Kupasula kwa Babiloni. Maliro padziko lapansi
1 Zitatha izi ndinaonamngelowina wakutsika mu Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake.
2 Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.
3 Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.
4 Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;
5 pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira mu Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.
6 Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa ntchito zake; m’chikhomo unathiramo, muuthirire chowirikiza.
7 Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.
8 Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.
9 Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,
10 chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.
11 Ndipo ochita malonda a m’dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;
12 malonda a golide, ndi asiliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;
13 ndi sinamoni ndi amomo, ndi zofukiza, ndimure, ndilubani, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng’ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magaleta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.
14 Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakuchokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.
15 Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali chifukwa cha kuopa chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo;
16 nadzanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golide ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale!
17 Pakuti mu ora limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere. Ndipo watsigiro aliyense, ndi yense wakupita panyanja pakutipakuti, ndi amalinyero, ndi onse amene amachita kunyanja, anaima patali,
18 nafuula poona utsi wa kutentha kwake, nanena, Mzinda uti ufanana ndi mzinda waukuluwo?
19 Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti mu ora limodzi unasanduka bwinja.
20 Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndiatumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.
21 Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.
22 Ndipo mau a anthu oimba zeze, ndi a oimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo mmisiri aliyense wa machitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;
23 ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m’dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.
24 Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/18-4b99d1333b3a26bf8e11e48fdb615898.mp3?version_id=1068—