Categories
AEFESO

AEFESO 5

1 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;

2 ndipo yendani m’chikondi mongansoKhristuanakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

3 Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

4 kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.

5 Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

6 Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

7 Chifukwa chake musakhale olandirana nao;

8 pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,

9 pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,

10 kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani;

11 ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;

12 pakuti zochitidwa nao m’tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.

13 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika.

14 Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.

15 Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;

16 akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.

17 Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani.

18 Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

19 ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu;

20 ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

21 ndi kumverana wina ndi mnzake m’kuopa Khristu.

Zoyenera m’banja la munthu

22 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.

23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

24 Komatu monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m’zinthu zonse.

25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m’malo mwake;

26 kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;

27 kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.

28 Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;

29 pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo;

30 pakuti tili ziwalo za thupi lake.

31 Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.

32 Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo.

33 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/5-43f656087d7fb0dd053cc1e9587b607d.mp3?version_id=1068—

Categories
AEFESO

AEFESO 6

1 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino.

2 Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),

3 kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

4 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

5 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwaKhristu;

6 si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;

7 akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai;

8 podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

9 Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.

Zida za Mulungu

10 Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.

11 Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m’zakumwamba.

13 Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

14 Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;

15 ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;

16 koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.

17 Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;

18 mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,

19 ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m’kunditsegulira m’kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino,

20 chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m’menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.

Tikiko apita naye kalatayo

21 Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;

22 amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.

23 Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.

24 Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m’chosaonongeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/6-ee0a8676fc9c50e57912570a3ac98a73.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Afilipi

inalembedwa ku mpingo woyamba umene Paulo anakhazikitsa ku Ulaya. Kalatayi inalembedwa pamene mtumwiyo anali m’ndende, ndipo pamene amavutitsidwa ndi Akhristu ena amene amatsutsana ndi Paulo ndipo iye anakhumudwa chifukwa cha chiphunzitso chonyenga mu mpingo wa Filipi. Komabe m’kalatayi muli chimwemwe ndi kutsimikizika mtima kumene kukupezeka chifukwa cha chikhulupiriro chozama mwa Yesu Khristu chimene Paulo anali nacho.

Chifukwa choyambirira cholembera kalatayi chinali kuwathokoza Akhristu a ku Filipi chifukwa cha mphatso imene iwo anatumiza kuti imuthandize panthawi imene iye anali kusowa. Tsono Pauloyo anagwiritsa ntchito mwayiwu pofuna kuwatsimikizira kuti iwo alimbike mtima ndi kuchilimika ngakhale iye anali pa mavuto amene anali mavuto awonso. Iye akuwadandaulira kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa ngati wa Yesu, m’malo mokhala moyo wodzikonda ndi wodzitukumula. Iye akuwakumbutsa kuti umodzi wao ndi Khristu ndi mphatso ya chisomo cha Mulungu chimene iwo analandira mwa chikhulupiriro, osati kudzera mu kumvera miyambo ya malamulo a Chiyuda. Iye akulemba za chimwemwe ndi mtendere zimene Mulungu amapereka kwa iwo amene amakhala moyanjana ndi Khristu.

Kalatayi imadziwika bwino chifukwa cha kutsindika pa mfundo ya chimwemwe, kudzidalira, umodzi, kupirira pa moyo wa Chikhristu. Ikuonetsanso chikondi chimene Paulo anali nacho pa mpingo wa ku Filipi.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-11

Zimene Paulo anakumana nazo 1.12-26

Moyo mwa Khristu 1.27—2.18

Chikonzero cha Paulo pa Timoteo ndi Epafrodito 2.19-30

Machenjezo pa adani komanso zoopsa 3.1—4.9

Paulo ndi anzake a ku Filipi 4.10-20

Mau omaliza 4.21-23

Categories
AFILIPI

AFILIPI 1

1 Paulo ndi Timoteo, akapolo a YesuKhristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang’anira ndi atumiki:

2 Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chikondi cha Paulo cha pa Afilipi. Zipatso za undende wake

3 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;

4 nthawi zonse m’pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,

5 chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

6 pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

7 monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m’mtima mwanga, kuti inu m’zomangira zanga, ndipo m’chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m’chisomo.

