Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yoyamba ya Paulo kwa Akorinto

inalembedwa pofuna kukonza mavuto okhudzana ndi moyo wa Chikhristu komanso chikhulupiriro amene anabuka mu mpingo umene Paulo anakhazikitsa ku Korinto. Mu nthawi imeneyo, unali mzinda waukulu Wachigriki wa malonda, ndipo unali likulu la dera la Akaya. Mzindawu umadziwika ndi malonda osiyanasiyana, miyambo yake yosiririka, za dama ndi zipembedzo zosiyanasiyana.

Nkhawa yaikulu ya mtumwi inali mavuto amene analipo, monga kugawikana ndi chigololo komanso mafunso okhudzana ndi kugonana ndi banja, chikumbumtima, dongosolo la mu mpingo, mphatso za Mzimu Woyera ndi kuuka kwa akufa. Paulo akugwiritsa ntchito Uthenga Wabwino pofuna kufotokozera zonsezi bwino lomwe.

Mu mutu 13, pamene akukamba za chikondi ngati mphatso ya mtengo wapatali ya Mulungu kwa anthu ake. Imeneyi ndi ndime yodziwika bwino mu bukuli.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-9

Kugawana mu mpingo 1.10—4.21

Za moyo wabanja ndikugonana koyenera 5.1—7.40

Akhristu ndi akunja 8.1—11.1

Moyo ndi chipembedzo cha mu mpingo 11.2—14.40

Kuukanso kwa Yesu ndi kwa okhulupirira 15.1-58

Chopereka cha Akhristu a ku Yudeya 16.1-4

Malonje ndi mau omaliza 16.5-24

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 1

1 Paulo, woitanidwa akhalemtumwiwaKhristuYesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo,

2 kwaMpingowa Mulungu wakukhala mu Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m’malo monse, ndiye wao, ndi wathu:

3 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chinapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;

5 kuti m’zonse munalemezedwa mwa Iye, m’mau onse, ndi chidziwitso chonse;

6 monga umboni wa Khristu unakhazikika mwa inu;

7 kotero kuti sichikusowani inu chaufulu chilichonse; pakulindira inu vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Khristu;

8 amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.

9 Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.

Malekano mu Mpingo wa ku Korinto

10 Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.

11 Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Koloe, kuti pali makani pakati pa inu.

12 Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.

13 Kodi Khristu wagawika? Kodi Paulo anapachikidwa chifukwa cha inu? Kapena kodi munabatizidwa m’dzina la Paulo?

14 Ndiyamika Mulungu kuti sindinabatize mmodzi yense wa inu, koma Krispo ndi Gayo;

15 kuti anganene mmodzi kuti mwabatizidwa m’dzina langa.

16 Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefanasi; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense.

Nzeru za Mulungu ndi nzeru za anthu

17 Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.

18 Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.

19 Pakuti kulembedwa,

Ndidzaononga nzeru za anzeru,

ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha.

20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?

21 Pakuti popeza m’nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.

22 Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru:

23 koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwaamitunduchinthu chopusa;

24 koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.

25 Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.

26 Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;

27 koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;

28 ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko;

29 kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.

30 Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;

31 kuti monga mwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/1-b38ecac648833b699fe0eb34517e06a1.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 2

Ulalikidwe wa Paulo

1 Ndipo ine, abale, m’mene ndinadza kwa inu, sindinadze ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu.

2 Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma YesuKhristu, ndi Iye wopachikidwa.

3 Ndipo ine ndinakhala nanu mofooka ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri.

4 Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m’chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;

5 kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

6 Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;

7 koma tilankhula nzeru ya Mulungu m’chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,

8 imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero;

9 koma monga kulembedwa,

Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve,

nisizinalowe mu mtima wa munthu,

zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.

10 Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.

11 Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

12 Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.

13 Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.

14 Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.

15 Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.

16 Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/2-f93c22eebf10f133797719affb741d52.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 3

Chifukwa cha malekano ao

1 Ndipo ine, abale, sindinathe kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwaKhristu.

2 Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;

3 pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

4 Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?

5 Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.

6 Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.

7 Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.

8 Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.

Akhristu ali nyumba ya Mulungu, Yesu ali maziko a nyumbayi

9 Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.

10 Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang’anire umo amangira pamenepo.

11 Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo YesuKhristu.

12 Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide,siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu,

13 ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.

14 Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho.

15 Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.

16 Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

17 Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

18 Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m’nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.

19 Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m’chenjerero lao;

20 ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake.

