Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU Mau Oyamba

Mau Oyamba

Bukuli lotsatira

2 Samuele

likupitiriza mbiri ya ufumu wa Israele kuyambira pa imfa ya Davide mpaka pa chaka ngati 850 BC.

Mau onena za mafumuwo aonetsa kuti mfumu ikakhala yokhulupirika kwa Mulungu, zake zimayenda bwino ndipo anthu ake amakhala pa mtendere; koma ikakhala yosamvera Mulungu ndi kumapembedza milungu ina, zinthu zimayenda moipa ndipo anthu amagwa m’mavuto ambiri. Mafumu akumpoto, ku Israele, analephera pa udindo wao; koma akum’mwera, ku Yuda, ena mwa iwo anali okanika, komabe ena anali okhulupirika. Pa masiku amenewo, Mulungu amatuma aneneri ake, anthu olimba mtima, kuti akachenjeze anthu ake, alekeretu kupembedza mafano ndipo azimvera Yehova Mulungu wao. Wina mwa iwo, wodziwika bwino anali Eliya amene anatsutsa ansembe otumikira Baala (mutu 18).

Za mkatimu

Davide atafa, mwana wake Solomoni alowa m’malo mwake

1.1—2.46

Ufumu wa Solomoni

3.1—11.43

a. Zaka zoyamba za ufumu wake

3.1—4.34

b. Amanga Kachisi wa Yehova

5.1—8.66

c. Zaka zotsiriza za ufumu wake

9.1—11.43

Ufumu wa Israele ugawika pawiri

12.1—22.53

a. Mafuko akumpoto aukira ufumu wa Rehobowamu

12.1—14.20

b. Mafumu olamulira Yuda ndi mafumu olamulira Israele

14.21—16.34

c. Mneneri Eliya

17.1—19.21

d. Mfumu Ahabu ya Israele

20.1—22.40

Mfumu Yehosafati ya Yuda ndi Mfumu Ahaziya ya Israele

22.41-53

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 1

Ukalamba wa Davide, atchula Solomoni wodzalowa m’malo mwake

1 Ndipo mfumu Davide anakalamba nachuluka masiku ake; ndipo iwo anamfunda ndi zofunda, koma iye sanafundidwe.

2 Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m’mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

3 Tsono anafunafuna m’malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.

4 Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwe.

5 Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.

6 Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.

7 Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.

8 Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natanimneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.

9 Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng’ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu;

10 koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomoni mbale wake, sanawaitane.

11 Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?

12 Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni.

13 Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirire mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?

14 Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.

15 Pamenepo Bateseba analowa kwa mfumu kuchipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.

16 Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?

17 Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.

18 Ndipo tsopano taonani, Adoniya walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.

19 Ndipo iye anapha ng’ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu kazembe wa nkhondo; koma Solomoni mnyamata wanu sanamuitane.

20 Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye.

21 Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa.

22 Ndipo taona, iye ali chilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo.

23 Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.

24 Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu?

25 Popeza iye watsika lero, nakapha ng’ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.

26 Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane.

27 Chinthu ichi chachitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitse mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?

28 Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Bateseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu.

29 Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m’nsautso monse,

30 zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m’malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.

31 Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya.

32 Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu.

33 Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni.

34 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.

35 Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m’malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda.

36 Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.

37 Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu momwemo akhalenso ndi Solomoni, nakuze mpando wake wachifumu upose mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.

38 Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.

39 Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.

40 Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang’ambika ndi phokoso lao.

41 Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yowabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi chiyani kuti m’mzinda muli chibumo?

42 Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.

43 Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomoni ufumu:

44 ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.

45 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo achokera kumeneko chikondwerere, ndi m’mzindamo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali.

46 Ndiponso Solomoni wakhala pa chimpando cha ufumu.

47 Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomoni lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wake wachifumu upose mpando wanu wachifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.

48 Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israele, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wachifumu, maso anga ali chipenyere.

49 Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anachita mantha, nanyamuka, napita yense njira yake.

50 Ndipo Adoniya anaopa chifukwa cha Solomoni, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.

51 Ndipo anthu anakauza Solomoni, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomoni, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomoni alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wake ndi lupanga.

52 Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.

53 Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/1-7c2571e08ed067f26ea7991072da72b6.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 2

Davide atapangira Solomoni amwalira

1 Pakuyandikira masiku ake a Davide akuti amwalire, analamulira Solomoni mwana wake, nati,

2 Ndimuka ine njira ya dziko lonse: limba mtima tsono, nudzionetse umunthu;

3 nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m’njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m’chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m’zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;

4 kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele.

5 Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m’chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.

6 Chita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wake waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

7 Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.

8 Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga.

9 Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda.

10 Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m’mzinda wa Davide.

11 Ndipo masiku ake akukhala Davide mfumu ya Israele anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu zitatu anakhala mfumu kuYerusalemu.

12 Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu.

Kulangidwa kwa Adoniya, Abiyatara, Yowabu ndi Simei

13 Pomwepo Adoniya mwana wa Hagiti anadza kwa Bateseba amai wake wa Solomoni, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.

14 Anatinso, Ndili nanu mau. Nati iye, Tanena.

15 Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisraele onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Yehova.

16 Ndipo tsopano, ndikupemphani pempho limodzi, musandikaniza. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Tanena.

17 Nati iye, Mundinenere kwa mfumu Solomoni, popeza sakukanizani, kuti andipatse Abisagi wa ku Sunamu akhale mkazi wanga.

18 Ndipo Bateseba anati, Chabwino, ndidzakunenera kwa mfumu.

19 Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja.

20 Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani.

21 Ndipo iye anati, Abisagi wa ku Sunamu apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu akhale mkazi wake.

22 Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya.

23 Pomwepo mfumu Solomoni analumbira pa Yehova, nati, Mulungu andilange naonjezepo, zedi Adoniya wadziphetsa yekha ndi mau awa.

24 Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wachifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe.

25 Ndipo mfumu Solomoni anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.

26 Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.

27 Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.

28 Ndipo mbiriyi inamfika Yowabu, pakuti Yowabu anapatukira kwa Adoniya, angakhale sanapatukire kwa Abisalomu. Ndipo Yowabu anathawira ku chihema cha Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.

29 Ndipo anamuuza mfumu Solomoni, kuti, Yowabu wathawira ku chihema cha Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomoni anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwere.

30 Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti.

31 Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa.

32 Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.

33 Motero mwazi wao udzabweranso pamutu wake wa Yowabu, ndi pamutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.

34 Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m’nyumba yakeyake kuchipululu.

35 Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m’malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m’malo mwa Abiyatara.

36 Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, nati kwa iye, Udzimangire nyumba mu Yerusalemu, nukhale komweko osatulukako kunka kwina konse.

37 Popeza tsiku lomwelo lakutuluka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pamutu wa iwe wekha.

38 Ndipo Simei anena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzachita kapolo wanu. Ndipo Simei anakhala mu Yerusalemu masiku ambiri.

39 Ndipo kunachitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simei, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati.

40 Ndipo Simei ananyamuka, namangirira mbereko pabulu wake, nanka ku Gati kwa Akisi kukafuna akapolo ake; namuka Simei, nabwera nao akapolo ake kuchokera ku Gati.

41 Ndipo anamuuza Solomoni, kuti, Simei wachoka ku Yerusalemu kunka ku Gati, nabweranso.

42 Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritse pa Yehova ndi kukuchenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakutuluka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.

43 Sunasunga chifukwa ninji lumbiro la pa Yehova, ndi lamulo lija ndinakulamulira iwe?

44 Tsono mfumu inanenanso ndi Simei, Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini.

45 Koma mfumu Solomoni adzadalitsika, ndi mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova ku nthawi yamuyaya.

46 Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m’dzanja la Solomoni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/2-a312443f757d205e3b33dd96f11b1c9f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 3

Solomoni akwatira mwana wa Farao

1 Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndiFaraomfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozingaYerusalemu.

2 Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo.

3 Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m’malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.

Yehova aonekera Solomoni m’kulota usiku ku Gibiyoni

4 Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi paguwalo la nsembe.

5 Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m’kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.

6 Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino.

7 Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m’malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa.

8 Ndipo kapolo wanu ndili pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka mu unyinji wao.

9 Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?

10 Ndipo mau amenewa anakondweretsa Ambuye kuti Solomoni anapempha chimenechi.

11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha chimenechi, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso chuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera milandu;

12 taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.

13 Ndiponso zimene sunazipemphe adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse.

14 Ndipo ukadzayenda m’njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.

15 Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima kulikasa la chipanganocha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.

Solomoni aweruza mlandu wa akazi awiri aja

16 Pamenepo analowa kwa mfumu akazi awiri, ndiwo adama, naima pamaso pake.

17 Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m’nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m’nyumbamo.

18 Ndipo kunachitika kuti tsiku lachitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m’nyumbamo, koma ife awiri m’nyumbamo.

19 Ndipo mwana wa mnzangayu anamwalira usiku, pokhala iyeyu anamgonera.

20 Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndili m’tulo, namuika m’mfukato mwake, naika mwana wake wakufa m’mfukato mwanga.

21 Ndipo pouka ine m’mawa kuyamwitsa mwana wanga ndaona, ngwakufa, koma nditamzindikira m’mawa ndaona si mwana wanga wobala ine ai.

22 Ndipo mkazi winayo anati, Iai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, Iai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu.

23 Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, Iai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu.

24 Niti mfumu, Kanditengereni chimpeni. Ndipo iwo anabwera ndi chimpeni kwa mfumu.

25 Mfumu niti, Dula pakati mwana wamoyoyu, nupatse mmodzi chipinjiri, ndi wina chipinjiri chake.

26 Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wake analankhula ndi mfumu, popeza mtima wake unalira mwana wake, nati, Ha? Mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.

27 Pamenepo mfumu inayankha, niti, Mumpatse wachifundoyo mwana wamoyo, osamupha konse, uyo ndiye amake.

28 Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/3-09fc7c43517c60a7ac047a6ab396c132.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 4

Nduna za Solomoni, ukulu wa ufumu wake

1 Ndipo mfumu Solomoni anali mfumu ya Israele yense.

2 Ndipo akulu a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe,

3 Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,

4 ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe,

5 ndi Azariya mwana wa Natani anayang’anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,

6 ndi Ahisara anayang’anira banja la mfumu, ndi Adoniramu mwana wa Abida anali wamsonkho.

7 Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang’anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka.

8 Ndipo maina ao ndiwo: Benihuri anatengetsa ku mapiri a Efuremu;

9 Benedekere ku Makazi ndi Saalibimu ndi Betesemesi ndi Elonibetehanani;

10 Benihesedi ku Aruboti ndi Soko ndi dziko lonse la Hefere;

11 Benabinadabu ku mtunda wa Dori, mkazi wake ndiye Tafati mwana wa Solomoni;

12 Baana mwana wa Ahiludi ku Taanaki ndi Megido ndi Beteseani konse, ali pafupi ndi Zaretani kunsi kwa Yezireele, kuyambira ku Beteseani kufikira ku Abele-Mehola, kufikiranso kundunji ku Yokomeamu;

13 Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;

14 Abinadabu mwana wa Ido ku Mahanaimu;

15 Ahimaazi ku Nafutali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomoni;

16 Baana mwana wa Husai ku Asere ndi ku Bealoti;

17 Yehosafati mwana wa Paruwa ku Isakara;

18 Simei mwana wa Ela ku Benjamini;

19 Gebere mwana wa Uri ku dziko la Giliyadi, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi la Ogi mfumu ya Basani; munalibe kapitao wina m’deramo.

20 Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.

21 Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.

22 Ndipo zakudya za Solomoni zofikira tsiku limodzi zinali miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,

23 ng’ombe zonenepa khumi, ndi ng’ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.

24 Pakuti analamulira dziko lonse lili tsidya lino la Yufurate, kuyambira ku Tifisa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya lino la Yufurate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko.

25 Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.

26 Ndipo Solomoni anali nazo zipinda za akavalo a magaleta ake zikwi khumi mphambu ziwiri.

27 Ndipo akapitao aja anatengetsera chakudya Solomoni ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomoni, munthu yense m’mwezi mwake, sanalole kanthu kasoweke.

28 Barelenso ndi udzu wa akavalo ndingamiraanabwera nazo kumalo kwao, munthu yense monga momwe anamuuzira.

Nzeru ya Solomoni

29 Ndipo Mulungu anampatsa Solomoni nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m’mphepete mwa nyanja.

30 Ndipo nzeru ya Solomoni inaposa nzeru za anthu onse akum’mawa, ndi nzeru zonse za ku Ejipito.

31 Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira.

