chilamulo cha Yehova adachilamulira Israele;
41 ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;
42 ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kuchipata.
43 Ndipo anachoka anthu onse, yense kunyumba yake, nabwera Davide kudalitsa nyumba yake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/16-a516b991ed143e460b336de6737dc9fa.mp3?version_id=1068—