Categories
MATEYU

MATEYU 12

Yesu mbuye wa Sabata

1 Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku laSabatapakati pa minda ya tirigu; ndipoophunziraake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.

2 KomaAfarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata.

3 Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?

4 Kuti analowa m’nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.

5 Kapena simunawerenge kodi m’chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe mu Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo?

6 Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano.

7 Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa,

8 pakutiMwana wa Munthuali mwini tsiku la Sabata.

Yesu achiritsa wa dzanja lopuwala

9 Ndipo Iye anachokera pamenepo, nalowa m’sunagogemwao;

10 ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu.

11 Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m’dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa?

12 Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata.

13 Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake.

14 Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga.

15 Koma Yesu m’mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse,

16 nawalimbitsira mau kuti asamuwulule Iye;

17 kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesayamneneriuja, kuti,

18 Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha,

wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye;

pa Iye ndidzaika Mzimu wanga,

ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.

19 Sadzalimbana, sadzafuula;

ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m’makwalala;

20 bango lophwanyika sadzalithyola,

ndi nyali yofuka sadzaizima,

kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.

21 Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.

Za Yesu ndi Belezebulu

22 Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.

23 Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?

24 Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake yaBelezebulu, mkulu wa ziwanda.

25 Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mzinda uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;

26 ndipo ngatiSatanaamatulutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?

27 Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu.

28 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m’banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m’banja lake.

30 Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

31 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa.

32 Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.

Mitengo ndi zipatso zao

33 Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.

34 Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m’kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.

35 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’chuma chake choipa.

36 Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.

37 Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Chizindikiro cha Yona

38 Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona chizindikiro cha Inu.

39 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri;

40 pakuti monga Yona anali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.

41 Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.

42 Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.

43 Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.

44 Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.

45 Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.

Abale a Yesu

46 Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.

47 Ndipo munthu anati kwa Iye, Onani, amai wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu.

48 Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani, ndipo abale anga ndi ayani?

49 Ndipo anatambalitsa dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga!

50 Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/12-28dbc587e4da56abfa4d83a83c6b6694.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 13

Fanizo la Wofesa

1 Tsiku lomwelo Yesu anatuluka m’nyumbamo, nakhala pansi m’mbali mwa nyanja.

2 Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m’ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.

3 Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m’mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.

4 Ndipo m’kufesa kwake zina zinagwa m’mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nkulusira izo.

5 Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhale nalo dothi lakuya.

6 Ndipo m’mene dzuwa linakwera zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.

7 Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nkuzitsamwitsa izo.

8 Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.

9 Amene ali ndi makutu, amve.

10 Ndipoophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m’mafanizo?

11 Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.

12 Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.

13 Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m’mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa.

14 Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati,

Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;

pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse.

15 Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa,

ndipo m’makutu ao anamva mogontha,

ndipo maso ao anatsinzina;

kuti asaone konse ndi maso,

asamve ndi makutu,

asazindikire ndi mtima wao,

asatembenuke,

ndipo ndisawachiritse iwo.

16 Koma maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.

17 Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimve.

Kumasulira kwa fanizo la wofesa

18 Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja.

19 Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m’mbali mwa njira.

20 Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;

21 ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing’ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.

22 Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.

23 Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.

Fanizo la namsongole

24 Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m’munda mwake;

25 koma m’mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.

26 Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.

27 Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m’munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?

28 Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi?

29 Koma iye anati, Iai, kuti kapena m’mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.

30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m’nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m’nkhokwe yanga.

Fanizo la kambeu kampiru ndi la chotupitsa mkate

31 Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pake;

32 kamene kakhaladi kakang’ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nkubindikira mu nthambi zake.

33 Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m’miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.

34 Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m’mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo;

35 kuti chikachitidwe chonenedwa ndimneneri, kuti,

Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;

ndidzawulula zinthu zobisika

chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.

Yesu awatanthauzira fanizo la namsongole

36 Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m’nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m’munda.

37 Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiyeMwana wa Munthu;

38 Ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;

39 ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwoangelo.

40 Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, motero mudzakhala m’chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

41 Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,

42 ndipo adzawataya iwo m’ng’anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

43 Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.

Fanizo la chuma chobisika, la ngale, la khoka

44 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m’munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.

45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino:

46 ndipo m’mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.

47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m’nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;

48 limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m’mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m’zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.

49 Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,

50 nadzawataya m’ng’anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

51 Mwamvetsa zonsezi kodi? Iwo anati kwa Iye, Inde.

52 Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m’chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.

Ampeputsa Yesu ku Nazarete

53 Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko.

54 Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m’sunagogemwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?

55 Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda?

56 Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?

57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.

58 Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/13-dfbdf9eb0ea1c92c57dd0bd532be25da.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 14

Herode amupha Yohane Mbatizi

1 Nthawi imeneyoHerodemfumu anamva mbiri ya Yesu,

2 nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.

3 Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m’nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.

4 Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye.

5 Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iyemneneri.

6 Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.

7 Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chilichonse akapempha.

8 Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m’mbale mutu wa Yohane Mbatizi.

9 Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe;

10 ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m’nyumba yandende.

11 Ndipo anautenga mutu wake m’mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake.

12 Ndipoophunziraake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.

Yesu achulukitsa mikate poyamba paja

13 Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m’ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m’midzi.

14 Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao.

15 Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.

16 Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye.

17 Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tilibe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.

18 Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine.

19 Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m’mene anayang’ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.

20 Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.

21 Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

Yesu ayenda panyanja

22 Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m’ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.

23 Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m’phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.

24 Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao.

25 Ndipo pa ulonda wachinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja.

26 Koma m’mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo anafuula ndi mantha.

27 Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.

28 Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa Inu pamadzi.

29 Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m’ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.

30 Koma m’mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!

31 Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang’ono, wakayikiranji mtima?

32 Ndipo pamene iwo analowa m’ngalawamo, mphepo inaleka.

33 Ndipo iwo amene anali m’ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.

34 Ndipo pamene iwo anaoloka, anafika kumtunda, ku Genesarete.

35 Ndipo m’mene amuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse kudziko lonse lozungulira, nadza nao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda;

36 ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/14-25fa18e7c226f893b2233c32ad645011.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 15

Miyambo ya makolo

1 Pomwepo anadza kwa YesuAfarisindi alembi, ochokera kuYerusalemu, nati,

2 Ophunziraanu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya.

3 Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?

4 Pakuti Mulungu anati,

Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo,

Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.

5 Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu;

6 iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.

7 Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti,

8 Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao;

koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

9 Koma andilambira Ine kwachabe,

ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

10 Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;

11 si chimene chilowa m’kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m’kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.

12 Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho?

13 Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa.

14 Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m’mbuna.

15 Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli.

16 Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala chipulukirire?

17 Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m’kamwa zipita m’mimba, ndipo zitayidwa kuthengo?

18 Koma zakutuluka m’kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu.

19 Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;

20 izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai.

Mkazi wa ku Kanani

21 Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni.

22 Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m’malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.

23 Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.

24 Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israele.

25 Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine.

26 Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu.

27 Koma iye anati, Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.

28 Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.

Yesu achulukitsa mikate pachiwiri paja

29 Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m’phiri, nakhala pansi pamenepo.

30 Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa;

31 kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.

32 Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.

33 Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m’chipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu?

34 Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang’ono.

35 Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse;

36 natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.

37 Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala.

38 Ndipo anadyawo anali amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana.

39 Ndipo m’mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m’ngalawa, nafika m’malire a Magadani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/15-10faaa21fdd55fe869e07ce0afe69552.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 16

Afarisi ndi Asaduki afuna chizindikiro

1 NdipoAfarisindiAsadukianadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba.

2 Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwee; popeza thambo lili lacheza.

3 Ndipo m’mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira.

4 Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo.

5 Ndipoophunziraanadza kutsidya linalo, naiwala kutenga mikate.

6 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang’anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.

7 Ndipo iwo anafunsana wina ndi mnzake, nati, Sitinatenge mikate.

8 Koma Yesu, m’mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang’ono, mufunsana chifukwa ninji wina ndi mnzake, kuti simunatenga mikate?

9 Kodi chikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi madengu angati munawatola?

10 Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi madengu angati munawatola?

11 Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki.

12 Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauze kupeza chotupitsa cha mikate, koma chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.

Chivomerezo cha Petro

13 Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kutiMwana wa Munthundiye yani?

14 Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.

15 Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani?

16 Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinuKhristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.

17 Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.

18 Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazikaMpingowanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.

19 Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.

20 Pamenepo analamulira ophunzira kuti asauze munthu kuti Iye ndiye Khristu.

21 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke kuYerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.

22 Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai.

23 Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga,Satanaiwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.

Za kusenza mtanda wake

24 Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.

25 Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.

26 Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?

27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndiangeloake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.

28 Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/16-39483d6034dad44f37928c6e43b1f582.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 17

Mawalitsidwe a Yesu paphiri

1 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha paphiri lalitali;

2 ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.

3 Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi Iye.

4 Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.

5 Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.

6 Ndipo pameneophunziraanamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukulu.

7 Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa.

8 Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha.

9 Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikiraMwana wa Munthuadadzauka kwa akufa.

10 Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?

11 Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse;

12 koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.

13 Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi.

Yesu achiritsa wodwala khunyu

14 Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati,

15 Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m’madzi.

16 Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa.

17 Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.

18 Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

19 Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoze bwanji kuchitulutsa?

20 Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching’ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.

22 Ndipo m’mene anali kutsotsa mu Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m’manja a anthu;

23 ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.

Yesu apereka msonkho

24 Ndipo pofika ku Kapernao amene aja akulandira ndalama za ku Kachisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?

25 Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m’nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?

26 Ndipo m’mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu.

27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/17-8f2d2fb14755b40db3475f33d329e8e4.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 18

Wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba

1 Nthawi yomweyoophunziraanadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?

2 Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,

3 nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

4 Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.

5 Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira Ine;

6 koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m’khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.

7 Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.

8 Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m’moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m’moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.

9 Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m’moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa muGehenawamoto, uli ndi maso awiri.

10 Yang’anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kutiangeloao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

12 Nanga muyesa bwanji? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?

13 Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.

14 Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang’ono awa atayike.

Makhululukidwe

15 Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.

16 Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.

17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uuzeMpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndiwamsonkho.

18 Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula padziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.

19 Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira.

20 Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pao.

Fanizo la wamangawa wopanda chifundo

21 Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi?

22 Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.

23 Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ake.

24 Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.

25 Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.

26 Chifukwa chake kapoloyo anagwada pansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.

27 Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi chisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.

28 Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.

29 Pamenepo kapolo mnzakeyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.

30 Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m’nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.

31 Chifukwa chake m’mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa.

32 Pomwepo mbuye wake anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine;

33 kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?

34 Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse.

35 Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/18-dc8177a52b99e04d7d3ce56d3055d03b.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 19

Za kalata ya chilekaniro

1 Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordani.

2 Ndipo makamu aakulu a anthu anamtsata; ndipo Iye anawachiritsa kumeneko.

3 NdipoAfarisianadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?

4 Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,

5 nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?

6 Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.

7 Iwo ananena kwa Iye, Nanga chifukwa ninji Mose analamula kupatsa kalata yachilekaniro, ndi kumchotsa?

8 Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.

9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.

10 Ophunziraananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.

11 Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa.

12 Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m’mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.

Yesu adalitsa ana

13 Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.

14 Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

15 Ndipo Iye anaika manja ake pa ito, nachokapo.

Munthu mwini chuma

16 Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nao moyo wosatha?

17 Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m’moyo, sunga malamulo.

18 Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,

19 Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

20 Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani?

21 Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.

22 Koma mnyamatayo m’mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.

23 Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba.

24 Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kutingamiraipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.

25 Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?

26 Ndipo Yesu anawayang’ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.

27 Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?

28 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m’kubadwanso, pameneMwana wa Munthuadzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.

29 Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.

30 Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/19-44a92acb5aa8c399405d0fd9dff90847.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 20

Fanizo la antchito olembedwa mwinamwina

1 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m’munda wake wampesa.

2 Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.

3 Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo;

4 ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.

5 Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi.

6 Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?

7 Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.

8 Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.

9 Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi.

10 Ndipo m’mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka.

11 Koma m’mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,

12 nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing’ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.

13 Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi?

14 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.

15 Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?

16 Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.

Funso la ana a Zebedeo

17 Ndipo pamene Yesu analikukwera kuYerusalemu, anatengaophunzirakhumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,

18 Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipoMwana wa Munthuadzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,

19 nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.

20 Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.

21 Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.

22 Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.

23 Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.

24 Ndipo m’mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.

25 Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo.

26 Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

27 ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:

28 monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.

Akhungu a ku Yeriko

29 Ndipo pamene iwo analikutuluka mu Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye.

30 Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m’mphepete mwa njira; m’mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide.

31 Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.

32 Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?

33 Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye.

34 Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/20-f62cb8509cd814b40546f113af6fba13.mp3?version_id=1068—

Categories
MATEYU

MATEYU 21

Yesu alowa mu Yerusalemu

1 Ndipo pamene iwo anayandikira kuYerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumizaophunziraawiri,

2 nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.

3 Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.

4 Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndimnenerikuti,

5 Tauzani mwana wamkazi waZiyoni,

Taona, mfumu yako idza kwa iwe,

wofatsa ndi wokwera pabulu,

ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.

6 Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza;

7 nabwera ndi bulu ndi mwana wake, naika pa iwo zovala zao, nakhala Iye pamenepo.

8 Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m’njiramo.

9 Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m’dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!

10 Ndipo m’mene adalowa mu Yerusalemu mzinda wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu?

11 Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.

Yesu ayeretsa Kachisi kachiwiri

12 Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;

13 nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.

14 Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa.

15 Koma ansembe aakulu ndi alembi, m’mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,

16 nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?

17 Ndipo Iye anawasiya, natuluka m’mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.

Mkuyu wofota

18 Ndipo mamawa, m’mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala.

19 Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.

20 Ndipo ophunzira poona ichi anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?

21 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja, chidzachitidwa.

22 Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m’kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.

Ubatizo wa Yohane

23 Ndipo m’mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?

24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:

25 Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?

26 Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.

27 Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.

Fanizo la ana aamuna awiri

28 Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.

29 Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita.

30 Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite.

31 Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kutiamisonkhondi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.

32 Popeza Yohane anadza kwa inu m’njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m’mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.

Fanizo la olima munda wampesa

33 Mveranifanizolina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.

34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.

35 Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.

36 Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachitira iwo momwemo.

37 Koma pambuyo pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu.

38 Koma olimawo m’mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.

39 Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.

40 Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani?

41 Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.

42 Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m’malembo,

Mwala umene anaukana omanga nyumba

womwewu unakhala mutu wa pangodya:

Ichi chinachokera kwa Ambuye,

ndipo chili chozizwitsa m’maso mwathu?

43 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.

44 Ndipo iye wakugwa pamwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.

45 Ndipo ansembe aakulu ndiAfarisi, pakumva mafanizo ake, anazindikira kuti alikunena za iwo.

46 Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, chifukwa anamuyesa mneneri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/21-357443a40e1bd9b8689f2630fef23159.mp3?version_id=1068—