32 Ndipo ananena miyambo zikwi zitatu, ndipo nyimbo zake zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu.

33 Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikirahisopewophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.

34 Ndipo anafikapo anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomoni, ochokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/4-f8a539c7ba3207d646076aa12d2976fb.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 5

Solomoni apangana ndi Hiramu za mirimo yomanga nayo Kachisi

1 Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m’malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.

2 Ndipo Solomoni anatumiza mau kwa Hiramu, nati,

3 Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.

4 Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera.

5 Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m’malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.

6 Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.

7 Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.

8 Ndipo Hiramu anatumiza kwa Solomoni, nati, Ndazimva zija munatumiza kwa inezo, ndidzachita chifuniro chanu chonse, kunena za mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa.

9 Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya.

10 Tsono Hiramu anapatsa Solomoni mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa monga momwe anafuniramo.

11 Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka.

12 Ndipo Yehova anapatsa Solomoni nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, iwo awiri napangana pamodzi.

13 Ndipo mfumu Solomoni anasonkhetsa athangata mwa Aisraele onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu.

14 Ndipo anawatuma ku Lebanoni mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebanoni, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.

15 Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m’mapiri;

16 osawerenga akapitao a Solomoni akuyang’anira ntchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira ntchito.

17 Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema.

18 Ndipo omanga nyumba a Solomoni ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/5-a94387d73da7401437c9a579377876e8.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 6

Za mamangidwe a Kachisi

1 Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m’dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m’mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.

2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m’litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m’mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu.

3 Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m’litali mwake munali mikono makumi awiri monga m’mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.

4 Ndipo m’nyumbamo anamanga mazenera a sefa wokhazikika.

5 Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kachisi, ndi chipinda chamkati; namanga zipinda zozinga.

6 Chipinda chapansicho kupingasa kwake kunali mikono isanu, chapakaticho kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi, chachitatucho kupingasa kwake mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anachepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m’makoma a nyumba.

7 Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m’nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.

8 Khomo lolowera m’zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kufikira ku zipinda za pakati, ndi kutuluka m’zapakatizo kulowa m’zachitatuzo.

9 Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza.

10 Ndipo anamanga zipindazo zogundana ndi nyumba yonseyo, chipinda chilichonse msinkhu wake mikono isanu; ndipo anazilumikizitsa kunyumba ndi mitengo yamkungudza.

11 Ndipo mau a Yehova anafika kwa Solomoni, nati,

12 Kunena za nyumba ino ulikuimanga, ukamayenda iwe m’malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.

13 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele.

14 Tsono Solomoni anamanga nyumbayo naitsiriza.

15 Ndipo anatchinga makoma a nyumba m’katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, natchinga m’katimo ndi matabwa, nayala pansi m’nyumbamo matabwa amlombwa.

16 Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m’kati mwa nyumba m’tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.

17 Ndipo nyumbayo, ndiyo Kachisi wa kutsogolo kwa chipindacho, inali ya mikono makumi anai.

18 Ndipo m’kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gadaa; munali mikungudza yokhayokha simunaoneke mwala ai.

19 Ndipo anakonza m’kati mwa nyumba m’tsogolo mwake, kuikamolikasa la chipanganola Yehova.

20 Ndipo m’kati mwa chipindacho, m’litali mwake munali mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golide wayengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza.

21 Momwemo Solomoni anakuta m’kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide.

22 Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golide mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali chakuno cha chipinda chamkati analikuta ndi golide.

23 Ndipo m’chipinda chamkatimo anasema mitengo yaazitonaakerubiawiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi.

24 Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi.

25 Ndi kerubi winayo msinkhu wake unali mikono khumi; akerubi onse awiri anafanana muyeso wao ndi msinkhu wao.

26 Msinkhu wa kerubi mmodzi unali mikono khumi, ndi wa kerubi wina momwemo.

27 Ndipo anaika akerubiwo m’chipinda cha m’katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.

28 Ndipo anawakuta akerubi ndi golide.

29 Nalemba m’makoma onse akuzinga chipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, m’katimo ndi kumbuyo kwake.

30 Ndipo anakuta ndi golide pansi pake pa nyumba m’katimo ndi kunja.

31 Ndipo pa khomo la chipinda chamkati anapanga zitseko za mtengo wa azitona, chitando cha khomolo chinali limodzi la magawo asanu a khoma lake.

