Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 21

Kufunsira kwa Zedekiya, kuyankha kwa Yeremiya

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,

2 Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.

3 Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya:

4 Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m’manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.

5 Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m’mkwiyo, ndi m’kupsa mtima, ndi mu ukali waukulu.

6 Ndipo ndidzakantha okhalamo m’mzinda uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi mliri waukulu.

7 Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m’mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m’dzanja la adani ao, ndi m’dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.

8 Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa.

9 Iye amene akhala m’mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.

10 Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.

Aneneratu motsutsa mbumba yachifumu ya Yuda

11 Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:

12 Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m’mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m’dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.

13 Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m’chigwa, ndi pa thanthwe la m’chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m’zokhalamo zathu?

14 Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m’nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/21-05eda18790608ead0517e8b517a6043d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *