Achenjeza osamvera kuti adzalangidwa
1 Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.
2 Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m’njira mosati mwabwino, kutsata maganizo aoao;
3 anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m’minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;
4 amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m’malo am’tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m’mbale zao;
5 amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m’mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.
6 Taonani, chalembedwa pamaso panga; sindidzakhala chete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa chifuwa chao,
7 zoipa zanuzanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandichitira mwano pazitunda; chifukwa chake Ine ndidzayesa ntchito yao yakale ilowe pa chifuwa chao.
8 Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m’tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m’menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.
9 Ndipo ndidzatulutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira cholowa chao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi chigwa cha Akori chidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.
11 Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosakaniza;
12 ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m’maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwere nacho.
13 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;
14 taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.
15 Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;
16 chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m’dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m’dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.
Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano
17 Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.
18 Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilengaYerusalemuwosangalala, ndi anthu ake okondwa.
19 Ndipo ndidzasangalala mu Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.
20 Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.
21 Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake.
22 Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.
23 Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbeu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa ao adzakhala pamodzi ndi iwo.
24 Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
25 Mmbulu ndimwanawankhosazidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng’ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m’phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/65-317aa8a113c4878d9e93f71a6e1f42fd.mp3?version_id=1068—