Categories
1 PETRO

1 PETRO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yoyamba ya Petro

analembera Akhristu, amene panopa akutchedwa “anthu osankhika a Mulungu”, amene anabalalika m’dera lonse la dziko limene masiku ano limatchedwa Turkey. Cholinga chenicheni cha kalatayi ndicho kuwalimbikitsa owerengawo, amene amakumana ndi mazunzo osiyanasiyana ndipo amasautsidwa chifukwa cha chikhulupiriro chao. Olembayo akuchita izi powakumbutsa awerengiwo za Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu umene imfa yake, kuuka kwake ndi lonjezano la kubweranso kwake, zinawapatsa chiyembekezo. Chifukwa chake iwowa ayenera kuvomereza zakuti adzazunzika ndipo apirire m’masautso. Iwo atsimikizike kuti kuzunzidwaku ndiko mayeso a kulimba kwa chikhulupiriro chao ndipo adzalandira mphotho “pa vumbulutso la Yesu Khristu” (1.7).

Kuphatikizapo chilimbikitso chimenechi m’nthawi ya mazunzo, olembayo akuwalimbikitsa awerengi ake kuti akhale m’moyo monga anthu amene ali ake a Khristu.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Kukumbutsa za chipulumutso cha Mulungu 1.3-12

Kulimbikitsana za khalidwe la moyo woyera 1.13—2.10

Udindo wa Mkhristu pa nthawi ya mazunzo 2.11—4.19

Kudzichepetsa ndi utumiki wa Chikhristu 5.1-11

Mau omaliza 5.12-14

Categories
1 PETRO

1 PETRO 1

1 Petro,mtumwiwa YesuKhristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya,

2 monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m’chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.

Chiyamiko chifukwa cha chipulumutso

3 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;

4 kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,

5 amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.

6 M’menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,

7 kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;

8 amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:

9 ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu.

10 Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani;

11 ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.

12 Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu iziangeloalakalaka kusuzumiramo.

Awadandaulira atsate kuyera mtima

13 Mwa ichi, podzimanga m’chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m’vumbulutso la Yesu Khristu;

14 monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

15 komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse;

16 popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

17 Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;

18 podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndisiliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu:

19 koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wamwanawankhosawopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:

20 amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi,

21 chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.

22 Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;

23 inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

24 Popeza,

Anthu onse akunga udzu,

ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu.

Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;

25 koma Mau a Ambuye akhala chikhalire.

Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/1-43096c9571a0529f5c5a13314c96a8ee.mp3?version_id=1068—

Categories
1 PETRO

1 PETRO 2

1 Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,

2 lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;

3 ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;

4 amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,

5 inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa YesuKhristu.

6 Chifukwa kwalembedwa m’lembo,

Taona, ndiika muZiyonimwala wotsiriza wa pangodya,

wosankhika, wa mtengo wake;

ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.

7 Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo osakhulupirira,

Mwala umene omangawo anaukana,

womwewo unayesedwa mutu wa pangodya.

8 Ndipo,

Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa.

Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.

9 Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

10 inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.

Za mayendedwe ao pakati pa akunja. Agonje kwa akulu

11 Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

12 ndipo mayendedwe anu mwaamitunduakhale okoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.

13 Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;

14 kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.

15 Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;

16 monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.

17 Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.

Zoyenera anyamata Akhristu

18 Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.

19 Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.

20 Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.

21 Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;

22 amene sanachite tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;

23 amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;

24 amene anasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.

25 Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang’anira wa moyo wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/2-a6a9dc170e2ed5072df95902e5ad68a9.mp3?version_id=1068—

Categories
1 PETRO

1 PETRO 3

Zoyenera akazi ndi amuna

1 Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;

2 pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.

3 Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala;

4 koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.

5 Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;

6 monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse.

7 Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.

Za chikondano. Za kulola masautso monga anachita Ambuye

8 Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;

9 osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

10 Pakuti,

Iye wofuna kukonda moyo,

ndi kuona masiku abwino,

aletse lilime lake lisanene choipa,

ndi milomo yake isalankhule chinyengo;

11 ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino;

afunefune mtendere ndi kuulondola.

12 Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama,

ndi makutu ake akumva pembedzo lao;

koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.

13 Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino?

14 Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;

15 koma mumpatulikitse AmbuyeKhristum’mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;

16 ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.

17 Pakuti, kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu.

18 Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;

19 m’menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m’ndende,

20 imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalawa, m’menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;

21 chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;

22 amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; paliangelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/3-d85d740e4c0742439815e88e9f221c74.mp3?version_id=1068—

Categories
1 PETRO

1 PETRO 4

1 PopezaKhristuadamva zowawa m’thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m’thupi walekana nalo tchimo;

2 kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.

