Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 12

1 Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?

2 Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m’kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.

3 Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.

4 Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.

5 Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m’dziko lamtendere, udzachita chiyani m’kudzikuza kwa Yordani?

6 Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakufuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino.

Dziko lipasuka. Aneneratu za olipasula

7 Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m’dzanja la adani.

8 Cholowa changa chandisandukira mkango wa m’nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda.

9 Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m’thengo, mudze nazo zidye.

10 Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.

11 Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.

12 Akufunkha afika pa mapiri oti see m’chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.

13 Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

14 Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m’dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.

15 Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake.

16 Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira paliBaala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.

17 Koma ngati sakumva, ndidzazula mtundu umene wa anthu, kuuzula ndi kuuononga, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/12-a5de94c9e171e6ad6eab1ad83382b277.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *