Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 32

Yeremiya atsekeredwa m’kaidi nagula munda wa Hanamele

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara.

2 Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangiraYerusalemumisasa; ndipo Yeremiyamnenerianatsekeredwa m’bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.

3 Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m’dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,

4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m’dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m’dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;

5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?

6 Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

7 Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.

8 Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m’bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m’dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.

9 Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri asiliva.

10 Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m’miyeso.

11 Ndipo ndinatenga kalata yogulira, yina yosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi yina yovundukuka;

12 ndipo ndinapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata yogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m’bwalo la kaidi.

13 Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti,

14 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga makalata awa, kalata yogulira, yosindikizidwa, ndi kalata yovundukuka, nuwaike m’mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.

15 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yampesa idzagulidwanso m’dziko muno.

Pemphero la Yeremiya

16 Ndipo nditapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,

17 Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;

18 amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m’chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;

19 wamkulu mu upo, wamphamvu m’ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;

20 amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m’dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, mu Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;

21 ndipo munatulutsa anthu anu Israele m’dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;

22 ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi;

23 ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m’chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;

24 taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m’dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.

25 Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mzinda waperekedwa m’manja a Ababiloni.

Mulungu anenetsa kuti Aisraele adzalangidwa, nalonjeza kuwalanditsanso

26 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,

27 Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondikanika Ine?

28 Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mzindawu m’dzanja la Ababiloni, m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda,

29 ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukiziraBaala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.

30 Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.

31 Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;

32 chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu.

33 Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m’mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.

34 Koma anaika zonyansa zao m’nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.

35 Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m’chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa chaMoleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m’mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.

36 Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mzinda umene, munena inu, waperekedwa m’dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri:

37 Taonani, ndidzawasokolotsa m’maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m’kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,

38 ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;

39 ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;

40 ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m’mitima yao, kuti asandichokere.

41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m’dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

42 Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa choipa chonsechi, chomwecho ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonjeza.

43 Ndipo minda idzagulidwa m’dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m’dzanja la Ababiloni.

44 Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m’dziko la Benjamini, ndi m’malo ozungulira Yerusalemu, ndi m’mizinda ya Yuda, ndi m’mizinda ya kumtunda, ndi m’mizinda ya kuchidikha, ndi m’mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/32-da42984124ea1c020c25599dfc686e82.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *