Categories
GENESIS

GENESIS 10

Mbumba ya Nowa

1 Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.

2 Ana aamuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi.

3 Ndi ana aamuna a Gomeri: Asikenazi, ndi Rifati, ndi Togarima.

4 Ndi ana aamuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu.

5 Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m’maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m’mitundu yao.

6 Ndi ana aamuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani.

7 Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani.

8 Ndipo Kusi anabala Nimirodi; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu padziko lapansi.

9 Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: chifukwa chake kunanenedwa, Monga Nimirodi mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.

10 Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m’dziko la Sinara.

11 M’dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,

12 ndi Reseni pakati pa Ninive ndi Kala: umenewo ndi mzinda waukulu.

13 Ejipito ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabu, ndi Nafituhimu,

14 ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m’menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori.

15 Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti,

16 ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi;

17 ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini;

18 ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira.

19 Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.

20 Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m’maiko ao, m’mitundu yao.

21 Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana.

22 Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu.

23 Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli ndi Getere, ndi Masi.

24 Aripakisadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Eberi.

25 Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m’masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.

26 Ndipo Yokotani anabala Alimodadi, ndi Selefi, ndi Hazara-Maveti, ndi Yera;

27 ndi Hadoramu ndi Uzali, ndi Dikila;

28 ndi Obala, ndi Abimaele, ndi Sheba;

29 ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani.

30 Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefari phiri la kum’mawa.

31 Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m’maiko ao, m’mitundu yao.

32 Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m’mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/10-7e41bde1cc25a3dcdff6ca361f150c7d.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 11

Nsanja ya Babiloni

1 Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.

2 Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum’mawa, anapeza chigwa m’dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko.

3 Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.

4 Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.

5 Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mzinda ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu.

6 Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita.

7 Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.

8 Ndipo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mzinda.

9 Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi.

Mibadwo ya Semu

10 Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri;

11 ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

12 Ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu nabala Sela;

13 ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana aamuna ndi aakazi.

14 Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Eberi;

15 ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Eberi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

16 Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi;

17 ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelegi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

18 Ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Reu;

19 ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi zinai, atabala Reu, nabala ana aamuna ndi aakazi.

20 Ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziwiri, nabala Serugi:

21 ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi ziwiri, atabala Serugi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

22 Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori:

23 ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi.

24 Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera:

25 ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi.

26 Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani.

27 Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.

28 Ndipo anafa Harani pamaso pa atate wake Tera m’dziko la kubadwa kwake, mu Uri wa kwa Akaldeya.

29 Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.

30 Koma Sarai anali wouma; analibe mwana.

31 Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.

32 Masiku a Tera anali zaka mazana awiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera mu Harani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/11-68e116a8407f3d88dfca544dcfed1e03.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 12

Kuitanidwa kwa Abramu

1 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;

2 ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;

3 ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.

4 Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.

5 Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.

6 Ndipo Abramu anapitirira m’dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m’dzikomo nthawi yomweyo.

7 Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.

8 Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum’mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum’mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.

9 Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera.

Abramu atsikira ku Ejipito

10 Ndipo munali njala m’dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m’dziko m’menemo.

11 Ndipo panali pamene anayandikira kulowa mu Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;

12 ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.

13 Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.

14 Ndipo panali pamene Abramu analowa mu Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.

15 Ndipo akalonga ake aFaraoanamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao.

16 Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng’ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndingamira.

17 Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu.

18 Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako?

19 Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke.

20 Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m’njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/12-99232a7e451920dc935bf1a62779fa87.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 13

Abramu ndi Loti alekana

1 Ndipo anakwera Abramu kuchoka ku Ejipito, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera.

2 Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng’ombe ndisilivandi golide.

3 Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Betele, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja pakati pa Betele ndi Ai;

4 kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova.

5 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndi mahema.

6 Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.

7 Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m’dzikomo.

8 Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.

9 Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.

10 Ndipo Loti anatukula maso ake nayang’ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.

11 Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum’mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.

12 Ndipo Abramu anakhala m’dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m’mizinda ya m’chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.

13 Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.

Mulungu alonjeza kwa Abramu kumpatsa Kanani

14 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang’anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum’mawa, ndi kumadzulo:

15 chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.

16 Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.

17 Tauka, nuyendeyende m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.

18 Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/13-0d859721be73dee8c1227b976e2c9850.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 14

Abramu alanditsa Loti

1 Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,

2 iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari).

3 Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere).

4 Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka.

5 Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,

6 ndi Ahori paphiri lao Seiri kufikira ku Eliparani, kumene kuli m’mbali mwa chipululu.

7 Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.

8 Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari) ndipo anawathira nkhondo m’chigwa cha Sidimu;

9 ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kumenyana ndi asanu.

10 Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m’menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.

11 Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka.

12 Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala mu Sodomu, ndi chuma chake, namuka.

13 Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.

14 Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.

15 Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.

16 Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.

Melkizedeki adalitsa Abramu

17 Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu),

18 NdipoMelkizedekimfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.

19 Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;

20 ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m’dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.

21 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha.

22 Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi

23 kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeretsa Abramu;

24 koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Anere, Esikolo, ndi Mamure, iwo atenge gawo lao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/14-e21f85045f673ae5046216240cd4da91.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 15

Mulungu apangana ndi Abramu

1 Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m’masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.

2 Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?

3 Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m’nyumba mwanga adzalowa m’malo mwanga.

4 Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m’malo mwako; koma iye amene adzatuluka m’chuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m’malo mwako.

