Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 20

Nkhondo pakati pa Ahabu ndi Benihadadi

1 Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.

2 Natumiza mithenga kumzinda kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati kwa iye,

3 Atero Benihadadi,Silivawako ndi golide wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.

4 Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndili nazo.

5 Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golide wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;

6 koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m’nyumba mwako, ndi m’nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa.

7 Pamenepo mfumu ya Israele anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti munthu uyu akhumba choipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golide wanga; ndipo sindinamkaniza.

8 Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musavomereze.

9 Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba mundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzachita, koma ichi sindingachichite. Nichoka mithengayo, nimbwezera mau.

10 Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.

11 Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo.

12 Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m’misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamzindapo.

13 Ndipo taonani,mnenerianadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m’dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.

14 Nati Ahabu, Mwa yani? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.

15 Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israele onse zikwi zisanu ndi ziwiri.

16 Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m’misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.

17 Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kutuluka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, Mu Samariya mwatuluka anthu.

18 Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m’nkhondo, agwireni, amoyo.

19 Tsono anatuluka m’mzinda anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata.

20 Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.

21 Tsono mfumu ya Israele inatuluka, nikantha apakavalo ndi apamagaleta, nawapha Aaramuwo maphedwe aakulu.

22 Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.

23 Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m’mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu.

24 Tsono chitani ichi, chotsani mafumu aja yense ku malo ake, muike m’malo mwao akazembe.

25 Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magaleta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pachidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.

26 Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele.

27 Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.

28 Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m’dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

29 Ndipo awa anakhala m’misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israele anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.

30 Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m’mzinda, m’chipinda cha m’katimo.

31 Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m’chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.

32 Motero anavala chiguduli m’chuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israele, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.

33 Tsono anthuwo anamyang’anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m’galeta mwake.

34 Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza mizinda ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda mu Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera mu Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.

35 Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha.

36 Ndipo ananena naye, Popeza sunamvere mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha. Ndipo m’mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.

37 Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha.

38 Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pake.

39 Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m’malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva,

40 Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.

41 Ndipo iye anafulumira kuchotsa mpango kumaso kwake, ndi mfumu ya Israele inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.

42 Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m’dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m’malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m’malo mwa anthu ake.

43 Pamenepo mfumu ya Israele inanka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samariya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/20-37c338fe2b6fe8a8db8bc73014964727.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 21

Yezebele aphetsa Naboti

1 Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezireele anali ndi munda wampesa, unali mu Yezireelemo, m’mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samariya.

2 Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m’malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.

3 Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang’ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.

4 Ndipo Ahabu analowa m’nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M’mwemo anagona pa kama wake, nayang’ana kumbali, nakana kudya mkate.

5 Koma Yezebele mkazi wake anadza kwa iye, nati kwa iye, Muchitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?

6 Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezireele, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m’malo mwake; koma anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wampesa.

7 Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine.

8 M’mwemo analemba makalata m’dzina la Ahabu nakhomerapo chizindikiro chake, natumiza makalatawo kwa akulu ndi omveka anali m’mzinda mwake, nakhala naye, Naboti.

9 Ndipo analemba m’makalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;

10 ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.

11 Ndipo anthu aja a mzinda wake, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m’mzinda mwake, anachita monga Yezebele anawatumizira, monga munalembedwa m’makalata amene iye anawatumizira.

12 Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.

13 Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m’mzinda, namponya miyala, namupha.

14 Pomwepo anatuma mau kwa Yezebele, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa.

15 Ndipo kunali, atamva Yezebele kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebele anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wampesa wa Naboti Myezireele uja anakana kukugulitsani ndi ndalama, popeza Naboti sali ndi moyo, koma wafa.

16 Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti Myezireele wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wampesa wa Naboti, kuulandira.

Eliya auza Ahabu za kuonongeka kwa mbumba yake

17 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

18 Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israele, akhala mu Samariya; taona, ali ku munda wampesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.

19 Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.

20 Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.

21 Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele;

22 ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.

23 Ndipo za Yezebele yemwe Yehova ananena, nati, Agalu adzadya Yezebele ku linga la Yezireele.

24 Mwana aliyense wa Ahabu amene adzafera m’mzinda, agalu adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m’mlengalenga zidzamudya.

25 Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.

26 Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele.

27 Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang’amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang’anyang’a.

28 Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

29 Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m’masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/21-c02d66f8ac8156ac43718c71950356dc.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 22

Ahabu apangana ndi Yehosafati

1 Ndipo Aaramu ndi Aisraele anakhala chete zaka zitatu, osathirana nkhondo.

2 Koma kunachitika chaka chachitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israele.

3 Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m’dzanja la mfumu ya Aramu.

4 Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M’mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako.

5 Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israele, Funsira ku mau a Yehova lero.

6 Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m’dzanja la mfumu.

7 Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibemneneriwina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?

8 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.

9 Tsono mfumu ya Israele anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Imila.

10 Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.

11 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.

12 Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, ndipo mudzachita mwai; popeza Yehova adzaupereka m’dzanja la mfumu.

Mikaya anenera motsutsa Ahabu

13 Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m’kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.

14 Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.

15 Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m’dzanja la mfumu.

16 Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokhazokha m’dzina la Yehova?

17 Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake.

18 Pamenepo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuze kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa?

19 Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m’mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.

20 Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.

21 Pamenepo mzimu wina unatuluka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani?

22 Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m’kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.

23 Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m’kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena choipa cha inu.

24 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe?

25 Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m’chipinda cha pakati kubisala.

26 Pamenepo inati mfumu ya Israele, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu;

27 ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m’kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.

28 Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.

Ahabu aphedwa mu nkhondo ya pa Aramu

29 Tsono mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Giliyadi.

30 Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.

31 Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu aang’ono kapena aakulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha.

32 Ndipo kunali, akapitao a magaleta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israele imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anafuula.

33 Ndipo pamene akapitao a magaleta anaona kuti sindiye mfumu ya Israele, anabwerera osampirikitsa.

34 Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.

35 Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m’galeta mwake kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unatuluka m’bala pa phaka la galeta.

36 Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumzinda kwao, ndi yense ku dziko la kwao.

37 Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samariya, naika mfumu mu Samariya.

38 Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.

39 Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi mizinda yonse adaimanga, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

40 Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ake; ndi Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Yehosafati mfumu ya Yuda

41 Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda chaka chachinai cha Ahabu mfumu ya Israele.

42 Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu muYerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili.

43 Ndipo anayenda m’njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.

44 Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele.

45 Tsono machitidwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

46 Ndipo anachotsa m’dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wake Asa.

47 Ndipo mu Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.

48 Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuke, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere.

49 Pamenepo Ahaziya mwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m’zombo. Koma Yehosafati anakana.

50 Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ake, naikidwa ndi makolo ake m’mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Ahaziya mfumu Israele

51 Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m’chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.

52 Nachita choipa pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya atate wake, ndi ya amake, ndi ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene adachimwitsa Israele.

53 NatumikiraBaala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele, monga umo anachitira atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/22-9f1097c9a2d8df5e1ab4d1ed3bbfede1.mp3?version_id=1068—