8 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m’phamphu la mwa Khristu Yesu.

9 Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m’chidziwitso, ndi kuzindikira konse;

10 kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;

11 odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

12 Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;

13 kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m’bwalo lonse la alonda, ndi kwa ena onse;

14 ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.

15 Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndeu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima;

16 ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino;

17 koma ena alalikira Khristu mochokera m’chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m’zomangira zanga.

18 Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m’choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m’menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

19 Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;

20 monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m’thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.

21 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula.

22 Koma ngati kukhala ndi moyo m’thupi ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha.

23 Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;

24 koma kukhalabe m’thupi ndiko kufunika koposa, chifukwa cha inu.

25 Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu;

26 kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke mu Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.

Akhristu alimbike, ayanjane, adzichepetse, atsate kuyeramtima

27 Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

28 osaopa adani m’kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

29 kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye,

30 ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/1-dd656493ec3aca52a10af61b5e35bb07.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI 2

1 Ngati tsono muli chitonthozo mwaKhristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,

2 kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;

3 musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

4 munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

5 Mukhale nao mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu,

6 ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu,

7 koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu;

8 ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

9 Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,

10 kuti m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,

11 ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.

12 Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;

13 pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.

14 Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani,

15 kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m’dziko lapansi,

16 akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m’tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.

17 Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

18 momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

Paulo atamula Timoteo ndi Epafrodito amithenga ake a kwa Afilipi

19 Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.

20 Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona.

21 Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Khristu.

22 Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.

23 Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posachedwa m’mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani;

24 koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.

25 Koma ndinayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiyemtumwiwanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;

26 popeza anali wolakalaka inu nonse, navutika mtima chifukwa mudamva kuti anadwala.

27 Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.

28 Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso chindichepere chisoni.

29 Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa;

30 pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/2-e415894e19e698ab75291549413459ec.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI 3

Awachenjeza asatsate atumwi onyenga. Aonetsere zipatso za Mzimu

1 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.

2 Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula;

3 pakuti ife ndifemdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwaKhristuYesu, osakhulupirira m’thupi;

4 ndingakhale inenso ndili nako kakukhulupirira m’thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m’thupi, makamaka ineyu;

5 wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo,Mfarisi;

6 monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m’lamulo wokhala wosalakwa ine.

7 Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu.

8 Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,

9 ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;

10 kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;

11 ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.

12 Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.

13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo,

14 ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

15 Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu;

16 chokhachi, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.

17 Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang’anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.

18 Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;

19 chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m’manyazi ao, amene alingirira za padziko.

20 Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;

21 amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/3-6660fa076a251e637ea74e6e52140887.mp3?version_id=1068—

Categories
AFILIPI

AFILIPI 4

1 Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.

2 Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.

3 Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m’goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m’buku la Moyo.

4 Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

6 Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

7 Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwaKhristuYesu.

8 Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

9 Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.

Paulo ayamika Afilipi popeza adamtumiza zomthandizira

10 Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.

11 Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.

12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

13 Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

14 Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m’chisautso changa.

15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m’chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane naneMpingoumodzi wonse m’makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;

16 pakuti mu Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.

17 Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.

18 Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.

19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi,Amen.

21 Perekani moni kwa woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine akupatsani moni.

22 Oyera mtima onse akupatsani inu moni, koma makamaka iwo a banja laKaisara.

23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/4-407964e8d6b92417e3642b890fa40bbe.mp3?version_id=1068—

Categories
AKOLOSE

AKOLOSE Mau Oyamba

Mau Oyamba

Kolose unali mzinda wina wa ku Asiya, kuvuma kwa Efeso. Paulo si amene adayambitsa mpingo kumeneko, komabe amausamala, poti adatuma anthu ake ku Koloseko kuchokera ku Efeso. Paulo anamva kuti aphunzitsi ena onyenga akusokoneza mpingo umenewo; iwo akuti ofuna kumdziwa Mulungu ndi kupulumuka ayenera kupembedza mafumu ndi akuluakulu akumwamba, ayeneranso kuumbalidwa ndi kutsata miyambo ndi malamulo ena okhudza zakudya ndi zina zotere.