32 Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo wa azitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nawakuta ndi golide; inde anakutanso ndi golide akerubi ndi migwalangwayo.

33 Momwemo anapanganso mphuthu za azitona za pa khomo la Kachisi, chitando chake chinali limodzi la magawo anai a khoma;

34 ndi zitseko ziwiri za mitengo yamlombwa pa khomo lina; panali chitseko chopatukana, ndi pa linzake panali chitseko chopatukana.

35 Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nakuta zolembazo ndi golide wopsapsala.

36 Ndipo bwalo la m’kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.

37 Maziko ake a nyumba ya Yehova anaikidwa m’chaka chachinai m’mwezi wa Zivi.

38 Ndipo m’chaka chakhumi ndi chimodzi m’mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/6-e86176dddbb0248d3de17d427c6ab100.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 7

Mamangidwe a nyumba ya Solomoni

1 Koma nyumba ya iye yekha Solomoni anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yake yonse.

2 Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m’litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.

3 Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu.

4 Ndipo panali mazenera m’mizere itatuyo, zenera limodzi lopenyana ndi linzake mizere itatu.

5 Ndipo makomo onse ndi mphuthu zonse zinali zaphwamphwa maonekedwe ake, ndipo zenera limodzi linapenyana ndi linzake mizere itatu.

6 Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m’litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo.

7 Ndipo anamanga khonde la mpando wachifumu loweruziramo iye, ndilo khonde la milandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja.

8 Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m’bwalo lina la m’tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi waFarao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli.

9 Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, malingana ndi miyeso yake, yocheka ndi mipeni ya manomano m’katimo ndi kunjako, kuyambira kumaziko kufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikulu.

10 Ndipo maziko ake anali a miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yaikulu, miyala ya mikono khumi, ndi miyala ya mikono isanu ndi itatu.

11 Ndi pamwamba pake panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wake, ndi mitengo yamkungudza.

12 Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.

Zokometsera ndi zipangizo za Kachisi

13 Ndipo mfumu Solomoni anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Tiro.

14 Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse.

15 Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wake wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo chingwe cha mikono khumi mphambu iwiri chinayesa thupi la nsanamira imodzi.

16 Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.

17 Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.

18 M’mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo.

19 Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa chipinda cholowera chinali ngati akakombo malembedwe ake, a mikono inai.

20 Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m’mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo.

21 Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa chipinda cholowera cha Kachisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, natcha dzina lake Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, natcha dzina lake Bowazi.

22 Ndipo pamwamba pa nsanamirazo panali ngati akakombo malembedwe ake; motero anaitsiriza ntchito ya nsanamirazo.

23 Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira.

24 Ndipo m’khosi mwake munali ngati zikho zozinganiza m’mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m’mizere iwiri poyengedwa thawalelo.

25 Linasanjikika pa ng’ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum’mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo mbuyo zao zinayang’anana.

26 Ndipo kuchindikira kwake kunali ngati chikhato cha munthu, ndipo mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi ziwiri.

27 Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m’litali mwake mwa phaka limodzi mikono inai, ndi msinkhu wake mikono itatu.

28 Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano.

29 Ndipo pa matsekezerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng’ombe ndiakerubi, ndi pamwamba pa mbano panali chosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng’ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.

30 Ndipo phaka lililonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngodya zake zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.

31 Ndipo pakamwa pake m’katimo pamwamba pa chosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pake panali posadamuka, monga mapangidwe ake a chosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pake panali zolemba ndi matsekerezo ake anali aphwamphwa, si ozunguniza.

32 Ndipo njinga zinai zinali pansi pa matsekerezo, ndi mitanda ya njinga inali m’mphakamo, ndi msinkhu wa njinga imodzi unali mkono umodzi ndi nusu.

33 Ndipo mapangidwe a njinga analingana ndi mapangidwe a njinga za galeta, mitanda yake ndi mkombero wake ndi nthiti zake ndi mtima wake zonsezo zinayengedwa.

34 Ndipo panali ngati mapewa anai pansi pangodya zinali za phaka limodzi, mapewawo anali a phaka lomwelo.

35 Ndipo pamwamba pa phaka panali khoma lozunguniza, msinkhu wake nusu ya mkono; ndi pamwamba pa phaka panali mbano zake ndi matsekerezo a phaka lomwelo.

36 Ndipo m’mapanthi mwa mbano zake ndi pa matsekerezo ake analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ake a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira.

37 Motero anapanga maphaka khumiwo, anafanana mayengedwe ao muyeso wao ndi maonekedwe ao.

38 Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m’mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.

39 Ndipo anaika maphaka asanu ku dzanja lamanja la nyumba, ndi maphaka asanu ku dzanja lamanzere la nyumba; naika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum’mawa kupenya kumwera.

40 Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga ntchito yonse anaichitira mfumu Solomoni ya m’nyumba ya Yehova.

41 Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo,

42 ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,

43 ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi zili pa maphakawo,

44 ndi thawale limodzilo, ndi ng’ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale;

45 ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomoni za m’nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira.

46 Mfumu inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m’dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zaretani.

47 Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseke.

48 Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m’nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera;

49 ndi zoikaponyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide;

50 ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m’katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi.

51 Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizosilivandi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/7-9f24b842eece38c7b3d4a14d1eea6afc.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 8

Aika likasa mu Kachisi

1 Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni muYerusalemu, kukatengalikasa la chipanganocha Yehova m’mzinda wa Davide, ndiwoZiyoni.

2 Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m’mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri.

3 Ndipo akulu onse a Israele anadza, ansembe nanyamula likasa.

4 Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndichihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m’chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

5 Ndipo mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye linali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng’ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.

6 Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko aakerubi.

7 Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zake.

8 Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.

9 Munalibe kanthu m’likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m’dziko la Ejipito.

10 Ndipo kunachitika atatuluka ansembe m’malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova.

11 Ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

Mau a Solomoni popereka Kachisi kwa Mulungu

12 Pamenepo Solomoni anati, Yehova ananena kuti adzakhala m’mdima waukulu.

13 Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.

14 Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yake, nidalitsa msonkhano wonse wa Israele. Ndi msonkhano wonse wa Israele unaimirira.

15 Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m’kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,

16 Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m’dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele.

17 Ndipo Davide atate wanga anafuna m’mtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

18 Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m’mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti m’mtima mwako unatero.

19 Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m’chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.

20 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake analankhulawo, ndipo ndauka ndine m’malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

21 Ndipo ndakonzera malo likasalo, m’mene muli chipangano cha Yehova, chimene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa m’dziko la Ejipito.

22 Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati,

23 Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu wolingana ndi Inu m’thambo la kumwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,

24 wakusungira mtumiki wanu Davide atate wanga chimene mudamlonjezacho; munalankhulanso m’kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.

25 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.

26 Ndipo tsopano, Mulungu wa Israele, atsimikizike mau anu amene munalankhula ndi mtumiki wanu Davide atate wanga.

27 Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

28 Koma mucheukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwake kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;

29 kuti maso anu atsegukire nyumba ino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno.

30 Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.

31 Ngati munthu akachimwira mnzake, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m’nyumba ino;

32 mverani Inu pamenepo m’mwambamo, ndipo chitani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga chilungamo chake.

33 Ndipo anthu anu Aisraele akawakantha adani ao chifukwa cha kuchimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m’nyumba muno;

34 pamenepo mverani Inu mu Mwambamo, ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

35 Pamene kumwamba kwatsekera, ndipo kulibe mvula chifukwa cha kuchimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;

36 pamenepo mverani Inu mu Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula padziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao.

37 M’dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m’dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;

38 tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba ino;

39 pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;

40 kuti aope Inu masiku onse akukhala iwowo m’dziko limene Inu munapatsa makolo ao.

41 Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisraele, koma wakufumira m’dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu,

42 popeza adzamva za dzina lanu lalikulu ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika kunyumba ino;

43 mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisraele, ndi kuti adziwe kuti nyumba ino ndaimangayi yatchedwa dzina lanu.

