Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 10

Mfumu yaikazi ya ku Sheba adzacheza kwa Solomoni ku Yerusalemu

1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.

2 Nafika kuYerusalemundi ulendo wake waukulu, ndingamirazakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m’mtima mwake.

3 Ndipo Solomoni anamyankha miyambi yake yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamfotozere iye.

4 Ndipo pamene mfumu yaikazi ya ku Sheba adaona nzeru zonse za Solomoni, ndi nyumba adaimangayo,

5 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m’nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.

6 Ndipo anati kwa mfumu, Idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya machitidwe anu ndi nzeru zanu.

7 Koma sindinakhulupirire mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.

8 Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.

9 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo.

10 Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikenso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni.

11 Ndipo zombo za Hiramu zotengera golide ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali.

12 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafike kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa.

13 Ndipo mfumu Solomoni ananinkha mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse anachipempha iye, osawerenga chimene Solomoni anamninkha mwa ufulu wake. Momwemo iye anabwerera namukanso ku dziko lake, iyeyo ndi anyamata ake.

Chuma ndi ukulu wa Solomoni

14 Tsono kulemera kwake kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi kunali matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide.

15 Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera.

16 Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri zagolide wonsansantha, chikopa chimodzi chinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi.

17 Ndi malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, lihawo limodzi linapangidwa ndi miyeso ya mina itatu ya golide; ndipo mfumu inazisungira zonse m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

18 Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wachifumu waminyanga, naukuta ndi golide woyengetsa.

19 Mpandowo wachifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wachifumu panali pozunguniza kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m’mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m’mbali mwa manjawo.

20 Ndipo anaimika mikango khumi ndi iwiri mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m’dziko lililonse lina simunapangidwe wotere.

21 Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni.

22 Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisisi zinafika kamodzi zitapita zaka zitatu, zili nazo golide, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.

23 Ndipo mfumu Solomoni anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru.

24 Ndipo anthu onse a padziko anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m’mtima mwake.

25 Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wake, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zovala, ndimure, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.

26 Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m’mizinda yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu mu Yerusalemu.

27 Ndipo mfumu inachulukitsa siliva ngati miyala mu Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m’madambo.

28 Ndipo akavalo a Solomoni anachokera ku Ejipito; anthu a malonda a mfumu anawagula magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake.

29 Ndipo galeta limodzi linachokera kutuluka mu Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/10-2ec8f930cef00f896daa78370bdfb2b3.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 11

Solomoni adzipereka kupembedza mafano, Mulungu aipidwa naye

1 Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi waFarao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;

2 a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda.

3 Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana aakazi a mafumu, ndi akazi aang’ono mazana atatu; ndipo akazi ake anapambutsa mtima wake.

4 Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhale wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.

5 Tsono Solomoni anatsata Asitaroti fano la anthu a Sidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni.

6 Ndipo Solomoni anachita choipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wake.

7 Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndiMolekifano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo paYerusalemu.

8 Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe milungu yao.

9 Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri,

10 namlamulira za chinthu chomwechi, kuti asatsate milungu ina, koma iye sanasunge chimene Yehova anachilamula.

11 Chifukwa chake Yehova ananena ndi Solomoni, Popeza chinthu ichi chachitika ndi iwe, ndipo sunasungechipanganochanga ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung’ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako.

12 Koma m’masiku ako sindidzatero chifukwa cha Davide atate wako, koma ndidzaung’ambira m’manja mwa mwana wako;

13 komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.

Mulungu amuutsira Solomoni adani

14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, ndiye Hadadi Mwedomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu.

15 Pakuti pamene Davide adali mu Edomu, ndipo Yowabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse mu Edomu;

16 pakuti Yowabu ndi Aisraele onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse mu Edomu;

17 Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wake pamodzi naye, kunka ku Ejipito, Hadadiyo akali mwana.

18 Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.

19 Ndipo Farao anamkomera mtima ndithu Hadadiyo, nampatsa mkazi ndiye mbale wa mkazi wake, mbale wake wa Tapenesi mkazi wamkulu wa mfumu.

20 Ndipo mbale wa Tapenesi anamuonera Genubati mwana wake, ameneyo Tapenesi anamletsera kuyamwa m’nyumba ya Farao, ndipo Genubati anakhala m’banja la Farao pamodzi ndi ana aamuna a Farao.