5 Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang’anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.

6 Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.

7 Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.

8 Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?

9 Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng’ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda.

10 Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.

11 Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo.

12 Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.

13 Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;

14 ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.

15 Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m’mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino.

16 Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.

17 Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng’anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto unadutsa pakati pa mabanduwo.

18 Tsiku lomwelo Yehova anapanganachipanganondi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:

19 Akeni ndi Akenizi, Akadimoni,

20 ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Arefaimu,

21 ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ayebusi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/15-43828ba51bf786711580ac93910f8240.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 16

Sarai ndi Hagara

1 Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara.

2 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.

3 Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m’dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake.

4 Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m’maso mwake.

5 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m’maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.

6 Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m’dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m’maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake.

7 Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m’chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.

8 Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai.

9 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake.

10 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.

Kubadwa kwa Ismaele

11 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.

12 Ndipo iye adzakhala munthu wa m’thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse.

13 Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang’ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine?

14 Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.

15 Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismaele.

16 Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/16-4e0f84f573f45472129af5d1822ed9cb.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 17

Dzina la Abramu lisinthika likhale Abrahamu

1 Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.

2 Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi Ine ndi iwe, ndipo ndidzachulukitsa iwe kwambiri.

3 Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Mulungu ananena naye kuti,

4 Koma Ine, taona, pangano langa lili ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu.

5 Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.

6 Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe.

7 Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m’mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.

8 Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.

Mulungu aika chizindikiro cha kudulidwa

9 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m’mibadwo yao.

10 Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.

11 Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu.

12 A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m’mibadwo mwanu, amene abadwa m’nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.

13 Azidulidwatu amene abadwa m’nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m’thupi mwako pangano losatha.

14 Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.

Dzina la Sarai lisinthika likhale Sara

15 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.

16 Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.

17 Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m’mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?

18 Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu!

19 Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.

20 Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.

21 Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.

22 Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu.

23 Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m’nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.

24 Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, pamene anadulidwa m’khungu lake.

25 Ndipo Ismaele mwana wake anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m’khungu lake.

26 Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismaele mwana wake.

27 Ndipo amuna onse a m’nyumba mwake obadwa m’nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/17-8ae272d8bb58fa4e56092068b5f8cbac.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 18

Amithenga atatu amuonekera Abrahamu

1 Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.

2 Ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,

3 Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;

4 nditengetu madzi pang’ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;

5 ndipo ndidzatenga chakudya pang’ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.

6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m’hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.

7 Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng’ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.

8 Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng’ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya.

9 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m’hemamo.

10 Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.

11 Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi;

12 ndipo Sara anaseka m’mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?

13 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?

14 Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.

15 Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka.

16 Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang’ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.

17 Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita?

18 Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye?

19 Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.

20 Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu,

21 ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.

Abrahamu apempherera a ku Sodomu

22 Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.

23 Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?

24 Kapena alipo olungama makumi asanu m’kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?

25 Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?

26 Ndipo anati Yehova, Ndikapeza mu Sodomu olungama makumi asanu m’kati mwa mzinda, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo.

27 Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:

28 kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.

29 Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m’menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai.

30 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m’menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m’menemo sindidzachita.

31 Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m’menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.

32 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m’menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.

33 Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/18-c9c3040893da0e8085753567f42b711e.mp3?version_id=1068—

Categories
GENESIS

GENESIS 19

Chionongeko cha Sodomu ndi Gomora

1 Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.

2 Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m’nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m’mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m’khwalalamu usiku wonse.

3 Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m’nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.

4 Koma asanagone, anthu a m’mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m’mbali zonse;

5 ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe.

6 Ndipo Loti anatulukira kwa iwo pakhomo, natseka chambuyo pakhomo pake.

7 Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere.

8 Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa.

9 Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko.

10 Koma anthu aja anatulutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m’nyumba, natseka pakhomo.

11 Ndipo anachititsa khungu m’maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang’ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.

12 Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nao m’mzinda muno, utuluke nao m’malo muno:

13 popeza ife tidzaononga malo ano, chifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge.

14 Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m’malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.

15 Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m’mphulupulu ya mzinda.

16 Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda.

17 Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.

18 Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;

19 taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;

20 taonanitu, mzinda uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung’ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung’ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo.

21 Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mzinda uwu umene wandiuza.

22 Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mzindawo Zowari.

23 Ndipo dzuwa lidakwera padziko pamene Loti anafika ku Zowari.

24 Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala yasulufurendi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;

25 ndipo anaononga mizindayo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m’mizindamo, ndi zimene zimera panthaka.

26 Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere.

27 Ndipo Abrahamu analawira m’mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova:

28 ndipo anayang’anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng’anjo.

29 Ndipo panali pamene Mulungu anaononga mizinda ya m’chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga mizinda m’mene anakhalamo Loti.

Gwero la Amoni ndi Mowabu

30 Ndipo Loti anabwera kutuluka mu Zowari nakhala m’phiri ndi ana aakazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala mu Zowari, ndipo anakhala m’phanga, iye ndi ana ake aakazi.

31 Woyamba ndipo anati kwa wamng’ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe padziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita padziko lonse lapansi:

32 tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu.

33 Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.

34 Ndipo panali m’mamawa, woyamba anati kwa wamng’ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.

35 Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng’ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.

36 Ndipo ana aakazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao.

37 Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.

38 Wamng’ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benami; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/19-5c1a175bc18a5f137e91263c6417b042.mp3?version_id=1068—