44 Akatuluka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse Inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika kumzinda uno munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;

45 pamenepo mverani Inu mu Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

46 Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,

47 ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m’dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;

48 ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m’dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, kumzinda munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;

49 pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao mu Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao,

50 ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;

51 pakuti awa ndi anthu anu ndithu, ndi cholowa chanu chimene munatulutsa mu Ejipito, m’kati mwa ng’anjo ya chitsulo;

52 kuti maso anu akatsegukire pembedzero la kapolo wanu ndi pembedzero la anthu anu Aisraele, kuwamvera m’mene monse akafuula kwa Inu.

53 Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a padziko lapansi akhale cholowa chanu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munatulutsa makolo athu mu Ejipito, Yehova Mulungu Inu.

Solomoni adalitsa Aisraele

54 Ndipo kunali kuti atatsiriza Solomoni kupemphera kwa Yehova pemphero ndi pembedzero lino lonse, ananyamuka ku guwa la nsembe la Yehova pomwe analikugwada pa mabondo ake, ndi manja ake otambasulira kumwamba.

55 Naimirira, nadalitsa msonkhano wonse wa Israele ndi mau okweza, nati,

56 Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ake Aisraele, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayike mau amodzi a mau ake onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wake.

57 Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;

58 kuti atitembenuzire kwa Iye yekha mitima yathu iyende m’njira zake zonse, ndi kusunga malamulo ake onse ndi malemba ake ndi maweruzo ake, amene anawalamulira makolo athu.

59 Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wake, ndi mlandu wa anthu ake Aisraele, mlandu wa tsiku pa tsiku lake;

60 kuti anthu onse a padziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina.

61 Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m’malemba ake ndi kusunga malamulo ake, monga lero lino.

62 Ndipo mfumu ndi anthu onse a Israele pamodzi naye anaphera nsembe pamaso pa Yehova.

63 Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng’ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.

64 Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.

65 Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.

66 Tsiku lachisanu ndi chitatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israele anthu ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/8-5b38975e3a3a2c6df02695805ca42d53.mp3?version_id=1068—

Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 9

Mulungu aonekanso kwa Solomoni

1 Ndipo kunali, atatsiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,

2 Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.

3 Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.

4 Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzichita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,

5 pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele.

6 Koma mukadzabwerera pang’ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira;

7 pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m’dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.

8 Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali ino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba ino?

9 Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adatulutsa makolo ao m’dziko la Ejipito, natsata milungu ina, nailambira, naitumikira; chifukwa chake Yehova anawagwetsera choipa chonsechi.

Za midzi adaimanga Solomoni, ndi zombo zake

10 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m’mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

11 popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu mizinda makumi awiri m’dziko la Galileya.

12 Ndipo Hiramu anatuluka ku Tiro kukaona mizinda adampatsa Solomoniyo, koma siinamkomere.

13 Nati, Mizinda ino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naitcha dzina lao, Dziko lachikole, kufikira lero lino.

14 Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri.

15 Ndipo chifukwa chake cha msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomoni ndi chimenechi; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga laYerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido, ndi Gezere.

16 PakutiFaraomfumu ya Aejipito adakwera nalanda Gezere, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m’mzindamo, naupereka kwaulere kwa mwana wake mkazi wa Solomoni.

17 Ndipo Solomoni anamanganso Gezere, ndi Betehoroni wakunsi,

18 ndi Baalati, ndi Tamara wa m’chipululu m’dziko muja,

19 ndi mizinda yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi mizinda yosungamo magaleta ake, ndi mizinda yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga mu Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m’dziko lonse la ufumu wake.

20 Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israele,

21 ana ao amene adatsala m’dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.

22 Koma Solomoni sanawayese ana a Israele akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi akazembe ake, ndi oyang’anira magaleta ake ndi apakavalo ake.

23 Amenewo anali akulu a akapitao oyang’anira ntchito ya Solomoni, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira ntchito aja.

24 Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m’mzinda wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.

25 Ndipo chaka chimodzi Solomoni anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, paguwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira paguwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.

26 Ndipo mfumu Solomoni anamanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere uli pafupi ndi Eloti, m’mphepete mwa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.

27 Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m’zombozo amalinyero ozolowera m’nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni.

28 Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/9-340a5e320f52ecea436b49a753e6b1b3.mp3?version_id=1068—