21 Ndipo atamva Hadadi ku Ejipito kuti Davide anagona ndi makolo ake, ndi kuti Yowabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.

22 Tsono Farao anati kwa iye, Koma chikusowa iwe nchiyani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.

23 Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba.

24 Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, nakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.

25 Ndipo iye anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, kuonjezerapo choipa anachichita Hadadi, naipidwa nao Aisraele, nakhala mfumu ya ku Aramu.

Mneneri Ahiya agawira Yerobowamu ufumuwo

26 Ndipo Yerobowamu mwana wa Nebati Mwefuremu wa ku Zereda mnyamata wa Solomoni, dzina la amake ndiye Zeruya, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lake pa mfumu.

27 Ndipo chifukwa chakukweza iye dzanja lake pa mfumu ndi chimenechi: Solomoni anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mzinda wa Davide atate wake.

28 Ndipo munthu ameneyo Yerobowamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomoni anamuona mnyamatayo kuti ngwachangu, anamuika akhale woyang’anira wa ntchito yonse ya nyumba ya Yosefe.

29 Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobowamu anatuluka mu Yerusalemu, ndipomneneriAhiya wa ku Silo anampeza m’njira; tsono iyeyo anavaliratu chovala chatsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo,

30 Ndipo Ahiyayo anagwira chovala chake chatsopano, naching’amba khumi ndi pawiri.

31 Nati kwa Yerobowamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Taona ndidzaung’amba ufumu m’dzanja la Solomoni ndi kukupatsa iwe mafuko khumi.

32 Koma iye adzakhala nalo fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi cha Yerusalemu, mzinda umene ndinausankha m’mafuko onse a Israele.

33 Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m’njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.

34 Koma sindidzalanda ufumu wonse m’dzanja lake, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ake onse, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, chifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.

35 Koma ndidzalanda ufumu m’dzanja la mwana wake, ndi kupatsa iwe mafuko khumi amene.

36 Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.

37 Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzachita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israele.

38 Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m’njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.

39 Ndipo chifukwa cha ichi ndidzazunza mbumba ya Davide, koma si masiku onse ai.

40 Chifukwa chake Solomoni anafuna kupha Yerobowamu, ndipo Yerobowamu anathawira ku Ejipito kwa Sisake mfumu ya Aejipito, nakhala mu Ejipito kufikira imfa ya Solomoni.

Imfa ya Solomoni

41 Ndipo machitidwe otsiriza a Solomoni, ndi ntchito zake zonse anazichita, ndi nzeru zake, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a Solomoni?

42 Ndipo masiku amene Solomoni anakhala mfumu ya Aisraele onse mu Yerusalemu anali zaka makumi anai.

43 Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m’mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/11-dd5ba1b79cc9176ebcf45d0c871ce2eb.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 12

Rehobowamu samvera uphungu wa akulu

1 Ndipo Rehobowamu ananka ku Sekemu, popeza Aisraele onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu.

2 Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali mu Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito.

3 Ndipo anatuma kukamuitana. Ndipo Yerobowamu ndi msonkhano wonse wa Israele anadza, nalankhulana ndi Rehobowamu, nati,

4 Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.

5 Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka.

6 Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?

7 Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala chikhalire atumiki anu.

8 Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa achinyamata anzake oimirira pamaso pake,

9 nati kwa iwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenza ife?

10 Ndipo achinyamata anzake ananena naye, nati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m’chuuno mwa atate wanga.

11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

12 Ndipo Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu.

13 Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo,

14 nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

15 Potero mfumu siinamvere anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.

16 Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m’mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang’aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.

17 Koma ana aja a Israele akukhala m’mizinda ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao.

18 Pamenepo mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehobowamu anafulumira kulowa m’galeta wake kuthawira kuYerusalemu.

19 Motero Aisraele anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.

20 Ndipo kunali, atamva Aisraele onse kuti Yerobowamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisraele onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma fuko lokha la Yuda.

21 Ndipo Rehobowamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi fuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israele, kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni.

22 Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semayamneneriwa Mulungu, nati,

23 Lankhula kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,

24 Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.

Kupembedza mafano kwa Yerobowamu

25 Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m’mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele.

