Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 10

Tisayese dala Mulungu monga Israele

1 Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;

2 nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m’nyanja,

3 nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;

4 namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiyeKhristu.

5 Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwere nao; pakuti anamwazika m’chipululu.

6 Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.

7 Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.

8 Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.

9 Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.

10 Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.

11 Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.

12 Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.

13 Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Za kupembedza mafano, za kuyanjana ndi ziwanda

14 Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

15 Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena.

16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?

17 Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.

18 Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?

19 Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?

20 Koma nditi kuti zimeneamitunduapereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

21 Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

22 Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?

Mkhristu ndiye mfulu koma wosamalira ena

23 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24 Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.

25 Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbumtima;

26 pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.

27 Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbumtima.

28 Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.

29 Ndinena chikumbumtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbumtima cha wina?

30 Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo?

31 Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

32 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapenaMpingowa Mulungu;

33 monga inenso ndikondweretsa onse m’zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/10-7ee5c8f016dffdb4a67765fd2cac3f0f.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 11

1 Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanzaKhristu.

Za akazi mu Mpingo wa Ambuye

2 Ndipo ndikutamandani kuti m’zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.

3 Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.

4 Mwamuna yense woveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake.

5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.

6 Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.

7 Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9 pakutinso mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi;

10 koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa chaangelo.

11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.

12 Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu.

13 Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?

14 Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chinyozetsa iye?

15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.

16 Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapenaMpingowa Mulungu.

Zosayenera pa madyerero a chikondi. Machitidwe a Mgonero wa Ambuye

17 Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.

18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo.

19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.

20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

21 pakuti pakudyaku yense ayamba watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

22 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m’menemo? Sindikutamani.

23 Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;

24 ndipo m’mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.

25 Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.

26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.

27 Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.

29 Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.

30 Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.

31 Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.

32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

33 Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.

34 Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/11-3a196396f2b1e62185a8dd66e86996d8.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 12

Mphatso za Mzimu zisiyana

1 Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.

2 Mudziwa kuti pamene munaliamitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.

3 Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

4 Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.

5 Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.

6 Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.

7 Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

8 Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:

9 kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10 ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11 Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna.

Thupi ndi limodzi, zingakhale ziwalo zisiyana

12 Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonsoKhristu.

13 Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m’thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

14 Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri.

15 Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?

16 Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindili diso, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?

17 Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza?

18 Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m’thupi, monga anafuna.

19 Koma ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi, likadakhala kuti thupi?

20 Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.

21 Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.

22 Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofooka m’thupi, zifunika;

23 ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m’thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa.

24 Koma zokoma zathu zilibe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho;

25 kuti kusakhale chisiyano m’thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.

26 Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.

27 Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

28 Ndipotu Mulungu anaika ena muMpingo, poyambaatumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.

29 Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa?

30 Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau?

31 Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/12-19cbda32c38bca83612cbbe29e58f93b.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 13

Kuposa kwa Chikondi

1 Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi aangelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.

2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.

3 Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.

4 Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,

5 sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;

6 sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;

7 chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.

8 Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.

9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

10 Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.

11 Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.

12 Pakuti tsopano tipenya m’kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.

13 Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/13-59be74f2e331cc2e9e24b4a393cdee84.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 14

Mphatso ya kunenera iposa ya malilime

1 Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere.

2 Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.

3 Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.

4 Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangiriraMpingo.

5 Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.

6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m’vumbulutso, kapena m’chidziwitso, kapena m’chinenero, kapena m’chiphunzitso?

7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa?

8 Pakuti ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?

9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.

10 Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.

11 Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.

12 Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.

13 Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.

14 Pakuti ngati ndipemphera m’lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.

15 Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.

16 Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzatiAmenbwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?

17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe.

18 Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19 koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m’lilime.

20 Abale, musakhale ana m’chidziwitso, koma m’choipa khalani makanda, koma m’chidziwitso akulu misinkhu.

21 Kwalembedwa m’chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22 Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.

23 Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?

24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

25 zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

Chipembedzo chichitike molongosoka

26 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.

27 Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.

28 Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

29 Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.

30 Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo.

31 Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;

32 ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

33 pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

34 Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.

35 Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.

36 Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha?

37 Ngati wina ayesa kuti alimneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.

38 Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.

39 Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.

40 Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/14-73ce4af24a4d9a4a6d78295b4fe5a292.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 15

Za kuuka kwa akufa

1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,

2 umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.

3 Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kutiKhristuanafera zoipa zathu, monga mwa malembo;

4 ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;

5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;

6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;

7 pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwaatumwionse;

8 ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.

9 Pakuti ine ndili wamng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalondaMpingowa Mulungu.

10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.

11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira.

12 Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?

13 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwe;

14 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.

15 Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitse, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.

16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwe;

17 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m’machimo anu.

18 Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika.

19 Ngati tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.

20 Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.

21 Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.

22 Pakuti monga mwaAdamuonse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

23 Koma yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.

24 Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.

25 Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.

26 Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.

27 Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.

28 Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

29 Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?

30 Nanga ifenso tili m’moopsa bwanji nthawi zonse?

31 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwaKhristuYesu, Ambuye wathu.

32 Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.

33 Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.

34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.

35 Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?

36 Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa;

37 ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina;

38 koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lakelake.

39 Nyama yonse siili imodzimodzi; koma ina ndi ya anthu, ndi ina ndiyo nyama ya zoweta, ndi ina ndiyo nyama ya mbalame, ndi ina ya nsomba.

40 Palinso matupi am’mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam’mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.

41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi mu ulemerero.

42 Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi;

43 lifesedwa m’mnyozo, liukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m’chifooko, liukitsidwa mumphamvu;

44 lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.

45 Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.

46 Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu.

47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.

48 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.

49 Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo.

50 Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.

51 Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,

52 m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.

53 Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa.

54 Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m’chigonjetso.

55 Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?

56 Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo:

57 koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

58 Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/15-2f7b137e8c952e88d37426bd21f54b15.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 16

Zopereka za kwa Akhristu a ku Yerusalemu

1 Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangizaMipingoya ku Galatiya, motero chitani inunso.

2 Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.

3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi makalata, apite nayo mphatso yanu kuYerusalemu.

4 Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.

Za maulendo akudza, ndi malonje a Paulo

5 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya;

6 ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.

7 Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.

8 Koma ndidzakhala ku Efeso kufikiraPentekoste.

9 Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.

10 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;

11 chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.

12 Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.

13 Dikirani, chilimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.

14 Zanu zonse zichitike m’chikondi.

15 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba chaAkaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

16 kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito.

17 Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.

18 Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muzindikire otere.

19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m’nyumba yao.

20 Akupatsani moni abale onse. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.

21 Ndikupereka moni ine Paulo ndi dzanja langa.

22 Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.

23 Chisomo cha Ambuye YesuKhristuchikhale ndi inu.

24 Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/16-ace8df393251fd7d667478e3f41aadd2.mp3?version_id=1068—