Tsono Paulo awalembera kalatayi kuti atsutse zabodzazi pofotokoza uthenga weniweni wa Chikhristu, makamaka izi zakuti Yesu Khristu yekha ali ndi mphamvu zopulumutsira anthu, koma zimene amalalika aphunzitsi aja zimangosokoneza anthu ndi kuwalekanitsa ndi Khristu. Mulungutu adalenga zinthu zonse kudzera mwa Khristu ndipo amabwezera zonsezo kwa Iye mwini wake kudzera mwa Khristu yemweyo. Anthu a padziko lonse lapansi angayembekeze kupulumuka pokhapo atakhala mwa Khristu ndi kumaphatikana naye. Zotsatira zake nzakuti iwowo aongolere moyo wao potsata zomwe iye Paulo akuwaphunzitsazi.

Potuma Titiko ku Filipi kuti akapereke kalatayi, Paulo atumanso mnyamata wina womperekeza, dzina lake Onesimo; ameneyu ndiye kapolo uja amene nkhani yake ipezeka m’kalata yomwe Paulo adalembera Filemoni.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-8

Za makhalidwe ndi ntchito za Khristu 1.9—2.19

Za moyo watsopano wokhala mwa Khristu 2.20—4.6

Mau otsiriza 4.7-18

Categories
AKOLOSE

AKOLOSE 1

1 Paulo,mtumwiwaKhristuYesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,

2 kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a mu Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.

Za chikhulupiriro ndi chikondano cha a ku Kolose. Paulo awapempherera. Yesu Khristu ali maonekedwe a Mulungu wolenga zonse, mutu wa Mpingo

3 Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu YesuKhristundi kupempherera inu nthawi zonse,

4 popeza tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu, ndi chikondi muli nacho kwa oyera mtima onse;

5 chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m’mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,

6 umene udafikira kwa inu; monganso m’dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu, kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira chisomo cha Mulungu m’choonadi;

7 monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiye mtumiki wokhulupirika wa Khristu chifukwa cha ife;

8 amenenso anatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu.

9 Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,

10 kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu;

11 olimbikitsidwa m’chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,

12 ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m’kuunika;

13 amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;

14 amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m’kukhululukidwa kwa zochimwa zathu;

15 amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse;

16 pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.

17 Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.

18 Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.

19 Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire,

20 mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za mu Mwamba.

21 Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m’chifuwa chanu m’ntchito zoipazo,

22 koma tsopano anakuyanjanitsani m’thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake;

23 ngatitu, mukhalabe m’chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.

Machitachita a Paulo mu utumiki wake

24 Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m’thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;

25 amene ndinakhala mtumiki wake, monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakuchitira inu, wakukwaniritsa mau a Mulungu,

26 ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake,

27 kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati paamitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;

28 amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;

29 kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/COL/1-af9ee1f2352534de984b6d2c0c2545e8.mp3?version_id=1068—

Categories
AKOLOSE

AKOLOSE 2

1 Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m’thupi;

2 kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m’chikondi, kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu, ndiyeKhristu,

3 amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.

Asatsate ziphunzitso zonyenga

4 Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.

5 Pakuti ndingakhale ndili kwina m’thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.

6 Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye,

7 ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.

8 Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;

9 pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m’thupi,

10 ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

11 amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m’mavulidwe a thupi, mumdulidwewa Khristu;

12 popeza munaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m’chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.

13 Ndipo inu, pokhala akufa m’zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m’mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;

14 adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m’zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;

15 atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.

16 Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m’chakudya, kapena chakumwa, kapena m’kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena laSabata;

17 ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Khristu.

18 Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwaangelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,

19 kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.

20 Ngati munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji kuzoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m’dziko lapansi,

21 usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,

22 (ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?

23 Zimene zili naotu manenedwe a nzeru m’kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/COL/2-200496f5d3547476493b061eaa284529.mp3?version_id=1068—