26 Ndipo Yerobowamu ananena m’mtima mwake, Ufumuwu udzabwereranso kunyumba ya Davide.

27 Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m’nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.

28 Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang’ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m’dziko la Ejipito.

29 Ndipo anaimika mmodzi ku Betele, naimika wina ku Dani.

30 Koma chinthu ichi chinasanduka tchimo, ndipo anthu ananka ku mmodziyo wa ku Dani.

31 Iye namanga nyumba za m’misanje, nalonga anthu achabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai.

32 Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang’ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.

33 Ndipo anapereka nsembe paguwa la nsembe analimanga mu Betele, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chitatu, m’mwezi umene anaulingirira m’mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israele madyerero, napereka nsembe paguwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/12-c0e79f61082c4b47edb3093168dfd90e.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 13

Mneneri adzudzula Yerobowamu

1 Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m’mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.

2 Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.

3 Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang’ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.

4 Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.

5 Ndiponso guwalo linang’ambika, ndi phulusa la paguwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova.

6 Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.

7 Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.

8 Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.

9 Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

10 Tsono iye anayenda njira ina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Betele.

Mneneri wosamverayo aphedwa ndi mkango

11 Ndipo ku Betele kunakhalamneneriwokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo mu Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.

12 Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? Popeza ana ake adaona njira analowera munthu wa Mulungu anachokera ku Yudayo.

13 Nanena ndi ana ake, Ndimangireni mbereko pabulu. Namangira iwo mbereko pabulu, naberekekapo iye.

14 Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anachokera ku Yuda? Nati, Ndine amene.

15 Tsono ananena naye, Tiye kwathu, ukadye mkate.

16 Nati iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano;

17 pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

18 Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.

19 Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi.

20 Ndipo kunachitika iwo ali chikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo,

21 nafuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anachokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova Pokhala sunamvere mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,

22 koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.

23 Ndipo kunachitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pabulu mneneri amene anambwezayo.

24 Ndipo atachoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha ndipo mtembo wake unagwera m’njiramo, bulu naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.

25 Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m’njiramo, ndi mkango uli chiimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m’mzinda m’mene munakhala mneneri wokalamba uja.

26 Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvere mau a Yehova; chifukwa chake Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.

27 Iye nanena ndi ana ake, nati, Ndimangireni mbereko pabulu. Namangira mbereko.

28 Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m’njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.

29 Ndipo mneneri ananyamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pabulu, nabwera nao, nalowa m’mzinda mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika.

30 Ndipo mtembo wake anauika m’manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!

31 Ndipo kunachitika, atamuika iye, ananena ndi ana ake, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m’manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ake.

32 Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m’mizinda ya ku Samariya, adzachitika ndithu.

33 Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere panjira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje.

34 Ndimo umu munali tchimo la nyumba ya Yerobowamu, limene linaidula ndi kuiononga padziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/13-c686484e846f8b4e0efabb57a67ede4a.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 14

Ahiya aneneratu kugwa kwa Yerobowamu

1 Nthawi yomweyo Abiya mwana wa Yerobowamu anadwala.

2 Ndipo Yerobowamu ananena ndi mkazi wake, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiyamneneriuja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.

3 Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi chigulu cha uchi, numuke kwa iye; adzakuuza m’mene umo akhalire mwanayo.

4 Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka nanka ku Silo, nalowa m’nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanathe kupenya, popeza maso ake anali tong’o, chifukwa cha ukalamba wake.

5 Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobowamu akudza kukufunsa za mwana wake, popeza adwala; udzanena naye mwakutimwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.

6 Ndipo kunachitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ake alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobowamu, wadzizimbaitsiranji? Pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.

7 Kauze Yerobowamu, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa pakati pa anthu ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisraele,

8 ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanane ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga;

9 koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;

10 chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka mu Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse.

11 Agalu adzadya aliyense wa Yerobowamu wakufa m’mzinda; ndi mbalame za m’mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.

12 Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m’mzinda mwanayo adzatsirizika.

13 Ndipo Aisraele onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobowamu adzalowa m’manda; pakuti mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israele m’nyumba ya Yerobowamu.

14 Ndiponso Yehova adzadziukitsira mfumu ya Israele, idzaononga nyumba ya Yerobowamu tsiku lomwelo; nchiyani ngakhale tsopano apa?

15 Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m’dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.

