Categories
1 ATESALONIKA

1 ATESALONIKA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mzinda wa Tesalonika unali likulu la dziko la Masedoniya lokhala mu ulamuliro wa Aroma. Paulo adayambitsa mpingo kumeneko, atachoka ku Filipi. Koma Ayuda ataona kuti Paulo akulalika uthenga wa Chikhristu kwa anthu a mitundu ina okonda zachiyuda namakopa ambiri mwa iwo, adachita naye dumbo, namadana naye ndi kumvutitsa; mwakuti Paulo adachoka kumeneko kupita ku Bereya. Atafika ku Korinto, Timoteo, mnzake womthandiza pa ntchito yolalikira, adadzampeza namusimbira za m’mene mpingo ukuyendera ku Tesalonika.

Paulo anawalembera kalatayi kuti awalimbitse mtima ndi kuyankha mafunso ao, makamaka pa nkhani yokhudza kubweranso kwa Ambuye. Akuwakumbutsa za m’mene iyeyo ankakhalira pakati pao. Akulakalaka kukawayenderanso. Paulo akugwiritsa ntchito mwayiwu kuti awauze za Akhristu amene anamwalira kale, Khristu asanabwere. Kodi nanga Khristuyo adzabweranso liti? Paulo akuwauza kuti akonzekere modekha ndi kuyembekezera kubweranso kwa Ambuye.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1

Kuyamikira ndi kuyamika 1.2—3.13

Chilimbikitso pa moyo wa Chikhristu wabwino 4.1-12

Malangizo pakubweranso kwa Khristu 4.13—5.11

Machenjezo omaliza 5.12-22

Mau omaliza 5.23-28

Categories
1 ATESALONIKA

1 ATESALONIKA 1

1 Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwaMpingowa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye YesuKhristu:Chisomo kwa inu ndi mtendere.

Zipatso za Uthenga Wabwino ku Tesalonika

2 Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m’mapemphero athu;

3 ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;

4 podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, chisankhidwe chanu,

5 kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m’mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.

6 Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m’mene mudalandira mauwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;

7 kotero kuti munayamba kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupirira mu Masedoniya ndi muAkaya.

8 Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati mu Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m’malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.

9 Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,

10 ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife kumkwiyo ulinkudza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TH/1-0dcf0da58c93390180e7a1f4f31a65b7.mp3?version_id=1068—

Categories
1 ATESALONIKA

1 ATESALONIKA 2

Za utumiki wake wa kwa Atesalonika

1 Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhale opanda pake;

2 koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.

3 Pakuti kudandaulira kwathu sikuchokera kukusochera, kapena kuchidetso, kapena m’chinyengo;

4 komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.

5 Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;

6 kapena sitinakhale ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsani mongaatumwiaKhristu.

7 Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m’mene mlezi afukata ana ake a iye yekha;

8 kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.

9 Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.

10 Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;

11 monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,

12 ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.

13 Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.

14 Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza aMipingoya Mulungu yokhala mu Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;

15 amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;

16 natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.

Paulo alira kuonanso Atesalonika. Akondwera pa uthenga anabwera nao Timoteo

17 Koma ife, abale, angakhale adatichotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi chilakolako chachikulu;

18 chifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; komaSatanaanatiletsa.

19 Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m’kufika kwake?

20 Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TH/2-5a950346687d3e302a2da49c9c780a4d.mp3?version_id=1068—

Categories
1 ATESALONIKA

1 ATESALONIKA 3

1 Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidavomereza mtima atisiye tokha ku Atene;

2 ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu mu Uthenga Wabwino waKhristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;

3 kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife tichite izi.

4 Pakutinso, pamene tinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa.

5 Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.

6 Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu;

7 chifukwa cha ichi tasangalala pa inu, abale, m’kupsinjika kwathu konse ndi chisautso chathu chonse, mwa chikhulupiriro chanu;

8 pakuti tsopano tili ndi moyo, ngati inu muchilimika mwa Ambuye.

9 Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;

10 ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?

11 Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m’njira yakufika kwa inu;

12 koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m’chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu;

13 kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m’chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TH/3-c14cd554bd2306b6577435d351831c8b.mp3?version_id=1068—

Categories
1 ATESALONIKA

1 ATESALONIKA 4

Atsate kuyeramtima, chikondano, ndi khama

1 Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.

2 Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.

3 Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;

4 yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu,

5 kosati m’chisiriro cha chilakolako chonyansa, mongansoamitunduosadziwa Mulungu;

6 asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m’menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.

7 Pakuti Mulungu sanaitane ife titsate chidetso, koma chiyeretso.

8 Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.

9 Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake;

10 pakutinso munawachitira ichi abale onse a mu Masedoniya yense. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa,

11 ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;

12 kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.

Za kuuka kwa akufa ndi kubwera kwa Yesu

13 Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.

14 Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.

15 Pakuti ichi tinena kwa inu m’mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.

16 Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau amngelowamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwaKhristuadzayamba kuuka;

17 pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m’mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.

18 Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TH/4-d85a9cd35e8efbb215f682e9b3ba105f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 ATESALONIKA

1 ATESALONIKA 5

1 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani.

2 Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.

3 Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.

4 Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala;

5 pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima;

6 chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.

7 Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.

8 Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.

9 Pakuti Mulungu sanatiike ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu YesuKhristu,

10 amene anafa m’malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.

11 Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.

Malangizo

12 Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu;

13 ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.

14 Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.

15 Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.

16 Kondwerani nthawi zonse;

17 Pempherani kosaleka;

18 M’zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

19 Musazime Mzimuyo;

20 Musanyoze manenero;

21 Yesani zonse; sungani chokomacho,

22 Mupewe maonekedwe onse a choipa.

23 Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

24 Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita.

25 Abale, tipempherereni ife.

26 Perekani moni kwa abale onse ndi chipsompsono chopatulika.

27 Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.

28 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale nanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TH/5-62778f54b9d8326e313739afcac3fa13.mp3?version_id=1068—