21 Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu;

22 ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu;

23 koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/3-d6ab084e105bccde0d74c47193e7fa22.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 4

Atumiki a Khristu ndi ogawira zinsinsi za Mulungu

1 Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki aKhristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.

2 Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang’ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.

4 Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m’menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.

5 Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Kudzikuza kwa Akorinto, kudzichepetsa kwa Atumwi

6 Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.

7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?

8 Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.

9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ifeatumwiotsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwaangelo, ndi kwa anthu.

10 Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.

11 Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;

12 ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

13 ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

14 Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa.

15 Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwaKhristuYesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.

16 Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

17 Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo muMipingoyonse.

18 Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.

19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

20 Pakuti ufumu wa Mulungu suli m’mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani?

21 Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/4-96c635c252617c83e02222b74e6da626.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 5

Za chigololo mu Mpingo wa ku Korinto. Awadzudzulapo

1 Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwaamitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.

2 Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.

3 Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndilipo,

4 m’dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,

5 kumpereka iye wochita chotere kwaSatana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye Yesu.

6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse?

7 Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. PakutinsoPaskawathu waphedwa, ndiyeKhristu;

8 chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.

9 Ndinalembera inu m’kalata ija, kuti musayanjane ndi achigololo;

10 si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m’dziko lapansi;

11 koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.

12 Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m’katimo simuwaweruze ndi inu,

13 koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/5-8de96fb35045b32164ccac34373262e7.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 6

Awadzudzula pa milandu ya pakati pa abale

1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?

2 Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?

3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruzaangelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?

4 Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe muMpingo?

5 Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,

6 koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?

7 Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?

8 Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu.

9 Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

10 kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

11 Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye YesuKhristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Matupi athu ali ziwalo za Khristu

12 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.

13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;

14 koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.

15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai.

16 Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.

17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.

18 Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.

19 Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

20 Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/6-b5158dd682c61c8a882f6284dbf8cfc3.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 7

Mau a za ukwati

1 Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.

2 Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

3 Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.

4 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.

5 Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kutiSatanaangakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.

6 Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.

7 Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.

8 Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.

9 Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

10 Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,

11 komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

12 Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

13 Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.

14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.

15 Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.

16 Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?

17 Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika muMipingoyonse.

18 Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.

19 Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.

20 Yense akhale m’maitanidwe m’mene anaitanidwamo.

21 Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko.

22 Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo waKhristu.

23 Munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu.

24 Yense, m’mene anaitanidwamo, abale, akhale momwemo ndi Mulungu.

25 Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

26 Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo ino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.

27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.

28 Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m’thupi, ndipo ndikulekani.

29 Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;

30 ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;

31 ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.

32 Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye;

33 koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake.

34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

35 Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.

36 Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe.

37 Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino.

38 Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa.

39 Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.

40 Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/7-660ef4124678503544bd0fac8fb79874.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 8

Kunena za kudya nyama yoperekedwa nsembe kwa mafano

1 Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.

2 Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.

3 Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.

4 Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.

5 Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m’mwamba, kapena padziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

6 koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi YesuKhristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

7 Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.

8 Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako.

9 Koma yang’anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofookawo.

10 Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya mu Kachisi wa fano, kodi chikumbumtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

11 Pakuti mwa chidziwitso chako wofookayo atayika, ndiye mbale amene Khristu anamfera.

12 Koma pakuchimwira abale, ndi kulasa chikumbumtima chao chofooka, muchimwira kotero Khristu.

13 Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/8-438bb66241a7b56ca0560c0f2ca78999.mp3?version_id=1068—

Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 9

Ufulu ndi ulamuliro wa mtumwiyo

1 Kodi sindine mfulu? Kodi sindinemtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?

2 Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.

3 Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi:

4 Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?

5 Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?

6 Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito?

7 Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

8 Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo?

9 Pakuti m’chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng’ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng’ombe?

10 Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao.

11 Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi nchachikulu ngati ife tituta za thupi lanu?

12 Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino waKhristu.

13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

14 Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

Kudzipereka kwa mtumwiyo. Makani a liwiro a Mkhristu

15 Koma ine sindinachite nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.

16 Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.

17 Pakuti ngati ndichita ichi chivomerere, mphotho ndili nayo; koma ngati si chivomerere, anandikhulupirira mu udindo.

18 Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.

19 Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.

20 Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhale ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21 kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

22 Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.

23 Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

24 Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.

25 Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.

26 Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga;

27 koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/9-5728bf7e7c2e3d49a4a549508372b2d1.mp3?version_id=1068—