16 Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele.

17 Ndipo mkazi wa Yerobowamu ananyamuka nachoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yake anatsirizika mwanayo.

18 Ndipo anamuika, namlira Aisraele, monga mwa mau a Yehova anawalankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya mneneri.

19 Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m’mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m’buku la machitidwe a mafumu a Israele.

20 Ndipo masiku akukhala Yerobowamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye ndi makolo ake, nalowa ufumu m’malo mwake Nadabu mwana wake.

Yuda aipsidwa mwa Rehobowamu

21 Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri muYerusalemu, m’mzinda m’mene Yehova adausankha m’mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni.

22 Ndipo Ayuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, namchititsa nsanje ndi zoipa zao anazichitazo, zakuposa zija adazichita makolo ao.

23 Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse;

24 panalinso anyamata ochitirana dama m’dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa zaamitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele.

25 Ndipo kunachitika, Rehobowamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisake mfumu ya Aejipito anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu,

26 nachotsa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni.

27 Ndipo mfumu Rehobowamu anapanga m’malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m’manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

28 Ndipo kunachitika, pakulowa mfumu m’nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku chipinda cha olindirirawo.

29 Tsono, machitidwe ake ena a Rehobowamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

30 Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku ao onse.

31 Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m’mzinda wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m’malo mwake Abiya mwana wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/14-7d83cd5b429292db28f1edb377b63c3a.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 15

Abiya atsata zoipa za atate wake Rehobowamu

1 Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda.

2 Anakhala mfumu zaka zitatu muYerusalemu, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu.

3 Nayenda iye m’zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.

4 Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali mu Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;

5 chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.

6 Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wake.

7 Ndipo machitidwe ake ena a Abiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.

8 Nagona Abiya ndi makolo ake, namuika anthu m’mzinda wa Davide; Asa mwana wake nalowa ufumu m’malo mwake.

Maweruzidwe okoma a Asa

9 Ndipo chaka cha makumi awiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda.

10 Nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi anai mphambu chimodzi, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu.

11 Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake.

12 Nachotsa m’dziko anyamata aja adama, nachotsanso mafano onse anawapanga atate ake.

13 Ndipo anamchotsera Maaka amake ulemu wa make wa mfumu, popeza iye anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fano lake, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.

14 Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.

15 Ndipo analonga m’nyumba ya Yehova zinthu zija atate wake adazipereka; napereka zinthu zina iye mwini zasilivandi zagolide ndi zotengera.

Nkhondo ya pakati pa Asa ndi Baasa

16 Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.

17 Ndipo Baasa mfumu ya Israele anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

18 Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m’nyumba ya Yehova chuma chili m’nyumba ya mfumu, nazipereka m’manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,

19 Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.

20 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumizinda ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali.

21 Tsono Baasa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza.

22 Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Baasa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.

23 Ndipo machitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yake yonse, ndi zonse anazichita, ndi mizinda anaimanga, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wake anadwala mapazi ake.

24 Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m’mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m’malo mwake.

Baasa akantha mbumba ya Yerobowamu nakhala mfumu ya Israele

25 Ndipo Nadabu mwana wa Yerobowamu analowa ufumu wa Israele chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.

26 Nachita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya atate wake, ndi m’tchimo lomwelo iye akachimwitsa nalo Aisraele.

27 Ndipo Baasa mwana wa Ahiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira chiwembu; ndipo Baasa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisraele onse adamangira misasa Gibetoni.

28 Inde Baasa anamupha chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m’malo mwake.

29 Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo;

30 chifukwa cha machimo a Yerobowamu, amene adachimwa nao, nachimwitsa nao Aisraele, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.

31 Ndipo machitidwe ena a Nadabu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

32 Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.

33 Tsono Baasa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israele chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makumi awiri mphambu zinai.

34 Ndipo anachimwa pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya Yerobowamu, ndi m’tchimo lake iye anachimwitsa nalo Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/15-ceed90c0e8bb1f7e94e0a846c62ad7c8.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 16

Yehu aneneratu kugwa kwa Baasa

1 Ndipo mau a Yehova akutsutsa Baasa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati,

2 Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m’njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao;

3 taona, ndidzachotsa psiti Baasa ndi nyumba yake, ndipo ndidzafanizitsa nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati.

4 Agalu adzadya aliyense wa Baasa amene adzafera m’mzinda, ndipo amene adzafera m’thengo zidzamudya mbalame za m’mlengalenga.

5 Tsono machitidwe ena a Baasa, ndi ntchito zake, ndi mphamvu zake, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

6 Nagona Baasa ndi makolo ake, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wake analowa ufumu m’malo mwake.

7 Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja lamneneriYehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha.

Ela, Zimri, ndi Omuri, mafumu a Israele

8 Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa analowa ufumu wa Israele ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.

9 Ndipo mnyamata wake Zimiri, ndiye woyang’anira dera lina la magaleta ake, anampangira chiwembu; koma iye anali mu Tiriza kumwa ndi kuledzera m’nyumba ya Ariza, ndiye woyang’anira nyumba mu Tiriza.

10 Nalowamo Zimiri, namkantha, namupha chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri za Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m’malo mwake.

11 Ndipo kunali, atalowa ufumu wake, nakhala pa mpando wachifumu wake, anawakantha onse a m’nyumba ya Baasa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ake, kapena wa mabwenzi ake.

12 Motero Zimiri anaononga nyumba yonse ya Baasa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Baasa, mwa dzanja la Yehu mneneri,

13 chifukwa cha machimo onse a Baasa, ndi machimo a Ela mwana wake anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao.

14 Tsono machitidwe ena a Ela, ndi ntchito zake zonse, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

15 Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.

16 Koma anthu aja omangira misasa anamva kuti Zimiri wachita chiwembu, nakanthanso mfumu; chifukwa chake tsiku lomwelo Aisraele onse a kumisasa anamlonga Omuri kazembe wa nkhondo akhale mfumu ya Israele.

17 Ndipo Omuri anachoka ku Gibetoni, ndi Aisraele onse naye, nakamangira misasa Tiriza.

18 Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m’mzinda, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa;

19 chifukwa cha machimo ake anachimwawo, pakuchita choipa pamaso pa Yehova; popeza anayenda m’njira ya Yerobowamu, ndi m’tchimo lake anachimwa nalolo, nachimwitsa nalo Aisraele.

20 Machitidwe ena tsono a Zimiri, ndi chiwembu anachichitacho, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

21 Pamenepo anthu a Israele anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omuri.

22 Koma anthu akutsata Omuri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omuri nakhala mfumu.

23 Chaka cha makumi atatu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anayamba kukhala mfumu ya Israele, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi chimodzi.

24 Ndipo anagula kwa Semeri chitunda cha Samariya ndi matalente awiri asiliva, namanga pachitundapo, natcha dzina lake la mzinda anaumanga Samariya, monga mwa dzina la Semeri mwini chitundacho.

25 Koma Omuri anachimwa pamaso pa Yehova, nachita zoipa koposa onse adamtsogolerawo.

26 Nayenda m’njira yonse ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao.

27 Ndipo machitidwe ena a Omuri anawachita, ndi mphamvu yake anaionetsa, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

28 Nagona Omuri ndi makolo ake, naikidwa mu Samariya; ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu m’malo mwake.

Ahabu mfumu yoipa ya Israele

29 Ndipo chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omuri analowa ufumu wa Israele, nakhala Ahabu mwana wa Omuri mfumu ya Israele mu Samariya zaka makumi awiri mphambu ziwiri.

30 Ndipo Ahabu mwana wa Omuri anachimwa pamaso pa Yehova koposa onse adamtsogolerawo.

31 Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m’machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikiraBaala, namgwadira.

32 Nammangira Baala guwa la nsembe m’nyumba ya Baala anaimanga mu Samariya.

33 Ahabu anapanganso chifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israele adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.

34 M’masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/16-afc4a0776823fd263ed6a299d9dc59fc.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 17

Mneneri Eliya ku Keriti

1 Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.

2 Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,

3 Choka kuno, nutembenukire kum’mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordani.

4 Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makwangwala kukudyetsa kumeneko.

5 Momwemo iye anamuka, nachita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordani.

6 Ndipo makwangwala anamtengera mkate ndi nyama m’mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.

7 Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m’dziko.

Eliya aukitsa mwana wa wamasiye ku Zarefati

8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,

9 Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Sidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.

