Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 6

Kudzikana kwa Paulo mu utumiki wake

1 Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,

2 (pakuti anena,

M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,

ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza.

Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);

3 osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe;

4 koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m’kupirira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja,

5 m’mikwingwirima, m’ndende, m’maphokoso, m’mavutitso, m’madikiro, m’masalo a chakudya;

6 m’mayeredwe, m’chidziwitso, m’chilekerero, m’kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m’chikondi chosanyenga;

7 m’mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,

8 mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;

9 monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;

10 monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Awadandaulira akhale oyera mtima

11 M’kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.

12 Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu.

13 Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.

14 Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?

15 NdipoKhristuavomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

16 Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

17 Chifukwa chake,

Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye,

Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka;

ndipo Ine ndidzalandira inu,

18 ndipo ndidzakhala kwa inu Atate,

ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi,

anena Ambuye Wamphamvuyonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/6-2f305d5fa545ff181abdc72c9d1cce3c.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 7

Paulo akondwera pa kudza kwa Tito, ndi pa zipatso za kalata yake woyamba

1 Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.

2 Tipatseni malo; sitinamchitire munthu chosalungama, sitinaipse munthu, sitinachenjerere munthu.

3 Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.

4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m’chisautso chathu chonse.

5 Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m’katimo mantha.

6 Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;

7 koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene anatonthozedwa nacho mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa.

8 Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata ija, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata ija inakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.

9 Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m’kanthu kalikonse.

10 Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.

11 Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M’zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m’menemo.

12 Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.

13 Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m’chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.

14 Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m’choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.

15 Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.

16 Ndikondwera kuti m’zonse ndilimbika mtima za inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/7-2d8cf32422bf33858840569909690cc8.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 8

Chipereko cha kwa Akhristu aumphawi a ku Yerusalemu

1 Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwaMipingoya ku Masedoniya,

2 kuti m’chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.

3 Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yao,

4 anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;

5 ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.

6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.

7 Koma monga muchulukira m’zonse, m’chikhulupiriro, ndi m’mau, ndi m’chidziwitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m’chisomo ichi.

8 Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.

9 Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu YesuKhristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.

10 Ndipo m’menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.

11 Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m’chimene muli nacho.

12 Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.

13 Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;

14 koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu.

15 Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinamtsalire; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichinamsowe.

16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

17 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake.

18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli mu Mipingo yonse;

19 ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m’chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;

20 ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira;

21 pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

22 Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m’zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu.

23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.

24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/8-6d21823f6abb21f2ae46439c7efd2c04.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 9

1 Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;

2 pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kutiAkayaanakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.

3 Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m’menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;

4 kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m’kulimbika kumene.

5 Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.

6 Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.

7 Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

8 Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m’zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;

9 monga kwalembedwa,

Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka;

chilungamo chake chikhale kunthawi yonse.

10 Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;

11 polemeretsedwa inu m’zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.

12 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;

13 popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino waKhristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;

14 ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.

15 Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/9-5838a978a1e6dc31be2fcc956b07afcf.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 10

Ulamuliro wa Paulo mtumwi

1 Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere waKhristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;

2 koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.

3 Pakuti pakuyendayenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi,

4 (pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);

5 ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;

6 ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.

7 Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.

8 Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;

9 kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa makalatawo.

10 Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.

11 Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa makalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m’machitidwe pokhala tili pomwepo.

12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.

13 Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.

14 Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikire kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Khristu:

15 osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,

16 kukalalikira Uthenga Wabwino m’tsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale.

17 Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;

18 pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/10-8cece938ecbeb348f6b313093016baac.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 11

Za atumwi onyenga

1 Bwenzi mutandilola pang’ono ndi chopusacho! Komanso mundilole.

2 Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwaKhristu.

3 Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.

4 Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.

5 Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewere konse ndiatumwioposatu.

6 Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m’manenedwe, koma sinditero m’chidziwitso, koma m’zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.

7 Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?

8 Ndinalanda zaMipingoina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu;

9 ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m’zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.

10 Choonadi cha Khristu chili mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali zaAkaya.

11 Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.

12 Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m’mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.

13 Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Khristu.

14 Ndipo kulibe kudabwa; pakutiSatanayemwe adzionetsa ngatimngelowa kuunika.

15 Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao.

Kumva zowawa kwa Paulo chifukwa cha Uthenga Wabwino

16 Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang’ono.

17 Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m’kulimbika kumene kwa kudzitamandira.

18 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.

19 Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.

20 Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.

21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m’mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.

22 Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisraele? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.

23 Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m’zivutinso mochulukira, m’ndende mochulukira, m’mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.

24 Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.

25 Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m’kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

26 paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwaamitundu, moopsa m’mzinda, moopsa m’chipululu, moopsa m’nyanja, moopsa mwa abale onyenga;

27 m’chivutitso ndi m’cholemetsa, m’madikiro kawirikawiri, m’njala ndi ludzu, m’masalo a chakudya kawirikawiri, m’chisanu ndi umaliseche.

28 Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse.

29 Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?

30 Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga.

31 Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.

32 Mu Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mzinda wa Adamasiko kuti andigwire ine;

33 ndipo mwa zenera, mudengu, ananditsitsa pakhoma, ndipo ndinapulumuka m’manja mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/11-a3d287abbab31e12cc6d042b243ecbe5.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 12

Masomphenya a Paulo ndi munga m’thupi lake

1 Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye.

2 Ndidziwa munthu wa mwaKhristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m’thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.

3 Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m’thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu),

4 kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.

5 Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; koma chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m’zofooka zanga.

6 Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.

7 Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo waSatanakuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.

8 Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.

9 Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

10 Chifukwa chake ndisangalala m’mafooko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’mazunzo, m’zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.

Kusadzikonda kwa Paulo

11 Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndiatumwioposatu m’kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.

12 Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m’chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.

13 Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndiMipingoyotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi.

14 Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.

15 Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?

16 Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wochenjera ine, ndinakugwirani ndi chinyengo.

17 Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakuchenjererani naye kodi?

18 Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?

Malangizo otsiriza, zolawirana

19 Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu.

20 Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;

21 kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/12-344eb5cb7551bd612ac179b066d89567.mp3?version_id=1068—

Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 13

1 Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.

2 Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;

3 popeza mufuna chitsimikizo, chaKhristuwakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;

4 pakuti anapachikidwa mu ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

5 Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa.

6 Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitili osatsimikizidwa.

7 Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.

8 Pakuti sitikhoza kanthu pokana choonadi, koma povomereza choonadi.

9 Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu.

10 Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.

11 Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.

12 Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.

13 Oyera mtima onse akupatsani moni.

14 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/13-cafd3d8a2218b22ceeac103769253bb1.mp3?version_id=1068—

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba

Pamene uthenga wabwino wonena za Yesu unayamba kulalikidwa ndi kulandiridwa pakati pa anthu amene sanali Ayuda, funso lalikulu limene limafunsidwa linali lakuti:

Kodi ndikoyenera kuti munthu atsatire Malamulo a Mose ngati akufuna kukhala Mkhristu?

Paulo ananena kuti izi sizinali zoyenera. Iye anatinso chofunika pa moyo wotsatira Khristu ndi ndicho chakuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhulupirira Khristu basi. Komabe pakati pa mipingo ya ku Galatiya, limene linali dera la ku Asiya, panali anthu amene anabwera ndi kumasutsana ndi Paulo ponena kuti munthu ayenera kutsata Malamulo a Mose ngati akufuna alungamitsidwe ndi Mulungu.

Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Agalatiya

inalembedwa pofuna kukonza chiphunzitso cholakwikachi chimene ena anabweretsa ndi kupotoza nacho anthu anzao. Paulo anayamba pa kuteteza udindo wake monga mtumwi wa Yesu Khristu. Iye anatsindika mfundo yakuti maitanidwe ake kukhala mtumwi anachokera kwa Mulungu, osati kwa munthu, ndiponso kuti utumiki wake unali wa kwa anthu sanali Ayuda. Kenaka akufotokoza kuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhapokha pamene akhulupirira. Mu mitu yomalizira, Paulo akutionetsa kuti khalidwe labwino la Chikhristu limachokera ku chikondi chimene chimapezeka pamene munthu wakhulupirira Yesu.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-10

Ulamuliro wa Paulo pokhala mtumwi 1.11—2.21

Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu 3.1—4.31

Ufulu ndi udindo wa Mkhristu 5.1—6.10

Mau omaliza 6.11-18

Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 1

1 Paulo,mtumwi(wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa YesuKhristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),

2 ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwaMipingoya ku Galatiya:

3 Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,

4 amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m’nyengo ya pansi pano ino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;

5 yemweyo akhale nao ulemerero kunthawi za nthawi.Amen.

Kupatuka kwa Agalatiya. Utumiki wa Paulo uchokera kwa Mulungu

6 Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m’chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina;

7 umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.

8 Koma ngakhale ife, kapenamngelowochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.

9 Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.

10 Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.

11 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.

12 Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa vumbulutso la Yesu Khristu.

13 Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,

14 ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.

15 Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,

16 kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwaamitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi:

17 kapena kukwera kunka kuYerusalemusindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.

18 Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.

19 Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

20 Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.

21 Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.

22 Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu;

23 koma analinkumva kokha, kuti, Iye wakutilondalonda ife kale, tsopano alalikira chikhulupirirocho adachipasula kale;

24 ndipo analemekeza Mulungu mwa ine.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/1-2989d8251c665c21feacbd381510f64b.mp3?version_id=1068—