3 Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro chaamitundu, poyendayenda inu m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

4 m’menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano;

5 amenewo adzamwerengera Iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.

6 Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m’thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.

7 Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero;

8 koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;

9 mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:

10 monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;

11 akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi.Amen.

12 Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:

13 koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.

14 Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.

15 Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;

16 koma akamva zowawa ngati Mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili.

17 Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?

18 Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?

19 Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m’manja a Wolenga wokhulupirika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/4-ed7d7b89bc35350a2703baa0e8242e8e.mp3?version_id=1068—

Categories
1 PETRO

1 PETRO 5

Zoyenera akulu ndi anyamata; adzichepetse, adikire

1 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa zaKhristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:

2 Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

3 osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

4 Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.

5 Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.

6 Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;

7 ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

8 Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

9 ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.

10 Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

11 Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi.Amen.

12 Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m’chimenechi muimemo.

13 Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.

14 Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi.

Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/5-25fadd4395781cab59ea834bbbd162f1.mp3?version_id=1068—

Categories
2 PETRO

2 PETRO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata yachiwiri ya Petro

kwa gulu lalikulu la Akhristu oyambirira. Cholinga chenicheni cha kalatayi ndicho kulimbana ndi zonena za aphunzitsi onyenga ndi makhalidwe oipa amene amabwera chifukwa cha chiphunzitsochi. Yankho lake la mavutowa lipezeka pogwiritsitsa chidziwitso chenicheni cha Mulungu ndi cha Ambuye Yesu Khristu. Chidziwitso chimenechi chinaperekedwa ndi anthu amene iwo eni adamuona Yesu chamaso namumva iye akulalikira. Wolembayo akukhudzidwa makamaka ndi chiphunzitso chakuti Khristu sadzabweranso. Iye akunena kuti kuchedwa kubweranso kwa Khristu ndi chifukwa chakuti, “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (3.9)

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Maitanidwe a Chikhristu 1.3-21

Aphunzitsi onyenga 2.1-22

Kubweranso komaliza kwa Khristu 3.1-18

Categories
2 PETRO

2 PETRO 1

1 Simoni Petro, kapolo ndimtumwiwa YesuKhristukwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m’chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m’chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.

Atsate zokoma za Chikhristu

3 Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha;

4 mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m’chilakolako.

5 Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso;

6 ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo;

7 ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.

8 Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.

9 Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woiwala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale.

10 Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;

11 pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.

12 Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m’choonadi chili ndi inu.

13 Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m’msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;

14 podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.

15 Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi.

16 Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake.

17 Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;

18 ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.

19 Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;

20 ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha,

21 pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2PE/1-71295bbdadf2fa4c414f5949746af942.mp3?version_id=1068—

Categories
2 PETRO

2 PETRO 2

Za aphunzitsi onyenga

1 Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m’tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.

2 Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.

3 Ndipo m’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.

4 Pakuti ngati Mulungu sanalekerereangeloadachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;

5 ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;

6 ndipo pakuisandutsa makala mizinda ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza;

7 ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja

8 (pakuti wolungamayo pokhala pakati pao. Ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zao zosaweruzika).

9 Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;

10 koma makamaka iwo akutsata za thupi, m’chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;

11 popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano.

12 Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m’kuononga kwao,

13 ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m’madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu;

14 okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;

15 posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;

16 koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwamneneriyo.

17 Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.

18 Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;

19 ndi kuwalonjeza ufulu, pamene iwo eni ali akapolo a chivundi; pakuti chimene munthu agonjetsedwa nacho, adzakhala kapolo wa chimenecho.

20 Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi YesuKhristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.

21 Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.

22 Chidawachitikira iwo monga mwa mwambi woona uja, Galu wabwerera kumasanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2PE/2-b4724893991f11df8bd263118d252f55.mp3?version_id=1068—

Categories
2 PETRO

2 PETRO 3

Kubwera kwa Ambuye

1 Okondedwa, iyi ndiye kalata yachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;

2 kuti mukumbukire mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwaatumwianu;

3 ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,

4 ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.

5 Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;

6 mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;

7 koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.

8 Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.

9 Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m’mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.

11 Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo,

12 akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m’menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.

13 Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.

14 Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.

15 Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani;

16 monganso m’makalata ake onse pokamba momwemo za izi; m’menemo muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni.

17 Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.

18 Koma kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi YesuKhristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2PE/3-4a10fa243ba5b8877a15dcc5d114703e.mp3?version_id=1068—