10 Tsono iye ananyamuka nanka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mzinda; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang’ono m’chikho, ndimwe.

11 Ndipo m’mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m’dzanja lako.

12 Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m’mbiya, ndi mafuta pang’ono m’nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.

13 Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma yamba wandiotcherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.

14 Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova padziko lapansi.

15 Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m’nyumba ake, masiku ambiri.

16 Mbiya ya ufa siidathe, ndi nsupa ya mafuta siinachepe, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.

17 Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yake, analeka kupuma.

18 Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?

19 Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m’mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini.

20 Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake?

21 Nafungatira katatu pa mwanayo, nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m’chifuwa mwake.

22 Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.

23 Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m’nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.

24 Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m’kamwa mwanuwo ngoona.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/17-feb934d66651e8d5cf6e90d0755b48b2.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 18

Eliya ndi Abaala ku Karimele

1 Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya chaka chachitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.

2 Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu mu Samariya.

3 Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang’anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;

4 pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m’phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.

5 Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.

6 Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yake yekha, ndi Obadiya njira ina yekha.

7 Ndipo Obadiya ali m’njira taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?

8 Ndipo anamyankha, nati, Ndine amene; kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera.

9 Iye nati, Ndachimwanji kuti mupereka kapolo wanu m’dzanja la Ahabu kundipha?

10 Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.

11 Ndipo tsopano mukuti, Kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera.

12 Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.

13 Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m’kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m’phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?

14 Ndipo tsopano inu mukuti, Kauze mbuye wako Eliya wabwera, ndipo adzandipha.

15 Koma Eliya anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndikhala pamaso pake, zedi, ndionekadi pamaso pake lero.

16 Ndipo Obadiya anauka kukomana ndi Ahabu, namuuza, ndipo Ahabu ananka kukomana ndi Eliya.

17 Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo?

18 Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.

19 Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.

20 Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israele, namemeza aneneri onse kuphiri la Karimele.

21 Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.

22 Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekhamneneriwa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu.

23 Atipatse tsono ng’ombe ziwiri; ndipo adzisankhire iwo eni ng’ombe imodzi, naiduledule, naiike pankhuni osasonkhapo moto; ndipo ine ndidzakonza ng’ombe yinayo, ndi kuiika pankhuni osasonkhapo moto.

24 Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anavomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.

25 Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Baala, Dzisankhireni ng’ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza muchuluka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.

26 Ndipo iwo anatenga ng’ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m’mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.

27 Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.

28 Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali chuchuchu.

29 Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.

30 Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.

31 Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.

32 Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m’dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mchera, ukulu wake ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo.

33 Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng’ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.

34 Nati, Bwerezaninso kawiri; nabwerezanso. Nati, Bwerezani katatu; nabwereza katatu.

35 Ndipo madzi anayenda pozinga guwa la nsembe, nadzazanso mcherawo ndi madzi.

36 Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.

37 Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.

38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera.

39 Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.

40 Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.

41 Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo wa mvula yambiri.

42 Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimele, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.

43 Ndipo anati kwa mnyamata wake, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.

44 Ndipo kunali kachisanu ndi chiwiri anati, Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni.

45 Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikulu. Ndipo Ahabu anayenda m’galeta, namuka ku Yezireele.

46 Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m’chuuno mwake, nathamanga m’tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/18-a066bcde6a066783c5c065731f904850.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 19

Eliya athawa Yezebele

1 Ndipo Ahabu anauza Yezebele zonse anazichita Eliya, ndi m’mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo.

2 Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.

3 Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.

4 Koma iye mwini analowa m’chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.

5 Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.

6 Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.

7 Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika.

8 Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.

Eliya kuphiri la Horebu

9 Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?

10 Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiyachipanganochanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.

11 Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang’amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m’mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m’chivomezicho.

12 Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m’motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.

13 Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?

14 Nati iye, Ndachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele ataya chipangano chanu, nagumula maguwa la nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.

15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kuchipululu kunka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaele akhale mfumu ya Aramu;

16 ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhalemnenerim’malo mwako.

17 Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu.

18 Ndiponso ndidasiya mu Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadiraBaalamaondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.

19 Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng’ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.

20 Ndipo iye anasiya ng’ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndiyambe ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?

21 Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng’ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng’ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/19-48172288e3b76673a661e5e4daa0369f.mp3?version_id=1068—