Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 29

Kalata ya Yeremiya wolembera kwa Ayuda otengedwa kunka ku Babiloni

1 Amenewa ndi mau a kalata ija anatumiza Yeremiya mneneri kuchokera kuYerusalemukunka kwa akulu otsala a m’nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadinezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babiloni;

2 anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,

3 anatumiza kalatayo m’dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,

4 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am’nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni:

5 Mangani nyumba, khalani m’menemo; limani minda, idyani zipatso zake;

6 tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.

7 Nimufune mtendere wa mzinda umene ndinakutengerani am’nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.

8 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

9 Pakuti anenera kwa inu zonama m’dzina langa; sindinatume iwo, ati Yehova.

10 Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang’anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.

11 Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.

12 Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.

13 Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

14 Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.

15 Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri mu Babiloni.

16 Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m’mzinda uno, abale anu amene sanatulukire pamodzi ndi inu kundende;

17 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.

18 Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m’maufumu onse a dziko lapansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;

19 chifukwa sanamvere mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.

20 Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m’ndende, amene ndachotsa mu Yerusalemu kunka ku Babiloni.

21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m’dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu;

22 ndipo am’nsinga onse a Yuda amene ali mu Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaotcha m’moto;

23 chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m’dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.

24 Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza makalata m’dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti,

26 Yehova anakuyesa iwe wansembe m’malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m’nyumba ya Yehova, oyang’anira munthu yense wamisala, wodziyesamneneri, kuti umuike iye m’zigologolo ndi m’goli.

27 Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,

28 popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m’menemo; limani minda, idyani zipatso zao?

29 Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m’makutu a Yeremiya mneneri.

30 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti,

31 Uwatumizire mau am’nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Chifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtume, ndipo anakukhulupiritsani zonama;

32 chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/29-cea3dcb5f5a7a4399bde9f4c85037465.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *